طه

Taa-Haa

Taa-Haa · Surah 20 · Ayahs: 135 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. Tâ-Hâ [1]

    1. Allah wapamwamba wayamba Sura iyi ndi malembo awa awiri potchalenja omwe akutsutsa zoti Qur’an idachokera kwa Allah, kuti atalemba yawo Qur’an yomwe malembo ake omwewa omwe iwo akuwadziwa bwino ndipo amawayankhula. Koma alephera kutalitali kulemba buku ndi nzeru zawo monga ili. Ndipo kulephera kwawo kulemba buku longa ili, ndiumboni kuti bukuli lidachokera kwa Allah.
  2. مَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ لِتَشۡقَىٰٓ

    Open ayah 20:2

    Sitidakuvumbulutsire iwe Qur’an kuti uvutike (nayo).

  3. إِلَّا تَذۡكِرَةٗ لِّمَن يَخۡشَىٰ

    Open ayah 20:3

    Koma kuti ikhale ulaliki ndi chikumbutso kwa yemwe akuopa (ndikudzichepetsa kwa Allah).

  4. تَنزِيلٗا مِّمَّنۡ خَلَقَ ٱلۡأَرۡضَ وَٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلۡعُلَى

    Open ayah 20:4

    Chovumbulitsidwa chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi thambo lotukuka kumwamba.

  5. ٱلرَّحۡمَٰنُ عَلَى ٱلۡعَرۡشِ ٱسۡتَوَىٰ

    Open ayah 20:5

    (Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake).

  6. لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَمَا تَحۡتَ ٱلثَّرَىٰ

    Open ayah 20:6

    Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi za pakati pake ndi za pansi pa nthaka, nza Iye.

  7. وَإِن تَجۡهَرۡ بِٱلۡقَوۡلِ فَإِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ وَأَخۡفَى

    Open ayah 20:7

    Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu).[1]

    1. M’ndime iyi Allah akuuza munthu kuti Iye akudziwa zonse zimene munthu amayankhula mokweza mawu ndi zimene munthu amayankhula ndi anzake mobisa, ngakhalenso zomwe mtima wake umamnong’oneza.
  8. ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ لَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ

    Open ayah 20:8

    Allah! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Iye ali ndi maina abwino (ndi mbiri zabwinonso).

  9. وَهَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ

    Open ayah 20:9

    Ndipo kodi yakufika nkhani ya Mûsa? (Yomwe njododometsa)?[1]

    1. Ibun Abbas adati: “Izi zidali choncho Musa pamene adakwaniritsa chipangano cha nthawi imene adapangana ndi m’neneri Shuaibu chakuti amuwetere mbuzi kwa zaka 8 kapena 10, adachoka ulendo kubwerera kwawo ku Iguputo pamodzi ndi banja lake; ndipo adasokera njira. Udali usiku wamdima wozizira. Adayesa kupekesa moto kuti awothe koma adalephera. Ndipo ali choncho, adangoona moto chapatali kumbali yakumanja kwa njira. Pamene adauona adauganizira kuti ndi moto weniweni, pomwe udali moto woyera wakuunika kwa Allah. Udali kuyaka mu mtengo wamasamba obiriwira. Ndipo adangomva Mbuye wake akumuitana: “E iwe Musa! Ine ndine Mbuye wako. Ndikukuyankhula; vula nsapato zako.”
  10. إِذۡ رَءَا نَارٗا فَقَالَ لِأَهۡلِهِ ٱمۡكُثُوٓاْ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارٗا لَّعَلِّيٓ ءَاتِيكُم مِّنۡهَا بِقَبَسٍ أَوۡ أَجِدُ عَلَى ٱلنَّارِ هُدٗى 

    Open ayah 20:10

    Pamene adaona moto adauza banja lake: “Yembekezani (pano); ndithu ndaona moto; mwina ndingakakutengereni chikuni chamoto (kuti muothe), kapena ndikapeza ondiongolera njira pa motopo.

  11. فَلَمَّآ أَتَىٰهَا نُودِيَ يَٰمُوسَىٰٓ

    Open ayah 20:11

    Koma pamene adaudzera motowo Anaitanidwa (kuti), “E, iwe Mûsa!

  12. إِنِّيٓ أَنَا۠ رَبُّكَ فَٱخۡلَعۡ نَعۡلَيۡكَ إِنَّكَ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوٗى

    Open ayah 20:12

    Ndithu ine ndine Mbuye wako! Vula nsapato zakozo; ndithu iwe uli pa chigwa chopatulika, chotchedwa Tuwa.”

  13. وَأَنَا ٱخۡتَرۡتُكَ فَٱسۡتَمِعۡ لِمَا يُوحَىٰٓ

    Open ayah 20:13

    Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe).

  14. إِنَّنِيٓ أَنَا ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدۡنِي وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِذِكۡرِيٓ

    Open ayah 20:14

    Ndithu Ine ndine Allah palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine; choncho ndipembeze, pemphera Swala moyenera pondikumbukira.

  15. إِنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ أَكَادُ أُخۡفِيهَا لِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا تَسۡعَىٰ

    Open ayah 20:15

    Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita.[1]

    1. Womasulira Qur’an adati cholinga chakubisa kudza kwa tsiku la chimaliziro, ndi nthawi ya imfa ya munthu ndikuti Allah wapamwambamwamba adalamula kuti sangavomereze kulapa tsiku la chimaliziro litadza, ndi nthawi ya imfa itamufikira munthu. Anthu akadadziwa nthawi yeniyeni ya chimaliziro ndi nthawi yakudza kwa imfa yawo, akadakhala akuchita zinthu zoyipa naakhala ndi chiyembekezero choti adzalapa nthawi ikayandikira, nadzapulumuka kuchilango cha Allah. Koma Allah anabisa zimenezo kuti anthu akhale tcheru nthawi zonse ndikukhala okonzekera za imfa ndi za tsiku la chimaliziro kuti zingawadzere modzidzimutsa.
  16. فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنۡهَا مَن لَّا يُؤۡمِنُ بِهَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ فَتَرۡدَىٰ

    Open ayah 20:16

    Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”

  17. وَمَا تِلۡكَ بِيَمِينِكَ يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:17

    “Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”

  18. قَالَ هِيَ عَصَايَ أَتَوَكَّؤُاْ عَلَيۡهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِي وَلِيَ فِيهَا مَـَٔارِبُ أُخۡرَىٰ

    Open ayah 20:18

    (Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”[1]

    1. Womasulira adati yankho lakuti: “Iyi ndi ndodo yanga,” lidali yankho lokwana. Koma iye adaonjezera payankho mawu ena amene sadamufunse chifukwa chakuti pomwe adalipo padali pamalo poyenera kutambasula mawu pakuti Allah ndiye adali kuyankhula naye popanda mkhalapakati. Uku kudali kuti amve kukoma koyankhulana ndi Allah. Pajatu mawu a wokondedwa amatonthoza moyo ndipo amachotsa kutopa kwa mtundu uliwonse.
  19. قَالَ أَلۡقِهَا يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:19

    (Allah) adati: “Iponye iwe Mûsa!”

