غافر
Al-Ghaafir
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
حمٓ
Open ayah 40:1Hâ-Mîm.
تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
Open ayah 40:2Kuvumbulutsidwa kwa buku (ili) kwachokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
غَافِرِ ٱلذَّنۢبِ وَقَابِلِ ٱلتَّوۡبِ شَدِيدِ ٱلۡعِقَابِ ذِي ٱلطَّوۡلِۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ إِلَيۡهِ ٱلۡمَصِيرُ
Open ayah 40:3Wokhululuka machimo, Wolandira kulapa (kwa yemwe walapa), Wolanga mwaukali (kwa yemwe wapitiriza kunyoza Allah), Mwini kupereka mtendere. Palibe wopembedzedwa mwa choona koma Iye; kobwerera nkwa Iye.
مَا يُجَٰدِلُ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ إِلَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَلَا يَغۡرُرۡكَ تَقَلُّبُهُمۡ فِي ٱلۡبِلَٰدِ
Open ayah 40:4Sangatsutsane pa zisonyezo za Allah kupatula amene akanira. Choncho kusakunyenge kuyendayenda kwawo pa dziko (kunka nachita malonda ndi kupeza phindu lalikulu ndi malondawo popanda chovuta; posachedwa tiwalanga).
كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَعۡدِهِمۡۖ وَهَمَّتۡ كُلُّ أُمَّةِۭ بِرَسُولِهِمۡ لِيَأۡخُذُوهُۖ وَجَٰدَلُواْ بِٱلۡبَٰطِلِ لِيُدۡحِضُواْ بِهِ ٱلۡحَقَّ فَأَخَذۡتُهُمۡۖ فَكَيۡفَ كَانَ عِقَابِ
Open ayah 40:5Iwo kulibe, anthu a Nuh adakaniranso pamodzi ndi makamu a anthu omwe adali kuda aneneri, m’badwo wa Nuh utatha; ndipo m’badwo uliwonse udaikira mtima kuchita choipa pa mneneri wawo kuti am’gwire (ndi kumupha). Adali kutsutsana poteteza chachabe kuti ndi uwo (mtsutso wawowo) achotse choona. Ndipo ndidawaononga kotheratu. Tayang’ana, chidali bwanji chilango Changa (pa iwo!)
وَكَذَٰلِكَ حَقَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَنَّهُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ
Open ayah 40:6Chonchonso latsimikizika liwu la chilango pa amene akanira (iwe Mtumiki {s.a.w}) chifukwa iwo ndi anthu a ku Moto (kamba kosankhakukanira ndi kusiya kukhulupirira).
ٱلَّذِينَ يَحۡمِلُونَ ٱلۡعَرۡشَ وَمَنۡ حَوۡلَهُۥ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَيُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَيَسۡتَغۡفِرُونَ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْۖ رَبَّنَا وَسِعۡتَ كُلَّ شَيۡءٖ رَّحۡمَةٗ وَعِلۡمٗا فَٱغۡفِرۡ لِلَّذِينَ تَابُواْ وَٱتَّبَعُواْ سَبِيلَكَ وَقِهِمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ
Open ayah 40:7Amene akusenza Arsh (Mpando wachifumu) ndi amene ali mmphepete mwake, akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndiponso akumkhulupirira Iye; ndipo akupemphera chikhululuko amene akhulupirira (ponena kuti): “E Mbuye wathu! Chifundo ndi kudziwa kwanu kwakwanira pa chinthu chilichonse. Khululukirani amene alapa ndi kutsatira njira Yanu; ndipo apewetseni ku chilango cha Jahena!”
رَبَّنَا وَأَدۡخِلۡهُمۡ جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدتَّهُمۡ وَمَن صَلَحَ مِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَأَزۡوَٰجِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡۚ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Open ayah 40:8“E Mbuye wathu! Alowetseni ku Minda yamuyaya imene mudawalonjeza, ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo ndi akazi awo ndi ana awo. Ndithu inu ndi Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”
وَقِهِمُ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ وَمَن تَقِ ٱلسَّيِّـَٔاتِ يَوۡمَئِذٖ فَقَدۡ رَحِمۡتَهُۥۚ وَذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Open ayah 40:9“Ndipo apewetseni ku zoipa; tsono amene mudzampewetsa ku zoipa tsiku limenelo, ndiye kuti mwamchitira chifundo. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.”
