مريم
Maryam
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
كٓهيعٓصٓ
Open ayah 19:1Kâf-Hâ-Yâ- ‘Aîn-Sâd.
ذِكۡرُ رَحۡمَتِ رَبِّكَ عَبۡدَهُۥ زَكَرِيَّآ
Open ayah 19:2Ichi (ndi) chikumbutso cha chifundo cha Mbuye wako pa kapolo Wake Zakariya.
إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ نِدَآءً خَفِيّٗا
Open ayah 19:3Pamene adaitana Mbuye wake, kuitana kwa chinsinsi.
قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ ٱلۡعَظۡمُ مِنِّي وَٱشۡتَعَلَ ٱلرَّأۡسُ شَيۡبٗا وَلَمۡ أَكُنۢ بِدُعَآئِكَ رَبِّ شَقِيّٗا
Open ayah 19:4Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu mafupa anga afooka, ndipo mutu wanga wayaka (ukung’anima) ndi imvi; sindidali watsoka pokupemphani Mbuye wanga (koma nthawi iliyonse ndikakupemphani mumandivomereza)[1]
- Apa tanthauzo lake nkuti: “E Mbuye wanga! Palibe pamene mudalitaya pachabe pempho langa koma mudandizoloweza kuti ndikakupemphani mumandipatsa zomwe ndapempha. Choncho yankhaninso pempho langali.”
وَإِنِّي خِفۡتُ ٱلۡمَوَٰلِيَ مِن وَرَآءِي وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا فَهَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيّٗا
Open ayah 19:5“Ndipo ndithu ine ndikuopera abale anga (kuononga chipembedzo) pambuyo panga; ndipo mkazi wanga ndi chumba; choncho ndipatseni (mwana) mlowammalo wanga wochokera kwa Inu.”
يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنۡ ءَالِ يَعۡقُوبَۖ وَٱجۡعَلۡهُ رَبِّ رَضِيّٗا
Open ayah 19:6“Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)”
يَٰزَكَرِيَّآ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ ٱسۡمُهُۥ يَحۡيَىٰ لَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ مِن قَبۡلُ سَمِيّٗا
Open ayah 19:7(Adauzidwa): “E iwe Zakariya! Ife tikukuuza nkhani yabwino yakuti ubereka mwana dzina lake Yahya palibe patsogolo pake amene tidamutcha dzina longa lake.”
قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا وَقَدۡ بَلَغۡتُ مِنَ ٱلۡكِبَرِ عِتِيّٗا
Open ayah 19:8(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingapeze bwanji mwana pomwe mkazi wanga ndi nkhalamba yosabereka ndipo ine ndafikanso pa ukulu wopyola muyeso?”
قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞ وَقَدۡ خَلَقۡتُكَ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ تَكُ شَيۡـٔٗا
Open ayah 19:9Adati: “Ndimomwemo. Mbuye wako wanena (kuti): ‘Izi nzofewa kwa Ine; ndithu ndidakulenga kale pomwe iwe sudali kanthu.”
قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةٗۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَ لَيَالٖ سَوِيّٗا
Open ayah 19:10Adati: “Mbuye wanga ndipatseni chizindikiro (chodziwitsa kuti mkazi wanga ali ndi pakati).” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu pomwe iwe uli bwinobwino.”
فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنَ ٱلۡمِحۡرَابِ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ أَن سَبِّحُواْ بُكۡرَةٗ وَعَشِيّٗا
Open ayah 19:11Ndipo adatuluka kuchipinda chopemphelera ndikuonekera kwa anthu ake, ndipo adawalozera (pomwe sadathe kuyankhula) kuti: “Lemekezani Allah m’mawa ndi madzulo.”
يَٰيَحۡيَىٰ خُذِ ٱلۡكِتَٰبَ بِقُوَّةٖۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحُكۡمَ صَبِيّٗا
Open ayah 19:12“E iwe Yahya! Gwira buku ili mwamphamvu (ndi mwachidwi).” Ndipo tidampatsa nzeru ali mwana.
وَحَنَانٗا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَوٰةٗۖ وَكَانَ تَقِيّٗا
Open ayah 19:13Ndi chisoni chochokera kwa Ife ndi kumuyeretsa (mwanayo), ndipo adali woopa (Allah).
وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَيۡهِ وَلَمۡ يَكُن جَبَّارًا عَصِيّٗا
Open ayah 19:14Komanso wochitira zabwino makolo ake ndipo sadali wodzitukumula (kwa anthu) kapena kunyoza (Allah).
