الإسراء
Al-Israa
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِيٓ أَسۡرَىٰ بِعَبۡدِهِۦ لَيۡلٗا مِّنَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ إِلَى ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡأَقۡصَا ٱلَّذِي بَٰرَكۡنَا حَوۡلَهُۥ لِنُرِيَهُۥ مِنۡ ءَايَٰتِنَآۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
Open ayah 17:1۞ Ulemelero ngwa Yemwe adayendetsa kapolo Wake usiku (umodzi) kuchokera mu Msikiti Wopatulika (wa Makka) kupita ku Msikiti wakutali (wa Baitul-Muqaddas), womwe tidazidalitsa zomwe zauzungulira. (Tidampititsa kumeneko) kuti timsonyeze zina mwa zisonyezo Zathu; ndithu Iye (Allah) Ngwakumva, Ngowona ( chilichonse).[1]
- Mneneri Muhammad (s.a.w) pamene adakwezedwa kumwamba adaona zisonyezo zikuluzikulu za Allah monga Munda wa mtendere, Moto, mtengo wotchedwa Sidratul- Muntaha, Angelo, Aneneri ndi zina zododometsa.
وَءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدٗى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَلَّا تَتَّخِذُواْ مِن دُونِي وَكِيلٗا
Open ayah 17:2Ndipo Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) tidaliika kukhala chiongoko kwa ana a Israyeli (Allah adawauza): “Musadzipangire atetezi kusiya Ine.”
ذُرِّيَّةَ مَنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٍۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَبۡدٗا شَكُورٗا
Open ayah 17:3(Ndiponso adawauza kuti: “E inu) Mbumba ya amene tidawanyamula pamodzi ndi Nuh! (Khalani othokoza monga tate wanu.) Ndithu iye adali kapolo wothokoza kwambiri.”
وَقَضَيۡنَآ إِلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ لَتُفۡسِدُنَّ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَّتَيۡنِ وَلَتَعۡلُنَّ عُلُوّٗا كَبِيرٗا
Open ayah 17:4Ndipo tidawazindikiritsa ana a Israyeli m’bukulo, kuti: “Ndithu inu muononga pa dziko kawiri, ndipo mudzapyola malire pochita zoipa, kupyola malire kwakukulu.
فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ أُولَىٰهُمَا بَعَثۡنَا عَلَيۡكُمۡ عِبَادٗا لَّنَآ أُوْلِي بَأۡسٖ شَدِيدٖ فَجَاسُواْ خِلَٰلَ ٱلدِّيَارِۚ وَكَانَ وَعۡدٗا مَّفۡعُولٗا
Open ayah 17:5Ndipo likadzafika lonjezo (lakupatsidwa chilango chakuononga) koyamba mkuononga kuwiriko, tidzawakhwirizira pa inu anthu athu, eni kumenya nkhondo mwaukali, adzakhala akuzungulira mkatikati mwa nyumba (zanu), ndipo lidali lonjezo lochitika.
ثُمَّ رَدَدۡنَا لَكُمُ ٱلۡكَرَّةَ عَلَيۡهِمۡ وَأَمۡدَدۡنَٰكُم بِأَمۡوَٰلٖ وَبَنِينَ وَجَعَلۡنَٰكُمۡ أَكۡثَرَ نَفِيرًا
Open ayah 17:6Kenako tidakubwezerani kupambana pa iwo (omwe adakugonjetsani poyamba); ndipo tidakupatsani chuma ndi ana, ndi kukudalitsani kukhala ndi gulu lochuluka.
إِنۡ أَحۡسَنتُمۡ أَحۡسَنتُمۡ لِأَنفُسِكُمۡۖ وَإِنۡ أَسَأۡتُمۡ فَلَهَاۚ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ لِيَسُـُٔواْ وُجُوهَكُمۡ وَلِيَدۡخُلُواْ ٱلۡمَسۡجِدَ كَمَا دَخَلُوهُ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَلِيُتَبِّرُواْ مَا عَلَوۡاْ تَتۡبِيرًا
Open ayah 17:7(Tidati kwa iwo): “Ngati muchita bwino (pomumvera Allah), ubwino ngwanu (pa dziko lapansi ndi pa tsiku la Chimaliziro); ngati muipitsa (ponyoza Allah), kuipako kuli pa inu nokha. Choncho pamene idadza nthawi ya lonjezo lachilango chomaliza, (tidakutumizirani adani anu) kuti apereke kunyozeka pa nkhope zanu, ndikutinso alowe mu Nsikiti monga adalowera mnthawi yoyamba, ndikuti aononge chilichonse chimene achigonjetsa; kuononga kwakukulu.”
عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يَرۡحَمَكُمۡۚ وَإِنۡ عُدتُّمۡ عُدۡنَاۚ وَجَعَلۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ حَصِيرًا
Open ayah 17:8“(Koma ngati mudzalungama mzochita zanu), Mbuye wanu adzakuchitirani chifundo; ndipo ngati mudzabwereranso (ku machitidwe anu okhota), tidzabwereranso (kukulangani). Ndipo taikonza Jahannam kukhala ndende ya osakhulupirira.”
إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَهۡدِي لِلَّتِي هِيَ أَقۡوَمُ وَيُبَشِّرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ أَجۡرٗا كَبِيرٗا
Open ayah 17:9Ndithu iyi Qur’an ikuongolera ku njira yoongoka ndi kuwasangalatsa okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti ndithu iwo adzalandira malipiro aakulu (pa tsiku la chiweruziro);
وَأَنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمٗا
Open ayah 17:10Ndikutinso omwe sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro tawakonzera chilango chowawa.
وَيَدۡعُ ٱلۡإِنسَٰنُ بِٱلشَّرِّ دُعَآءَهُۥ بِٱلۡخَيۡرِۖ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ عَجُولٗا
Open ayah 17:11Ndipo munthu amafulumira kupempha zoipa monga momwenso amafulumilira kupempha zabwino; ndithu munthu ngwaphuma (mzochita zake).
وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ ءَايَتَيۡنِۖ فَمَحَوۡنَآ ءَايَةَ ٱلَّيۡلِ وَجَعَلۡنَآ ءَايَةَ ٱلنَّهَارِ مُبۡصِرَةٗ لِّتَبۡتَغُواْ فَضۡلٗا مِّن رَّبِّكُمۡ وَلِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ وَكُلَّ شَيۡءٖ فَصَّلۡنَٰهُ تَفۡصِيلٗا
Open ayah 17:12Ndipo tapanga usiku ndi usana (mkusinthana-sinthana kwake) monga zisonyezo ziwiri (zosonyeza umodzi wa Allah ndi mphamvu Zake zoposa); ndipo tidachifafaniza chisonyezo cha usiku (kuti chisakhale ndi kuunika) ndipo chisonyezo cha usana tidachipanga kuti chikhale ndi kuunika; kuti mufunefune ubwino wochokera kwa Mbuye wanu, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka ndichiwerengero (cha miyezi ndi masiku); ndipo chinthu chilichonse (chofunika pa chipembedzo ndi za m’dziko), tachilongosola bwinobwino, mwatsatanetsatane.