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُنَادَوۡنَ لَمَقۡتُ ٱللَّهِ أَكۡبَرُ مِن مَّقۡتِكُمۡ أَنفُسَكُمۡ إِذۡ تُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلۡإِيمَٰنِ فَتَكۡفُرُونَ
Open ayah 40:10Ndithu amene akanira adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Mkwiyo wa Allah pa inu udali waukulu kuposa mkwiyo wanu pa mitima yanu (yomwe yakulowetsani ku chilango) pamene mudali kuitanidwa ku chikhulupiliro, (ku Chisilamu); ndipo mudali kukanira.”
قَالُواْ رَبَّنَآ أَمَتَّنَا ٱثۡنَتَيۡنِ وَأَحۡيَيۡتَنَا ٱثۡنَتَيۡنِ فَٱعۡتَرَفۡنَا بِذُنُوبِنَا فَهَلۡ إِلَىٰ خُرُوجٖ مِّن سَبِيلٖ
Open ayah 40:11Adzanena: “E Mbuye wathu! Mudatipatsa imfa kawiri; (imfa yoyamba tisanabadwe, ndipo imfa ya chiwiri pa dziko). Ndipo mudatipatsa moyo kawiri; (moyo woyamba wa pa dziko lapansi, ndipo moyo wachiwiri wakuuka kwa akufa). Choncho tavomereza machimo athu. Kodi pali njira yotulukira (ku chilango kuno)?”
ذَٰلِكُم بِأَنَّهُۥٓ إِذَا دُعِيَ ٱللَّهُ وَحۡدَهُۥ كَفَرۡتُمۡ وَإِن يُشۡرَكۡ بِهِۦ تُؤۡمِنُواْۚ فَٱلۡحُكۡمُ لِلَّهِ ٱلۡعَلِيِّ ٱلۡكَبِيرِ
Open ayah 40:12Zimenezi nchifukwa chakuti akapemphedwa Allah Yekha, mudali kutsutsa. Koma akaphatikizidwa (ndi milungu yabodza) mudali kukhulupirira. Choncho chiweruzo ncha Allah, Wotukuka, Wamkulu!
هُوَ ٱلَّذِي يُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ وَيُنَزِّلُ لَكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ رِزۡقٗاۚ وَمَا يَتَذَكَّرُ إِلَّا مَن يُنِيبُ
Open ayah 40:13Iye ndi Yemwe akukuonetsani zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Yake yoposa), ndipo akukutsitsirani madzi kumwamba chifukwa cha inu kuti abweretse zokupatsani moyo (monga chakudya ndi zina). Koma palibe amene akukumbukira kwenikweni kupatula amene watembenukira (kwa Allah).
فَٱدۡعُواْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Open ayah 40:14Choncho mpempheni Allah pomuyeretsera mapemphero Ake ngakhale (kumuyeretsera kwanu kwa mapempheroko) kuwaipire okanira.
رَفِيعُ ٱلدَّرَجَٰتِ ذُو ٱلۡعَرۡشِ يُلۡقِي ٱلرُّوحَ مِنۡ أَمۡرِهِۦ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ لِيُنذِرَ يَوۡمَ ٱلتَّلَاقِ
Open ayah 40:15Iye Ngotukuka ulemelero, Mwini Arsh (Mpando wachifumu); amapereka chivumbulutso (Chake) mwa lamulo lake kwa yemwe wamfuna mwa akapolo Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku lokumana (anthu onse).
يَوۡمَ هُم بَٰرِزُونَۖ لَا يَخۡفَىٰ عَلَى ٱللَّهِ مِنۡهُمۡ شَيۡءٞۚ لِّمَنِ ٱلۡمُلۡكُ ٱلۡيَوۡمَۖ لِلَّهِ ٱلۡوَٰحِدِ ٱلۡقَهَّارِ
Open ayah 40:16Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Allah). Ndipo palibe chilichonse chidzabisidwa kwa Allah (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa): “Kodi ufumu ngwayani lero? Ngwa Allah, Mmodzi yekha, Wogonjetsa, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”
ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡۚ لَا ظُلۡمَ ٱلۡيَوۡمَۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ
Open ayah 40:17Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe kupondereza lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu Allah Ngwachangu (pa) chiwerengero Chake.
وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡأٓزِفَةِ إِذِ ٱلۡقُلُوبُ لَدَى ٱلۡحَنَاجِرِ كَٰظِمِينَۚ مَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنۡ حَمِيمٖ وَلَا شَفِيعٖ يُطَاعُ
Open ayah 40:18Achenjeze (iwe Mtumiki {s.a.w}) za tsiku lomwe lili pafupi (Qiyâma), pamene mitima idzakhala ku mmero (chifukwa cha mantha oopsa) atadzadzidwa ndi nkhawa. Wodzichitira chinyengo sazakhala ndi bwenzi ngakhale mpulumutsi womveredwa (powateteza iwo).