  20. فَأَلۡقَىٰهَا فَإِذَا هِيَ حَيَّةٞ تَسۡعَىٰ 

    Open ayah 20:20

    Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga. [1]

    1. Ibun Abbas adati ndodoyi idasanduka chinjoka chachimuna chomwe chidali kumeza miyala ndi mitengo. Pamene Musa adachiona chikumeza chilichonse adachiopa. Nkhaniyi ikupezeka m’buku la Qurtubi, volume 11, tsamba la 190.
  21. قَالَ خُذۡهَا وَلَا تَخَفۡۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا ٱلۡأُولَىٰ

    Open ayah 20:21

    (Allah) adati: “Igwire, usaope. Tiibwezera m’chikhalidwe chake Choyamba.”

  22. وَٱضۡمُمۡ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٍ ءَايَةً أُخۡرَىٰ

    Open ayah 20:22

    “Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”[1]

    1. Ibun Kathiri adati Musa ankati akalilowetsa dzanjalo mkhwapa mwake kenako nkulitulutsa, limatuluka lili kung’anima ngati chiditswa chamwezi popanda chonyansa chilichonse. Ichi chidali china mwa zozizwitsa zake.
  23. لِنُرِيَكَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا ٱلۡكُبۡرَى

    Open ayah 20:23

    “Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”

  24. ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ

    Open ayah 20:24

    “Pita kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.”

  25. قَالَ رَبِّ ٱشۡرَحۡ لِي صَدۡرِي

    Open ayah 20:25

    (Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”

  26. وَيَسِّرۡ لِيٓ أَمۡرِي

    Open ayah 20:26

    “Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”

  27. وَٱحۡلُلۡ عُقۡدَةٗ مِّن لِّسَانِي

    Open ayah 20:27

    “Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”[1]

    1. Musa adali wachibwibwi koma chibwibwi chake sichinali chachibadwa. Kuyamba kwa chibwibwi chake kudali motere: Kumayambiliro amoyo wake adali kukhala m’nyumba ya Farawo. Ndipo nthawi ina Farawo adamuika pamiyendo yake iye ali mwana. Musa adakoka ndevu za Farawo ndi dzanja lake. Ndipo Farawo adakwiya natsimikiza zomupha. Ndipo Asiya, mkazi wake, adati kwa iye: “Iyeyu sazindikira. Ndipo ndikusonyeza zimenezo kuti udziwe.Yandikitsani kwa iye makala awiri ndi ngale ziwiri. Ngati atola ngalezo ndiye kuti akuzindikira. Koma akatola khala lamoto, apo uzindikira kuti ameneyu sazindikira kanthu. Choncho Farawo adamuyandikizira zonsezo ndipo iye adatola khala lamoto nkuliponya mkamwa mwake. Potero palirime lake padali kachipsera. Nkhaniyi ikupezeka m’buku la Tabariyi, volume 16 tsamba 159.
  28. يَفۡقَهُواْ قَوۡلِي

    Open ayah 20:28

    “Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”

  29. وَٱجۡعَل لِّي وَزِيرٗا مِّنۡ أَهۡلِي

    Open ayah 20:29

    “Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”

  30. هَٰرُونَ أَخِي 

    Open ayah 20:30

    “M’bale wanga Harun.”

  31. ٱشۡدُدۡ بِهِۦٓ أَزۡرِي

    Open ayah 20:31

    “Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”

  32. وَأَشۡرِكۡهُ فِيٓ أَمۡرِي

    Open ayah 20:32

    “Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”

  33. كَيۡ نُسَبِّحَكَ كَثِيرٗا

    Open ayah 20:33

    “Kuti tikulemekezeni kwambiri.”

  34. وَنَذۡكُرَكَ كَثِيرًا

    Open ayah 20:34

    “Ndi kukutamandani kwabasi.”

  35. إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرٗا

    Open ayah 20:35

    “Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”

  36. قَالَ قَدۡ أُوتِيتَ سُؤۡلَكَ يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:36

    (Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”

  37. وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَيۡكَ مَرَّةً أُخۡرَىٰٓ

    Open ayah 20:37

    “Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”

  38. إِذۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ أُمِّكَ مَا يُوحَىٰٓ

    Open ayah 20:38

    “Pamene mayi wako tidamuzindikiritsa zimene tidamzindikiritsa (kuti azichite).”

  39. أَنِ ٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلتَّابُوتِ فَٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلۡيَمِّ فَلۡيُلۡقِهِ ٱلۡيَمُّ بِٱلسَّاحِلِ يَأۡخُذۡهُ عَدُوّٞ لِّي وَعَدُوّٞ لَّهُۥۚ وَأَلۡقَيۡتُ عَلَيۡكَ مَحَبَّةٗ مِّنِّي وَلِتُصۡنَعَ عَلَىٰ عَيۡنِيٓ

    Open ayah 20:39

    (Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”

  40. إِذۡ تَمۡشِيٓ أُخۡتُكَ فَتَقُولُ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ مَن يَكۡفُلُهُۥۖ فَرَجَعۡنَٰكَ إِلَىٰٓ أُمِّكَ كَيۡ تَقَرَّ عَيۡنُهَا وَلَا تَحۡزَنَۚ وَقَتَلۡتَ نَفۡسٗا فَنَجَّيۡنَٰكَ مِنَ ٱلۡغَمِّ وَفَتَنَّٰكَ فُتُونٗاۚ فَلَبِثۡتَ سِنِينَ فِيٓ أَهۡلِ مَدۡيَنَ ثُمَّ جِئۡتَ عَلَىٰ قَدَرٖ يَٰمُوسَىٰ 

    Open ayah 20:40

    (Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa![1]

    1. Omasulira adati: Pamene adamtola Musa akubanja la Farawo sadali kuyamwa bele la mkazi aliyense, amakana, chifukwa Allah adamuletsa kuyamwa mawere aakazi ena oyamwitsa. Ndipo mayi wake adali ndi madandaulo ndi chisoni atamponya mumtsinje, ndipo adamulamula mlongo wake kunka nafufuza za mwanayo. Pamene adafika kunyumba ya Farawo, adamuona. Adati: “Kodi ndikulondolereni mkazi wokhulupirika, waulemu kuti azikuyamwitsirani mwanayo?” Ndipo iwo adati: “Pita kamtenge.” Choncho adadza ndi mayi wa Musa. Pamene adatulutsa bere lake, Musa adayamwa. Choncho mkazi wa Farawo adasangalala kwabasi namuuza make Musa: “Dzikhala pamodzi nane kunyumba yachifumu.” Iye adati: “Sindingathe kusiya nyumba yanga ndi ana anga. Koma ndimtenga ndipo ndikhala ndikudza naye nthawi iliyonse ukamufuna.” Mkazi wa Farawo adavomereza ndi kumchitira zabwino mayiyo. Ili ndilo tanthauzo la mawu a Allah akuti: “Tidakubwezera kwa mayi wako kuti diso lake litonthole, asadandaule.”
  41. وَٱصۡطَنَعۡتُكَ لِنَفۡسِي

    Open ayah 20:41

    Ndipo ndakusankha ndekha (kuti ukhale Mtumiki Wanga).

