الفرقان
Al-Furqaan
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
تَبَارَكَ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡفُرۡقَانَ عَلَىٰ عَبۡدِهِۦ لِيَكُونَ لِلۡعَٰلَمِينَ نَذِيرًا
Open ayah 25:1Watukuka Mwini kupereka madalitso, Yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo Wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse.
ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَخَلَقَ كُلَّ شَيۡءٖ فَقَدَّرَهُۥ تَقۡدِيرٗا
Open ayah 25:2(Allah) Yemwe Ngwake ufumu wa kumwamba ndi wa pansi. Ndipo sadabale mwana ndipo alibenso wothandizana naye pa ufumu (Wake). Adalenga chinthu chilichonse ndikuchilinga mlingo wake.
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗ لَّا يَخۡلُقُونَ شَيۡـٔٗا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ وَلَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ ضَرّٗا وَلَا نَفۡعٗا وَلَا يَمۡلِكُونَ مَوۡتٗا وَلَا حَيَوٰةٗ وَلَا نُشُورٗا
Open ayah 25:3Ndipo m’malo mwa Iye (Mulungu weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza. Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa.
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ إِفۡكٌ ٱفۡتَرَىٰهُ وَأَعَانَهُۥ عَلَيۡهِ قَوۡمٌ ءَاخَرُونَۖ فَقَدۡ جَآءُو ظُلۡمٗا وَزُورٗا
Open ayah 25:4Ndipo osakhulupirira akunena: “Ichi sikanthu (Qur’an imene Muhammad {s.a.w} wadza nayo) koma ndi chonama chimene wachipeka, ndipo pachimenechi amthandiza anthu ena (eni mabuku).” Kunena zoona, iwo (osakhulupirira) adza ndi chinyengo ndi bodza (pazonena zawozi). [1]
- Osakhulupilira amumzinda wa Makka adali kuinyoza Qur’an namati ndi buku labodza limene walipeka yekhayekha Muhammad (s.a.w) ndikumamnamizira Allah kuti ndiye walivumbulutsa. Amatinso anthu a mabuku ndiwo adamthandiza kulipeka. Zonena zawozi nzabodza zokhazokha chifukwa Qur’an yomwe Muhammad (s.a.w) akuiwerengayo ili m’Charabu osati m’Chiyuda.
وَقَالُوٓاْ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٱكۡتَتَبَهَا فَهِيَ تُمۡلَىٰ عَلَيۡهِ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلٗا
Open ayah 25:5Ndipo (osakhulupirira) akunena: “Iyi (Qur’an) ndi nthano za anthu akale zomwe (Muhammad {s.a.w}) adazilembetsa. Choncho zikulakatulidwa kwa iye m’mawa ndi madzulo (kuti aloweze).”
قُلۡ أَنزَلَهُ ٱلَّذِي يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ كَانَ غَفُورٗا رَّحِيمٗا
Open ayah 25:6Nena: “Adaivumbulutsa Yemwe akudziwa zobisika za m’thambo ndi m’nthaka. Ndithu Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, (nchifukwa chake sakukulangani mwachangu pazimene mukunenazi).”
وَقَالُواْ مَالِ هَٰذَا ٱلرَّسُولِ يَأۡكُلُ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشِي فِي ٱلۡأَسۡوَاقِ لَوۡلَآ أُنزِلَ إِلَيۡهِ مَلَكٞ فَيَكُونَ مَعَهُۥ نَذِيرًا
Open ayah 25:7Ndipo akunena: “Ndi Mtumiki wanji uyu, womadya chakudya nkumayenda m’misika? Kodi bwanji sadatumizidwe mngelo kwa iye kuti azikhala naye limodzi uku akuchenjeza?”[1]
- Amamunenera zachipongwe Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti: “Nchiyani watiposa uyu pamene akudzitcha yekha kuti ndi Mtumiki? lye akudya chakudya monga momwe ife tidyera, ndipo akuyendayenda m’misika kunka nafunafuna zokhalira moyo monga anthu ena onse achitira. Akadakhaladi Mtumiki ndiye kuti Allah akadampatsa zosowa zake zonse. Ngati alidi Mtumiki bwanji Allah sadamtsitsire angelo kumwamba kuti azimthandiza? Zikadatero apo tikadamkhulupilira.’’