وَكُلَّ إِنسَٰنٍ أَلۡزَمۡنَٰهُ طَٰٓئِرَهُۥ فِي عُنُقِهِۦۖ وَنُخۡرِجُ لَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ كِتَٰبٗا يَلۡقَىٰهُ مَنشُورًا
Open ayah 17:13Ndipo munthu aliyense tammangilira mkhosi mwake zochita zake; ndipo tsiku la Qiyâma tidzamtulutsira kaundula (momwe muli zochita zake), adzampeza wovundukulidwa.
ٱقۡرَأۡ كِتَٰبَكَ كَفَىٰ بِنَفۡسِكَ ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكَ حَسِيبٗا
Open ayah 17:14(Kudzanenedwa kwa iye:) “Werenga kaundula wako (kupyolera m’mphamvu za Allah ngakhale pa dziko lapansi siunkatha kuwerenga); mzimu wako ukwanira lero kudziwerengera.”
مَّنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۗ وَمَا كُنَّا مُعَذِّبِينَ حَتَّىٰ نَبۡعَثَ رَسُولٗا
Open ayah 17:15Amene waongoka (potsatira njira ya choonadi) ndithu wadzipindulira yekha, ndipo amene wapotoka (ku njira ya choonadi) ndithu wadzitaya iye mwini. Ndipo msenzi wosenza machimo sadzasenza mtolo wa machimo a wina. Ndipo Ife siolanga (zolengedwa) kufikira titatumiza mtumiki (kuti azidziwitse choonadi. Zikakana ndipomwe timazilanga).
وَإِذَآ أَرَدۡنَآ أَن نُّهۡلِكَ قَرۡيَةً أَمَرۡنَا مُتۡرَفِيهَا فَفَسَقُواْ فِيهَا فَحَقَّ عَلَيۡهَا ٱلۡقَوۡلُ فَدَمَّرۡنَٰهَا تَدۡمِيرٗا
Open ayah 17:16Ndipo tikafuna kuononga mudzi (pamene eni mudziwo akuchita zoipa), timawalamula opeza bwino a m’menemo (kuti asiye zoipa). Koma akapitiriza kuononga kwawo m’menemo, apo ndipo liwu (la kuwaononga) limatsimikizidwa pa iwo ndipo timauononga, kuononga kwakukulu.
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِنۢ بَعۡدِ نُوحٖۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Open ayah 17:17Ndimibadwo ingati imene tidaiononga pambuyo pa Nuh! Ndipo akukwanira Mbuye wako kudziwa bwinobwino ndi kuona bwinobwino uchimo wa akapolo Ake. (Palibe chobisika kwa Iye m’zochitachita za anthu).
مَّن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعَاجِلَةَ عَجَّلۡنَا لَهُۥ فِيهَا مَا نَشَآءُ لِمَن نُّرِيدُ ثُمَّ جَعَلۡنَا لَهُۥ جَهَنَّمَ يَصۡلَىٰهَا مَذۡمُومٗا مَّدۡحُورٗا
Open ayah 17:18Amene afuna zachangu (zosangalatsa za m’dziko ndikumaikirapo mtima pa izo), timpatsiratu mwachangu pa dziko lapansi chimene tikufuna kwa amene tafuna (kumpatsa;) koma (tsiku la chimaliziro) tamkonzera Jahannam adzailowa ali wonyozeka, wopirikitsidwa apa ndi apo.
وَمَنۡ أَرَادَ ٱلۡأٓخِرَةَ وَسَعَىٰ لَهَا سَعۡيَهَا وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ كَانَ سَعۡيُهُم مَّشۡكُورٗا
Open ayah 17:19Ndipo amene afuna tsiku la chimaliziro (mzochita zake) ndikuligwilira ntchito yake yeniyeni uku ali okhulupirira, iwowo khama lawo lidzakhala lolandiridwa.
كُلّٗا نُّمِدُّ هَٰٓؤُلَآءِ وَهَٰٓؤُلَآءِ مِنۡ عَطَآءِ رَبِّكَۚ وَمَا كَانَ عَطَآءُ رَبِّكَ مَحۡظُورًا
Open ayah 17:20Onse awa, (abwino ndi oipa), timawapatsa awa ndi awa mwazopatsa za Mbuye wako; ndipo zopatsa za Mbuye wako sizotsekerezedwa (kuti zisamfike kapolo Wake).
ٱنظُرۡ كَيۡفَ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ وَلَلۡأٓخِرَةُ أَكۡبَرُ دَرَجَٰتٖ وَأَكۡبَرُ تَفۡضِيلٗا
Open ayah 17:21Taona (ndi diso lolingalira) m’mene tawasiyanitsira mkupeza bwino, ena nkukhala pamwamba pa anzawo (pa chuma ndi pa moyo wangwiro); ndipo pa tsiku la chimaliziro kusiyana kwawo pa masitepe ndi ulemelero, nkwakukulu kwabasi.
لَّا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَقۡعُدَ مَذۡمُومٗا مَّخۡذُولٗا
Open ayah 17:22Usadzipangire mulungu wina ndi kumphatika kwa Allah; kuti ungadzakhale wodzudzulidwa (kwa Allah) ndikusiidwa wopanda m’thandizi.
۞وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّآ إِيَّاهُ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًاۚ إِمَّا يَبۡلُغَنَّ عِندَكَ ٱلۡكِبَرَ أَحَدُهُمَآ أَوۡ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَآ أُفّٖ وَلَا تَنۡهَرۡهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوۡلٗا كَرِيمٗا
Open ayah 17:23Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye Yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati m’modzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo, ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu.[1]
- M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.
وَٱخۡفِضۡ لَهُمَا جَنَاحَ ٱلذُّلِّ مِنَ ٱلرَّحۡمَةِ وَقُل رَّبِّ ٱرۡحَمۡهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيرٗا
Open ayah 17:24Ndipo afungatire ndi phiko lodzichepetsa powachitira chisoni, ndipo nena: “Mbuye wanga achitireni chisoni (makolo anga) monga momwe ankandilelera ku ubwana.”
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا فِي نُفُوسِكُمۡۚ إِن تَكُونُواْ صَٰلِحِينَ فَإِنَّهُۥ كَانَ لِلۡأَوَّٰبِينَ غَفُورٗا
Open ayah 17:25Mbuye wanu akudziwa kwambiri zomwe zili m’maganizo mwanu; ngati muli ofuna kuchita zabwino, (kwa makolo anu Iye akudziwa. Ndipo ngati mutawalakwira, kenako ndikulapa), ndithu Iye ndi Mwini kukhululukira otembenukira kwa Iye.
وَءَاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِ وَلَا تُبَذِّرۡ تَبۡذِيرًا
Open ayah 17:26Ndipo mnansi wako, masikini ndi wapaulendo (yemwe alibe choyendera) mpatse gawo lake (la chuma chako) ndipo usamwaze (chuma chako) mosakaza.
إِنَّ ٱلۡمُبَذِّرِينَ كَانُوٓاْ إِخۡوَٰنَ ٱلشَّيَٰطِينِۖ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِرَبِّهِۦ كَفُورٗا
Open ayah 17:27Ndithu omwaza chuma mosakaza ndiabale a satana (otsatira satana), ndipo satana ngosathokoza kwa Mbuye wake.
وَإِمَّا تُعۡرِضَنَّ عَنۡهُمُ ٱبۡتِغَآءَ رَحۡمَةٖ مِّن رَّبِّكَ تَرۡجُوهَا فَقُل لَّهُمۡ قَوۡلٗا مَّيۡسُورٗا
Open ayah 17:28Ndipo ngati ukuwapewa opempha (pamene ulibe chowapatsa) pamene ukufunafuna chifundo cha Mbuye wako chomwe ukuchiyembekezera, nena kwa iwo mau ofewa (ponena kuti: “Ndikapeza chokupatsani, ndikuninkhani.”)
وَلَا تَجۡعَلۡ يَدَكَ مَغۡلُولَةً إِلَىٰ عُنُقِكَ وَلَا تَبۡسُطۡهَا كُلَّ ٱلۡبَسۡطِ فَتَقۡعُدَ مَلُومٗا مَّحۡسُورًا
Open ayah 17:29Ndipo mkono wako usaukhalitse ngati kuti wamangidwa kukhosi kwako, ndiponso usautambasule mosayenera, ungadzakhale wodzudzulidwa ndiwosowa.[1]
- Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana.
إِنَّ رَبَّكَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Open ayah 17:30Ndithu Mbuye wako amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndikulichepetsa (kwa amene wamfuna). Ndithu Iye Ngodziwa bwino; wopenya bwino za akapolo Ake.
وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُمۡ خَشۡيَةَ إِمۡلَٰقٖۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُهُمۡ وَإِيَّاكُمۡۚ إِنَّ قَتۡلَهُمۡ كَانَ خِطۡـٔٗا كَبِيرٗا
Open ayah 17:31Ndipo musaphe ana anu poopa umphawi. Ife ndi amene tikuwapatsa iwo ndi inu. Ndithu kupha anawo ndi tchimo lalikulu.
وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلزِّنَىٰٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةٗ وَسَآءَ سَبِيلٗا
Open ayah 17:32Ndipo musachiyandikire chiwerewere; ndithu (icho) ndi uve (chonyansa chachikulu), ndiponso ndi njira yoipa.
وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَمَن قُتِلَ مَظۡلُومٗا فَقَدۡ جَعَلۡنَا لِوَلِيِّهِۦ سُلۡطَٰنٗا فَلَا يُسۡرِف فِّي ٱلۡقَتۡلِۖ إِنَّهُۥ كَانَ مَنصُورٗا
Open ayah 17:33Ndipo musaphe munthu amene Allah waletsa (kumupha) koma mwachoonadi (poweruza oweruza zakuphedwa ngati utam’gwera mulandu woyenera kuphedwa). Ndipo amene waphedwa mopanda chilungamo, tapereka mphamvu kwa mlowammalo wake (wa wophedwayo atafuna angamuphenso kapena kumsiya ndikulandirapo dipo); koma asapyole malire mukuphako. Ndithu iye ngothandizidwa ndi Shariya.
وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ بِٱلۡعَهۡدِۖ إِنَّ ٱلۡعَهۡدَ كَانَ مَسۡـُٔولٗا
Open ayah 17:34Ndipo musachiyandikire chuma cha wamasiye (pochidya mosayenera) koma pokhapokha m’njira yomwe ili yabwino, kufikira atakula, (apo tsono apatsidwe chumacho); ndipo kwaniritsani lonjezo, popeza lonjezo lidzafunsidwa (tsiku la Qiyâma).
وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ إِذَا كِلۡتُمۡ وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٞ وَأَحۡسَنُ تَأۡوِيلٗا
Open ayah 17:35Ndipo kwaniritsani mlingo pamene mulinga, ndipo yesani ndi sikelo zabwino, zimenezo ndi zabwino (kwa inu) ndiponso mathero (ake) ngabwino.
وَلَا تَقۡفُ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۚ إِنَّ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡبَصَرَ وَٱلۡفُؤَادَ كُلُّ أُوْلَٰٓئِكَ كَانَ عَنۡهُ مَسۡـُٔولٗا
Open ayah 17:36Ndipo usazitsate (pongoziyankhulayankhula kapena kuzichita) zomwe sukuzidziwa; ndithu makutu, maso ndi mtima zonsezo zidzafunsidwa.
وَلَا تَمۡشِ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَحًاۖ إِنَّكَ لَن تَخۡرِقَ ٱلۡأَرۡضَ وَلَن تَبۡلُغَ ٱلۡجِبَالَ طُولٗا
Open ayah 17:37Ndipo usayende padziko modzitukumula; ndithu iwe sungang’ambe nthaka ndiponso sungalifikire phiri m’kutalika.
كُلُّ ذَٰلِكَ كَانَ سَيِّئُهُۥ عِندَ رَبِّكَ مَكۡرُوهٗا
Open ayah 17:38Zonsezi kuipa kwake nkonyansidwa kwa Mbuye wako.
ذَٰلِكَ مِمَّآ أَوۡحَىٰٓ إِلَيۡكَ رَبُّكَ مِنَ ٱلۡحِكۡمَةِۗ وَلَا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتُلۡقَىٰ فِي جَهَنَّمَ مَلُومٗا مَّدۡحُورًا
Open ayah 17:39Izi ndi zina mwa za nzeru zomwe Mbuye wako wakuvumbulutsira. Usakhale ndi mulungu wina ndi kumphatikiza kwa Allah, kuti ungadzaponyedwe ku Jahannam uli wodzudzulidwa ndi wopirikitsidwa apa ndi apo.
أَفَأَصۡفَىٰكُمۡ رَبُّكُم بِٱلۡبَنِينَ وَٱتَّخَذَ مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنَٰثًاۚ إِنَّكُمۡ لَتَقُولُونَ قَوۡلًا عَظِيمٗا
Open ayah 17:40Kodi Mbuye wanu wakusankhirani ana aamuna, ndipo mwini wadzipangira ana aakazi achingelo? Ndithu inu mukunena liwu lalikulu.