  42. ٱذۡهَبۡ أَنتَ وَأَخُوكَ بِـَٔايَٰتِي وَلَا تَنِيَا فِي ذِكۡرِي

    Open ayah 20:42

    Pita iwe ndi m’bale wako ndi zozizwitsa Zanga, ndipo musatope (musasiye) kundikumbukira.

  43. ٱذۡهَبَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ

    Open ayah 20:43

    Pitani kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.

  44. فَقُولَا لَهُۥ قَوۡلٗا لَّيِّنٗا لَّعَلَّهُۥ يَتَذَكَّرُ أَوۡ يَخۡشَىٰ

    Open ayah 20:44

    Kamuuzeni mawu ofewa mwina akalingalira (uthengawo) kapena akaopa.

  45. قَالَا رَبَّنَآ إِنَّنَا نَخَافُ أَن يَفۡرُطَ عَلَيۡنَآ أَوۡ أَن يَطۡغَىٰ

    Open ayah 20:45

    (Iwo) adati: “Mbuye wathu ndithu ife tikuopa kuti angatimbwandire kapena kutipyolera malire (tisananene kanthu).”

  46. قَالَ لَا تَخَافَآۖ إِنَّنِي مَعَكُمَآ أَسۡمَعُ وَأَرَىٰ

    Open ayah 20:46

    (Allah) adati: “Musaope. Ndithu Ine ndili nanu pamodzi. ndikumva, ndiponso ndikuona.”

  47. فَأۡتِيَاهُ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولَا رَبِّكَ فَأَرۡسِلۡ مَعَنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَا تُعَذِّبۡهُمۡۖ قَدۡ جِئۡنَٰكَ بِـَٔايَةٖ مِّن رَّبِّكَۖ وَٱلسَّلَٰمُ عَلَىٰ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلۡهُدَىٰٓ

    Open ayah 20:47

    Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”

  48. إِنَّا قَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡنَآ أَنَّ ٱلۡعَذَابَ عَلَىٰ مَن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ

    Open ayah 20:48

    “Ndithu zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chiwapeza amene akutsutsa (zimenezi) ndikuzitembenukira kumbali.”

  49. قَالَ فَمَن رَّبُّكُمَا يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:49

    (Farawo) adati: “Kodi Mbuye wanu ndani, iwe Mûsa?”

  50. قَالَ رَبُّنَا ٱلَّذِيٓ أَعۡطَىٰ كُلَّ شَيۡءٍ خَلۡقَهُۥ ثُمَّ هَدَىٰ 

    Open ayah 20:50

    (Mûsa) adati: “Mbuye wathu ndi yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake, kenako adachiongolera (kutsata chimene chikulingana ndi chilengedwe chake).”

  51. قَالَ فَمَا بَالُ ٱلۡقُرُونِ ٱلۡأُولَىٰ

    Open ayah 20:51

    (Farawo) adati: “Nanga mibadwo yakale ili bwanji, (imene idapita iwe usadadze?”)

  52. قَالَ عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّي فِي كِتَٰبٖۖ لَّا يَضِلُّ رَبِّي وَلَا يَنسَى

    Open ayah 20:52

    (Mûsa) adati: “Kudziwa kwa zimenezo nkwa Mbuye wanga, m’kaundula (Wake momwe mwasonkhanitsidwa chilichonse), Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala.

  53. ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدٗا وَسَلَكَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلٗا وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجٗا مِّن نَّبَاتٖ شَتَّىٰ

    Open ayah 20:53

    Yemwe adakupangirani nthaka monga choyala, ndipo m’menemo adakuikirani njira ndikutsitsa madzi kuchokera kumwamba.” Ndipo kupyolera m’madziwo tidameretsa mmera wosiyanasiyana.

  54. كُلُواْ وَٱرۡعَوۡاْ أَنۡعَٰمَكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ

    Open ayah 20:54

    Idyani ndikudyetsa ziweto zanu. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru.

  55. ۞مِنۡهَا خَلَقۡنَٰكُمۡ وَفِيهَا نُعِيدُكُمۡ وَمِنۡهَا نُخۡرِجُكُمۡ تَارَةً أُخۡرَىٰ

    Open ayah 20:55

    Kuchokera (m’nthaka) umu tidakulengani, ndipo momwemo tidzakubwezani, ndipo kuchokera m’menemo tidzakutulutsani nthawi ina (muli moyo).

  56. وَلَقَدۡ أَرَيۡنَٰهُ ءَايَٰتِنَا كُلَّهَا فَكَذَّبَ وَأَبَىٰ

    Open ayah 20:56

    Ndipo, ndithu tidamuonetsa (Farawo) zozizwitsa zathu zonse, koma adatsutsa ndipo adakana.

  57. قَالَ أَجِئۡتَنَا لِتُخۡرِجَنَا مِنۡ أَرۡضِنَا بِسِحۡرِكَ يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:57

    Adati: “Kodi watidzera kuti utitulutse m’dziko lathu, ndi matsenga ako, E, iwe Mûsa!

  58. فَلَنَأۡتِيَنَّكَ بِسِحۡرٖ مِّثۡلِهِۦ فَٱجۡعَلۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكَ مَوۡعِدٗا لَّا نُخۡلِفُهُۥ نَحۡنُ وَلَآ أَنتَ مَكَانٗا سُوٗى

    Open ayah 20:58

    Choncho nafe tikubweretsera matsenga onga amenewo! Choncho ika lonjezo (la msonkhano) pakati pathu ndi iwe; lonjezo lomwe tisaliswe ife ndi iwe, (tidzakumane) pamalo poyenera.”

  59. قَالَ مَوۡعِدُكُمۡ يَوۡمُ ٱلزِّينَةِ وَأَن يُحۡشَرَ ٱلنَّاسُ ضُحٗى

    Open ayah 20:59

    (Mûsa) adati: “Lonjezo lanu likhale pa tsiku lodzikongoletsa (tsiku la chikondwelero), ndipo anthu adzasonkhanitsidwe m’mawa.”