أَوۡ يُلۡقَىٰٓ إِلَيۡهِ كَنزٌ أَوۡ تَكُونُ لَهُۥ جَنَّةٞ يَأۡكُلُ مِنۡهَاۚ وَقَالَ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلٗا مَّسۡحُورًا
Open ayah 25:8“Kapena kuponyeredwa nkhokwe (za chuma), kapena kukhala ndi munda ndikumadya m’menemo?” Ndipo osalungama akuti: “Ndithudi, mukutsatira munthu wolodzedwa.”
ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَٰلَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلٗا
Open ayah 25:9Ona momwe akukuponyera mafanizo (omwe sali oyenerana nawe, nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa wamisala, wabodza, wophunzitsidwa ndi anthu ena) choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yoongoka yokunenera).
تَبَارَكَ ٱلَّذِيٓ إِن شَآءَ جَعَلَ لَكَ خَيۡرٗا مِّن ذَٰلِكَ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَيَجۡعَل لَّكَ قُصُورَۢا
Open ayah 25:10Watukuka Mwini kupereka madalitso ambiri, Yemwe akafuna, akuchitira zabwino kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa tsiku lachimaliziro) Minda yamtendere yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; ndipo adzakupangira nyumba zikuluzikulu zachifumu.
بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلسَّاعَةِۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِمَن كَذَّبَ بِٱلسَّاعَةِ سَعِيرًا
Open ayah 25:11Koma akutsutsa zanthawi ya Qiyâma. ndipo tawakonzera Moto woyaka (iwo) amene akutsutsa zanthawi ya Qiyâma (ya chimaliziro).
إِذَا رَأَتۡهُم مِّن مَّكَانِۭ بَعِيدٖ سَمِعُواْ لَهَا تَغَيُّظٗا وَزَفِيرٗا
Open ayah 25:12(Motowo) ukadzawaona (naonso nkuuona) kuchokera pa malo apatali, (iwo) adzamva mkwiyo wa Motowo ndi mkokomo wake.
وَإِذَآ أُلۡقُواْ مِنۡهَا مَكَانٗا ضَيِّقٗا مُّقَرَّنِينَ دَعَوۡاْ هُنَالِكَ ثُبُورٗا
Open ayah 25:13Ndipo akadzaponyedwa m’menemo, pamalo opanika uku manja atanjatidwa chakukhosi, pamenepo adzaitana imfa (kuti iwafike, afe apumule ku masautsowo).
لَّا تَدۡعُواْ ٱلۡيَوۡمَ ثُبُورٗا وَٰحِدٗا وَٱدۡعُواْ ثُبُورٗا كَثِيرٗا
Open ayah 25:14(Tidzawauza): “Lero musaitane imfa imodzi, koma itanani imfa zambiri (ndipo simupeza mpumulo koma mazunzo okhaokha).”
قُلۡ أَذَٰلِكَ خَيۡرٌ أَمۡ جَنَّةُ ٱلۡخُلۡدِ ٱلَّتِي وُعِدَ ٱلۡمُتَّقُونَۚ كَانَتۡ لَهُمۡ جَزَآءٗ وَمَصِيرٗا
Open ayah 25:15Nena (kwa osakhulupirira): “Kodi izi ndizo zabwino, kapena munda wamuyaya umene alonjezedwa oopa Allah kuti udzakhale mphoto (yabwino) kwa iwo ndi kobwerera (kotamandika)?”
لَّهُمۡ فِيهَا مَا يَشَآءُونَ خَٰلِدِينَۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ وَعۡدٗا مَّسۡـُٔولٗا
Open ayah 25:16“M’menemo adzapeza chilichonse chomwe adzafune. Adzakhala nthawi yaitali. Mtenderewu ndi lonjezo lochokera kwa Mbuye wako pa iwo lomwe adampempha kuti adzawakwaniritsire.”
وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ فَيَقُولُ ءَأَنتُمۡ أَضۡلَلۡتُمۡ عِبَادِي هَٰٓؤُلَآءِ أَمۡ هُمۡ ضَلُّواْ ٱلسَّبِيلَ
Open ayah 25:17Ndipo (kumbuka) tsiku limene adzawasonkhanitse (awa osakhulupirira) ndi omwe adali kuwapembedza (monga Isa (Yesu), Uzairi ndi angelo) kusiya Allah; adzanena (Allah kuuza amene ankalambiridwawo): “Kodi ndinu mudasokeretsa anthu angawa, kapena ndi okha adasokera njira.”
قَالُواْ سُبۡحَٰنَكَ مَا كَانَ يَنۢبَغِي لَنَآ أَن نَّتَّخِذَ مِن دُونِكَ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ وَلَٰكِن مَّتَّعۡتَهُمۡ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ نَسُواْ ٱلذِّكۡرَ وَكَانُواْ قَوۡمَۢا بُورٗا
Open ayah 25:18Adzanena: “E ulemelero ukhale kwa inu! Sizidali zoyenera kwa ife kudzikonzera atetezi mmalo mwa Inu, (nanji kuuza anthu kuti azitipembedza). Koma mudawasangalatsa iwo ndi makolo awo kufikira adaiwala malangizo (Anu). Ndipo adali anthu oonongeka.”
فَقَدۡ كَذَّبُوكُم بِمَا تَقُولُونَ فَمَا تَسۡتَطِيعُونَ صَرۡفٗا وَلَا نَصۡرٗاۚ وَمَن يَظۡلِم مِّنكُمۡ نُذِقۡهُ عَذَابٗا كَبِيرٗا
Open ayah 25:19(Allah adzati): “Ndithu yakutsutsani (milungu yanuyo) pa zimene mwanena (kuti iwo adakusokeretsani). Ndipo simutha kudzichotsera (chilango) ngakhale (kupeza) chithandizo.” Ndipo, ndithudi amene achite zoipa mwa inu, tidzamulawitsa chilango chachikulu.
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّآ إِنَّهُمۡ لَيَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشُونَ فِي ٱلۡأَسۡوَاقِۗ وَجَعَلۡنَا بَعۡضَكُمۡ لِبَعۡضٖ فِتۡنَةً أَتَصۡبِرُونَۗ وَكَانَ رَبُّكَ بَصِيرٗا
Open ayah 25:20Ndipo palibe pamene tidatuma atumiki patsogolo pako koma ndithu iwo, adali kudya chakudya; ankayendanso m’misika. Ndipo tawasankha ena mwa inu kuti akhale mayeso kwa ena (popereka masautso kwa olungama). kodi mupirira? Ndipo, Mbuye wako ali Wopenya (chilichonse).
۞وَقَالَ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ نَرَىٰ رَبَّنَاۗ لَقَدِ ٱسۡتَكۡبَرُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ وَعَتَوۡ عُتُوّٗا كَبِيرٗا
Open ayah 25:21۞ Ndipo amene alibe chiyembekezo chakukumana Nafe akunena: “Bwanji angelo satumidwa kwa ife? Kapena timuone Mbuye wathu (kuti atitsimikizire kuti ndiwedi Mtumiki wake”? Ndipo Allah akunena): “Ndithu adzitukumula mmitima mwawo ndipo anyoza; kunyoza kwakukulu.”
يَوۡمَ يَرَوۡنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ لَا بُشۡرَىٰ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُجۡرِمِينَ وَيَقُولُونَ حِجۡرٗا مَّحۡجُورٗا
Open ayah 25:22Tsiku lowaona angelo, sikudzakhala chisangalalo tsiku limenelo kwa ochimwa, (koma lidzakhala tsiku lochoka moyo wawo). Ndipo adzanena (tsiku limenelo): “Ha! Allah atitchinjirize kwambiri.” (Koma mawu awa, sadzathandiza chilichonse).