يَعۡلَمُ خَآئِنَةَ ٱلۡأَعۡيُنِ وَمَا تُخۡفِي ٱلصُّدُورُ
Open ayah 40:19Iye (Allah ) akudziwa kuyang’ana kwa maso a chinyengo ndi zimene zifuwa zikubisa (mzobisika zonse).
وَٱللَّهُ يَقۡضِي بِٱلۡحَقِّۖ وَٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَقۡضُونَ بِشَيۡءٍۗ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
Open ayah 40:20Ndipo Allah amaweruza mwa chilungamo. Koma omwe akuwapembedza kusiya Allah, saweruza chilichonse (chifukwa cha kufooka ndi kulephera kwawo). Ndithu Allah Yekha ndiye Wakumva, Woona (chilichonse).
۞أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ كَانُواْ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَانُواْ هُمۡ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗ وَءَاثَارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُ بِذُنُوبِهِمۡ وَمَا كَانَ لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن وَاقٖ
Open ayah 40:21Kodi sadayende padziko ndikuona momwe mathero a anthu akale adalili? Adali opambana panyonga ndi mzochitachita zawo za mdziko kuposa iwo, (monga kumanga nyumba zikuluzikulu). Koma Allah adawaononga, psiti! chifukwa cha machimo awo, ndipo adalibe mtetezi ku chilango cha Allah.
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَانَت تَّأۡتِيهِمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَكَفَرُواْ فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ قَوِيّٞ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ
Open ayah 40:22Zimenezo nchifukwa chakuti ankawadzera aneneri awo ndi zizizwa zoonekera poyera, koma adazikanira. Choncho Allah adawaononga motheratu. Iye Ngwanyonga zambiri, Wolanga mokhwima.
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ
Open ayah 40:23Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa ndi zizizwa zathu ndi zisonyezo zamphamvu zoonekera poyera,
إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَقَٰرُونَ فَقَالُواْ سَٰحِرٞ كَذَّابٞ
Open ayah 40:24Kwa Farawo ndi Haamana ndi Kaaruna. Ndipo adati: “(Uyu) ndi wamatsenga, wabodza.”
فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡحَقِّ مِنۡ عِندِنَا قَالُواْ ٱقۡتُلُوٓاْ أَبۡنَآءَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ وَٱسۡتَحۡيُواْ نِسَآءَهُمۡۚ وَمَا كَيۡدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ
Open ayah 40:25Ndipo pamene (Mûsa) adawadzera ndi choona chochokera kwa Ife, (Farawo pamodzi ndi omtsatira) adati: “Iphani ana achimuna a amene akhulupirira naye limodzi; ndipo siyani ana awo achikazi.” Koma ndale za okanira sizakanthu, nzotaika.
وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ ذَرُونِيٓ أَقۡتُلۡ مُوسَىٰ وَلۡيَدۡعُ رَبَّهُۥٓۖ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يُبَدِّلَ دِينَكُمۡ أَوۡ أَن يُظۡهِرَ فِي ٱلۡأَرۡضِ ٱلۡفَسَادَ
Open ayah 40:26Ndipo Farawo adati: “Ndilekeni ndimuphe Mûsa; ampemphe Mbuye wakeyo (kuti ampulumutse kwa ine). Ine ndikuopera kuti angasinthe chipembedzo chanu, kapena kufalitsa chisokonezo pa dziko.”
وَقَالَ مُوسَىٰٓ إِنِّي عُذۡتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُم مِّن كُلِّ مُتَكَبِّرٖ لَّا يُؤۡمِنُ بِيَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ
Open ayah 40:27Ndipo Mûsa adati (kwa Farawo pa modzi ndi anthu ake): “Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye wanga amenenso ali Mbuye wanu (ku chiwembu) chochokera kwa aliyense wodzikweza, wosakhulupirira za tsiku la chiwerengero.
وَقَالَ رَجُلٞ مُّؤۡمِنٞ مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَكۡتُمُ إِيمَٰنَهُۥٓ أَتَقۡتُلُونَ رَجُلًا أَن يَقُولَ رَبِّيَ ٱللَّهُ وَقَدۡ جَآءَكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ مِن رَّبِّكُمۡۖ وَإِن يَكُ كَٰذِبٗا فَعَلَيۡهِ كَذِبُهُۥۖ وَإِن يَكُ صَادِقٗا يُصِبۡكُم بَعۡضُ ٱلَّذِي يَعِدُكُمۡۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ كَذَّابٞ
Open ayah 40:28Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!”