  60. فَتَوَلَّىٰ فِرۡعَوۡنُ فَجَمَعَ كَيۡدَهُۥ ثُمَّ أَتَىٰ 

    Open ayah 20:60

    Ndipo Farawo adabwerera ndikusonkhanitsa matsenga ake, ndipo kenako adabwera (ndi amatsenga ake pa tsiku la chipanganolo).[1]

    1. Ibun Abbas adati: Amatsenga adali okwana 72. Ndipo wamatsenga aliyense adagwirizira m’manja mwake chingwe ndi ndodo. Izi zidalembedwa m’buku la Tabari, Volume 11, tsamba 214.
  61. قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ وَيۡلَكُمۡ لَا تَفۡتَرُواْ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا فَيُسۡحِتَكُم بِعَذَابٖۖ وَقَدۡ خَابَ مَنِ ٱفۡتَرَىٰ

    Open ayah 20:61

    Mûsa adawauza: “Tsoka kwa inu! Musampekere bodza Allah, kuopera kuti angakuphwasuleni ndi chilango. Ndipo, ndithu wataika amene akupeka bodza.”

  62. فَتَنَٰزَعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَىٰ

    Open ayah 20:62

    Choncho (amatsengawo) adakangana pakati pawo pa zinthu zawo ndipo adakambirana mwachinsinsi.

  63. قَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَٰنِ لَسَٰحِرَٰنِ يُرِيدَانِ أَن يُخۡرِجَاكُم مِّنۡ أَرۡضِكُم بِسِحۡرِهِمَا وَيَذۡهَبَا بِطَرِيقَتِكُمُ ٱلۡمُثۡلَىٰ

    Open ayah 20:63

    (Iwo) adati (mkunong’onezana kwawo): “Ndithu anthu awiriwa ndi amatsenga; kupyolera mmatsenga awo akufuna kukutulutsani m’dziko mwanu, ndikuchotsa chikhalidwe chanu chomwe chili chabwino.”

  64. فَأَجۡمِعُواْ كَيۡدَكُمۡ ثُمَّ ٱئۡتُواْ صَفّٗاۚ وَقَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡيَوۡمَ مَنِ ٱسۡتَعۡلَىٰ

    Open ayah 20:64

    “Choncho sonkhanitsani matsenga anu (onse), kenako mudze (kwa iwo) mutandanda pamzere; ndithu lero, apambana amene akhale wapamwamba.”

  65. قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَلۡقَىٰ

    Open ayah 20:65

    (Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukhale ndiwe woyamba kuponya (matsenga ako), kapena tikhale oyamba ndife kuponya?”

  66. قَالَ بَلۡ أَلۡقُواْۖ فَإِذَا حِبَالُهُمۡ وَعِصِيُّهُمۡ يُخَيَّلُ إِلَيۡهِ مِن سِحۡرِهِمۡ أَنَّهَا تَسۡعَىٰ

    Open ayah 20:66

    (Mûsa) adati: “Koma inu ndinu muponye!” (Choncho adaponya matsengawo). Mwadzidzidzi zingwe zawo ndi ndodo zawo zamatsenga awo, zimaoneka pamaso pake (Mûsa) kuti zikuyenda mothamanga.

  67. فَأَوۡجَسَ فِي نَفۡسِهِۦ خِيفَةٗ مُّوسَىٰ

    Open ayah 20:67

    Ndipo Mûsa adadzazidwa ndi mantha mu mtima mwake.

  68. قُلۡنَا لَا تَخَفۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡأَعۡلَىٰ

    Open ayah 20:68

    Tidati: “Usaope (zomwe ukuzionazi), ndithu iwe ukhala wopambana.”

  69. وَأَلۡقِ مَا فِي يَمِينِكَ تَلۡقَفۡ مَا صَنَعُوٓاْۖ إِنَّمَا صَنَعُواْ كَيۡدُ سَٰحِرٖۖ وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّاحِرُ حَيۡثُ أَتَىٰ

    Open ayah 20:69

    “Ndipo ponya chimene chili kudzanja lako ladzanjadzanja (ndodo); chimeza zomwe apanga; ndithu iwo apanga matsenga a mfiti ndipo mfiti siingapambane paliponse pamene yadza.”[1]

    1. Ibun Kathir adati: Pamene Musa adaponya ndodo idasanduka chinjoka chachikulu chokhala ndi miyendo ndi khosi ndi mutu ndi mano. Chidayamba kutsatira zingwezo ndi ndodozo mpaka chidameza zonsezo uku anthu akuona masomphenya masana. Amatsenga ataona zimenezo, adazindikira mwachitsimikizo kuti kusanduka kwa ndodoyo kukhala chinjoka sikudali kwaufiti kapena matsenga. Koma chidali choonadi chopanda chipeneko. Ndipo pamenepo onse adagwa ndi kulambira Allah. Tero chizizwa cha Allah chidatsimikizika. Koma zopanda pake zidapita pachabe.
  70. فَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سُجَّدٗا قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ هَٰرُونَ وَمُوسَىٰ 

    Open ayah 20:70

    Choncho amatsenga adagwa molambira uku akuti: “Tamkhulupirira Mbuye wa Harun ndi Mûsa.”

  71. قَالَ ءَامَنتُمۡ لَهُۥ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِي عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحۡرَۖ فَلَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفٖ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمۡ فِي جُذُوعِ ٱلنَّخۡلِ وَلَتَعۡلَمُنَّ أَيُّنَآ أَشَدُّ عَذَابٗا وَأَبۡقَىٰ

    Open ayah 20:71

    (Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”[1]

    1. Imam Qurtubi adati: Ndithudi Farawo pa mawu akewa adalinga kuti asokoneze anthu kuti asatsatire amatsengawo kuopera kuti angakhulupirire monga iwo adakhulupilira.
  72. قَالُواْ لَن نُّؤۡثِرَكَ عَلَىٰ مَا جَآءَنَا مِنَ ٱلۡبَيِّنَٰتِ وَٱلَّذِي فَطَرَنَاۖ فَٱقۡضِ مَآ أَنتَ قَاضٍۖ إِنَّمَا تَقۡضِي هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَآ

    Open ayah 20:72

    (Amatsenga) adati: “Sitisankha iwe kusiya zomwe zatidzera; zisonyezo zachoonadi zoonekera poyera! Ndipo tikumlumbilira Yemwe adatilenga, (sitikusankha iwe), chita zomwe ufuna kuchita; ndithu iwe utha kupititsa chiweruzo chokhudzana ndi moyo uno wapansi, basi.”

