الشعراء
Ash-Shu'araa
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
طسٓمٓ
Open ayah 26:1Tâ-Sîn-Mîm.
تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ
Open ayah 26:2Izi ndi Ayah (ndime) za buku (la Qur’an) lofotokoza chilichonse (chofunika m’chipembedzo).
لَعَلَّكَ بَٰخِعٞ نَّفۡسَكَ أَلَّا يَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:3Mwina iwe (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) udziononga wekha (ndi madandaulo) chifukwa chakuti (iwo) sadakhale okhulupirira.
إِن نَّشَأۡ نُنَزِّلۡ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ ءَايَةٗ فَظَلَّتۡ أَعۡنَٰقُهُمۡ لَهَا خَٰضِعِينَ
Open ayah 26:4Tikadafuna, tikadawatsitsira chizizwa kuchokera kumwamba; kotero kuti makosi awo akadadzichepetsa ndi chizizwacho, (sakadatha kucheukira kwina koma sitifuna kukakamiza anthu kuti akhale Asilamu).[1]
- Mtumiki Muhammad (s.a.w) adali kuwawidwa mtima kwambiri poona kuti anthu sakuvomereza uthenga wachoonadi umene iye adadza nawo, ndipo adali kuwamvera chisoni kwambiri. Choncho Allah adamtonthoza pomuuza kuti: “Usadziphe wekha chifukwa chokhala ndi maganizo owamvera chisoni.” Allah akadafuna kuwaongola mowakakamiza akadatha kutero; koma sadafune.
وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن ذِكۡرٖ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ مُحۡدَثٍ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهُ مُعۡرِضِينَ
Open ayah 26:5Ndipo palibe pamene chikuwadzera chivumbulutso chatsopano chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri koma amazipatula ku icho (chivumbulutso).
فَقَدۡ كَذَّبُواْ فَسَيَأۡتِيهِمۡ أَنۢبَٰٓؤُاْ مَا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Open ayah 26:6Ndithu atsutsa; choncho posachedwapa ziwadzera nkhani zomwe adali kuzichitira chipongwe.
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ كَمۡ أَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجٖ كَرِيمٍ
Open ayah 26:7Kodi sadaone nthaka? Ndimmera ungati taumeretsa m’menemo kuchokera mu mtundu ulionse, wokongola?
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:8Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro (zosonyeza mphamvu za Allah). Koma ambiri a iwo sali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:9Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
وَإِذۡ نَادَىٰ رَبُّكَ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱئۡتِ ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Open ayah 26:10Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako adaitana (m’neneri) Mûsa; adamuuza: “Pita kwa anthu ochita zoipa.”
قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَۚ أَلَا يَتَّقُونَ
Open ayah 26:11Anthu a Farawo; (auze): “Kodi sawopa (Allah)?”
قَالَ رَبِّ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يُكَذِّبُونِ
Open ayah 26:12(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ine ndikuopa kuti anganditsutse.
وَيَضِيقُ صَدۡرِي وَلَا يَنطَلِقُ لِسَانِي فَأَرۡسِلۡ إِلَىٰ هَٰرُونَ
Open ayah 26:13Ndipo chingabanike chifuwa changa (ndi maganizo, chifukwa chakunditsutsa kwawo); ndiponso lirime langa siliyankhula momveka bwino. Choncho tumizaninso uthengawu kwa Harun (kuti tikhale awiri ndipo azikandithangata pantchito yangayi).
وَلَهُمۡ عَلَيَّ ذَنۢبٞ فَأَخَافُ أَن يَقۡتُلُونِ
Open ayah 26:14Ndipo iwowo ndili nawo mlandu ndipo ndikuopa kuti angandiphe (pobwezera chimene ndidawalakwira powaphera munthu wawo).
قَالَ كَلَّاۖ فَٱذۡهَبَا بِـَٔايَٰتِنَآۖ إِنَّا مَعَكُم مُّسۡتَمِعُونَ
Open ayah 26:15(Allah) adati: “Iyayi! Pitani pamodzi ndi zozizwa Zathu; ndithu Ife tikakhala nanu limodzi (pokuthangatani) uku tikumvetsera (zimene azikanena).”
فَأۡتِيَا فِرۡعَوۡنَ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:16“Choncho mpitireni Farawo, ndipo kamuuzeni kuti: “Ife ndi atumiki a Mbuye wa zolengedwa zonse.”
أَنۡ أَرۡسِلۡ مَعَنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Open ayah 26:17“(Tatumidwa) kuti uwapereke kwa ife ana a Israyeli (kuti tinke nawo ku Sham).”
قَالَ أَلَمۡ نُرَبِّكَ فِينَا وَلِيدٗا وَلَبِثۡتَ فِينَا مِنۡ عُمُرِكَ سِنِينَ
Open ayah 26:18(Farawo) adati (kwa Mûsa): “Kodi sitidakulere kwathu uli mwana, ndi kukhala nafe pa moyo wako zaka zambiri?”
وَفَعَلۡتَ فَعۡلَتَكَ ٱلَّتِي فَعَلۡتَ وَأَنتَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Open ayah 26:19“Ndipo udachita chochita chako chimene udachichita, ndipo iwe ndiwe mmodzi wa osathokoza!”
قَالَ فَعَلۡتُهَآ إِذٗا وَأَنَا۠ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ
Open ayah 26:20(Mûsa) adati: “Ndidachita zimenezo pomwe ine ndidali mmodzi wa osazindikira zinthu.”