وَسَلَٰمٌ عَلَيۡهِ يَوۡمَ وُلِدَ وَيَوۡمَ يَمُوتُ وَيَوۡمَ يُبۡعَثُ حَيّٗا
Open ayah 19:15Ndipo mtendere wa Allah udali pa iye kuyambira tsiku lomwe adabadwa ndi tsiku lomwe adamwalira, ndi tsiku limene adzaukitsidwa ku imfa kukhala wamoyo.
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَرۡيَمَ إِذِ ٱنتَبَذَتۡ مِنۡ أَهۡلِهَا مَكَانٗا شَرۡقِيّٗا
Open ayah 19:16Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa.[1]
- M’sura iyi muli nkhani zododometsa. Yoyamba njakubadwa kwa Yahya (Yohane) yemwe adabadwa kuchokera kwa nkhalamba ziwiri zotheratu; pomwe mwamuna adali ndi zaka 120 ndipo mkazi adali ndi zaka 98. Choncho kubadwa kwa Yahya kudali kododometsa. Koma kubadwa kwa Isa (Yesu) ndikumene kudali kododometsa zedi poti iye anabadwa kwa namwali wosakwatiwa. Tero iye anamubereka popanda mwamuna. Zonsezi Allah adafuna kuwadziwitsa anthu ndi kuwatsimikizira kuti Iye ali ndi mphamvu zolengera munthu popanda mwamuna.
فَٱتَّخَذَتۡ مِن دُونِهِمۡ حِجَابٗا فَأَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرٗا سَوِيّٗا
Open ayah 19:17Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni.
قَالَتۡ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيّٗا
Open ayah 19:18(Mariya) adati: “Ndithu ndikudzichinjiriza ndi (Allah) Mwini chifundo chambiri, kwa iwe ngati umaopa (Allah).”
قَالَ إِنَّمَآ أَنَا۠ رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَٰمٗا زَكِيّٗا
Open ayah 19:19(Mngelo) adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa mbuye wako, (ndadza) kuti ndikupatse mwana woyera.”
قَالَتۡ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَلَمۡ يَمۡسَسۡنِي بَشَرٞ وَلَمۡ أَكُ بَغِيّٗا
Open ayah 19:20Adati: “Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe sadandikhudze mwamuna (aliyense), ndipo ine sindili (mkazi) wachiwerewere?”
قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةٗ لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةٗ مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرٗا مَّقۡضِيّٗا
Open ayah 19:21(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”
۞فَحَمَلَتۡهُ فَٱنتَبَذَتۡ بِهِۦ مَكَانٗا قَصِيّٗا
Open ayah 19:22Choncho adatenga pakati pake, ndipo adachoka ndi pakatipo kunka kumalo akutali.[1]
- Izi zidachitika pamene Gabriele adauzira m’thumba la chovala cha Mariya. Ndipo mpweya udafika mpaka m’mimba mwake. Choncho atakhala ndi pakati anadzipatula kwa anthu kunka kutali ali ndi pakati pa mwana wakeyo kuti anthu angamdzudzule pokhala ndi mimba yosadziwika mwamuna wake.
فَأَجَآءَهَا ٱلۡمَخَاضُ إِلَىٰ جِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ قَالَتۡ يَٰلَيۡتَنِي مِتُّ قَبۡلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسۡيٗا مَّنسِيّٗا
Open ayah 19:23Ndipo matenda auchembere (atakwana), adampititsa ku thunthu la mtengo wa kanjedza (wouma kuti awutsamire pomubala mwanayo) adati: “Kalanga ine! Ndiponi ndikadafa izi zisanachitike ndikadakhala nditaiwalidwa ndithu.”
فَنَادَىٰهَا مِن تَحۡتِهَآ أَلَّا تَحۡزَنِي قَدۡ جَعَلَ رَبُّكِ تَحۡتَكِ سَرِيّٗا
Open ayah 19:24Kenaka (Mngelo) adamuitana kuchokera chapansi pake (kumuuza kuti): “Usadandaule. Ndithu Mbuye wako wakupangira kamtsinje pansi pako.”
وَهُزِّيٓ إِلَيۡكِ بِجِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ تُسَٰقِطۡ عَلَيۡكِ رُطَبٗا جَنِيّٗا
Open ayah 19:25Ndipo ligwedezere kumbali yako thunthu la mtengo wakanjedza (woumawo), zipatso zabwino zakupsa zikugwera.”[1]
- Omasulira adati: Adamulamula kuti agwedeze thunthu lamtengo wouma kuti aone chizizwa chachiwiri mtengo wouma pokhala wauwisi ndikubereka zipatso nthawi yomweyo zakupsa. Adamuonetsanso kasupe wamadzi okoma yemwe anafwamphuka uku iye akuona. Ndipo iye adali kudya zipatsozo nkumamwera madziwo. Uku kudali kumulimbikitsa mtima kuti asade nkhawa pokhala ndi mwana wopanda tate wake koma zonsezi wazichita ndi Allah.