  73. إِنَّآ ءَامَنَّا بِرَبِّنَا لِيَغۡفِرَ لَنَا خَطَٰيَٰنَا وَمَآ أَكۡرَهۡتَنَا عَلَيۡهِ مِنَ ٱلسِّحۡرِۗ وَٱللَّهُ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰٓ

    Open ayah 20:73

    “Ndithu takhulupirira Mbuye wathu kuti atikhululukire zolakwa zathu ndi matsenga amene watikakamiza (kuchita); ndipo Allah ndi Yemwe ali Wabwino ndi Wamuyaya (osati iwe).”

  74. إِنَّهُۥ مَن يَأۡتِ رَبَّهُۥ مُجۡرِمٗا فَإِنَّ لَهُۥ جَهَنَّمَ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحۡيَىٰ

    Open ayah 20:74

    Ndithu amene adzadze kwa Mbuye wake uku ali wamachimo, adzapeza moto wa Jahannam; sadzafa m’menemo, ndipo sadzakhalanso ndi moyo wabwino.

  75. وَمَن يَأۡتِهِۦ مُؤۡمِنٗا قَدۡ عَمِلَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلدَّرَجَٰتُ ٱلۡعُلَىٰ

    Open ayah 20:75

    Koma amene adzamdzera uku ali wokhulupirira, yemwe adachita ntchito zabwino, iwo ndi amene adzapeze ulemewero wapamwamba.

  76. جَنَّٰتُ عَدۡنٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ وَذَٰلِكَ جَزَآءُ مَن تَزَكَّىٰ

    Open ayah 20:76

    Minda yamuyaya, yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) pakuyenda mitsinje. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali. Ndipo zimenezo ndi mphoto za yemwe wadziyeretsa.

  77. وَلَقَدۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَسۡرِ بِعِبَادِي فَٱضۡرِبۡ لَهُمۡ طَرِيقٗا فِي ٱلۡبَحۡرِ يَبَسٗا لَّا تَخَٰفُ دَرَكٗا وَلَا تَخۡشَىٰ

    Open ayah 20:77

    Ndipo ndithu Mûsa tidamtumizira chivumbulutso, (tidamzindikiritsa kuti): “Yenda usiku ndi akapolo Anga (kutuluka m’dziko la Iguputo,) ndipo ukawapangire panyanja njira youma, ndipo usaope kukupeza adani ndiponso usaope (kumira).”

  78. فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ بِجُنُودِهِۦ فَغَشِيَهُم مِّنَ ٱلۡيَمِّ مَا غَشِيَهُمۡ

    Open ayah 20:78

    Choncho Farawo pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsata, ndipo m’nyanjamo chidawaphimba chimene chidawaphimba.

  79. وَأَضَلَّ فِرۡعَوۡنُ قَوۡمَهُۥ وَمَا هَدَىٰ

    Open ayah 20:79

    Ndipo Farawo adawasokeretsa anthu ake, ndipo sadawaongolere.

  80. يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ قَدۡ أَنجَيۡنَٰكُم مِّنۡ عَدُوِّكُمۡ وَوَٰعَدۡنَٰكُمۡ جَانِبَ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنَ وَنَزَّلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰ 

    Open ayah 20:80

    E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa.

  81. كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡ وَلَا تَطۡغَوۡاْ فِيهِ فَيَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبِيۖ وَمَن يَحۡلِلۡ عَلَيۡهِ غَضَبِي فَقَدۡ هَوَىٰ

    Open ayah 20:81

    Idyani zinthu zabwino zomwe takupatsani, ndipo musapyole malire pa zimenezo kuti mkwiyo Wanga usakutsikireni; ndipo amene mkwiyo Wanga wamtsikira, ndiye kuti ameneyo waonongeka.

  82. وَإِنِّي لَغَفَّارٞ لِّمَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا ثُمَّ ٱهۡتَدَىٰ

    Open ayah 20:82

    Ndipo ndithu Ine ndi Wokhululuka kwambiri kwa amene walapa ndi kukhulupirira, ndikuchita ntchito zabwino, kenako ndikutsata chiongoko mwaubwino.

  83. ۞وَمَآ أَعۡجَلَكَ عَن قَوۡمِكَ يَٰمُوسَىٰ

    Open ayah 20:83

    “Nchiyani chakufulumizitsa (kudza kuno) kusiya anthu ako, E, iwe Mûsa?”[1]

    1. Imam Zamakhshari adati: “Musa pamodzi ndi nthumwi zomwe adazisankha zochokera mwa anthu ake, adamka ku phiri monga panyengo yomwe idaikidwa. Kenako iye adatsogola nasiya m’buyo anthu chifukwa chakhumbo ndi kufunitsitsa kumva mawu a Mbuye wake.”
  84. قَالَ هُمۡ أُوْلَآءِ عَلَىٰٓ أَثَرِي وَعَجِلۡتُ إِلَيۡكَ رَبِّ لِتَرۡضَىٰ

    Open ayah 20:84

    Adati: “Iwo ali pambuyo panga akunditsata. Ndachita changu kudza kwa Inu, Mbuye wanga, kuti mundiyanje kwambiri.”

  85. قَالَ فَإِنَّا قَدۡ فَتَنَّا قَوۡمَكَ مِنۢ بَعۡدِكَ وَأَضَلَّهُمُ ٱلسَّامِرِيُّ

    Open ayah 20:85

    (Allah) adati: “Ndithu Ife tawayesa Mmayeso anthu ako pambuyo pako; tero Samiriyyu wawasokeretsa.”[1]

    1. Samiriyyu ameneyu adali wamatsenga, wachiphamaso (munafiq), wochokera ku mtundu wa anthu opembedza ng’ombe.
  86. فَرَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ غَضۡبَٰنَ أَسِفٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَمۡ يَعِدۡكُمۡ رَبُّكُمۡ وَعۡدًا حَسَنًاۚ أَفَطَالَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡعَهۡدُ أَمۡ أَرَدتُّمۡ أَن يَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبٞ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَخۡلَفۡتُم مَّوۡعِدِي

    Open ayah 20:86

    Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya ndi wodandaula. Adati: “E inu anthu anga! Kodi Mbuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kapena nyengo yalonjezolo idatalika kwa inu? Kapena mudafuna kuti mkwiyo ukutsikireni kuchokera kwa Mbuye wanu; tero mwaswa lonjezo langa”?

  87. قَالُواْ مَآ أَخۡلَفۡنَا مَوۡعِدَكَ بِمَلۡكِنَا وَلَٰكِنَّا حُمِّلۡنَآ أَوۡزَارٗا مِّن زِينَةِ ٱلۡقَوۡمِ فَقَذَفۡنَٰهَا فَكَذَٰلِكَ أَلۡقَى ٱلسَّامِرِيُّ

    Open ayah 20:87

    (Iwo) adati: “Sitidaswe lonjezo lako mwachifuniro chathu; koma tidasenzetsedwa mitolo ya zodzikometsera za anthu (ziwiya zagolide zomwe tidabwereka kwa akazi a chimisiri), ndipo tidaziponya (pa moto, ndipo zidasungunuka ndikupangidwa mwana wang’ombe.) Ndipo momwemonso Samiriyyu adaponya.”