فَفَرَرۡتُ مِنكُمۡ لَمَّا خِفۡتُكُمۡ فَوَهَبَ لِي رَبِّي حُكۡمٗا وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:21“Choncho ndidakuthawani pomwe ndidakuopani; tsono Mbuye wanga wandipatsa nzeru zoweruzira (zinthu), ndi kundisankha kukhala mmodzi wa atumiki.”
وَتِلۡكَ نِعۡمَةٞ تَمُنُّهَا عَلَيَّ أَنۡ عَبَّدتَّ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Open ayah 26:22“Ndipo kodi umenewu ndimtendere wonditonzera pomwe mudawaika muukapolo ana a Israyeli!”
قَالَ فِرۡعَوۡنُ وَمَا رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:23Farawo adati: “Kodi ndani Mbuye wa zolengedwayo?”
قَالَ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ
Open ayah 26:24(Mûsa) adati: “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo. (Amachita chilichonse m’menemo mmene wafunira; kupereka moyo ndi imfa).”
قَالَ لِمَنۡ حَوۡلَهُۥٓ أَلَا تَسۡتَمِعُونَ
Open ayah 26:25(Farawo) adauza omwe adali m’mphepete mwake (mwachipongwe): “Kodi simukumva (mawu achibwanawa)?”
قَالَ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 26:26(Mûsa adapitiriza kunena) adati: “Allah ndi Mbuye wanu komanso Mbuye wamakolo anu oyamba.”
قَالَ إِنَّ رَسُولَكُمُ ٱلَّذِيٓ أُرۡسِلَ إِلَيۡكُمۡ لَمَجۡنُونٞ
Open ayah 26:27(Farawo) adati (kwa anthu ake pofuna kuwakwiitsa): “Ndithu Mtumiki wanu amene watumidwa kwa inu, ngwamisala.”
قَالَ رَبُّ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُمۡ تَعۡقِلُونَ
Open ayah 26:28(Mûsa) adati: “Mbuye wakuvuma ndi kuzambwe, ndi zomwe ziri pakati pake ngati mumazindikira (zinthu, muzindikira izi).”
قَالَ لَئِنِ ٱتَّخَذۡتَ إِلَٰهًا غَيۡرِي لَأَجۡعَلَنَّكَ مِنَ ٱلۡمَسۡجُونِينَ
Open ayah 26:29(Farawo) adati: “Ngati udzipangira mulungu wina kusiya ine, ndikuchita kukhala mmodzi wa omangidwa kundende.”
قَالَ أَوَلَوۡ جِئۡتُكَ بِشَيۡءٖ مُّبِينٖ
Open ayah 26:30(Mûsa) adati: “Kodi ngakhale nditakubweretsera chinthu choonekera poyera (chosonyeza kuti zimene ndikunenazi ndizoona ndatumidwa ndi Allah)?”
قَالَ فَأۡتِ بِهِۦٓ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Open ayah 26:31(Farawo) adati: “Chibweretse, ngati uli mwa onena zoona.”
فَأَلۡقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعۡبَانٞ مُّبِينٞ
Open ayah 26:32Ndipo (Mûsa) adaponya (pansi) ndodo yake, mwadzidzidzi idasanduka njoka yopenyeka.
وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِيَ بَيۡضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ
Open ayah 26:33Ndipo adatulutsa dzanja lake; pompo lidali loyera (kwambiri) kwa (onse) openya.
قَالَ لِلۡمَلَإِ حَوۡلَهُۥٓ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمٞ
Open ayah 26:34(Farawo) adauza akuluakulu omwe adali m’mphepete mwake: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa kwambiri.”
يُرِيدُ أَن يُخۡرِجَكُم مِّنۡ أَرۡضِكُم بِسِحۡرِهِۦ فَمَاذَا تَأۡمُرُونَ
Open ayah 26:35“Akufuna kukutulutsani m’dziko lanu ndi matsenga ake; kodi nanga mukuti chiyani?”[1]
- Farawo adasimidwa, adatha nzeru zedi ndi mawu amene adali kutuluka m’kamwa mwa Musa kotero kuti adangoti kakasi, kusowa chonena, nayamba kuwafunsa nzeru ndi malangizo anthu ake pomwe iye ankadzitcha kuti ndi mulungu wodziwa zonse, wamphamvu zoposa.
قَالُوٓاْ أَرۡجِهۡ وَأَخَاهُ وَٱبۡعَثۡ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ
Open ayah 26:36(Anthu) adati (kwa Farawo): “Mpatse nthawi ndi m’bale wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) m’mizinda yonse osonkhanitsa anthu.”
يَأۡتُوكَ بِكُلِّ سَحَّارٍ عَلِيمٖ
Open ayah 26:37“Ndipo akubweretsera amatsenga onse odziwa kwabasi (kotero kuti adzampambana Mûsa).”
فَجُمِعَ ٱلسَّحَرَةُ لِمِيقَٰتِ يَوۡمٖ مَّعۡلُومٖ
Open ayah 26:38Choncho amatsenga adasonkhanitsidwa mu nthawi ya tsiku lodziwika.
وَقِيلَ لِلنَّاسِ هَلۡ أَنتُم مُّجۡتَمِعُونَ
Open ayah 26:39Ndipo anthu adauzidwa: “Kodi inu musonkhana? (Choncho, sonkhanani).”
لَعَلَّنَا نَتَّبِعُ ٱلسَّحَرَةَ إِن كَانُواْ هُمُ ٱلۡغَٰلِبِينَ
Open ayah 26:40“Mwina tingawatsatire amatsenga ngati iwo ndiamene apambane.”
فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالُواْ لِفِرۡعَوۡنَ أَئِنَّ لَنَا لَأَجۡرًا إِن كُنَّا نَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبِينَ
Open ayah 26:41Ndipo pamene amatsenga adadza, adati kwa Farawo: “Kodi tidzakhala ndi mphoto ngati ife ndife tipambane?”
قَالَ نَعَمۡ وَإِنَّكُمۡ إِذٗا لَّمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ
Open ayah 26:42(Farawo) adati: “Inde, (ndipo kuonjezera apo) ndithu inu mudzakhala mwa amene amakhala pafupi (ndi ine, monga nduna zanga).”
قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلۡقُواْ مَآ أَنتُم مُّلۡقُونَ
Open ayah 26:43Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zimene mufuna kuponya (zosonyeza kuya kwa matsenga anu).”
فَأَلۡقَوۡاْ حِبَالَهُمۡ وَعِصِيَّهُمۡ وَقَالُواْ بِعِزَّةِ فِرۡعَوۡنَ إِنَّا لَنَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبُونَ
Open ayah 26:44Choncho adaponya zingwe zawo ndi ndodo zawo, ndipo adati: “Kupyolera mu mphamvu za Farawo, ndithu ife ndife opambana.”
فَأَلۡقَىٰ مُوسَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ تَلۡقَفُ مَا يَأۡفِكُونَ
Open ayah 26:45Kenako Mûsa adaponya ndodo yake; mwadzidzidzi iyo idameza zabodza zomwe iwo adakonza.
فَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ
Open ayah 26:46Pamenepo amatsenga adadzigwetsa pansi molambira.
قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:47Adati: “Tamkhulupirira Mbuye wa zolengedwa.”
رَبِّ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ
Open ayah 26:48“Mbuye wa Mûsa ndi Harun.”
قَالَ ءَامَنتُمۡ لَهُۥ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِي عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحۡرَ فَلَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَۚ لَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفٖ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمۡ أَجۡمَعِينَ
Open ayah 26:49(Farawo) adati: “Ha! Mwamkhulupirira chotani ndisanakulolezeni? Ndithu iyeyu ndimkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Choncho posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni) ndithu ndidula manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa (podula mkono wakumanja ndi mwendo wakumanzere; kapena kudula mkono wakumanzere ndi mwendo wakumanja), ndipo kenako ndikupachikani nonsenu.”
قَالُواْ لَا ضَيۡرَۖ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ
Open ayah 26:50(Amatsenga) adati: “Palibe vuto, ndithu ife (tonse) tibwerera kwa Mbuye wathu.”
إِنَّا نَطۡمَعُ أَن يَغۡفِرَ لَنَا رَبُّنَا خَطَٰيَٰنَآ أَن كُنَّآ أَوَّلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:51“Ndithu ife tikuyembekezera kuti Mbuye wathu atikhululukire zolakwa zathu; pokhala oyamba mwa okhulupirira.”
۞وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَسۡرِ بِعِبَادِيٓ إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ
Open ayah 26:52Ndipo tidamvumbulutsira Mûsa (kuti): “Pita ndi anthu anga m’nthawi yausiku (musamuke m’dziko la Iguputo); ndithu inu mutsatidwa.”
فَأَرۡسَلَ فِرۡعَوۡنُ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ
Open ayah 26:53Choncho Farawo adatuma (owatuma) kuti asonkhanitse anthu m’mizinda (kuti aletse ana a Israyeli kutuluka).
إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَشِرۡذِمَةٞ قَلِيلُونَ
Open ayah 26:54(Adawauza otumidwa aja kuti auze anthu kuti): “Ndithu awa (ana a Israyeli) ndikagulu kochepa.
وَإِنَّهُمۡ لَنَا لَغَآئِظُونَ
Open ayah 26:55Ndipo ndithu iwo akutikwiitsa.
وَإِنَّا لَجَمِيعٌ حَٰذِرُونَ
Open ayah 26:56Koma ndithu ife tonse (ndife ochuluka komabe ngakhale zili choncho) tikuwaopa.”
فَأَخۡرَجۡنَٰهُم مِّن جَنَّٰتٖ وَعُيُونٖ
Open ayah 26:57Choncho tidawatulutsa m’minda ndi mwa akasupe.
وَكُنُوزٖ وَمَقَامٖ كَرِيمٖ
Open ayah 26:58Ndi m’nkhokwe za chuma ndi m’malo okongola.
كَذَٰلِكَۖ وَأَوۡرَثۡنَٰهَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Open ayah 26:59Momwemo ndi mmene tidawachitira ndipo tidawalowetsera chokolo zinthu zawo zonse kwa ana a Israyeli.
فَأَتۡبَعُوهُم مُّشۡرِقِينَ
Open ayah 26:60Choncho (anthu a Farawo ndi iye mwini) adawatsatira (ana a Israyeli) dzuwa litatuluka.
فَلَمَّا تَرَٰٓءَا ٱلۡجَمۡعَانِ قَالَ أَصۡحَٰبُ مُوسَىٰٓ إِنَّا لَمُدۡرَكُونَ
Open ayah 26:61Ndipo pamene magulu awiri adaonana (anthu a Farawo ndi anthu a Mûsa), anthu a Mûsa adati: “Ndithu ife tigwidwa.”
قَالَ كَلَّآۖ إِنَّ مَعِيَ رَبِّي سَيَهۡدِينِ
Open ayah 26:62(Mûsa) adati: “Iyayi! Ndithu Mbuye wanga ali nane pamodzi. Andiongolera (kuti ife tonse tipulumuke).”
فَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡبَحۡرَۖ فَٱنفَلَقَ فَكَانَ كُلُّ فِرۡقٖ كَٱلطَّوۡدِ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 26:63Ndipo tidam’vumbulutsira mawu Mûsa (akuti): “Menya nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo idagawikana, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu.
وَأَزۡلَفۡنَا ثَمَّ ٱلۡأٓخَرِينَ
Open ayah 26:64Ndipo tidawayandikitsa pamenepo anthu enawo, (Farawo ndi anthu ake nalowa pa njira yomweyo pambuyo pa Mûsa ndi anthu ake).
وَأَنجَيۡنَا مُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ
Open ayah 26:65Ndipo tidapulumutsa Mûsa ndi onse amene adali nawo (mpaka adaoloka nyanjayo, madzi ali chiimire mbali iyi ndi iyi).
ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
Open ayah 26:66Kenako tidawamiza enawo, (Farawo ndi anthu ake).
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:67Ndithu pa zimenezi pali lingaliro. Koma ambiri a iwo sali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:68Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa (amalanga ndi chilango choopsa omwe amunyoza); Wachisoni (kwa omkhulupirira ndi kumumvera).
وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ إِبۡرَٰهِيمَ
Open ayah 26:69Ndipo awerengere (osakhulupirira) nkhani ya (M’neneri) Ibrahim.
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَا تَعۡبُدُونَ
Open ayah 26:70Pamene adafunsa bambo wake ndi anthu ake (kuti); “Kodi mukupembedza chiyani?”
قَالُواْ نَعۡبُدُ أَصۡنَامٗا فَنَظَلُّ لَهَا عَٰكِفِينَ
Open ayah 26:71Adati: “Tikupembedza mafano; ndipo tipitiriza kuwapembedza.”
قَالَ هَلۡ يَسۡمَعُونَكُمۡ إِذۡ تَدۡعُونَ
Open ayah 26:72(Ibrahim) adati: “Kodi amakumvani mukawaitana?”
أَوۡ يَنفَعُونَكُمۡ أَوۡ يَضُرُّونَ
Open ayah 26:73“Kapena amakuthandizani (mukawapembedza) kapena amapereka masautso kwa inu (mukasiya kuwapembedza)?”
قَالُواْ بَلۡ وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا كَذَٰلِكَ يَفۡعَلُونَ
Open ayah 26:74(Iwo) adati: “Koma tidapeza makolo athu akuchita zimenezi.”
قَالَ أَفَرَءَيۡتُم مَّا كُنتُمۡ تَعۡبُدُونَ
Open ayah 26:75(Ibrahim) adati: “Kodi mukuwaona awa amene mwakhala mukuwapembedza,”
أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُمُ ٱلۡأَقۡدَمُونَ
Open ayah 26:76“Inu ndi makolo anu amene adatsogola?”
فَإِنَّهُمۡ عَدُوّٞ لِّيٓ إِلَّا رَبَّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:77“Ndithu iwo ndiadani anga, kupatula Mbuye wa zolengedwa zonse;”
ٱلَّذِي خَلَقَنِي فَهُوَ يَهۡدِينِ
Open ayah 26:78“Yemwe adandilenga, ndiponso Yemwe akundiongolera (kunjira yolungama);”
وَٱلَّذِي هُوَ يُطۡعِمُنِي وَيَسۡقِينِ
Open ayah 26:79“Ndiyemwe akundidyetsa ndi kundimwetsa.”
وَإِذَا مَرِضۡتُ فَهُوَ يَشۡفِينِ
Open ayah 26:80“Ndipo ndikadwala ndiyemwe amandichiritsa.”
وَٱلَّذِي يُمِيتُنِي ثُمَّ يُحۡيِينِ
Open ayah 26:81“Ndi Amene adzandipatsa imfa, ndipo (tsiku la Qiyâma) adzandidzutsa;”
وَٱلَّذِيٓ أَطۡمَعُ أَن يَغۡفِرَ لِي خَطِيٓـَٔتِي يَوۡمَ ٱلدِّينِ
Open ayah 26:82“Ndi Yemwe ndikuyembekezera kuti adzandikhululukira zolakwa zanga tsiku la malipiro.”
رَبِّ هَبۡ لِي حُكۡمٗا وَأَلۡحِقۡنِي بِٱلصَّٰلِحِينَ
Open ayah 26:83“E Mbuye wanga! Ndipatseni nzeru zoweruzira (zinthu), ndikundilumikiza ndi anthu abwino;”
وَٱجۡعَل لِّي لِسَانَ صِدۡقٖ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
Open ayah 26:84“Ndipatseni kutchulidwa kwabwino kwa anthu ena odza pambuyo;”
وَٱجۡعَلۡنِي مِن وَرَثَةِ جَنَّةِ ٱلنَّعِيمِ
Open ayah 26:85“Ndichiteni kukhala mmodzi mwa olandira Munda wamtendere;”
وَٱغۡفِرۡ لِأَبِيٓ إِنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ
Open ayah 26:86“Ndipo khululukirani bambo wanga; ndithu iye adali mmodzi wa osokera;”
وَلَا تُخۡزِنِي يَوۡمَ يُبۡعَثُونَ
Open ayah 26:87“Ndipo musadzandiyalutse pa tsiku loukitsidwa anthu (ku imfa);”
يَوۡمَ لَا يَنفَعُ مَالٞ وَلَا بَنُونَ
Open ayah 26:88“Tsiku lomwe chuma ndi ana sizidzathandiza (aliyense).”