فَكُلِي وَٱشۡرَبِي وَقَرِّي عَيۡنٗاۖ فَإِمَّا تَرَيِنَّ مِنَ ٱلۡبَشَرِ أَحَدٗا فَقُولِيٓ إِنِّي نَذَرۡتُ لِلرَّحۡمَٰنِ صَوۡمٗا فَلَنۡ أُكَلِّمَ ٱلۡيَوۡمَ إِنسِيّٗا
Open ayah 19:26Choncho udye ndi kumwa ndikutonthoza diso lako, (khala ndi mpumulo wabwino). Ndipo ukaona munthu aliyense (akafunsa za mwanayo), nena: “Ndithu ine ndalonjeza kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri kusala kuti lero sindiyankhula ndi munthu aliyense.”
فَأَتَتۡ بِهِۦ قَوۡمَهَا تَحۡمِلُهُۥۖ قَالُواْ يَٰمَرۡيَمُ لَقَدۡ جِئۡتِ شَيۡـٔٗا فَرِيّٗا
Open ayah 19:27Ndipo adadza naye (mwanayo) kwa anthu ake atamnyamula. (Anthu) adati: “E iwe Mariya! Ndithu wabwera ndi chinthu chachikulu; (chododometsa).”
يَٰٓأُخۡتَ هَٰرُونَ مَا كَانَ أَبُوكِ ٱمۡرَأَ سَوۡءٖ وَمَا كَانَتۡ أُمُّكِ بَغِيّٗا
Open ayah 19:28“E iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere.”[1]
- Katada adaati: Haaruna adali munthu wolungama kwambiri mu mtundu wa ana alsraeli. Adali wotchuka kwambiri pazakulungama. Choncho ana a Israeli adaili kufanizira Mariya ndi Haaruna chifukwa cha kulungama kwake; sikuti Mariya adali mlongo wake weniweni wa Haaruna yemwe adali m’bale wa Musa. Pakati pa Mariya ndi Haaruna padapita zaka chikwi chimodzi.
فَأَشَارَتۡ إِلَيۡهِۖ قَالُواْ كَيۡفَ نُكَلِّمُ مَن كَانَ فِي ٱلۡمَهۡدِ صَبِيّٗا
Open ayah 19:29(Mariya sadawayankhe) koma adaloza kwa iye (mwanayo kuti ayankhule naye). Ndipo iwo adati: “Timuyankhula chotani mwana yemwe ali m’chikuta?”
قَالَ إِنِّي عَبۡدُ ٱللَّهِ ءَاتَىٰنِيَ ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلَنِي نَبِيّٗا
Open ayah 19:30(Mwanayo) adanena: “Ine ndine kapolo wa Allah. Wandipatsa buku ndikundichita kukhala Mneneri.”
وَجَعَلَنِي مُبَارَكًا أَيۡنَ مَا كُنتُ وَأَوۡصَٰنِي بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ مَا دُمۡتُ حَيّٗا
Open ayah 19:31“Ndipo wandichita kukhala wodala paliponse pomwe ndili, ndipo wandilamula kuswali ndi kupereka Zakaat pomwe ndili moyo.”
وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَتِي وَلَمۡ يَجۡعَلۡنِي جَبَّارٗا شَقِيّٗا
Open ayah 19:32“Ndipo wandilangiza kuchitira mayi wanga zabwino, ndipo sadandichite kukhala wodzikuza, watsoka (woipa).”
وَٱلسَّلَٰمُ عَلَيَّ يَوۡمَ وُلِدتُّ وَيَوۡمَ أَمُوتُ وَيَوۡمَ أُبۡعَثُ حَيّٗا
Open ayah 19:33“Ndipo mtendere uli pa ine kuyambira tsiku lomwe ndidabadwa ndi tsiku limene ndidzamwalira, ndi tsiku limene ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku la chiweruziro) ndikukhala ndi moyo.”
ذَٰلِكَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَۖ قَوۡلَ ٱلۡحَقِّ ٱلَّذِي فِيهِ يَمۡتَرُونَ
Open ayah 19:34Uyu ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya; (awa ndi) mau owona omwe (Akhrisitu) akuwakaikira.
مَا كَانَ لِلَّهِ أَن يَتَّخِذَ مِن وَلَدٖۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓۚ إِذَا قَضَىٰٓ أَمۡرٗا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Open ayah 19:35Sikoyenera kwa Allah kudzipangira mwana. Iye (Allah) wapatukana ndi zimenezi. Akafuna chinthu, amangonena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo icho chimachitikadi.