يَٰقَوۡمِ لَكُمُ ٱلۡمُلۡكُ ٱلۡيَوۡمَ ظَٰهِرِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَمَن يَنصُرُنَا مِنۢ بَأۡسِ ٱللَّهِ إِن جَآءَنَاۚ قَالَ فِرۡعَوۡنُ مَآ أُرِيكُمۡ إِلَّا مَآ أَرَىٰ وَمَآ أَهۡدِيكُمۡ إِلَّا سَبِيلَ ٱلرَّشَادِ
Open ayah 40:29“E inu anthu anga! Ufumu walero ngwanu: mwagonjetsa dziko (la Iguputo). Ndani amene angatipulumutse ku chilango cha Allah ngati chitatidzera?” Farawo adati: “Sindikukupatsani maganizo koma okhawo ndikuwaona (kuti ndi abwino) ndiponso sindikukuwongolerani koma kunjira yoongoka.”
وَقَالَ ٱلَّذِيٓ ءَامَنَ يَٰقَوۡمِ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُم مِّثۡلَ يَوۡمِ ٱلۡأَحۡزَابِ
Open ayah 40:30Ndipo munthu wokhulupirira uja adanena: “E inu anthu anga! Ine ndikukuoperani (za tsiku la masautso) monga tsiku la magulu (omwe adaukira aneneri awo).”
مِثۡلَ دَأۡبِ قَوۡمِ نُوحٖ وَعَادٖ وَثَمُودَ وَٱلَّذِينَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡۚ وَمَا ٱللَّهُ يُرِيدُ ظُلۡمٗا لِّلۡعِبَادِ
Open ayah 40:31“Monga chikhalidwe cha anthu a Nuh, Âdi, Samudi ndi anthu omwe adadza pambuyo pawo. Koma Allah safuna kupondereza akapolo Ake.”
وَيَٰقَوۡمِ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ يَوۡمَ ٱلتَّنَادِ
Open ayah 40:32“Ndiponso anthu anga! Ine ndikukuoperani tsiku la kuitanizana (anthu).”
يَوۡمَ تُوَلُّونَ مُدۡبِرِينَ مَا لَكُم مِّنَ ٱللَّهِ مِنۡ عَاصِمٖۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ
Open ayah 40:33“Tsiku limene mudzathawa ndi kutembenuza misana yanu; pomwe simudzakhala ndi mtetezi ku chilango cha Allah; ndipo amene Allah wamulekelera kusokera (chifukwa cha zochita zake zoipa), ndiye kuti sangapeze muongoli.”
وَلَقَدۡ جَآءَكُمۡ يُوسُفُ مِن قَبۡلُ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا زِلۡتُمۡ فِي شَكّٖ مِّمَّا جَآءَكُم بِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَا هَلَكَ قُلۡتُمۡ لَن يَبۡعَثَ ٱللَّهُ مِنۢ بَعۡدِهِۦ رَسُولٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ مُّرۡتَابٌ
Open ayah 40:34Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri.
ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡۖ كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ وَعِندَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ قَلۡبِ مُتَكَبِّرٖ جَبَّارٖ
Open ayah 40:35Amene akutsutsana za zisonyezo za Allah popanda umboni uliwonse umene wawadzera. (Kutsutsa zisonyezo za Allah) nchokwiitsa Allah kwakukulu ndi kwa amene akhulupirira (mwa Allah). Momwemo ndi momwe Allah amadindira pamtima wa aliyense wodzikuza, wodzitukumula.
وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ يَٰهَٰمَٰنُ ٱبۡنِ لِي صَرۡحٗا لَّعَلِّيٓ أَبۡلُغُ ٱلۡأَسۡبَٰبَ
Open ayah 40:36Ndipo Farawo adati: “E iwe Haamana! Ndimangire chipilala kuti ndikafike kunjira,”
أَسۡبَٰبَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ فَأَطَّلِعَ إِلَىٰٓ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُۥ كَٰذِبٗاۚ وَكَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِفِرۡعَوۡنَ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ وَصُدَّ عَنِ ٱلسَّبِيلِۚ وَمَا كَيۡدُ فِرۡعَوۡنَ إِلَّا فِي تَبَابٖ
Open ayah 40:37“Njira za kumwamba kuti ndikamuone Mulungu wa Mûsa. Koma ndithu ine ndikudziwa kuti ameneyu ngonama.” Umo ndi momwe zochita zoipa za Farawo zidakongoletsedwera kwa iye, ndipo adatsekeretsedwa ku njira yoona, ndipo chiwembu cha Farawo sichakanthu, koma choonongeka.
وَقَالَ ٱلَّذِيٓ ءَامَنَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُونِ أَهۡدِكُمۡ سَبِيلَ ٱلرَّشَادِ
Open ayah 40:38Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.”
يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا مَتَٰعٞ وَإِنَّ ٱلۡأٓخِرَةَ هِيَ دَارُ ٱلۡقَرَارِ
Open ayah 40:39“E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.”
مَنۡ عَمِلَ سَيِّئَةٗ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَاۖ وَمَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ يُرۡزَقُونَ فِيهَا بِغَيۡرِ حِسَابٖ
Open ayah 40:40“Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.”
۞وَيَٰقَوۡمِ مَا لِيٓ أَدۡعُوكُمۡ إِلَى ٱلنَّجَوٰةِ وَتَدۡعُونَنِيٓ إِلَى ٱلنَّارِ
Open ayah 40:41“E inu anthu anga! Chifukwa ninji, ine ndikukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu mukundiitanira ku Moto?”
تَدۡعُونَنِي لِأَكۡفُرَ بِٱللَّهِ وَأُشۡرِكَ بِهِۦ مَا لَيۡسَ لِي بِهِۦ عِلۡمٞ وَأَنَا۠ أَدۡعُوكُمۡ إِلَى ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡغَفَّٰرِ
Open ayah 40:42“Mukundiitanira kuti ndimkane Allah, ndi kuphatikiza ndi milungu yonama yomwe ine sindikuidziwa, pomwe ine ndikukuitanirani kwa Mwini mphamvu zoposa, Wokhululuka kwambiri?”
لَا جَرَمَ أَنَّمَا تَدۡعُونَنِيٓ إِلَيۡهِ لَيۡسَ لَهُۥ دَعۡوَةٞ فِي ٱلدُّنۡيَا وَلَا فِي ٱلۡأٓخِرَةِ وَأَنَّ مَرَدَّنَآ إِلَى ٱللَّهِ وَأَنَّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ هُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ
Open ayah 40:43“Palibe chikaiko, ndithu zomwe mukundiitanirazo (kuti ndizipembedze) zilibe (kuyankha) pempho lililonse pano pa dziko lapansi ngakhale tsiku lachimaliziro. Ndipo kobwerera kwathu nkwa Allah basi. Ndipo, wopyola malire (a Allah) iwowo ndiwo anthu a ku Moto.”
فَسَتَذۡكُرُونَ مَآ أَقُولُ لَكُمۡۚ وَأُفَوِّضُ أَمۡرِيٓ إِلَى ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ بَصِيرُۢ بِٱلۡعِبَادِ
Open ayah 40:44“Choncho posachedwa, mudzakumbukira zimene ndikukuuzanizi. Ndipo ine ndikutula zinthu zanga kwa Allah, ndithu Allah akuona za anthu Ake.”
فَوَقَىٰهُ ٱللَّهُ سَيِّـَٔاتِ مَا مَكَرُواْۖ وَحَاقَ بِـَٔالِ فِرۡعَوۡنَ سُوٓءُ ٱلۡعَذَابِ
Open ayah 40:45Choncho Allah adam’teteza ku zoipa zomwe adam’tchera. Ndipo chilango choipa chidawazungulira anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini.)
ٱلنَّارُ يُعۡرَضُونَ عَلَيۡهَا غُدُوّٗا وَعَشِيّٗاۚ وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ أَدۡخِلُوٓاْ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ أَشَدَّ ٱلۡعَذَابِ
Open ayah 40:46Zilango za kumoto zikusonyezedwa kwa iwo mmawa ndi madzulo. Ndipo tsiku lomwe Qiyâma idzafika (kudzanenedwa): “Alowetseni anthu a Farawo ku chilango cha ukali kwambiri (choposa chomwe adalandira mmanda mwawo).”
وَإِذۡ يَتَحَآجُّونَ فِي ٱلنَّارِ فَيَقُولُ ٱلضُّعَفَٰٓؤُاْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا كُنَّا لَكُمۡ تَبَعٗا فَهَلۡ أَنتُم مُّغۡنُونَ عَنَّا نَصِيبٗا مِّنَ ٱلنَّارِ
Open ayah 40:47Ndipo (akumbutse) pamene azidzatsutsana m’Moto! Pamene ofooka (amene amatsatira) adzanena kwa omwe adali kudzikweza: “Ndithu ife tidali otsatira anu; kodi simungathe kutichotsera gawo lina la chilango cha Moto?”
قَالَ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا كُلّٞ فِيهَآ إِنَّ ٱللَّهَ قَدۡ حَكَمَ بَيۡنَ ٱلۡعِبَادِ
Open ayah 40:48Awo amene adadzikweza adzati: “Ndithu ife tonse tili mommuno. Ndithu Allah waweruza kale pakati pa akapolo (Ake). (Choncho palibe chilichonse chimene tingaphulepo).”