  88. فَأَخۡرَجَ لَهُمۡ عِجۡلٗا جَسَدٗا لَّهُۥ خُوَارٞ فَقَالُواْ هَٰذَآ إِلَٰهُكُمۡ وَإِلَٰهُ مُوسَىٰ فَنَسِيَ

    Open ayah 20:88

    Ndipo adawatulutsira (kuchokera m’golide wosungunukayo) mwana wang’ombe wokhala ndi thupi lokwanira, yemwe amatulutsa mawu (ngati kulira kwa ng’ombe), (iwo) adati: “Uyu ndi mulungu wanu ndiponso mulungu wa Mûsa, koma (Mûsa) wamuiwala, (choncho wapita kukamfuna ku phiri)!”

  89. أَفَلَا يَرَوۡنَ أَلَّا يَرۡجِعُ إِلَيۡهِمۡ قَوۡلٗا وَلَا يَمۡلِكُ لَهُمۡ ضَرّٗا وَلَا نَفۡعٗا

    Open ayah 20:89

    Kodi sadaone kuti (mwana wang’ombe) sabweza mawu kwa iwo, ndiponso sangathe kudzetsa matsautso kwa iwo ngakhale zothandiza.

  90. وَلَقَدۡ قَالَ لَهُمۡ هَٰرُونُ مِن قَبۡلُ يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا فُتِنتُم بِهِۦۖ وَإِنَّ رَبَّكُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَٱتَّبِعُونِي وَأَطِيعُوٓاْ أَمۡرِي 

    Open ayah 20:90

    Ndipo ndithu Harun adawauza kale (kuti): “E inu anthu anga! Ndithu inu mwasokonezeka ndi (chinthu) ichi. Ndithu Mbuye wanu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; choncho nditsateni, ndipo mverani lamulo langa, (siyani kupembedza fano ili).”

  91. قَالُواْ لَن نَّبۡرَحَ عَلَيۡهِ عَٰكِفِينَ حَتَّىٰ يَرۡجِعَ إِلَيۡنَا مُوسَىٰ

    Open ayah 20:91

    (Iwo) adati: “Sitisiya ngakhale pang’ono kumpembedza. Kufikira Mûsa abwelere kwa ife.”

  92. قَالَ يَٰهَٰرُونُ مَا مَنَعَكَ إِذۡ رَأَيۡتَهُمۡ ضَلُّوٓاْ

    Open ayah 20:92

    (Pamene Mûsa adabwerera) adati: “E iwe Harun! Nchiyani chidakuletsa pamene udawaona atasokera,”

  93. أَلَّا تَتَّبِعَنِۖ أَفَعَصَيۡتَ أَمۡرِي

    Open ayah 20:93

    Kuti usanditsate? Udanyozera lamulo langa?”

  94. قَالَ يَبۡنَؤُمَّ لَا تَأۡخُذۡ بِلِحۡيَتِي وَلَا بِرَأۡسِيٓۖ إِنِّي خَشِيتُ أَن تَقُولَ فَرَّقۡتَ بَيۡنَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَمۡ تَرۡقُبۡ قَوۡلِي

    Open ayah 20:94

    (Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”

  95. قَالَ فَمَا خَطۡبُكَ يَٰسَٰمِرِيُّ

    Open ayah 20:95

    (Mûsa) adati: “E iwe Samiriyyu! Nchiyani wachita?”

  96. قَالَ بَصُرۡتُ بِمَا لَمۡ يَبۡصُرُواْ بِهِۦ فَقَبَضۡتُ قَبۡضَةٗ مِّنۡ أَثَرِ ٱلرَّسُولِ فَنَبَذۡتُهَا وَكَذَٰلِكَ سَوَّلَتۡ لِي نَفۡسِي

    Open ayah 20:96

    (Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”[1]

    1. Samiriyyu adaona Gabrieli ali kudza kwa Musa atakwera hatchi. Choncho adakondwera mu mtima mwake kutapa mapazi ake. Tero ankati akaponya zomwe adatapazo pa chinthu chilichonse chakufa chinkauka. Ndipo pamene fano la mwana wang’ombe lidakonzedwa, iye adatenga dothi la mapazi a mthengayo nkuponya pa fanolo. Choncho fanolo lidayamba kutulutsa mawu ngati mwana wa ng’ombe.
  97. قَالَ فَٱذۡهَبۡ فَإِنَّ لَكَ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ أَن تَقُولَ لَا مِسَاسَۖ وَإِنَّ لَكَ مَوۡعِدٗا لَّن تُخۡلَفَهُۥۖ وَٱنظُرۡ إِلَىٰٓ إِلَٰهِكَ ٱلَّذِي ظَلۡتَ عَلَيۡهِ عَاكِفٗاۖ لَّنُحَرِّقَنَّهُۥ ثُمَّ لَنَنسِفَنَّهُۥ فِي ٱلۡيَمِّ نَسۡفًا

    Open ayah 20:97

    (Mûsa) adati: “ Choka, ndithu pa iwe (pali chilango) pa moyo (wako) choti uzingonena (kuti): “Musandikhudze musandikhudze.” (Ndipo palibe amene adzakuyandikira ndipo iwe sudzayandikira aliyense). Ndithu pa iwe pali lonjezo la (Allah) losaswedwa; ndipo muyang’ane mulungu wako, yemwe wakhala ukupitiriza kumpembedza. Timtentha, kenako chipala chakecho tichimwaza m’nyanja.

  98. إِنَّمَآ إِلَٰهُكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ وَسِعَ كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمٗا

    Open ayah 20:98

    Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire).

  99. كَذَٰلِكَ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ مَا قَدۡ سَبَقَۚ وَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ مِن لَّدُنَّا ذِكۡرٗا

    Open ayah 20:99

    Umo ndi momwe tikukusimbira nkhani za (zinthu) zomwe zidatsogola (za aneneri). Ndithu takupatsa uthenga waukulu kuchokera kwa Ife (omwe ndi Qur’an).

  100. مَّنۡ أَعۡرَضَ عَنۡهُ فَإِنَّهُۥ يَحۡمِلُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وِزۡرًا 

    Open ayah 20:100

    Amene aunyozere, ndithu iye tsiku la Qiyâma adzasenza mitolo (ya machimo).