وَإِنَّ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
Open ayah 19:36(Isa (Yesu) adati:) “Ndipo ndithu Allah ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu. Choncho mpembedzeni; iyi ndinjira yolunjika (yokufikitsani ku mtendere.)[1]
- Umu ndimomwe Isa (Yesu) adanenera za ukapolo wake kwa Allah. Iye sadali Mulungu kapena mwana wa Mulungu, kapena mmodzi wa atatu monga momwe Akhrisitu amanenera. Koma iye adali kapolo wa Allah ndiponso Mtumiki Wake. Allah adamulenga mwa mayi popanda bambo kuti akhale chisonyezo chosonyeza mphamvu za Allah zoposa.
فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن مَّشۡهَدِ يَوۡمٍ عَظِيمٍ
Open ayah 19:37Koma magulu (a Akhrisitu ndi Ayuda) adapatukana pakati pawo; (ena adamuyesa Isa (Yesu) kuti ndimwana wa Mulungu, ndipo ena adamuyesa Mulungu weniweni, pomwe Ayuda ankati ndi mwana wobadwa m’njira ya chiwerewere), choncho chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene sadakhulupirire pokaonekera tsiku lalikululo (kwa Allah).
أَسۡمِعۡ بِهِمۡ وَأَبۡصِرۡ يَوۡمَ يَأۡتُونَنَا لَٰكِنِ ٱلظَّٰلِمُونَ ٱلۡيَوۡمَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Open ayah 19:38Taona kumvetsetsa kwawo ndi kupenyetsetsa kwawo tsiku lodzatidzera, (kudzanenedwa kuti:) “Koma osalungama lero ali m’kusokera koonekera.”
وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡحَسۡرَةِ إِذۡ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٖ وَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Open ayah 19:39Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira.[1]
- Tsiku la Qiyâma (chimaliziro), anthu oipa adzadandaula kwambiri. Tsiku limenelo kwa iwo lidzakhala tsiku lamadandaulo okhaokha, osatinso chinachake. M’buku la swahihi la Musilim muli hadisi ya Abi Saidi Khuduriyi (r.a). Iye adati: Ndithu Mtumiki (s.a.w) adati: “Pamene anthu olungama adzalowa ku munda wa mtendere ndipo anthu oipa ku Moto, imfa idzadza tsiku la chimalizirolo. Idzaoneka ngati nkhosa yabwino. Ndipo idzaikidwa pakati pa Munda wa mtendere ndi Moto. Tsono kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Kenako kudzanenedwa: “E inu anthu a ku Moto! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi awo kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Ndipo kudzalamulidwa kuti izingidwe. Kenako kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Khalani muyaya m’menemo, palibe imfanso. Ndiponso inu eni Moto khalani muyaya mmenemo palibe imfanso.” Kenako Mtumiki (s.a.w) adawerenga Ayah (ndime) yakuti: “Achenjeze za tsiku lamadandaulo aakulu....”
إِنَّا نَحۡنُ نَرِثُ ٱلۡأَرۡضَ وَمَنۡ عَلَيۡهَا وَإِلَيۡنَا يُرۡجَعُونَ
Open ayah 19:40Ndithu Ife Tidzaitenga nthaka ndi amene ali pamenepo; (zonse zidzakhala za Ife) ndipo kwa Ife adzabwerera.
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِبۡرَٰهِيمَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقٗا نَّبِيًّا
Open ayah 19:41Ndipo mtchule m’buku ili, Ibrahim. Ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri.
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ لِمَ تَعۡبُدُ مَا لَا يَسۡمَعُ وَلَا يُبۡصِرُ وَلَا يُغۡنِي عَنكَ شَيۡـٔٗا
Open ayah 19:42(Akumbutse) pamene iye adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Bwanji mukupembedza zomwe sizimva ndiponso sizipenya, ndiponso Zosakupindulitsani chilichonse?”
يَٰٓأَبَتِ إِنِّي قَدۡ جَآءَنِي مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَمۡ يَأۡتِكَ فَٱتَّبِعۡنِيٓ أَهۡدِكَ صِرَٰطٗا سَوِيّٗا
Open ayah 19:43“E inu bambo wanga! Ndithu ine zandidzera nzeru (zomuzindikira Allah) zomwe sizidakudzereni; choncho nditsateni. Ndikutsogolereni ku njira yolungama.”