إِلَّا مَنۡ أَتَى ٱللَّهَ بِقَلۡبٖ سَلِيمٖ
Open ayah 26:89“Kupatula yemwe adzadza kwa Allah ndi mtima woyera (iye ndiamene adzathandizidwa patsikulo).”
وَأُزۡلِفَتِ ٱلۡجَنَّةُ لِلۡمُتَّقِينَ
Open ayah 26:90Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa kwa oopa (Allah),
وَبُرِّزَتِ ٱلۡجَحِيمُ لِلۡغَاوِينَ
Open ayah 26:91Ndipo Jahannam idzaonetsedwa kwa opotoka;
وَقِيلَ لَهُمۡ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡبُدُونَ
Open ayah 26:92Ndipo kudzanenedwa kwa iwo: “Ali kuti amene mudali kuwapembedza aja,
مِن دُونِ ٱللَّهِ هَلۡ يَنصُرُونَكُمۡ أَوۡ يَنتَصِرُونَ
Open ayah 26:93M’malo mwa Allah? Kodi angathe kukuthandizani kapena kudzithandiza okha?”
فَكُبۡكِبُواْ فِيهَا هُمۡ وَٱلۡغَاوُۥنَ
Open ayah 26:94Ndipo iwo ndi opotoka ena adzaponyedwa ndi nkhope zawo m’menemo (mu Jahannam).
وَجُنُودُ إِبۡلِيسَ أَجۡمَعُونَ
Open ayah 26:95Ndi magulu onse ankhondo a Iblis (omwe adali kukometsa kwa anthu zoipa ndi machimo).
قَالُواْ وَهُمۡ فِيهَا يَخۡتَصِمُونَ
Open ayah 26:96Adzanena (movomereza kulakwa kwawo) uku naonso ali m’menemo, akukangana (ndi anzawo omwe adawasokeretsa):
تَٱللَّهِ إِن كُنَّا لَفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
Open ayah 26:97“Ndikulumbira Allah, ndithu tidali m’kusokera kowonekera.
إِذۡ نُسَوِّيكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:98Pamene timakufananitsani ndi Mbuye wa zolengedwa.
وَمَآ أَضَلَّنَآ إِلَّا ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Open ayah 26:99Ndipo sadatisokeretse, koma oipa okha basi.
فَمَا لَنَا مِن شَٰفِعِينَ
Open ayah 26:100Choncho ife tilibe aomboli (otiombola),
وَلَا صَدِيقٍ حَمِيمٖ
Open ayah 26:101Ngakhalenso bwenzi wapamtima (woti angatipulumutse kumasautsowa).
فَلَوۡ أَنَّ لَنَا كَرَّةٗ فَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:102Tikadapeza mwayi wobwerera (ku moyo wa padziko), tikadakhala mwa okhulupirira.”
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:103Ndithu m’zimenezi, muli malingaliro akulu, koma ambiri a iwo sali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:104Ndipo ndithu Mbuye wako, ndiye Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
كَذَّبَتۡ قَوۡمُ نُوحٍ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:105Anthu a Nuh adatsutsa atumiki.
إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ نُوحٌ أَلَا تَتَّقُونَ
Open ayah 26:106Pamene adawauza Nuh m’bale wawo kuti: “Kodi simukuopa (Allah ngakhale nditakuuzani zoopsa zimene zikukudikirani)?”
إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Open ayah 26:107“Ndithu ine kwa inu ndine Mtumiki wokhulupirika;”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:108“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:109“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:110“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
۞قَالُوٓاْ أَنُؤۡمِنُ لَكَ وَٱتَّبَعَكَ ٱلۡأَرۡذَلُونَ
Open ayah 26:111(Iwo) adati: “Nchotani kuti tikukhulupirire iwe chikhalirecho anthu wamba ndi amene akukutsatira?”
قَالَ وَمَا عِلۡمِي بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Open ayah 26:112(Nuh) adati: “Sindikudziwa zimene adali kuchita (zomwe zachititsa kuti Allah awaongolere kunjira yoongoka).”
إِنۡ حِسَابُهُمۡ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّيۖ لَوۡ تَشۡعُرُونَ
Open ayah 26:113“Chiwerengero chawo sichili kwina koma kwa Mbuye wanga, mukadakhala mukuzindikira.”
وَمَآ أَنَا۠ بِطَارِدِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:114“Ndipo sindine wopirikitsa okhulupirira (ku chipembedzo cha Allah kuti inu olemekezeka muchikhulupirire).”
إِنۡ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Open ayah 26:115“Ine sikanthu , koma ndine mchenjezi woonekera.”
قَالُواْ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ يَٰنُوحُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمَرۡجُومِينَ
Open ayah 26:116(Iwo) adati: “Ngati susiya, iwe Nuh, (zonena zakozi) ndithu ukhala mmodzi mwa ogendedwa (miyala mpaka ufe).”
قَالَ رَبِّ إِنَّ قَوۡمِي كَذَّبُونِ
Open ayah 26:117(Nuh) adati (kwa Allah): “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga anditsutsa.”
فَٱفۡتَحۡ بَيۡنِي وَبَيۡنَهُمۡ فَتۡحٗا وَنَجِّنِي وَمَن مَّعِيَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:118Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pa iwo (chiweruzo chabwino), ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupirira.”
فَأَنجَيۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ
Open ayah 26:119Choncho, tidampulumutsa pamodzi ndi omwe adali naye m’chombo chodzadza (ndi chilichonse chamoyo chomwe chidalipo m’dziko, chachimuna ndi chachikazi chidaikidwa m’menemo).
ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا بَعۡدُ ٱلۡبَاقِينَ
Open ayah 26:120Pambuyo pake tidawamiza otsalawo.