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِيَذَّكَّرُواْ وَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا نُفُورٗا
Open ayah 17:41Ndipo ndithu talongosola lamulo la chinthu chilichonse mwatsatanetsatane m’Qur’an iyi kuti akumbukire, ndipo (oipa) siikuwaonjezera (china) koma kuida ndi kuithawa.
قُل لَّوۡ كَانَ مَعَهُۥٓ ءَالِهَةٞ كَمَا يَقُولُونَ إِذٗا لَّٱبۡتَغَوۡاْ إِلَىٰ ذِي ٱلۡعَرۡشِ سَبِيلٗا
Open ayah 17:42Nena: “Pakadakhala milungu ina pamodzi ndi Allah, monga momwe akunenera, ikadafuna njira yomufikira (Mbuye) Mwini Arsh (Mpando wa chifumu, ndi kumthira nkhondo).”
سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَقُولُونَ عُلُوّٗا كَبِيرٗا
Open ayah 17:43Wayera ndipo watukuka Allah ku zimene akunenazo; kutukuka kwakukulu (kwabasi).
تُسَبِّحُ لَهُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ ٱلسَّبۡعُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا يُسَبِّحُ بِحَمۡدِهِۦ وَلَٰكِن لَّا تَفۡقَهُونَ تَسۡبِيحَهُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورٗا
Open ayah 17:44Zonse zakumitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi zam’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo! Ndithudi Iye (Allah) Ngodekha, Ngokhululuka.
وَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ جَعَلۡنَا بَيۡنَكَ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ حِجَابٗا مَّسۡتُورٗا
Open ayah 17:45Ndipo ukamawerenga Qur’an (zikukhala ngati) taika chotchinga chosaonekera pakati pako ndi pakati pa amene sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro.
وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۚ وَإِذَا ذَكَرۡتَ رَبَّكَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِ وَحۡدَهُۥ وَلَّوۡاْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِمۡ نُفُورٗا
Open ayah 17:46Ndipo (ngati) taika zitsekelero m’mitima mwawo kuti angaizindikire, ndipo (ngati) mmakutu mwawo muli kulemera kwa ugonthi. Ndiponso ukamtchula m’Qur’an Mbuye wako Yekha, iwo akutembenuka ndi misana yawo moipidwa.
نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَسۡتَمِعُونَ بِهِۦٓ إِذۡ يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَ وَإِذۡ هُمۡ نَجۡوَىٰٓ إِذۡ يَقُولُ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلٗا مَّسۡحُورًا
Open ayah 17:47Ife tikudziwa chifukwa chomwe akuimvetsera (Qur’an), pamene akukumvetsera ndi pamene akunong’onezana awo achinyengo, pamene akunena awo oyipa (kuuza Asilamu kuti): “Inu simutsatira (wina) koma munthu wolodzedwa.”
ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَالَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلٗا
Open ayah 17:48Ona momwe akukufanizira ndi mafanizo abodza. (Nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa, nthawi zina akuti ndiwe mfiti!) Choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yeniyeni).
وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدٗا
Open ayah 17:49Ndipo akunena: “Kodi tikadzakhala mafupa odukaduka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
۞قُلۡ كُونُواْ حِجَارَةً أَوۡ حَدِيدًا
Open ayah 17:50Nena: “Khalani miyala kapena zitsulo.”
أَوۡ خَلۡقٗا مِّمَّا يَكۡبُرُ فِي صُدُورِكُمۡۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَاۖ قُلِ ٱلَّذِي فَطَرَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖۚ فَسَيُنۡغِضُونَ إِلَيۡكَ رُءُوسَهُمۡ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَۖ قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَرِيبٗا
Open ayah 17:51“Kapena cholengedwa chilichonse mwa zomwe zikuoneka kuti nzovuta kwambiri m’mitima mwanu (m’maganizo mwanu), (ngakhale mutakhala zimenezo, mudzaukitsidwa).” Pamenepo anena: “Ndani adzatibweza?” Nena: “Yemwe adakulengani pachiyambi.” Pamenepo adzakupukusira mitu yawo ndi kunena: “Zichitika liti zimenezo?” Nena: “Mwina zili pafupi!”
يَوۡمَ يَدۡعُوكُمۡ فَتَسۡتَجِيبُونَ بِحَمۡدِهِۦ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا
Open ayah 17:52“(Zidzakhala) pa tsiku lomwe adzakuitanani (Allah), ndipo inu mudzayankha momuyamikira, ndipo mudzaganizira kuti simudakhale (pa dziko lapansi) koma (kwa) nthawi yochepa.”
وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُواْ ٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ يَنزَغُ بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوّٗا مُّبِينٗا
Open ayah 17:53Ndipo auze akapolo Anga kuti (nthawi zonse) azinena zomwe zili zabwino; chifukwa satana amakhwirizira mikangano pakati pawo; ndithu satana kwa munthu, ndi m’dani woonekera.
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِكُمۡۖ إِن يَشَأۡ يَرۡحَمۡكُمۡ أَوۡ إِن يَشَأۡ يُعَذِّبۡكُمۡۚ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلٗا
Open ayah 17:54Mbuye wanu akukudziwani bwino. Ngati afuna akuchitirani chisoni (mukatembenukira kwa Iye), ndipo ngati afuna, akulangani (mukapitiriza kumnyoza); ndipo sitidakutumize kuti ukhale muyang’anili wawo.
وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِمَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ فَضَّلۡنَا بَعۡضَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ عَلَىٰ بَعۡضٖۖ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورٗا
Open ayah 17:55Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino onse ali kumwamba ndi pansi, ndithu tawapatsa ulemelero wambiri aneneri ena kuposa ena. Ndipo Daud tidampatsa Zaburi.
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِهِۦ فَلَا يَمۡلِكُونَ كَشۡفَ ٱلضُّرِّ عَنكُمۡ وَلَا تَحۡوِيلًا
Open ayah 17:56Nena: “Aitaneni amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Iye (Allah) kuti akuchotsereni masautso, sadzatha kukuchotserani vuto lililonse ngakhale kulisintha (kuti likhale chabwino).”
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ يَبۡتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ ٱلۡوَسِيلَةَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ وَيَرۡجُونَ رَحۡمَتَهُۥ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُۥٓۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحۡذُورٗا
Open ayah 17:57Iwo amene akuwapempha (naonso) akufunafuna njira yoziyandikitsira kwa Mbuye wawo (ngakhale) omwe ali pafupi mwa iwo (ndi Allah, monga angelo); naonso akuyembekezera chifundo chake ndi kuopa chilango chake; ndithu chilango cha Mbuye wako, nchoopedwa.