يَٰٓأَبَتِ لَا تَعۡبُدِ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ عَصِيّٗا
Open ayah 19:44“E bambo wanga! Musapembedze satana (potsatira malangizo ake). Ndithu satana ngopandukira (Allah) Mwini chifundo chambiri.”
يَٰٓأَبَتِ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يَمَسَّكَ عَذَابٞ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ فَتَكُونَ لِلشَّيۡطَٰنِ وَلِيّٗا
Open ayah 19:45E bambo wanga! Ndithu ine ndikuopa kuti chilango chingakukhudzeni chochokera kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri, ndipo potero mdzakhala bwenzi la satana.”
قَالَ أَرَاغِبٌ أَنتَ عَنۡ ءَالِهَتِي يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ لَأَرۡجُمَنَّكَۖ وَٱهۡجُرۡنِي مَلِيّٗا
Open ayah 19:46(Bambo wake) adati: “Kodi iwe ukuda milungu yanga, E iwe Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza milungu yanga) ndikugenda ndi miyala; choncho ndichokere kwa nthawi yaitali (tisaonanenso).”
قَالَ سَلَٰمٌ عَلَيۡكَۖ سَأَسۡتَغۡفِرُ لَكَ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ بِي حَفِيّٗا
Open ayah 19:47(Ibrahim) adati: “Mtendere ukhale pa inu! Ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga (ngakhale mwandipirikitsa). Ndithu iye amandichitira chisoni kwambiri.”
وَأَعۡتَزِلُكُمۡ وَمَا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَأَدۡعُواْ رَبِّي عَسَىٰٓ أَلَّآ أَكُونَ بِدُعَآءِ رَبِّي شَقِيّٗا
Open ayah 19:48“Ndipo ine ndikupatukirani ku zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah ndipo ndipempha Mbuye wanga; ndithu sindikhala watsoka popempha Mbuye wanga.”
فَلَمَّا ٱعۡتَزَلَهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۖ وَكُلّٗا جَعَلۡنَا نَبِيّٗا
Open ayah 19:49Ndipo pamene adawapatukira ndi zimene adali kuzipembedza kusiya Allah, tidampatsa iye Ishaq, ndi Ya’qub, ndipo aliyense wa iwo tidampanga kukhala m’neneri.
وَوَهَبۡنَا لَهُم مِّن رَّحۡمَتِنَا وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ لِسَانَ صِدۡقٍ عَلِيّٗا
Open ayah 19:50Ndipo tidawapatsa iwo chifundo Chathu, ndi kuwayikira iwo kutchulidwa kwabwino, kwapamwamba (pakati pa zolengedwa).
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مُوسَىٰٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ مُخۡلَصٗا وَكَانَ رَسُولٗا نَّبِيّٗا
Open ayah 19:51Ndipo mtchule Mûsa m’buku (ili). Ndithu iye adali wosankhidwa ndi woyeretsedwa: ndipo adali Mtumiki M’neneri.
وَنَٰدَيۡنَٰهُ مِن جَانِبِ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنِ وَقَرَّبۡنَٰهُ نَجِيّٗا
Open ayah 19:52Ndipo tidamuitana kumbali yakudzanjadzanja la phiri la Turi, ndipo tidamuyandikitsa ndi kuyankhula Nafe momunong’ oneza.
وَوَهَبۡنَا لَهُۥ مِن رَّحۡمَتِنَآ أَخَاهُ هَٰرُونَ نَبِيّٗا
Open ayah 19:53Ndipo mwachifundo Chathu tidampatsa (Mûsa) m’bale wake Harun kukhala mneneri (womuthangata)
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِسۡمَٰعِيلَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صَادِقَ ٱلۡوَعۡدِ وَكَانَ رَسُولٗا نَّبِيّٗا
Open ayah 19:54Mtchulenso m’buku (ili) Ismaila; ndithu iye adali woona palonjezo, ndipo adali Mtumiki Mneneri.
وَكَانَ يَأۡمُرُ أَهۡلَهُۥ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ وَكَانَ عِندَ رَبِّهِۦ مَرۡضِيّٗا
Open ayah 19:55Adali kulamula anthu ake Swala ndi Zakaat, ndipo kwa Mbuye wake adali woyanjidwa.
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِدۡرِيسَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقٗا نَّبِيّٗا
Open ayah 19:56Mtchulenso m’buku (ili) Idris, ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri.
وَرَفَعۡنَٰهُ مَكَانًا عَلِيًّا
Open ayah 19:57Ndipo tidamunyamula (kumuika pa) malo apamwamba.