وَقَدِمۡنَآ إِلَىٰ مَا عَمِلُواْ مِنۡ عَمَلٖ فَجَعَلۡنَٰهُ هَبَآءٗ مَّنثُورًا
Open ayah 25:23Ndipo tidzaidzera ntchito iliyonse (yabwino) imene adachita, ndipo tizaichita monga fumbi louluka (ponseponse, yopanda phindu chifukwa cha kusakhulupirira Allah kwawo.)
أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ يَوۡمَئِذٍ خَيۡرٞ مُّسۡتَقَرّٗا وَأَحۡسَنُ مَقِيلٗا
Open ayah 25:24Anthu a ku Munda wamtendere tsiku limenelo adzakhala ndi mokhala mwabwino, ndi pamalo pampumulo wabwino.
وَيَوۡمَ تَشَقَّقُ ٱلسَّمَآءُ بِٱلۡغَمَٰمِ وَنُزِّلَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ تَنزِيلًا
Open ayah 25:25Ndipo akumbutse za tsikulo pomwe thambo lidzang’ambika ndikudzetsa mitambo (yomwe idzachititsa chimdima ponseponse). Ndipo angelo adzatsika ambirimbiri.
ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّ لِلرَّحۡمَٰنِۚ وَكَانَ يَوۡمًا عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ عَسِيرٗا
Open ayah 25:26Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ngwa (Allah) Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa osakhulupirira.
وَيَوۡمَ يَعَضُّ ٱلظَّالِمُ عَلَىٰ يَدَيۡهِ يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي ٱتَّخَذۡتُ مَعَ ٱلرَّسُولِ سَبِيلٗا
Open ayah 25:27Ndipo tsiku (limenelo), wosalungama adzakukuta zala zake uku akunena: “Kalanga ine! Ndikadatsata njira ya Mtumiki.”
يَٰوَيۡلَتَىٰ لَيۡتَنِي لَمۡ أَتَّخِذۡ فُلَانًا خَلِيلٗا
Open ayah 25:28“E tsoka langa! Ndikadapanda kumchita uje kukhala bwenzi wanga. (nkadapulumuka lero).”
لَّقَدۡ أَضَلَّنِي عَنِ ٱلذِّكۡرِ بَعۡدَ إِذۡ جَآءَنِيۗ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِلۡإِنسَٰنِ خَذُولٗا
Open ayah 25:29“Ndithu adandisokeretsa kufikira ndidasiya ulaliki (wa Allah) utandidzera. Zoonadi, satana amataya munthu (akaona kuti wamgwetsa m’chionongeko).”
وَقَالَ ٱلرَّسُولُ يَٰرَبِّ إِنَّ قَوۡمِي ٱتَّخَذُواْ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ مَهۡجُورٗا
Open ayah 25:30Ndipo Mtumiki (adasuma kwa Mbuye wake) adati: “E Mbuye wanga! Ndithu anthu anga aisandutsa Qur’aniyi kukhala chinthu chosiidwa, (sakuiwerenga. Ndiponso sakutsata ziphunzitso zake).”
وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوّٗا مِّنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ هَادِيٗا وَنَصِيرٗا
Open ayah 25:31Momwemonso mneneri aliyense tidamkonzera mdani wochokera mwa (anthu) oipa. Ndipo Mbuye wako wakwana kukhala muongoli ndi mthandizi (wako).
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلۡقُرۡءَانُ جُمۡلَةٗ وَٰحِدَةٗۚ كَذَٰلِكَ لِنُثَبِّتَ بِهِۦ فُؤَادَكَۖ وَرَتَّلۡنَٰهُ تَرۡتِيلٗا
Open ayah 25:32Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji Qur’an yonse siidavumbulutsidwe nthawi imodzi kwa iye? Momwemo (ukuoneramo, tikuitumiza pang’onopang’ono) kuti tiulimbikitse mtima wako ndi iyo, ndipo taiyala, mkayalidwe kabwino.