  101. خَٰلِدِينَ فِيهِۖ وَسَآءَ لَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ حِمۡلٗا 

    Open ayah 20:101

    Adzakhala m’menemo m’chilango. Ndipo ndi zoipa zedi (kwa anthu) kusenza mitolo (imeneyo) tsiku la Qiyâma,

  102. يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِۚ وَنَحۡشُرُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ يَوۡمَئِذٖ زُرۡقٗا 

    Open ayah 20:102

    (Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha).

  103. يَتَخَٰفَتُونَ بَيۡنَهُمۡ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا عَشۡرٗا 

    Open ayah 20:103

    Adzanong’onezana pakati pawo (ponena kuti): “Simudakhalitse pa dziko lapansi koma masiku khumi okha basi.”

  104. نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَقُولُونَ إِذۡ يَقُولُ أَمۡثَلُهُمۡ طَرِيقَةً إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا يَوۡمٗا 

    Open ayah 20:104

    Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”

  105. وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡجِبَالِ فَقُلۡ يَنسِفُهَا رَبِّي نَسۡفٗا 

    Open ayah 20:105

    Ndipo akukufunsa zamapiri (kuti adzatani tsiku la Qiyâma); auze: “Mbuye wanga adzawagumulagumula ndikuwaululutsa (ngati fumbi).”

  106. فَيَذَرُهَا قَاعٗا صَفۡصَفٗا 

    Open ayah 20:106

    “Ndipo adzaisiya (nthaka yonse) ngati bwalo losalazidwa myaa!”

  107. لَّا تَرَىٰ فِيهَا عِوَجٗا وَلَآ أَمۡتٗا 

    Open ayah 20:107

    “Sudzaona kukhota m’menemo ngakhale chitunda (chikweza).”

  108. يَوۡمَئِذٖ يَتَّبِعُونَ ٱلدَّاعِيَ لَا عِوَجَ لَهُۥۖ وَخَشَعَتِ ٱلۡأَصۡوَاتُ لِلرَّحۡمَٰنِ فَلَا تَسۡمَعُ إِلَّا هَمۡسٗا 

    Open ayah 20:108

    Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi).

  109. يَوۡمَئِذٖ لَّا تَنفَعُ ٱلشَّفَٰعَةُ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَرَضِيَ لَهُۥ قَوۡلٗا 

    Open ayah 20:109

    Tsiku limenelo chiombolo (cha aliyense) sichidzathandiza, kupatula yemwe wapatsidwa chilolezo ndi (Allah) Wachifundo chambiri, ndi kumuyanja kuti alankhule.

  110. يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَلَا يُحِيطُونَ بِهِۦ عِلۡمٗا 

    Open ayah 20:110

    (Allah) akudziwa za patsogolo pawo ndi zapambuyo pawo. Ndipo iwo sangathe kumzindikira (Allah) mmene alili.

  111. ۞وَعَنَتِ ٱلۡوُجُوهُ لِلۡحَيِّ ٱلۡقَيُّومِۖ وَقَدۡ خَابَ مَنۡ حَمَلَ ظُلۡمٗا

    Open ayah 20:111

    Ndipo nkhope (tsiku limenelo) zidzalobodoka pamaso pa (Allah) Wamoyo wamuyaya, Wochita chilichonse. Ndithu adzataika kwathunthu yense wochita zosalungama.

  112. وَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَلَا يَخَافُ ظُلۡمٗا وَلَا هَضۡمٗا

    Open ayah 20:112

    Ndipo amene achite zabwino uku ali wokhulupirira, sadzaopa kuchitiridwa zoipa kapena kumchepetsera (choyenera chake).

  113. وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا وَصَرَّفۡنَا فِيهِ مِنَ ٱلۡوَعِيدِ لَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ أَوۡ يُحۡدِثُ لَهُمۡ ذِكۡرٗا

    Open ayah 20:113

    Ndipo momwemo taivumbulutsa (Qur’an) m’Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mwatsatanetsatane za machenjezo (amtundu uliwonse), kuti aope (Allah), ndikuti nthawi iliyonse (Qur’aniyo), iwapatse chikumbutso chatsopano.

  114. فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلۡمَلِكُ ٱلۡحَقُّۗ وَلَا تَعۡجَلۡ بِٱلۡقُرۡءَانِ مِن قَبۡلِ أَن يُقۡضَىٰٓ إِلَيۡكَ وَحۡيُهُۥۖ وَقُل رَّبِّ زِدۡنِي عِلۡمٗا

    Open ayah 20:114

    Chomwecho watukuka Allah, Mfumu ya choonadi, ndipo usaifulumizitse Qur’an (powerenga) chivumbulutso chake chisanamalizike kwa iwe, ndipo nena (popempha) kuti: “Mbuye wanga! Ndionjezereni nzeru (kuzindikira).”

  115. وَلَقَدۡ عَهِدۡنَآ إِلَىٰٓ ءَادَمَ مِن قَبۡلُ فَنَسِيَ وَلَمۡ نَجِدۡ لَهُۥ عَزۡمٗا

    Open ayah 20:115

    Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa).

  116. وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰ

    Open ayah 20:116

    Ndipo (kumbukirani) pamene tidauza angelo: “Muchitireni sajida (mugwadireni momulemekeza) Adam,” dipo adachita Sajida kupatula Iblis, adakana.

  117. فَقُلۡنَا يَٰٓـَٔادَمُ إِنَّ هَٰذَا عَدُوّٞ لَّكَ وَلِزَوۡجِكَ فَلَا يُخۡرِجَنَّكُمَا مِنَ ٱلۡجَنَّةِ فَتَشۡقَىٰٓ

    Open ayah 20:117

    Tsono tidati: “E iwe Adam! Ndithu uyu ndi mdani wako iwe ndi mkazi wako; choncho asakutulutseni m’Munda wamtendere, mungadzavutike.”

  118. إِنَّ لَكَ أَلَّا تَجُوعَ فِيهَا وَلَا تَعۡرَىٰ

    Open ayah 20:118

    “Ndithu iwe sumva njala m’menemo ndipo sukhala wamaliseche.”

  119. وَأَنَّكَ لَا تَظۡمَؤُاْ فِيهَا وَلَا تَضۡحَىٰ

    Open ayah 20:119

    “Ndipo iwe sumva ludzu m’menemo, ndiponso sumva kutentha (kwa dzuwa).”