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِن ذُرِّيَّةِ ءَادَمَ وَمِمَّنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٖ وَمِن ذُرِّيَّةِ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡرَٰٓءِيلَ وَمِمَّنۡ هَدَيۡنَا وَٱجۡتَبَيۡنَآۚ إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُ ٱلرَّحۡمَٰنِ خَرُّواْۤ سُجَّدٗاۤ وَبُكِيّٗا۩
Open ayah 19:58Iwowo ndi omwe adawadalitsa Allah, mwa aneneri mu ana a Adam, ndi (m’mbumba ya) amene tidawatenga pamodzi ndi Nuh (m’chombo), ndi m’mbumba ya Ibrahim ndi Israyeli, ndi amene tidawaongola ndi kuwasankha. Ndipo zikawerengedwa kwa iwo Ayah za (Allah) Mwini chifundo chambiri, amagwa ndi kulambira uku akulira.
۞فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفٌ أَضَاعُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّبَعُواْ ٱلشَّهَوَٰتِۖ فَسَوۡفَ يَلۡقَوۡنَ غَيًّا
Open ayah 19:59Koma pambuyo pa iwo padadza anthu oipa. Adasokoneza Swala (adasiya kupemphera) natsatira zilakolako zoipa; choncho adzakumana ndi chilango choipa.
إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ شَيۡـٔٗا
Open ayah 19:60Kupatula amene ati alape ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; iwowo adzalowa ku Munda wamtendere ndipo sadzachitidwa chinyengo pa chilichonse.
جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ عِبَادَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّهُۥ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَأۡتِيّٗا
Open ayah 19:61Munda wamuyaya umene (Allah) Wachifundo chambiri walonjeza akapolo Ake mobisika, ndithu lonjezo Lake ndilakudza.
لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا إِلَّا سَلَٰمٗاۖ وَلَهُمۡ رِزۡقُهُمۡ فِيهَا بُكۡرَةٗ وَعَشِيّٗا
Open ayah 19:62Sakamva m’menemo mawu achibwana, koma mawu a mtendere; ndipo akapeza rizq (chakudya) lawo m’menemo m’mawa ndi madzulo.
تِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِي نُورِثُ مِنۡ عِبَادِنَا مَن كَانَ تَقِيّٗا
Open ayah 19:63Umenewo ndiwo Munda wamtendere umene tikawapatsa ena mwa akapolo athu omwe adali oopa Allah.
وَمَا نَتَنَزَّلُ إِلَّا بِأَمۡرِ رَبِّكَۖ لَهُۥ مَا بَيۡنَ أَيۡدِينَا وَمَا خَلۡفَنَا وَمَا بَيۡنَ ذَٰلِكَۚ وَمَا كَانَ رَبُّكَ نَسِيّٗا
Open ayah 19:64(Mtumiki adapempha Gabriel kuti akhale akum’bwerera pafupipafupi. Ndipo Gabriel adamuuza kuti): “Ndipo sitimatsika koma mwa lamulo la Mbuye wako. Zapatsogolo pathu ndi zapambuyo pathu ndi zapakati pa zimenezi zonse Nzake (akuzidziwa bwinobwino). Ndipo Mbuye wako sali woiwala.”
رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا فَٱعۡبُدۡهُ وَٱصۡطَبِرۡ لِعِبَٰدَتِهِۦۚ هَلۡ تَعۡلَمُ لَهُۥ سَمِيّٗا
Open ayah 19:65“Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pa izo: Choncho mpembedze Iye basi. Ndipo pitiriza ndikupirira popembedza Iye. Kodi ukumudziwa (wina) yemwe ali wofanana Naye (Allah)?”
وَيَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَءِذَا مَا مِتُّ لَسَوۡفَ أُخۡرَجُ حَيًّا
Open ayah 19:66Ndipo munthu (wokanira) amanena: “Kodi ndikadzafa nzoonadi kuti Ndidzatulutsidwa (m’manda) nkukhala wamoyo?”
أَوَلَا يَذۡكُرُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ يَكُ شَيۡـٔٗا
Open ayah 19:67Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga kale pomwe sadali chilichonse?
فَوَرَبِّكَ لَنَحۡشُرَنَّهُمۡ وَٱلشَّيَٰطِينَ ثُمَّ لَنُحۡضِرَنَّهُمۡ حَوۡلَ جَهَنَّمَ جِثِيّٗا
Open ayah 19:68Choncho ndikulumbira Mbuye wako, ndithu tidzawasonkhanitsa iwo pamodzi ndi asatana; ndipo tidzawafikitsa m’mphepete mwa Jahannam uku atagwada.