وَلَا يَأۡتُونَكَ بِمَثَلٍ إِلَّا جِئۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَأَحۡسَنَ تَفۡسِيرًا
Open ayah 25:33Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino.
ٱلَّذِينَ يُحۡشَرُونَ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ إِلَىٰ جَهَنَّمَ أُوْلَٰٓئِكَ شَرّٞ مَّكَانٗا وَأَضَلُّ سَبِيلٗا
Open ayah 25:34Amene adzasonkhanitsidwe akukokedwa ndi nkhope zawo kunka ku Jahanama, iwowo adzakhala pamalo oipa ndipo ngosokera njira (yachoonadi).
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَا مَعَهُۥٓ أَخَاهُ هَٰرُونَ وَزِيرٗا
Open ayah 25:35Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Ndipo m’bale wake Harun (Aroni) tidamsankha kukhala nduna (yake).
فَقُلۡنَا ٱذۡهَبَآ إِلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَدَمَّرۡنَٰهُمۡ تَدۡمِيرٗا
Open ayah 25:36Choncho tidati: “Pitani kwa anthu omwe atsutsa zisonyezo Zathu. Tero, tidawaononga kotheratu.”
وَقَوۡمَ نُوحٖ لَّمَّا كَذَّبُواْ ٱلرُّسُلَ أَغۡرَقۡنَٰهُمۡ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ لِلنَّاسِ ءَايَةٗۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِلظَّٰلِمِينَ عَذَابًا أَلِيمٗا
Open ayah 25:37Naonso anthu a Nuh, pamene adatsutsa atumiki, tidawamiza, ndipo tidawachita kukhala phunziro kwa anthu, ndipo anthu osalungama tawakonzera chilango chowawa.
وَعَادٗا وَثَمُودَاْ وَأَصۡحَٰبَ ٱلرَّسِّ وَقُرُونَۢا بَيۡنَ ذَٰلِكَ كَثِيرٗا
Open ayah 25:38Nawonso Âdi, Asamudu ndi eni chitsime ndi mibadwo yambiri pakati pa iwo.
وَكُلّٗا ضَرَبۡنَا لَهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَۖ وَكُلّٗا تَبَّرۡنَا تَتۡبِيرٗا
Open ayah 25:39Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu).
وَلَقَدۡ أَتَوۡاْ عَلَى ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِيٓ أُمۡطِرَتۡ مَطَرَ ٱلسَّوۡءِۚ أَفَلَمۡ يَكُونُواْ يَرَوۡنَهَاۚ بَلۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ نُشُورٗا
Open ayah 25:40Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa.
وَإِذَا رَأَوۡكَ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي بَعَثَ ٱللَّهُ رَسُولًا
Open ayah 25:41Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?”
إِن كَادَ لَيُضِلُّنَا عَنۡ ءَالِهَتِنَا لَوۡلَآ أَن صَبَرۡنَا عَلَيۡهَاۚ وَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ حِينَ يَرَوۡنَ ٱلۡعَذَابَ مَنۡ أَضَلُّ سَبِيلًا
Open ayah 25:42“Ndithu adatsala pang’ono kutisokeretsa ku milungu yathu, tikadapanda kupirira pa milunguyo.” Posachedwapa adziwa, pamene adzaona chilango, (kuti) ndani wosokera zedi njira.
أَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ أَفَأَنتَ تَكُونُ عَلَيۡهِ وَكِيلًا
Open ayah 25:43Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)?
أَمۡ تَحۡسَبُ أَنَّ أَكۡثَرَهُمۡ يَسۡمَعُونَ أَوۡ يَعۡقِلُونَۚ إِنۡ هُمۡ إِلَّا كَٱلۡأَنۡعَٰمِ بَلۡ هُمۡ أَضَلُّ سَبِيلًا
Open ayah 25:44Kapena ukuganiza kuti ambiri a iwo akumva kapena kuzindikira? Iwo sali kanthu kena koma ali ngati ziweto. Ndipo iwo asokera kwambiri njira.