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:121Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:122Ndipo ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha.
كَذَّبَتۡ عَادٌ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:123Naonso Âdi adatsutsa atumiki.
إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ هُودٌ أَلَا تَتَّقُونَ
Open ayah 26:124Pamene m’bale wawo (Mneneri) Hûd adawafunsa kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”
إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Open ayah 26:125“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu;”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:126“Choncho, muopeni Allah ndipo mverani ine.”
وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:127“Ndipo pazimenezi sindikukupemphani malipiro; ndithu malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
أَتَبۡنُونَ بِكُلِّ رِيعٍ ءَايَةٗ تَعۡبَثُونَ
Open ayah 26:128“Kodi mukudzimangira nyumba pamalo paliponse pachitunda pokongola, moseweretsa?”
وَتَتَّخِذُونَ مَصَانِعَ لَعَلَّكُمۡ تَخۡلُدُونَ
Open ayah 26:129“Ndipo mukudzimangira (nyumba zonga) linga ngati kuti mukuona kuti mudzakhala muyaya?”
وَإِذَا بَطَشۡتُم بَطَشۡتُمۡ جَبَّارِينَ
Open ayah 26:130“Ndipo mukamamenya nkhondo mumamenya modzitukumula.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:131“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِيٓ أَمَدَّكُم بِمَا تَعۡلَمُونَ
Open ayah 26:132“Ndipo muopeni Yemwe adakupatsani zimene mukuzidziwa.”
أَمَدَّكُم بِأَنۡعَٰمٖ وَبَنِينَ
Open ayah 26:133“Adakupatsani ziweto ndi ana.”
وَجَنَّٰتٖ وَعُيُونٍ
Open ayah 26:134“Ndi minda ndi akasupe.”
إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Open ayah 26:135“Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”
قَالُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡنَآ أَوَعَظۡتَ أَمۡ لَمۡ تَكُن مِّنَ ٱلۡوَٰعِظِينَ
Open ayah 26:136Iwo adati: “Kwa ife nchimodzimodzi, utichenjeze kapena iwe usakhale mmodzi mwa ochenjeza.”
إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا خُلُقُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 26:137“Ndithu kutero (anthu ena kudzitcha atumiki a Allah), sikanthu koma ndi machitidwe a anthu akale.”
وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ
Open ayah 26:138“Ndipo ife sitidzalangidwa (monga momwe ukunenera).”
فَكَذَّبُوهُ فَأَهۡلَكۡنَٰهُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:139Choncho adamtsutsa, ndipo tidawaononga. Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:140Ndipo ndithu Mbuye wako ndiye Wamphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:141A Samudu (naonso) adatsutsa atumiki.
إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ صَٰلِحٌ أَلَا تَتَّقُونَ
Open ayah 26:142Pamene m’bale wawo Swalih adawauza kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”
إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Open ayah 26:143“Ndithu ine ndimtumiki wokhulupirika kwa inu.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:144“Choncho muopeni Allah ndipo mverani ine.”
وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:145“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi. Palibe kumene kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wa zolengedwa.”
أَتُتۡرَكُونَ فِي مَا هَٰهُنَآ ءَامِنِينَ
Open ayah 26:146“Kodi (mukuganizira kuti) mudzasiidwa mwamtendere pa izi zili pano (popanda imfa kukudzerani?)”
فِي جَنَّٰتٖ وَعُيُونٖ
Open ayah 26:147“M’minda ndi mu akasupe?”
وَزُرُوعٖ وَنَخۡلٖ طَلۡعُهَا هَضِيمٞ
Open ayah 26:148“Ndi (m’minda) yammera ndi mitengo yakanjedza yamikoko yakupsa yofewa?”
وَتَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتٗا فَٰرِهِينَ
Open ayah 26:149“Ndipo mukugoba nyumba m’mapiri mwaluso.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:150“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
وَلَا تُطِيعُوٓاْ أَمۡرَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ
Open ayah 26:151“Ndipo musamvere za awo opyola malire.”
ٱلَّذِينَ يُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا يُصۡلِحُونَ
Open ayah 26:152“Amene akuononga pa dziko, ndipo sakonza.”
قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلۡمُسَحَّرِينَ
Open ayah 26:153Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”
مَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا فَأۡتِ بِـَٔايَةٍ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Open ayah 26:154“Iwe suli kanthu, koma munthu ngati ife; tabwera ndi chozizwitsa, ngati ndiwedi mmodzi wa onena zoona!”
قَالَ هَٰذِهِۦ نَاقَةٞ لَّهَا شِرۡبٞ وَلَكُمۡ شِرۡبُ يَوۡمٖ مَّعۡلُومٖ
Open ayah 26:155Iye adati: “(Ndakubweretserani) ngamira iyi yaikazi; (koma) ili ndi gawo lake lakumwa, ndipo inu muli ndi gawo lanu lakutunga (madzi) patsiku lodziwika. (Tsiku lina lotunga rnadzi anthu).”
وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٖ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابُ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Open ayah 26:156“Ndipo musaikhudze ndi choipa chilichonse kuopera kuti chingakupezeni chilango cha tsiku lalikulu.”
فَعَقَرُوهَا فَأَصۡبَحُواْ نَٰدِمِينَ
Open ayah 26:157Koma iwo adaipha; ndipo adali odzinena (pamene chidadza chilango cha Allah).
فَأَخَذَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:158Choncho chilango (cha Allah) chidawaononga, ndithu pa zimenezi pali phunziro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:159Ndipo, ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; wachisoni chosatha.
كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:160Anthu a Luti adatsutsa atumiki.
إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ لُوطٌ أَلَا تَتَّقُونَ
Open ayah 26:161Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?”
إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Open ayah 26:162“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:163“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:164“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; palibe komwe kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wazolengedwa.”
أَتَأۡتُونَ ٱلذُّكۡرَانَ مِنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:165“Kodi mukugonana ndi amuna (anzanu) muzolengedwa (za Allah),
وَتَذَرُونَ مَا خَلَقَ لَكُمۡ رَبُّكُم مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ عَادُونَ
Open ayah 26:166“Ndikusiya amene Mbuye wanu adakulengerani kuti akhale akazi anu? Ndithu inu ndinu anthu olumpha malire.”
قَالُواْ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ يَٰلُوطُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُخۡرَجِينَ
Open ayah 26:167Iwo adati: “Ngati susiya (izi), E iwe Luti! ndithu ukhala mmodzi wa opirikitsidwa.”
قَالَ إِنِّي لِعَمَلِكُم مِّنَ ٱلۡقَالِينَ
Open ayah 26:168Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).”
رَبِّ نَجِّنِي وَأَهۡلِي مِمَّا يَعۡمَلُونَ
Open ayah 26:169“E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.”
فَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ
Open ayah 26:170Ndipo tidampulumutsa iye ndi onse a pa banja lake,
إِلَّا عَجُوزٗا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ
Open ayah 26:171Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo.
ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
Open ayah 26:172Titatero tidawaononga enawo.
وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرٗاۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلۡمُنذَرِينَ
Open ayah 26:173Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji, mvula ya ochenjezedwa!
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:174Ndithu pazimenezi pali malingaliro. Koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:175Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.
كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 26:176Anthu a m’dziko lamitengo yambiri (Madiana) adatsutsa atumiki.
إِذۡ قَالَ لَهُمۡ شُعَيۡبٌ أَلَا تَتَّقُونَ
Open ayah 26:177(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?”
إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Open ayah 26:178“Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Open ayah 26:179“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:180“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; kulibe malipiro anga koma kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
۞أَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُخۡسِرِينَ
Open ayah 26:181“Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).”
وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِ
Open ayah 26:182“Ndipo yesani ndi sikelo yolungama (yolondola).”
وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ
Open ayah 26:183“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo, ndiponso musayende padziko uku mukuononga.”
وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ وَٱلۡجِبِلَّةَ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 26:184“Ndipo muopeni amene adalenga inu ndiponso zolengedwa zoyamba (zimene zidanka kale).”
قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلۡمُسَحَّرِينَ
Open ayah 26:185Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”
وَمَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا وَإِن نَّظُنُّكَ لَمِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ
Open ayah 26:186“Ndipo iwe suli kanthu koma munthu ngati ife, ndipo ndithu tikukutsimikizira kuti ndiwe mmodzi wa abodza.”
فَأَسۡقِطۡ عَلَيۡنَا كِسَفٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Open ayah 26:187“Choncho tigwetsere zidutswa za thambo (kuti zitiononge) ngati uli mmodzi wa onena zoona.”
قَالَ رَبِّيٓ أَعۡلَمُ بِمَا تَعۡمَلُونَ
Open ayah 26:188(Shuaib) adati: “Mbuye wanga Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita. (Akadzaona kuti inu ngoyenera kulangidwa ndizidutswa za thambo, adzakulangani).”
فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَهُمۡ عَذَابُ يَوۡمِ ٱلظُّلَّةِۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ
Open ayah 26:189Koma adamutsutsa. Ndipo chidawagwera chilango chatsiku la mthunzi; ndithu chimenecho chidali chilango cha tsiku lalikulu.
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:190Ndithu pa zimenezi pali lingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.
وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 26:191Ndipo, ndithu Mbuye wako Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.
وَإِنَّهُۥ لَتَنزِيلُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 26:192Ndipo, ndithu iyi (Qur’an) ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse.
نَزَلَ بِهِ ٱلرُّوحُ ٱلۡأَمِينُ
Open ayah 26:193Mzimu Wokhulupirika (Jiburil) udaivumbulutsa.
عَلَىٰ قَلۡبِكَ لِتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُنذِرِينَ
Open ayah 26:194Pa mtima wako kuti ukhale mmodzi wa achenjezi,
بِلِسَانٍ عَرَبِيّٖ مُّبِينٖ
Open ayah 26:195M’chiyankhulo cha Chiarabu chomveka bwino.
وَإِنَّهُۥ لَفِي زُبُرِ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 26:196Ndipo ndithu izi (zomwe zili m’Qur’an) zilipo m’mabuku akale.
أَوَلَمۡ يَكُن لَّهُمۡ ءَايَةً أَن يَعۡلَمَهُۥ عُلَمَٰٓؤُاْ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Open ayah 26:197Kodi sipadapezeke chisonyezo kwa iwo kuti akuidziwa (Qur’an) odziwa mwa ana a Israyeli (kotero kuti ena alowa m’Chisilamu)?
وَلَوۡ نَزَّلۡنَٰهُ عَلَىٰ بَعۡضِ ٱلۡأَعۡجَمِينَ
Open ayah 26:198Ndipo tikadaivumbulutsa kwa wina amene sali Muarabu,
فَقَرَأَهُۥ عَلَيۡهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ مُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:199Kotero kuti nkuwawerengera momveka bwino, sakadaikhulupirira.
كَذَٰلِكَ سَلَكۡنَٰهُ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Open ayah 26:200Momwemo ndimo tidalowetsera kuitsutsa (Qur’an) m’mitima ya oipa.
لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ
Open ayah 26:201Sangaikhulupirire kufikira ataona chilango chowawa.
فَيَأۡتِيَهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Open ayah 26:202Choncho chidzawadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira.
فَيَقُولُواْ هَلۡ نَحۡنُ مُنظَرُونَ
Open ayah 26:203Tero adzayamba kunena: “Kodi ife tipatsidwa nthawi (yoti tilape)?”
أَفَبِعَذَابِنَا يَسۡتَعۡجِلُونَ
Open ayah 26:204Kodi akuchifulumizitsa chilango Chathu?
أَفَرَءَيۡتَ إِن مَّتَّعۡنَٰهُمۡ سِنِينَ
Open ayah 26:205Kodi ukuona bwanji, ngati titawasangalatsa zaka (zankhaninkhani).
ثُمَّ جَآءَهُم مَّا كَانُواْ يُوعَدُونَ
Open ayah 26:206Kenako nkuwadzera (chilango) chomwe adalonjezedwa,
مَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يُمَتَّعُونَ
Open ayah 26:207Sizidawathandize zomwe adali kusangalatsidwa nazozo.
وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا لَهَا مُنذِرُونَ
Open ayah 26:208Ndipo sitidauononge mudzi uliwonse koma udali ndi achenjezi.
ذِكۡرَىٰ وَمَا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
Open ayah 26:209(Kuti akhale) chikumbutso. Ndipo sitidali osalungama (powaononga popanda kuwachenjeza).
وَمَا تَنَزَّلَتۡ بِهِ ٱلشَّيَٰطِينُ
Open ayah 26:210Ndipo asatana sadaivumbulutse (iyi Qur’an monga osakhulupirira akunenera monyoza).
وَمَا يَنۢبَغِي لَهُمۡ وَمَا يَسۡتَطِيعُونَ
Open ayah 26:211Ndipo sikoyenera kwa iwo (kuivumbulutsa Qur’an) ndiponso sangathe.
إِنَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّمۡعِ لَمَعۡزُولُونَ
Open ayah 26:212Ndithu iwo ngotsekerezedwa kumvetsera (zimene angelo amalankhula kumwamba).
فَلَا تَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُعَذَّبِينَ
Open ayah 26:213Choncho usapembedze mulungu wina pamodzi ndi Allah, kuti ungakhale mwa olangidwa.
وَأَنذِرۡ عَشِيرَتَكَ ٱلۡأَقۡرَبِينَ
Open ayah 26:214Ndipo achenjeze abale ako a pafupi.
وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِمَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 26:215Ndipo fungatira ndi phiko lako amene akutsata mwa okhulupirira. (Ukhale wachifundo kwa iwo).
فَإِنۡ عَصَوۡكَ فَقُلۡ إِنِّي بَرِيٓءٞ مِّمَّا تَعۡمَلُونَ
Open ayah 26:216Ngati atakunyoza, nena: “Ine ndili kutali ndi zimene mukuchitazo.”
وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ
Open ayah 26:217Ndipo tsamira kwa (Mbuye wako) Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
ٱلَّذِي يَرَىٰكَ حِينَ تَقُومُ
Open ayah 26:218Yemwe akukuona pamene ukuimilira (pamapemphero).
وَتَقَلُّبَكَ فِي ٱلسَّٰجِدِينَ
Open ayah 26:219Ndikutembenukatembenuka kwako (pogwetsa mphumi yako pansi ndi kudzuka ndi kuimilira) pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi (polambira Allah).
إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Open ayah 26:220Ndithu Iye Ngwakumva; Ngodziwa chilichonse.
هَلۡ أُنَبِّئُكُمۡ عَلَىٰ مَن تَنَزَّلُ ٱلشَّيَٰطِينُ
Open ayah 26:221Kodi ndikuuzeni amene asatana amawatsikira?
تَنَزَّلُ عَلَىٰ كُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٖ
Open ayah 26:222Amamtsikira yense wabodza lamkunkhuniza; wamachimo.
يُلۡقُونَ ٱلسَّمۡعَ وَأَكۡثَرُهُمۡ كَٰذِبُونَ
Open ayah 26:223Amawaponyera (asatana anzawo a mu anthu) zimene azimva. Koma ambiri a iwo ngabodza.
وَٱلشُّعَرَآءُ يَتَّبِعُهُمُ ٱلۡغَاوُۥنَ
Open ayah 26:224Ndipo alakatuli (olakatula zopanda phindu) amatsatidwa ndi (anthu) opotoka.
أَلَمۡ تَرَ أَنَّهُمۡ فِي كُلِّ وَادٖ يَهِيمُونَ
Open ayah 26:225Kodi suona kuti iwo akungoyumbayumba m’chigwa chilichonse (chamawu)?
وَأَنَّهُمۡ يَقُولُونَ مَا لَا يَفۡعَلُونَ
Open ayah 26:226Ndithunso iwo akunena zomwe sachita.
إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَذَكَرُواْ ٱللَّهَ كَثِيرٗا وَٱنتَصَرُواْ مِنۢ بَعۡدِ مَا ظُلِمُواْۗ وَسَيَعۡلَمُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَيَّ مُنقَلَبٖ يَنقَلِبُونَ
Open ayah 26:227Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, ndikumamtchula Allah mowirikiza, ndikuzipulumutsa okha pambuyo pochitiridwa zoipa. Ndipo posachedwa amene adzichitira okha zoipa adziwa kotembenukira komwe adzatembenukire.