ثُمَّ لَنَنزِعَنَّ مِن كُلِّ شِيعَةٍ أَيُّهُمۡ أَشَدُّ عَلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ عِتِيّٗا
Open ayah 19:69Kenako, m’gulu lililonse tidzachotsamo yemwe adali wopyola malire polakwira (Allah) Mwini chifundo chambiri.
ثُمَّ لَنَحۡنُ أَعۡلَمُ بِٱلَّذِينَ هُمۡ أَوۡلَىٰ بِهَا صِلِيّٗا
Open ayah 19:70Ndipo Ife tikuwazindikira kwambiri amene ali oyenera kulowa m’Moto.
وَإِن مِّنكُمۡ إِلَّا وَارِدُهَاۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ حَتۡمٗا مَّقۡضِيّٗا
Open ayah 19:71Ndipo palibe aliyense mwa inu koma adzaifika (Jahannamyo). Ndithu ili ndi lamulo la Mbuye wako lomwe lidalamulidwa kale.
ثُمَّ نُنَجِّي ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْ وَّنَذَرُ ٱلظَّٰلِمِينَ فِيهَا جِثِيّٗا
Open ayah 19:72Ndipo kenako tidzawapulumutsa amene ankaopa Allah, ndipo osalungama tidzawasiya m’menemo atagwada.
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ خَيۡرٞ مَّقَامٗا وَأَحۡسَنُ نَدِيّٗا
Open ayah 19:73Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, omwe sadakhulupirire amanena kwa omwe akhulupirira: “Ndi gulu liti pa magulu awiri awa, (lanu ndi lathu) lomwe lili ndi pokhala pabwino ndikukhalanso ndi anthu olemekezeka?”
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَحۡسَنُ أَثَٰثٗا وَرِءۡيٗا
Open ayah 19:74Ndipo mibadwo yambiri tidaiononga patsogolo pawo, yomwe idali ndi ziwiya zabwino ndi maonekedwe abwino.
قُلۡ مَن كَانَ فِي ٱلضَّلَٰلَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَدًّاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ إِمَّا ٱلۡعَذَابَ وَإِمَّا ٱلسَّاعَةَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ هُوَ شَرّٞ مَّكَانٗا وَأَضۡعَفُ جُندٗا
Open ayah 19:75Nena: “Amene ali mkusokera, (Allah) Mwini chifundo chambiri amuonjezera nthawi yamoyo kufikira azione zomwe akulonjezedwa - kapena chilango kapena kudza nthawi (ya Qiyâma) - pamenepo ndipomwe adzadziwa kuti ndani mwini kukhala pamalo poipa, ndi mwini wa ankhondo ofooka (iwo kapena Asilamu)?”
وَيَزِيدُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱهۡتَدَوۡاْ هُدٗىۗ وَٱلۡبَٰقِيَٰتُ ٱلصَّٰلِحَٰتُ خَيۡرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابٗا وَخَيۡرٞ مَّرَدًّا
Open ayah 19:76Ndipo Allah amawaonjezera chiongoko amene aongoka. Ndipo zochita zabwino zonkerankera (mpaka tsiku lachimaliziro), ndizo zili zabwino kwa Mbuye wako monga mphoto, ndiponso ndiko kobwerera kwabwino, (osati za mdziko zomwe anthu osalungama akunyadira).
أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي كَفَرَ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالَ لَأُوتَيَنَّ مَالٗا وَوَلَدًا
Open ayah 19:77Kodi wamuona yemwe watsutsa Ayah Zathu ndikunena kuti: “Ndithu ndidzapatsidwa chuma ndi ana (pa tsiku lachimaliziro monga momwe andipatsira pano pa dziko?)”
أَطَّلَعَ ٱلۡغَيۡبَ أَمِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدٗا
Open ayah 19:78Kodi adadziwa zamseri, kapena adalandira lonjezo kwa Allah mwini chifundo Chambiri (kotero kuti ali ndi chikhulupiliro pa zimene akunenazo)?.
كَلَّاۚ سَنَكۡتُبُ مَا يَقُولُ وَنَمُدُّ لَهُۥ مِنَ ٱلۡعَذَابِ مَدّٗا
Open ayah 19:79Sichoncho, ndithu tikulemba zonse zomwe akunena, ndipo tidzamuonjezera nyengo yotalika m’chilango.
وَنَرِثُهُۥ مَا يَقُولُ وَيَأۡتِينَا فَرۡدٗا
Open ayah 19:80Ndipo tidzamlowa mmalo zimene akunenazi, (chuma ndi anawo), nadzatidzera ali yekhayekha (wopanda chuma ndi zonse zomwe ankanyadira).
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةٗ لِّيَكُونُواْ لَهُمۡ عِزّٗا
Open ayah 19:81Eti adzipangira milungu ina m’malo mwa Allah kuti milunguyo iwapatse mphamvu (ndi ulemelero).