وَإِن مِّن قَرۡيَةٍ إِلَّا نَحۡنُ مُهۡلِكُوهَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَوۡ مُعَذِّبُوهَا عَذَابٗا شَدِيدٗاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورٗا
Open ayah 17:58Ndipo sipadzapezeka mudzi uliwonse koma Ife tidzauphwasula tsiku la Qiyâma lisanadze, kapena tidzaulanga ndi chilango chaukali (ngati uli woyenerana ndi zimenezo). Izi zidalembedwa m’buku.
وَمَا مَنَعَنَآ أَن نُّرۡسِلَ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّآ أَن كَذَّبَ بِهَا ٱلۡأَوَّلُونَۚ وَءَاتَيۡنَا ثَمُودَ ٱلنَّاقَةَ مُبۡصِرَةٗ فَظَلَمُواْ بِهَاۚ وَمَا نُرۡسِلُ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّا تَخۡوِيفٗا
Open ayah 17:59Ndipo palibe chimene chikutiletsa kutumiza zizizwa (zomwe akuzipempha) koma kuti anthu akale adazitsutsa. Asamuda tidawapatsa ngamira yaikazi kuti ikhale chizindikiro choonekera (chozizwitsa) koma adaichitira zosayenera; ndipo sititumiza zizizwa ndi cholinga china, koma kuchenjeza.
وَإِذۡ قُلۡنَا لَكَ إِنَّ رَبَّكَ أَحَاطَ بِٱلنَّاسِۚ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلرُّءۡيَا ٱلَّتِيٓ أَرَيۡنَٰكَ إِلَّا فِتۡنَةٗ لِّلنَّاسِ وَٱلشَّجَرَةَ ٱلۡمَلۡعُونَةَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِۚ وَنُخَوِّفُهُمۡ فَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا طُغۡيَٰنٗا كَبِيرٗا
Open ayah 17:60Ndipo (kumbuka) pamene tidakuuza kuti ndithu Mbuye wako wawazungulira anthu (mowadziwa bwinobwino;) ndipo sitidawachite maloto omwe tidakuonetsa koma kuti akhale mayeso kwa anthu, (kuti kodi akhulupirira kapena sakhulupirira), ndiponso (kutchula kwa) rntengo wotembeleredwa m’Qur’an (ndimayetseronso kwa iwo;) ndipo tikuwachenjeza, koma (machenjezo athu) sakuwaonjezera china koma kulumpha malire kwakukulu basi.
وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ قَالَ ءَأَسۡجُدُ لِمَنۡ خَلَقۡتَ طِينٗا
Open ayah 17:61Ndipo (akumbutse) pamene tidauza angelo kuti: “Mugwadireni Adam.” Ndipo adamugwadira kupatula Iblis (iye) adati: “Kodi ndimugwadire yemwe mwamlenga ndi dongo?”
قَالَ أَرَءَيۡتَكَ هَٰذَا ٱلَّذِي كَرَّمۡتَ عَلَيَّ لَئِنۡ أَخَّرۡتَنِ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَأَحۡتَنِكَنَّ ذُرِّيَّتَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلٗا
Open ayah 17:62Adatinso (kwa Allah): “Kodi mukuona uyu amene mwampatsa ulemelero kuposa ine? Ngati mundipatsa nthawi mpaka tsiku la Qiyâma, ndithu ndiononga mbumba yake (yonse) kupatula ochepa basi.”
قَالَ ٱذۡهَبۡ فَمَن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ فَإِنَّ جَهَنَّمَ جَزَآؤُكُمۡ جَزَآءٗ مَّوۡفُورٗا
Open ayah 17:63(Allah) adati: “Choka! Amene adzakutsata mwa iwo, ndithu Jahannam ndiyo mphoto yanu mphoto yokwanira.”
وَٱسۡتَفۡزِزۡ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتَ مِنۡهُم بِصَوۡتِكَ وَأَجۡلِبۡ عَلَيۡهِم بِخَيۡلِكَ وَرَجِلِكَ وَشَارِكۡهُمۡ فِي ٱلۡأَمۡوَٰلِ وَٱلۡأَوۡلَٰدِ وَعِدۡهُمۡۚ وَمَا يَعِدُهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ إِلَّا غُرُورًا
Open ayah 17:64Ndipo apusitse amene ungawathe mwa iwo ndi liwu lako; ndipo asonkhanitsire gulu lako la nkhondo la okwera akavalo ndi loyenda ndi miyendo; tenga gawo lako pa chuma chawo ndi ana awo; ndipo alonjeze (malonjezo abodza).” Koma satana salonjeza china koma chinyengo basi.
إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٞۚ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ وَكِيلٗا
Open ayah 17:65“Ndithu akapolo Anga, ulibe nyonga pa iwo.” Ndipo Mbuye wako akukwanira kukhala mtetezi (wawo).
رَّبُّكُمُ ٱلَّذِي يُزۡجِي لَكُمُ ٱلۡفُلۡكَ فِي ٱلۡبَحۡرِ لِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِكُمۡ رَحِيمٗا
Open ayah 17:66Mbuye wanu ndi yemwe amakuyendetserani zombo pa nyanja kuti munke mufunafuna ubwino Wake. Ndithu Iye Ngwachisoni kwa inu.
وَإِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فِي ٱلۡبَحۡرِ ضَلَّ مَن تَدۡعُونَ إِلَّآ إِيَّاهُۖ فَلَمَّا نَجَّىٰكُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ أَعۡرَضۡتُمۡۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ كَفُورًا
Open ayah 17:67Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika.)
أَفَأَمِنتُمۡ أَن يَخۡسِفَ بِكُمۡ جَانِبَ ٱلۡبَرِّ أَوۡ يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗا ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ وَكِيلًا
Open ayah 17:68Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)?
أَمۡ أَمِنتُمۡ أَن يُعِيدَكُمۡ فِيهِ تَارَةً أُخۡرَىٰ فَيُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ قَاصِفٗا مِّنَ ٱلرِّيحِ فَيُغۡرِقَكُم بِمَا كَفَرۡتُمۡ ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ عَلَيۡنَا بِهِۦ تَبِيعٗا
Open ayah 17:69Kapena mwadziika pachitetezo kuti (Allah) sadzakubwezeraninso m’nyanjamo kachiwiri ndipo nkudzakutumizirani chimphepo chaukali ndikukumizani chifukwa cha kusakhulupirira (ndi kusathokoza kwanu,) kenako inu nkusapeza wokutetezani kwa Ife?