وَقَالَ ٱلَّذِينَ فِي ٱلنَّارِ لِخَزَنَةِ جَهَنَّمَ ٱدۡعُواْ رَبَّكُمۡ يُخَفِّفۡ عَنَّا يَوۡمٗا مِّنَ ٱلۡعَذَابِ
Open ayah 40:49Ndipo a ku Moto adzayankhula kwa (angelo) olondera Jahannam: “Mpempheni Mbuye wanu, atipeputsire chilangochi tsiku limodzi.”
قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ تَكُ تَأۡتِيكُمۡ رُسُلُكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِۖ قَالُواْ بَلَىٰۚ قَالُواْ فَٱدۡعُواْۗ وَمَا دُعَٰٓؤُاْ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٍ
Open ayah 40:50(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.”
إِنَّا لَنَنصُرُ رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَيَوۡمَ يَقُومُ ٱلۡأَشۡهَٰدُ
Open ayah 40:51Ndithu Ife timapulumutsa aneneri Athu ndi amene akhulupirira pa moyo wa dziko lapansi ndi tsiku limene zidzaimilira mboni (kupereka umboni).
يَوۡمَ لَا يَنفَعُ ٱلظَّٰلِمِينَ مَعۡذِرَتُهُمۡۖ وَلَهُمُ ٱللَّعۡنَةُ وَلَهُمۡ سُوٓءُ ٱلدَّارِ
Open ayah 40:52Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri.
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡهُدَىٰ وَأَوۡرَثۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡكِتَٰبَ
Open ayah 40:53Ndithu Mûsa tidampatsa chiongoko, ndipo tidawasiira buku ana a Israyeli.
هُدٗى وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Open ayah 40:54(Lomwe lidali) chiongoko ndi chikumbutso kwa eni nzeru.
فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لِذَنۢبِكَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِبۡكَٰرِ
Open ayah 40:55Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa.
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡ إِن فِي صُدُورِهِمۡ إِلَّا كِبۡرٞ مَّا هُم بِبَٰلِغِيهِۚ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
Open ayah 40:56Ndithu amene akutsutsana pa zisonyezo za Allah popanda umboni umene udawadzera, mmitima mwawo mulibe chilichonse koma kudzitukumula (ndikufuna ukulu), koma saufikira. Dzitchinjirize mwa Allah, ndithu Iye Ngwakumva, Ngopenya.
لَخَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ أَكۡبَرُ مِنۡ خَلۡقِ ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Open ayah 40:57Ndithu kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu. Koma anthu ambiri sakudziwa.
وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَلَا ٱلۡمُسِيٓءُۚ قَلِيلٗا مَّا تَتَذَكَّرُونَ
Open ayah 40:58Ndipo sali wolingana wakhungu ndi wopenya ndiponso amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi wochita zoipa. Zimene inu mukumbukira nzochepa, ndithu!
إِنَّ ٱلسَّاعَةَ لَأٓتِيَةٞ لَّا رَيۡبَ فِيهَا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يُؤۡمِنُونَ
Open ayah 40:59Ndithu Qiyâma idza; ndipo za iyo palibe chikaiko. Koma anthu ambiri sakhulupirira.
وَقَالَ رَبُّكُمُ ٱدۡعُونِيٓ أَسۡتَجِبۡ لَكُمۡۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِي سَيَدۡخُلُونَ جَهَنَّمَ دَاخِرِينَ
Open ayah 40:60Ndipo Mbuye wanu wanena: “Ndipempheni, ndikuyankhani; koma amene akudzikweza posiya kundipembedza, adzalowa ku Jahannam ali oyaluka.”
ٱللَّهُ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِتَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَشۡكُرُونَ
Open ayah 40:61Allah ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti mupumule mmenemo, ndi usana kukhala wounika (kuti muthe kuchita ntchito zanu). Ndithu Allah ndi Mwini kupereka ufulu kwa anthu. Koma anthu ambiri sathokoza.
ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖ لَّآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ
Open ayah 40:62Iyeyo ndiye Allah, Mbuye wanu; Mlengi wa chilichonse palibe wina wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Nanga kodi mukutembenuzidwa chotani (kuchoka ku zoona)!
كَذَٰلِكَ يُؤۡفَكُ ٱلَّذِينَ كَانُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ يَجۡحَدُونَ
Open ayah 40:63Momwemo ndi mmene adatembenuziridwa amene adali kutsutsa zisonyezo za Allah.