أَلَمۡ تَرَ إِلَىٰ رَبِّكَ كَيۡفَ مَدَّ ٱلظِّلَّ وَلَوۡ شَآءَ لَجَعَلَهُۥ سَاكِنٗا ثُمَّ جَعَلۡنَا ٱلشَّمۡسَ عَلَيۡهِ دَلِيلٗا
Open ayah 25:45Kodi sudaone momwe Mbuye wako wautambasulira mthunzi? Akadafuna, akadauchita kuti ukhale wokhazikika (wosasinthasintha). Ndipo talichita dzuwa kukhala chisonyezo chake. [1]
- Apa Allah akuti kodi sukuona luso la Allah pa zopangapanga Zake ndi mphamvu Zake zoposa momwe amautambasulira mthunzi nthawi yamasana kuti munthu akhale pamthunzi ndikupeza mpumulo wabwino kuchoka mkutentha kwa dzuwa. Pakadapanda mthunzi ndiye kuti munthu akadatenthedwa ndi dzuwa ndikusowetsedwa mtendere pa moyo wake. Ndipo Allah akadafuna akadauleka mthunzi kuti ukhale pamalo amodzi. Koma Iye ndi mphamvu Zake zoposa adaupanga kukhala wosinthasintha.
ثُمَّ قَبَضۡنَٰهُ إِلَيۡنَا قَبۡضٗا يَسِيرٗا
Open ayah 25:46Kenaka tikuufumbata kwa Ife m’kufumbata kwapang’onopang’ono (kufikira wonse wutachoka).
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِبَاسٗا وَٱلنَّوۡمَ سُبَاتٗا وَجَعَلَ ٱلنَّهَارَ نُشُورٗا
Open ayah 25:47Ndipo Iye ndi amene wakuchitirani usiku kukhala monga chovala, ndipo tulo monga mpumulo, ndipo usana wauchita kukhala monga nthawi youka (kuimfa).
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦۚ وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ طَهُورٗا
Open ayah 25:48Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kukhala nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula), ndipo kuchokera kumitambo tikutsitsa madzi oyera.
لِّنُحۡـِۧيَ بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗا وَنُسۡقِيَهُۥ مِمَّا خَلَقۡنَآ أَنۡعَٰمٗا وَأَنَاسِيَّ كَثِيرٗا
Open ayah 25:49Kuti ndi madziwo tiukitse dziko lakufa (lachilala), ndikumwetsa zina mwa zimene tidazilenga monga ziweto ndi anthu ochuluka.
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَٰهُ بَيۡنَهُمۡ لِيَذَّكَّرُواْ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورٗا
Open ayah 25:50Ndiponso ndithu tikuigawa (mvulayi) pakati pawo kuti akumbukire, ndipo anthu ambiri akukana (kuthokoza Allah) koma kupitiriza kusakhulupirira.
وَلَوۡ شِئۡنَا لَبَعَثۡنَا فِي كُلِّ قَرۡيَةٖ نَّذِيرٗا
Open ayah 25:51Ndipo tikadafuna, tikadatuma mchenjezi wawowawo m’mudzi uliwonse, (koma tatuma Muhammad {s.a.w} kuti akhale mchenjezi wa onse).
فَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَجَٰهِدۡهُم بِهِۦ جِهَادٗا كَبِيرٗا
Open ayah 25:52Choncho usawamvere osakhulupirira koma limbana nawo ndi iyo (Qur’an); kulimbana kwakukulu.
۞وَهُوَ ٱلَّذِي مَرَجَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ هَٰذَا عَذۡبٞ فُرَاتٞ وَهَٰذَا مِلۡحٌ أُجَاجٞ وَجَعَلَ بَيۡنَهُمَا بَرۡزَخٗا وَحِجۡرٗا مَّحۡجُورٗا
Open ayah 25:53Ndipo Iye (Allah) ndi Yemwe wazikumanitsa nyanja ziwiri, iyi yamadzi okoma othetsa ludzu ndi iyi yamadzi amchere owawa. Ndipo waika malire ndi chitsekerezo chotsekereza pakati pa izo.
وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ مِنَ ٱلۡمَآءِ بَشَرٗا فَجَعَلَهُۥ نَسَبٗا وَصِهۡرٗاۗ وَكَانَ رَبُّكَ قَدِيرٗا
Open ayah 25:54Ndipo Iye ndiye adalenga munthu ndi madzi ndiponso adamchitira chibale cha magazi ndi chibale cha ukwati. Ndipo Mbuye wako ali Wokhoza chilichonse.
وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُهُمۡ وَلَا يَضُرُّهُمۡۗ وَكَانَ ٱلۡكَافِرُ عَلَىٰ رَبِّهِۦ ظَهِيرٗا
Open ayah 25:55Ndipo (ena mwa anthu) akupembedza zina zake kusiya Allah, zomwe sizingawathandize ndiponso sizingawadzetsere masautso (atasiya kuzipembedza). Ndipo wosakhulupirira ndi mthandizi wa zoipa poukira Mbuye wake.
وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Open ayah 25:56Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira).
قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ إِلَّا مَن شَآءَ أَن يَتَّخِذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا
Open ayah 25:57Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).”
وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡحَيِّ ٱلَّذِي لَا يَمُوتُ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِهِۦۚ وَكَفَىٰ بِهِۦ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرًا
Open ayah 25:58Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake.
ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَسۡـَٔلۡ بِهِۦ خَبِيرٗا
Open ayah 25:59Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye.
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱسۡجُدُواْۤ لِلرَّحۡمَٰنِ قَالُواْ وَمَا ٱلرَّحۡمَٰنُ أَنَسۡجُدُ لِمَا تَأۡمُرُنَا وَزَادَهُمۡ نُفُورٗا۩
Open ayah 25:60Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano.
تَبَارَكَ ٱلَّذِي جَعَلَ فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجٗا وَجَعَلَ فِيهَا سِرَٰجٗا وَقَمَرٗا مُّنِيرٗا
Open ayah 25:61Watukuka Mwini kupereka madalitso Yemwe adakhazikitsa nyenyezi ku thambo, ndipo m’menemo adaika nyali (dzuwa) ndi mwezi wounika.
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ خِلۡفَةٗ لِّمَنۡ أَرَادَ أَن يَذَّكَّرَ أَوۡ أَرَادَ شُكُورٗا
Open ayah 25:62Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza.
وَعِبَادُ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلَّذِينَ يَمۡشُونَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ هَوۡنٗا وَإِذَا خَاطَبَهُمُ ٱلۡجَٰهِلُونَ قَالُواْ سَلَٰمٗا
Open ayah 25:63Ndipo akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri ndi omwe akuyenda pa dziko modzichepetsa, ndipo mbuli zikanena kwa iwo (mawu amwano), amaziyankha mawu abwino.
وَٱلَّذِينَ يَبِيتُونَ لِرَبِّهِمۡ سُجَّدٗا وَقِيَٰمٗا
Open ayah 25:64Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo.
وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا ٱصۡرِفۡ عَنَّا عَذَابَ جَهَنَّمَۖ إِنَّ عَذَابَهَا كَانَ غَرَامًا
Open ayah 25:65Ndi omwe akunena: “E Mbuye wathu tipewetsereni chilango cha Jahannam; ndithu chilango chake nchosasiyana nacho.”
إِنَّهَا سَآءَتۡ مُسۡتَقَرّٗا وَمُقَامٗا
Open ayah 25:66“Ndithu iyo ndi malo woipa; ndiponso pokhala poipa.”
وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَنفَقُواْ لَمۡ يُسۡرِفُواْ وَلَمۡ يَقۡتُرُواْ وَكَانَ بَيۡنَ ذَٰلِكَ قَوَامٗا
Open ayah 25:67Ndi omwe amati akamagawira anthu ena chuma chawo, samwaza pachabe ndiponso sachita umbombo, koma amachita mwapakatikati.