  120. فَوَسۡوَسَ إِلَيۡهِ ٱلشَّيۡطَٰنُ قَالَ يَٰٓـَٔادَمُ هَلۡ أَدُلُّكَ عَلَىٰ شَجَرَةِ ٱلۡخُلۡدِ وَمُلۡكٖ لَّا يَبۡلَىٰ 

    Open ayah 20:120

    Koma satana (adamsokoneza) pomunong’oneza (zoipa) adati: “E iwe Adam! Kodi ndikusonyeze mtengo wamuyaya ndi (wopatsa) ufumu wosatha?”[1]

    1. Satana wotembeleredwa adanena kwa iye m’njira yachinyengo kuti: “Kodi iwe Adam, ndikusonyeze mtengo wakuti amene wadya zipatso zake, adzakhala muyaya wosafa ndikupeza ufumu wonkerankera mtsogolo, wosatha? Umo ndi momwe zidaliri ndale za satana. Sizidali zomufunira zabwino Adam, koma kumuononga.
  121. فَأَكَلَا مِنۡهَا فَبَدَتۡ لَهُمَا سَوۡءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخۡصِفَانِ عَلَيۡهِمَا مِن وَرَقِ ٱلۡجَنَّةِۚ وَعَصَىٰٓ ءَادَمُ رَبَّهُۥ فَغَوَىٰ

    Open ayah 20:121

    Ndipo (onse awiri) adaudya, ndipo umaliseche wawo awiriwo udaonekera poyera; ndipo adayamba kudziphatika masamba a m’mundamo; ndipo Adam adalakwira Mbuye wake, choncho adasokera.

  122. ثُمَّ ٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَتَابَ عَلَيۡهِ وَهَدَىٰ

    Open ayah 20:122

    Kenako Mbuye wake adamsankha pomulandira kulapa kwake ndikumuongola.

  123. قَالَ ٱهۡبِطَا مِنۡهَا جَمِيعَۢاۖ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوّٞۖ فَإِمَّا يَأۡتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدٗى فَمَنِ ٱتَّبَعَ هُدَايَ فَلَا يَضِلُّ وَلَا يَشۡقَىٰ

    Open ayah 20:123

    (Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”

  124. وَمَنۡ أَعۡرَضَ عَن ذِكۡرِي فَإِنَّ لَهُۥ مَعِيشَةٗ ضَنكٗا وَنَحۡشُرُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَعۡمَىٰ

    Open ayah 20:124

    Ndipo amene anyozere ulaliki wanga, ndithu moyo wamavuto udzakhala pa iye ndipo tidzamuukitsa m’manda tsiku la chimaliziro ali wakhungu.”

  125. قَالَ رَبِّ لِمَ حَشَرۡتَنِيٓ أَعۡمَىٰ وَقَدۡ كُنتُ بَصِيرٗا

    Open ayah 20:125

    Adzanena: “Mbuye wanga! Chifukwa ninji mwandiukitsa ndili wakhungu, pomwe ndidali wopenya?”

  126. قَالَ كَذَٰلِكَ أَتَتۡكَ ءَايَٰتُنَا فَنَسِيتَهَاۖ وَكَذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمَ تُنسَىٰ

    Open ayah 20:126

    (Allah) adzanena: “Zimenezo nchifukwa chakuti zidakudzera Ayah zathu koma udaziiwala (chifukwa chosalabadira), momwemo lero uiwalidwa, (salabadilidwa).”

  127. وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَنۡ أَسۡرَفَ وَلَمۡ يُؤۡمِنۢ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦۚ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَشَدُّ وَأَبۡقَىٰٓ

    Open ayah 20:127

    Ndipo umo ndimomwe tidzamulipirire aliyense wopyola malire, wosakhulupirira Ayah za Mbuye wake. Ndipo chilango cha tsiku la chimaliziro nchaukali, ndiponso chamuyaya.

  128. أَفَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ

    Open ayah 20:128

    Kodi sizidadziwikebe kwa iwo kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo awa (osakhulupirira atsopano) akuyenda m’malo awo, (kodi saona zizindikiro zakuonongeka kwawo)? Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru.

  129. وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَكَانَ لِزَامٗا وَأَجَلٞ مُّسَمّٗى

    Open ayah 20:129

    Ndipo pakadapanda liwu lomwe lidatsogola kuchokera kwa Mbuye wako (lochedwetsera chilango) ndi nthawi yomwe idaikidwa, ndithu (chilango) chikadawafika (tsopano lomwe lino.)

  130. فَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ قَبۡلَ طُلُوعِ ٱلشَّمۡسِ وَقَبۡلَ غُرُوبِهَاۖ وَمِنۡ ءَانَآيِٕ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡ وَأَطۡرَافَ ٱلنَّهَارِ لَعَلَّكَ تَرۡضَىٰ 

    Open ayah 20:130

    Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma).

  131. وَلَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجٗا مِّنۡهُمۡ زَهۡرَةَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا لِنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَرِزۡقُ رَبِّكَ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰ

    Open ayah 20:131

    Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.

  132. وَأۡمُرۡ أَهۡلَكَ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱصۡطَبِرۡ عَلَيۡهَاۖ لَا نَسۡـَٔلُكَ رِزۡقٗاۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكَۗ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلتَّقۡوَىٰ

    Open ayah 20:132

    Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah).

  133. وَقَالُواْ لَوۡلَا يَأۡتِينَا بِـَٔايَةٖ مِّن رَّبِّهِۦٓۚ أَوَلَمۡ تَأۡتِهِم بَيِّنَةُ مَا فِي ٱلصُّحُفِ ٱلۡأُولَىٰ

    Open ayah 20:133

    Ndipo (osakhulupirira) adanena: “Chifukwa ninji sakutibweretsera chizizwa kuchokera kwa Mbuye wake?” Kodi sudawafike umboni woonekera wa zomwe zili m’mabuku akale? (Kodi sadakhutitsidwe ndi Qur’an chomwe ndi chizizwa chachikulu).”

  134. وَلَوۡ أَنَّآ أَهۡلَكۡنَٰهُم بِعَذَابٖ مِّن قَبۡلِهِۦ لَقَالُواْ رَبَّنَا لَوۡلَآ أَرۡسَلۡتَ إِلَيۡنَا رَسُولٗا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ مِن قَبۡلِ أَن نَّذِلَّ وَنَخۡزَىٰ

    Open ayah 20:134

    Ndipo ngati tikadawaononga ndi chilango, asanadze uyo (Mtumiki), akadanena: “Mbuye wathu! Bwanji osatitumizira mtumiki kuti titsate Ayah Zanu tisanayaluke ndi kunyozeka?”

  135. قُلۡ كُلّٞ مُّتَرَبِّصٞ فَتَرَبَّصُواْۖ فَسَتَعۡلَمُونَ مَنۡ أَصۡحَٰبُ ٱلصِّرَٰطِ ٱلسَّوِيِّ وَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ

    Open ayah 20:135

    Nena: “Aliyense (wa ife) akuyembekezera (mphoto yake); choncho yembekezerani. Posachedwapa mudziwa kuti kodi ndani mwini njira yolingana, ndipo ndani amene waongoka.”