ٱللَّهُ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ قَرَارٗا وَٱلسَّمَآءَ بِنَآءٗ وَصَوَّرَكُمۡ فَأَحۡسَنَ صُوَرَكُمۡ وَرَزَقَكُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡۖ فَتَبَارَكَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 40:64Allah ndi Amene adakupangirani nthaka kukhala pamalo anu okhalapo, ndi thambo kukhala ngati denga (losagwa); ndipo adakujambulani maonekedwe ndikukongoletsa maonekedwe anu; ndipo adakupatsani zinthu zabwino. Ameneyo ndiye Allah, Mbuye wanu. Choncho walemekezeka Allah, Mbuye wa zolengedwa.”
هُوَ ٱلۡحَيُّ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَٱدۡعُوهُ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَۗ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 40:65Iye Ngwamoyo Wamuyaya; palibe wopembedzedwa wina, koma Iye. Choncho mpembedzeni momuyeretsera chipembedzo. (Musapembedze milungu ina mophatikiza ndi Iye). Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa.
۞قُلۡ إِنِّي نُهِيتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَمَّا جَآءَنِيَ ٱلۡبَيِّنَٰتُ مِن رَّبِّي وَأُمِرۡتُ أَنۡ أُسۡلِمَ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 40:66Nena: “Ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah, pamene zidandidzera zisonyezo zoonekera kuchokera kwa Mbuye wanga; ndipo ndalamulidwa kugonjera Mbuye wa zolengedwa zonse.”
هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن تُرَابٖ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٖ ثُمَّ مِنۡ عَلَقَةٖ ثُمَّ يُخۡرِجُكُمۡ طِفۡلٗا ثُمَّ لِتَبۡلُغُوٓاْ أَشُدَّكُمۡ ثُمَّ لِتَكُونُواْ شُيُوخٗاۚ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ مِن قَبۡلُۖ وَلِتَبۡلُغُوٓاْ أَجَلٗا مُّسَمّٗى وَلَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ
Open ayah 40:67Iye ndi Amene adakulengani kuchokera ku dothi, kenako kuchokera ku dontho la umuna, kenako kuchokera mmagazi; kenako ndikukutulutsani muli khanda; ndipo kenako (adakusiyani) kuti mufike nthawi yanyonga zanu. Ndipo kenako (adakulekani) kuti mukhale nkhalamba. Ndipo ena a inu amapatsidwa imfa asadaifike (nthawi ya ukalamba) nkuti muifikire nthawi imene yaikidwa; (zoterezi nkuti inu) mukhale ndi nzeru.
هُوَ ٱلَّذِي يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ فَإِذَا قَضَىٰٓ أَمۡرٗا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Open ayah 40:68Iye ndi Yemwe amapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo akafuna kuchita chinthu ndithu amanena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo chimachitika.
أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ أَنَّىٰ يُصۡرَفُونَ
Open ayah 40:69Kodi sukuona amene akutsutsana za zisonyezo za Allah? Kodi nchotani akutembenuzidwa (kusiya choonadi?)
ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِٱلۡكِتَٰبِ وَبِمَآ أَرۡسَلۡنَا بِهِۦ رُسُلَنَاۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Open ayah 40:70Amene alitsutsa buku ndi zomwe tidawatuma nazo atumiki athu; koma posachedwa adziwa.
إِذِ ٱلۡأَغۡلَٰلُ فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ وَٱلسَّلَٰسِلُ يُسۡحَبُونَ
Open ayah 40:71Pamene magoli ali m’makosi mwawo ndi unyolo (uli mmiyendo) akukokedwa,
فِي ٱلۡحَمِيمِ ثُمَّ فِي ٱلنَّارِ يُسۡجَرُونَ
Open ayah 40:72M’madzi otentha, kenako m’moto akuotchedwa.
ثُمَّ قِيلَ لَهُمۡ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡ تُشۡرِكُونَ
Open ayah 40:73Kenako adzauzidwa: “Ili kuti (milungu) imene mudali kuiphatikiza (ndi Allah),”
مِن دُونِ ٱللَّهِۖ قَالُواْ ضَلُّواْ عَنَّا بَل لَّمۡ نَكُن نَّدۡعُواْ مِن قَبۡلُ شَيۡـٔٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Open ayah 40:74“Mmalo mopembedza Allah?” Adzanena: “Yatisowa, koma chiyambire kale sitidali kupembedza chilichonse (kupatula Inu).” Umo ndi momwe Allah akuwalekelera kusokera okanira.
ذَٰلِكُم بِمَا كُنتُمۡ تَفۡرَحُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَبِمَا كُنتُمۡ تَمۡرَحُونَ
Open ayah 40:75“Izi, (zimene zakupezani ku Moto kuno), nchifukwa chakuti mudali kudzikweza pa dziko mosayenera. Ndiponso chifukwa chakuti mudali kunyada.