كَلَّاۚ سَيَكۡفُرُونَ بِعِبَادَتِهِمۡ وَيَكُونُونَ عَلَيۡهِمۡ ضِدًّا
Open ayah 19:82Iyayi! Idzawakanira mapemphero awo ndikuwaukira.
أَلَمۡ تَرَ أَنَّآ أَرۡسَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ تَؤُزُّهُمۡ أَزّٗا
Open ayah 19:83Kodi suona kuti Ife timawatuma asatana kwa osakhulupirira ndipo akuwakhwirizira kwambiri (kuchita zoipa)?
فَلَا تَعۡجَلۡ عَلَيۡهِمۡۖ إِنَّمَا نَعُدُّ لَهُمۡ عَدّٗا
Open ayah 19:84Choncho, usawachitire changu (kuti alangidwe tsopano), ndithu Ife tikuwawerengera chiwerengero (cha masiku awo; masiku akakwana, tiwalanga).
يَوۡمَ نَحۡشُرُ ٱلۡمُتَّقِينَ إِلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ وَفۡدٗا
Open ayah 19:85(Kumbukira iwe Mtumiki) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa oopa (Allah) kunka nawo kwa Mwini chifundo Chambiri ali m’magulumagulu monga nthumwi (Zake kuti apatsidwe ulemu).
وَنَسُوقُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ وِرۡدٗا
Open ayah 19:86Ndipo oipa tidzawakusa kunka nawo ku Moto ali ndi ludzu lalikulu monga momwe ziweto zimathamangira kupita kumadzi zikakhala ndi ludzu lalikulu).
لَّا يَمۡلِكُونَ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَنِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدٗا
Open ayah 19:87Sadzakhala ndi mphamvu yoombolera (ena) koma kupatula omwe adagwiritsa lonjezo la (Allah) Mwini chifundo chambiri.
وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدٗا
Open ayah 19:88Ndipo (osakhulupirira omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu) akuti: “(Allah) Mwini chifundo chambiri wadzipangira mwana!”
لَّقَدۡ جِئۡتُمۡ شَيۡـًٔا إِدّٗا
Open ayah 19:89Ndithu mwadza ndi chinthu choipitsitsa (pazimene mukunenazi).
تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِنۡهُ وَتَنشَقُّ ٱلۡأَرۡضُ وَتَخِرُّ ٱلۡجِبَالُ هَدًّا
Open ayah 19:90Thambo layandikira kusweka ndi mawuwo, ndipo nthaka kuphwasuka, ndipo mapiri kugwa ndikudukaduka.
أَن دَعَوۡاْ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدٗا
Open ayah 19:91Chifukwa chakumunamizira (Allah) Mwini chifundo chambiri kuti ali ndi mwana.
وَمَا يَنۢبَغِي لِلرَّحۡمَٰنِ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا
Open ayah 19:92Ndipo nkosayenera kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri kudzipangira mwana.
إِن كُلُّ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّآ ءَاتِي ٱلرَّحۡمَٰنِ عَبۡدٗا
Open ayah 19:93Palibe aliyense yemwe ali kumwamba ndi pansi koma adzadza kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri ali kapolo (Wake).
لَّقَدۡ أَحۡصَىٰهُمۡ وَعَدَّهُمۡ عَدّٗا
Open ayah 19:94Ndithu (Allah) wawadziwa mokwanira ndipo adzawawerenga aliyense payekhapayekha.
وَكُلُّهُمۡ ءَاتِيهِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَرۡدًا
Open ayah 19:95Ndipo, aliyense wa iwo adzadza kwa Iye (Allah) ali payekhapayekha.
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَيَجۡعَلُ لَهُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وُدّٗا
Open ayah 19:96Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, (Allah) Mwini chifundo chambiri adzaika chikondi pakati pawo.
فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لِتُبَشِّرَ بِهِ ٱلۡمُتَّقِينَ وَتُنذِرَ بِهِۦ قَوۡمٗا لُّدّٗا
Open ayah 19:97Ndithu taifewetsa (Qur’an) m’chiyankhulo chako kuti ndi iyo uwawuze nkhani zabwino oopa Allah ndipo ndi iyo uwachenjeze anthu amakani.
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هَلۡ تُحِسُّ مِنۡهُم مِّنۡ أَحَدٍ أَوۡ تَسۡمَعُ لَهُمۡ رِكۡزَۢا
Open ayah 19:98Kodi ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Kodi ukumuona mmodzi wa iwo, kapena ukumva mgugu wawo?