وَٱلَّذِينَ لَا يَدۡعُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ وَلَا يَقۡتُلُونَ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَلَا يَزۡنُونَۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ يَلۡقَ أَثَامٗا
Open ayah 25:68Ndi omwe sapembedza milungu ina poiphatikiza ndi Allah, ndiponso saapha munthu yemwe Allah adaletsa kumupha kupatula pakakhala choonadi ndiponso saachita chigololo. Ndipo amene achite zimenezi, apeza masautso (pompano pa dziko lapansi).
يُضَٰعَفۡ لَهُ ٱلۡعَذَابُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَيَخۡلُدۡ فِيهِۦ مُهَانًا
Open ayah 25:69Chilango chidzawonjezeredwa kwa iye tsiku la Qiyâma, ndipo adzakhala m’chilango muyaya uku ali wonyozeka.
إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ عَمَلٗا صَٰلِحٗا فَأُوْلَٰٓئِكَ يُبَدِّلُ ٱللَّهُ سَيِّـَٔاتِهِمۡ حَسَنَٰتٖۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورٗا رَّحِيمٗا
Open ayah 25:70Kupatula amene walapa, naakhulupirira, ndikuchita ntchito yabwino. Tsono iwowo, Allah adzawasinthira zoipa zawo kukhala zabwino. Ndipo Allah ali Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
وَمَن تَابَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَإِنَّهُۥ يَتُوبُ إِلَى ٱللَّهِ مَتَابٗا
Open ayah 25:71Ndipo amene akulapa ndikuchita zabwino, ndithu iye akulapa mwachoonadi kwa Allah.
وَٱلَّذِينَ لَا يَشۡهَدُونَ ٱلزُّورَ وَإِذَا مَرُّواْ بِٱللَّغۡوِ مَرُّواْ كِرَامٗا
Open ayah 25:72Omwenso sachitira umboni za bodza, ndipo akadutsa pamalo pa zachibwana, amadutsa mwaulemu.
وَٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَمۡ يَخِرُّواْ عَلَيۡهَا صُمّٗا وَعُمۡيَانٗا
Open ayah 25:73Ndiponso omwe amati akakumbutsidwa Ayah za Mbuye wawo, samazigwera mwa ugonthi ndi mwakhungu.
وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا هَبۡ لَنَا مِنۡ أَزۡوَٰجِنَا وَذُرِّيَّٰتِنَا قُرَّةَ أَعۡيُنٖ وَٱجۡعَلۡنَا لِلۡمُتَّقِينَ إِمَامًا
Open ayah 25:74Ndi omwenso akunena: “E Mbuye wathu! Tipatseni mwa akazi athu ndi ana athu chotonthoza maso, ndipo tichiteni kukhala atsogoleri a oopa Allah.”
أُوْلَٰٓئِكَ يُجۡزَوۡنَ ٱلۡغُرۡفَةَ بِمَا صَبَرُواْ وَيُلَقَّوۡنَ فِيهَا تَحِيَّةٗ وَسَلَٰمًا
Open ayah 25:75Iwo adzalipidwa zipinda (za pamwamba ku Jannah) chifukwa cha mavuto omwe adawapirira. Ndipo akalandira m’menemo ulemu ndi mtendere.
خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ حَسُنَتۡ مُسۡتَقَرّٗا وَمُقَامٗا
Open ayah 25:76Akakhala m’menemo nthawi yaitali; akongolerenji malo okhazikika ndi kukhalamo.
قُلۡ مَا يَعۡبَؤُاْ بِكُمۡ رَبِّي لَوۡلَا دُعَآؤُكُمۡۖ فَقَدۡ كَذَّبۡتُمۡ فَسَوۡفَ يَكُونُ لِزَامَۢا
Open ayah 25:77Nena: “Ndithu Mbuye wanga sakadalabadira chilichonse pa inu pakadapanda mapemphero anu, (akadakulangani pompano pa dziko lapansi.) Komabe inu mwatsutsa (uthenga wa aneneri). Choncho chilango chidzakugweranibe.”