ٱدۡخُلُوٓاْ أَبۡوَٰبَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ فَبِئۡسَ مَثۡوَى ٱلۡمُتَكَبِّرِينَ
Open ayah 40:76Lowani m’makomo a Jahannam; mukhala mmenemo nthawi yaitali. Taonani kuipa malo a odzikweza!”
فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞۚ فَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعۡضَ ٱلَّذِي نَعِدُهُمۡ أَوۡ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيۡنَا يُرۡجَعُونَ
Open ayah 40:77Chonco pirira, ndithu lonjezo la Allah ndiloona. Mwina tikusonyeza zina mwa zomwe tawalonjeza, kapena tikupatsa imfa (usadazione. Basi, palibe chikaiko, zichitika chifukwa chakuti onse) adzabwezedwa kwa Ife.
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا رُسُلٗا مِّن قَبۡلِكَ مِنۡهُم مَّن قَصَصۡنَا عَلَيۡكَ وَمِنۡهُم مَّن لَّمۡ نَقۡصُصۡ عَلَيۡكَۗ وَمَا كَانَ لِرَسُولٍ أَن يَأۡتِيَ بِـَٔايَةٍ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ فَإِذَا جَآءَ أَمۡرُ ٱللَّهِ قُضِيَ بِٱلۡحَقِّ وَخَسِرَ هُنَالِكَ ٱلۡمُبۡطِلُونَ
Open ayah 40:78Ndithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira (nkhani zawo ndi maina awo). Ena mwa iwo sitidakusimbire. Sikudali kotheka kwa mtumiki aliyense kudzetsa chozizwitsa mwa yekha, koma ndi chifuniro cha Allah. Ndipo lamulo la Allah likadzadza, kudzaweruzidwa mwa choonadi. Ndipo ochita zachabe panthawi imeneyo adzataika; (adzaluza).
ٱللَّهُ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَنۡعَٰمَ لِتَرۡكَبُواْ مِنۡهَا وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Open ayah 40:79Allah ndi Yemwe wakupangirani nyama kuti mudzizikwera zina mwa izo, ndipo zina mwa izo kuti muzidya.
وَلَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ وَلِتَبۡلُغُواْ عَلَيۡهَا حَاجَةٗ فِي صُدُورِكُمۡ وَعَلَيۡهَا وَعَلَى ٱلۡفُلۡكِ تُحۡمَلُونَ
Open ayah 40:80Ndipo mmenemo mulinazo zokuthandizani zambiri; ndipo kupyolera mzimenezo mukupeza zokhumba za mitima yanu; pa izo, ndi pa zombo, mukunyamulidwa.
وَيُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ فَأَيَّ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ تُنكِرُونَ
Open ayah 40:81Ndipo (Iye) amakuonetsani zisonyezo Zake. Kodi ndi ziti m’zisonyezo za Allah zimene mukuzikana?
أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَانُوٓاْ أَكۡثَرَ مِنۡهُمۡ وَأَشَدَّ قُوَّةٗ وَءَاثَارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Open ayah 40:82Kodi sadayende padziko ndikuona momwe adalili mathero a omwe adali patsogolo pawo? Adali ochuluka kwambiri kuposa iwo; ndiponso adali anyonga kwambiri ndi ochulukitsa zomangamanga mdziko. Koma sizidawathandize zimene adali kuchita.
فَلَمَّا جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَرِحُواْ بِمَا عِندَهُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Open ayah 40:83Koma pamene atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, adakondwera ndi kudziwa komwe adali nako, (ndipo sadalabadire zomwe atumiki adadza nazo). Choncho zidawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe.
فَلَمَّا رَأَوۡاْ بَأۡسَنَا قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَحۡدَهُۥ وَكَفَرۡنَا بِمَا كُنَّا بِهِۦ مُشۡرِكِينَ
Open ayah 40:84Ndipo pamene adachiona chilango Chathu, adanena (kuti): “Takhulupirira mwa Allah Yekha, ndipo tikuzikana zimene tidali kumphatikiza nazo.”
فَلَمۡ يَكُ يَنفَعُهُمۡ إِيمَٰنُهُمۡ لَمَّا رَأَوۡاْ بَأۡسَنَاۖ سُنَّتَ ٱللَّهِ ٱلَّتِي قَدۡ خَلَتۡ فِي عِبَادِهِۦۖ وَخَسِرَ هُنَالِكَ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Open ayah 40:85Koma chikhulupiliro chawo sichidali chowathandiza panthawi imeneyo, pomwe adali atachiona kale chilango Chathu. Ichi ndi chizolowezi cha Allah chomwe chidapita pa akapolo (Ake onse kuti chilango chikadza, kulapa sikuvomerezedwa). Choncho pamenepo, okanira adaluza.