۞وَلَقَدۡ كَرَّمۡنَا بَنِيٓ ءَادَمَ وَحَمَلۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّمَّنۡ خَلَقۡنَا تَفۡضِيلٗا
Open ayah 17:70Ndipo ndithu tawalemekeza ana a Adam; ndipo tawapatsa zokwera pa ntunda ndi pa nyanja; tawapatsa zopatsa zabwino kwambiri; ndipo tawapatsa ulemelero kuposa zambiri m’zomwe tidalenga; ulemelero waukulu kwabasi.
يَوۡمَ نَدۡعُواْ كُلَّ أُنَاسِۭ بِإِمَٰمِهِمۡۖ فَمَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَقۡرَءُونَ كِتَٰبَهُمۡ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلٗا
Open ayah 17:71(Akumbutse za) tsiku lomwe tidzaitana anthu onse m’dzina la mneneri wawo; choncho, amene adzapatsidwe akaundula awo ndi dzanja lamanja iwo adzawerenga akaundula awowo (mwachisangalalo), ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pa (kachinthu kakang’ono monga) kaulusi ka mkati mwa njere ya kanjeza.
وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِۦٓ أَعۡمَىٰ فَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلٗا
Open ayah 17:72Ndipo amene ali wakhungu pano (pa dziko lapansi posapenya zizindikiro) adzakhalanso wakhungu pa tsiku la chimaliziro, ndipo adzakhala wosokera kwambiri njira (kumeneko).
وَإِن كَادُواْ لَيَفۡتِنُونَكَ عَنِ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ لِتَفۡتَرِيَ عَلَيۡنَا غَيۡرَهُۥۖ وَإِذٗا لَّٱتَّخَذُوكَ خَلِيلٗا
Open ayah 17:73Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo).
وَلَوۡلَآ أَن ثَبَّتۡنَٰكَ لَقَدۡ كِدتَّ تَرۡكَنُ إِلَيۡهِمۡ شَيۡـٔٗا قَلِيلًا
Open ayah 17:74Ndipo tikadapanda kukulimbikitsa, ukadapendekera kwa iwo, kupendekera kwa pang’ono.
إِذٗا لَّأَذَقۡنَٰكَ ضِعۡفَ ٱلۡحَيَوٰةِ وَضِعۡفَ ٱلۡمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيۡنَا نَصِيرٗا
Open ayah 17:75Tero ndithu tikadakulawitsa chilango chachikulu cha moyo (wa pa dziko lapansi) ndi chilango chachikulu utafa; kenako siukadapeza mthandizi wokupulumutsa kwa Ife.
وَإِن كَادُواْ لَيَسۡتَفِزُّونَكَ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ لِيُخۡرِجُوكَ مِنۡهَاۖ وَإِذٗا لَّا يَلۡبَثُونَ خِلَٰفَكَ إِلَّا قَلِيلٗا
Open ayah 17:76Ndipo padatsala pang’ono kuti akusowetse mtendere m’dziko ili (la Makka) kuti akutulutse m’menemo; koma pambuyo pako sakadakhala (ndi moyo) kupatula (nthawi) yochepa.
سُنَّةَ مَن قَدۡ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِن رُّسُلِنَاۖ وَلَا تَجِدُ لِسُنَّتِنَا تَحۡوِيلًا
Open ayah 17:77Chimenechi ndi chikhalidwe cha omwe tidawatuma patsogolo pako mwa atumiki Athu, ndipo supeza kusintha pachikhalidwe Chathu.
أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِدُلُوكِ ٱلشَّمۡسِ إِلَىٰ غَسَقِ ٱلَّيۡلِ وَقُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِۖ إِنَّ قُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِ كَانَ مَشۡهُودٗا
Open ayah 17:78Pemphera Swala (za Farazi), dzuwa likapendeka mpaka mu mdima wausiku (zomwe ndi Swala za Dhuhri, Asri, Maghrib ndi Isha), ndipo pempheranso Swala ya Fajir: ndithu Swala ya Fajir amaichitira umboni (angelo).
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَتَهَجَّدۡ بِهِۦ نَافِلَةٗ لَّكَ عَسَىٰٓ أَن يَبۡعَثَكَ رَبُّكَ مَقَامٗا مَّحۡمُودٗا
Open ayah 17:79Ndipo pakati pa usiku, dzuka mtulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma.)
وَقُل رَّبِّ أَدۡخِلۡنِي مُدۡخَلَ صِدۡقٖ وَأَخۡرِجۡنِي مُخۡرَجَ صِدۡقٖ وَٱجۡعَل لِّي مِن لَّدُنكَ سُلۡطَٰنٗا نَّصِيرٗا
Open ayah 17:80Ndipo nena (mawu awa pomwe ukupemphera): “Mbuye wanga! Ndilowetseni, kulowetsa kwabwino (paliponse pamene ndikulowa), ndiponso nditulutseni, kutulutsa kwabwino (paliponse pamene ndikutuluka); ndipatseni mphamvu zochokera kwa Inu zondithandiza ndi kugonjetsera adani.”
وَقُلۡ جَآءَ ٱلۡحَقُّ وَزَهَقَ ٱلۡبَٰطِلُۚ إِنَّ ٱلۡبَٰطِلَ كَانَ زَهُوقٗا
Open ayah 17:81Ndipo nena: “Choonadi chafika, ndipo chachabe chachoka; ndithu chachabe ndichochoka (ngakhale patapita nthawi yaitali).”
وَنُنَزِّلُ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِ مَا هُوَ شِفَآءٞ وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ وَلَا يَزِيدُ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا خَسَارٗا
Open ayah 17:82Ndipo tikuivumbulutsa Qur’an yomwe imachiritsa (matenda a mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira. Komabe osalungama siikuwaonjezera (kanthu kena) koma kutayika.
وَإِذَآ أَنۡعَمۡنَا عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ أَعۡرَضَ وَنَـَٔا بِجَانِبِهِۦ وَإِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ كَانَ يَـُٔوسٗا
Open ayah 17:83Ndipo tikampatsa chisomo munthu, (monga moyo wangwiro ndikupeza bwino), amatembenuka (ndikusiya kutikumbukira ndikutipempha), ndipo amadziika kutali (ndi Ife chifukwa chakudzitama ndikudzikuza), koma masautso akamkhudza, (monga matenda ndi umphawi) amataya mtima kwambiri.
قُلۡ كُلّٞ يَعۡمَلُ عَلَىٰ شَاكِلَتِهِۦ فَرَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَنۡ هُوَ أَهۡدَىٰ سَبِيلٗا
Open ayah 17:84Nena (iwe Mneneri, kwa osakhulupirira a Chikuraishi,): “Aliyense (wa ife ndi inu) akuchita ntchito (zake ndikuyenda panjira yake) ndipo Mbuye wanu Ngodziwa kwambiri za yemwe ali panjira yolondola (potsatira choonadi).”
وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلرُّوحِۖ قُلِ ٱلرُّوحُ مِنۡ أَمۡرِ رَبِّي وَمَآ أُوتِيتُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِ إِلَّا قَلِيلٗا
Open ayah 17:85Ndipo akukufunsa (iwe, Muhammad (s.a.w), anthu ako mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za Mzimu. Nena: “Mzimu ndi chinthu chomwe akuchidziwa Mbuye wanga Yekha; ndipo inu simudapatsidwe nzeru (zozindikilira zinthu) koma pang’ono chabe, (poyerekeza ndi nzeru za Allah).”
وَلَئِن شِئۡنَا لَنَذۡهَبَنَّ بِٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ بِهِۦ عَلَيۡنَا وَكِيلًا
Open ayah 17:86Ndipo tikadafuna kufufuta Qur’an (pachifuwa chako) yomwe takuvumbulutsira, (tikadatha kutero). Kenako sukadapeza kwa Ife wokuimilira ndi kukupulumutsa.
إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّ فَضۡلَهُۥ كَانَ عَلَيۡكَ كَبِيرٗا
Open ayah 17:87Koma (taisiya mu mtima mwako) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Mbuye wako; ndithu ubwino Wake pa iwe ngwaukulu.
قُل لَّئِنِ ٱجۡتَمَعَتِ ٱلۡإِنسُ وَٱلۡجِنُّ عَلَىٰٓ أَن يَأۡتُواْ بِمِثۡلِ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لَا يَأۡتُونَ بِمِثۡلِهِۦ وَلَوۡ كَانَ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٖ ظَهِيرٗا
Open ayah 17:88Nena: “Ngakhale atasonkhana anthu ndi ziwanda (mothandizana) kuti abwere ndi buku longa ili la Qur’an (mukayalidwe ka mawu ndi matanthauzo ake), sangathe kubweretsa longa ilo, ngakhale atathandizana wina ndi mnzake.”
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٖ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورٗا
Open ayah 17:89Ndipo ndithu tawalongosolera anthu, m’Qur’an iyi; mkulongosola kwa njira zosiyanasiyana ndikupereka fanizo lamtundu uliwonse. Ndipo anthu ambiri akukana (zonsezo) koma kusakhulupirira basi.
وَقَالُواْ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ تَفۡجُرَ لَنَا مِنَ ٱلۡأَرۡضِ يَنۢبُوعًا
Open ayah 17:90Ndipo (pamene adalephera kubwera ndi Qur’an yawo,) adati: “Sitingakukhulupirire mpaka utatitulutsira kasupe wosaphwa m’dziko (lathu ili la Makka).”
أَوۡ تَكُونَ لَكَ جَنَّةٞ مِّن نَّخِيلٖ وَعِنَبٖ فَتُفَجِّرَ ٱلۡأَنۡهَٰرَ خِلَٰلَهَا تَفۡجِيرًا
Open ayah 17:91Kapena ukhale ndi munda wazipatso za kanjedza ndi mphesa (kuno ku Makka), ndipo utulutse mitsinje yambiri pakati pa mundapo.
أَوۡ تُسۡقِطَ ٱلسَّمَآءَ كَمَا زَعَمۡتَ عَلَيۡنَا كِسَفًا أَوۡ تَأۡتِيَ بِٱللَّهِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ قَبِيلًا
Open ayah 17:92Kapena utigwetsere zidutswa za thambo pa mitu yathu monga momwe umatiopsezera, apo ayi, um’bweretse Allah ndi angelo (kuti) tionane nawo nkhope kwa nkhope (mwamasomphenya.)”
أَوۡ يَكُونَ لَكَ بَيۡتٞ مِّن زُخۡرُفٍ أَوۡ تَرۡقَىٰ فِي ٱلسَّمَآءِ وَلَن نُّؤۡمِنَ لِرُقِيِّكَ حَتَّىٰ تُنَزِّلَ عَلَيۡنَا كِتَٰبٗا نَّقۡرَؤُهُۥۗ قُلۡ سُبۡحَانَ رَبِّي هَلۡ كُنتُ إِلَّا بَشَرٗا رَّسُولٗا
Open ayah 17:93Kapena ukhale ndi nyumba ya golide, kapena ukwere kumwamba. Ndipo sitikukhulupirira kukwera kwako pokhapokha utatibweretsera buku (lochokera kwa Allah lomwe likulongosola za kuona kwako), kuti tidziliwerenga.” Nena (kwa iwo): “Mbuye wanga alemekezeke ndikupatukana ndi mbiri zopunguka! Ine sindine kanthu koma munthu, mtumiki (monga atumiki ena).”
وَمَا مَنَعَ ٱلنَّاسَ أَن يُؤۡمِنُوٓاْ إِذۡ جَآءَهُمُ ٱلۡهُدَىٰٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَبَعَثَ ٱللَّهُ بَشَرٗا رَّسُولٗا
Open ayah 17:94Ndipo palibe chimene (Amushirikina a m’Makka) chawaletsa kukhulupirira choona pamene chiongoko chawadzera, koma kunena kwawo (kwa umbuli) kwakuti: “Kodi Allah amatuma munthu kukhala Mtumiki (Wake)?
قُل لَّوۡ كَانَ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَلَٰٓئِكَةٞ يَمۡشُونَ مُطۡمَئِنِّينَ لَنَزَّلۡنَا عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَلَكٗا رَّسُولٗا
Open ayah 17:95Nena: “Padziko pakadakhala angelo omayendayenda ndi okhazikika (m’malo awo ndi m’nyumba zawo), tikadawatsitsira m’ngelo monga mtumiki kuchokera kumwamba.”
قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Open ayah 17:96Nena: “(Ngati mukutsutsa uthenga wanga) Allah wakwanira kukhala Mboni (ndi Muweruzi) pakati panga ndi pakati panu (zakuona kwa uthenga wanga kwa inu). Ndithu Iye Ngodziwa za akapolo Ake (zilakolako zawo) Ngowona (zochita zawo).
وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُمۡ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِهِۦۖ وَنَحۡشُرُهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ عُمۡيٗا وَبُكۡمٗا وَصُمّٗاۖ مَّأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ كُلَّمَا خَبَتۡ زِدۡنَٰهُمۡ سَعِيرٗا
Open ayah 17:97Ndipo yemwe Allah wamuongola, (chifukwa cha kukonzeka kwake kwa ubwino), iyeyo ndi amene waongoka; ndipo amene wamulekelera kusokera, (chifukwa cha kuipa kwa khalidwe lake), simungampezere athandizi kupatula Iye (Allah). Ndipo pa tsiku la chiweruziro tidzawasonkhanitsa uku akukokedwa ndi nkhope zawo ali osapenya, osalankhula ndi osamva. Malo awo okhala ndi ku Jahannam. Nthawi iliyonse (Motowo) ukatotobwa, tidzauonjezera kwa iwo kuyaka mwaukali.
ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُم بِأَنَّهُمۡ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدًا
Open ayah 17:98(Chilango) chimenecho ndiyo mphoto yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo zisonyezo (zomwe tidasonyeza kwa iwo), ndi kunena kwawo koti: “Kodi tikadzakhala mafupa ndi zidutswa zonyenyekanyenyeka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
۞أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۡ وَجَعَلَ لَهُمۡ أَجَلٗا لَّا رَيۡبَ فِيهِ فَأَبَى ٱلظَّٰلِمُونَ إِلَّا كُفُورٗا
Open ayah 17:99Kodi (onyalanyaza) sadadziwebe kuti Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka Ngokhoza kulenga ena onga iwo? Ndipo wawaikira nthawi (yodziwika) yopanda chikaiko, (yowaukitsira ku imfa). Koma achinyengo akukana (zonsezi) koma kusakhulupirira basi.
قُل لَّوۡ أَنتُمۡ تَمۡلِكُونَ خَزَآئِنَ رَحۡمَةِ رَبِّيٓ إِذٗا لَّأَمۡسَكۡتُمۡ خَشۡيَةَ ٱلۡإِنفَاقِۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ قَتُورٗا
Open ayah 17:100Nena (kwa opembedza mafano): “Mukadakhala kuti muli nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wanga, mukadachita umbombo (posagawira ena) kuopa umphawi. Ndipo munthu ali ndi khalidwe loumira.”
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ تِسۡعَ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖۖ فَسۡـَٔلۡ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِذۡ جَآءَهُمۡ فَقَالَ لَهُۥ فِرۡعَوۡنُ إِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰمُوسَىٰ مَسۡحُورٗا
Open ayah 17:101Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa zizizwa zoonekera zisanu ndi zinayi (komabe osakhulupirira sadazikhulupirire). Afunse ana a Israyeli pamene adawadzera (Musayo), Farawo adati kwa iye (Mûsa): “Ndithu ine ndikukuona iwe Mûsa kuti walodzedwa.”
قَالَ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَآ أَنزَلَ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ بَصَآئِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰفِرۡعَوۡنُ مَثۡبُورٗا
Open ayah 17:102(Mûsa) adati: “Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza (mitsutso) iyi kupatula Mbuye wathambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farawo kuti waonongeka.”
فَأَرَادَ أَن يَسۡتَفِزَّهُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ فَأَغۡرَقۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ جَمِيعٗا
Open ayah 17:103Choncho (Farawo) adafuna kuwatulutsa m’dziko (la Iguputo Mûsa ndi ana a Israyeli) koma tidammiza iye ndi onse omwe adali naye.
وَقُلۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ لِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱسۡكُنُواْ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ جِئۡنَا بِكُمۡ لَفِيفٗا
Open ayah 17:104(Mûsa ndi anthu ake tidawapulumutsa). Ndipo tidati, kwa ana a Israyeli, pambuyo pake (pommiza Farawo): “Khalani m’dziko (loyera la Shami); ndipo likazadza lonjezo la moyo winawo, tidzakubweretsani nonsenu (muli m’chipwirikiti.)”
وَبِٱلۡحَقِّ أَنزَلۡنَٰهُ وَبِٱلۡحَقِّ نَزَلَۗ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Open ayah 17:105Ndipo chifukwa chobweretsa choonadi pa dziko tidaitumiza (Qur’an); ndipo mwachoonadi, yavumbulutsidwa. Ndipo sitidakutume (ndi china) koma kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino, ndi wochenjeza (osakhulupirira).
وَقُرۡءَانٗا فَرَقۡنَٰهُ لِتَقۡرَأَهُۥ عَلَى ٱلنَّاسِ عَلَىٰ مُكۡثٖ وَنَزَّلۡنَٰهُ تَنزِيلٗا
Open ayah 17:106Ndipo Qur’an iyi taigawa (m’zigawo zosiyanasiyana poivumbulutsa pang’onopang’ono) kuti uwawerengere anthu mwa chifatse ndipo taivumbulutsa pang’onopang’ono.
قُلۡ ءَامِنُواْ بِهِۦٓ أَوۡ لَا تُؤۡمِنُوٓاْۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهِۦٓ إِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ يَخِرُّونَۤ لِلۡأَذۡقَانِۤ سُجَّدٗاۤ
Open ayah 17:107Nena (kwa osakhulupirira a m’Makka mowachenjeza): “Ikhulupirireni (iyi Qur’an) kapena musaikhulupirire, (zonse zili m’chifuniro chanu.) Ndithu amene adapatsidwa nzeru kale (yozindikira za m’mabuku a Allah Qur’an isanadze) ikamalakatulidwa kwa iwo (Qur’aniyi) amagwa ndi zibwano zawo molambira.
وَيَقُولُونَ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِن كَانَ وَعۡدُ رَبِّنَا لَمَفۡعُولٗا
Open ayah 17:108Ndipo amanena: “Mbuye wathu Ngoyera! Ndithu lonjezo la Mbuye wathu ndi lokwaniritsidwa!”
وَيَخِرُّونَ لِلۡأَذۡقَانِ يَبۡكُونَ وَيَزِيدُهُمۡ خُشُوعٗا۩
Open ayah 17:109Ndipo amagwa ndi zibwano zawo uku akulira, ndipo (Qur’an) imawaonjezera kudzichepetsa.
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱللَّهَ أَوِ ٱدۡعُواْ ٱلرَّحۡمَٰنَۖ أَيّٗا مَّا تَدۡعُواْ فَلَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَلَا تَجۡهَرۡ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتۡ بِهَا وَٱبۡتَغِ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلٗا
Open ayah 17:110Nena (kwa Amushirikina): “Mpempheni Allah, m’dzina la Allah kapena mpempheni m’dzina la Rahman; (dzina) lililonse, limene mungamtchulire (zithandizabe); Iye ali nawo maina abwino. Ndipo usawerenge (Qur’an) pa Swala yako ndi mawu okweza, ndiponso usatsitse mawu kwambiri, koma tsata njira yolingana pakati pa zimenezo (pokweza kwambiri kapena kutsitsa zedi).”
وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي لَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلِيّٞ مِّنَ ٱلذُّلِّۖ وَكَبِّرۡهُ تَكۡبِيرَۢا
Open ayah 17:111Ndipo nena: “Kutamandidwa kwabwino nkwa Allah, yemwe saadadzipangire mwana, ndipo alibe m’phatikizi mu ufumu (Wake); ndipo alibe mthandizi (womthandiza) mkufooka; ndipo mkuzeni, kumkuza kwakukulu!”