الحج
Al-Hajj
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡۚ إِنَّ زَلۡزَلَةَ ٱلسَّاعَةِ شَيۡءٌ عَظِيمٞ
Open ayah 22:1E inu anthu! Opani Mbuye wanu (ndipo kumbukirani tsiku la Kiyâma). Ndithu kugwedezeka kwa Kiyâma ndichinthu chachikulu (kwabasi).
يَوۡمَ تَرَوۡنَهَا تَذۡهَلُ كُلُّ مُرۡضِعَةٍ عَمَّآ أَرۡضَعَتۡ وَتَضَعُ كُلُّ ذَاتِ حَمۡلٍ حَمۡلَهَا وَتَرَى ٱلنَّاسَ سُكَٰرَىٰ وَمَا هُم بِسُكَٰرَىٰ وَلَٰكِنَّ عَذَابَ ٱللَّهِ شَدِيدٞ
Open ayah 22:2Tsiku limene mudzaione (Qiyâmayo), mkazi aliyense woyamwitsa adzaiwala (mwana wake) womuyamwitsa, ndipo (mkazi) aliyense wapakati adzataya pakati pake; ndipo udzawaona anthu ataledzera, pomwe sadaledzere; koma ndi chilango chaukali cha Allah (chimene chawapeza).
وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِي ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَيَتَّبِعُ كُلَّ شَيۡطَٰنٖ مَّرِيدٖ
Open ayah 22:3Ndipo alipo ena mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ndipo akutsatira satana aliyense wolakwa.
كُتِبَ عَلَيۡهِ أَنَّهُۥ مَن تَوَلَّاهُ فَأَنَّهُۥ يُضِلُّهُۥ وَيَهۡدِيهِ إِلَىٰ عَذَابِ ٱلسَّعِيرِ
Open ayah 22:4(Za satana), kwalembedwa kuti amene amsankhe kukhala bwenzi lake, ndithu iye amsokeretsa ndi kumtsogolera ku chilango cha Moto.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي رَيۡبٖ مِّنَ ٱلۡبَعۡثِ فَإِنَّا خَلَقۡنَٰكُم مِّن تُرَابٖ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٖ ثُمَّ مِنۡ عَلَقَةٖ ثُمَّ مِن مُّضۡغَةٖ مُّخَلَّقَةٖ وَغَيۡرِ مُخَلَّقَةٖ لِّنُبَيِّنَ لَكُمۡۚ وَنُقِرُّ فِي ٱلۡأَرۡحَامِ مَا نَشَآءُ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى ثُمَّ نُخۡرِجُكُمۡ طِفۡلٗا ثُمَّ لِتَبۡلُغُوٓاْ أَشُدَّكُمۡۖ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ وَمِنكُم مَّن يُرَدُّ إِلَىٰٓ أَرۡذَلِ ٱلۡعُمُرِ لِكَيۡلَا يَعۡلَمَ مِنۢ بَعۡدِ عِلۡمٖ شَيۡـٔٗاۚ وَتَرَى ٱلۡأَرۡضَ هَامِدَةٗ فَإِذَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهَا ٱلۡمَآءَ ٱهۡتَزَّتۡ وَرَبَتۡ وَأَنۢبَتَتۡ مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٖ
Open ayah 22:5E inu anthu! Ngati muli m’chikaiko za kuuka ku imfa, (ndipo mukuona kuti nzosatheka, yang’anani mmene tidakulengerani). Ndithu Ife tidakulengani ndi dothi, ndipo (timakulengani) ndi dontho la umuna, komanso (umunawo udasanduka) gawo lamagazi, kenako gawo la mnofti woumbidwa (chithunzi cha munthu) ndi wosaumbidwa, kuti tikulongosolereni (kukhoza Kwathu;) ndipo Ife timachikhazikitsa mchiberekero; chimene tifuna kufikira nthawi yake yoyikidwa kenako timakutulutsani muli khanda, (tsono timakulerani) kuti mufike pa nsinkhu wanu. Ndipo ena mwa inu amamwalira (asanakule), pomwe ena mwa inu amabwezedwa ku moyo wofooka (waukalamba) kotero kuti asadziwe chilichonse pambuyo pakuti adali wodziwa. Ndipo umaiona nthaka ili chetee, koma tikatsitsa madzi pamwamba pake, imagwedezeka ndi kufufuma, ndi kumeretsa mtundu uliwonse wa mmera wokongola.[1]
- Munthu amene ali ndi chikaiko za kuuka ku imfa, pafunika kuti aganizire zomwe zili m’ndime iyi yolemekezeka kuti aone komwe wachokera ndi komwe wafika. Kenako aone nthaka polingalira mozama momwe imakhalira yachilala. Koma mvula ikaivumbwira ndikudzuka, kuti adziwe kuti amene akuchita zimenezi palibe chomwe angalephere.
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّهُۥ يُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَأَنَّهُۥ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Open ayah 22:6Zimenezo (monga kulenga munthu ndi kumeretsa mmera, ndi umboni wosonyeza) kuti Allah Woona alipo; ndikuti Iye amaukitsa akufa, ndiponso Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
وَأَنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٞ لَّا رَيۡبَ فِيهَا وَأَنَّ ٱللَّهَ يَبۡعَثُ مَن فِي ٱلۡقُبُورِ
Open ayah 22:7Ndipo, ndithu Qiyâma idza; palibe chikaiko pa zimenezi, ndipo ndithu Allah adzawatulutsa amene ali m’manda.
وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِي ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَلَا هُدٗى وَلَا كِتَٰبٖ مُّنِيرٖ
Open ayah 22:8Ndipo alipo mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika, (koma makani basi ndi kungotsata zimene akuziganizira).[1]
- Kutsutsana pa zinthu za chipembedzo popanda kudziwa ndi kukhala ndi umboni wokwanira nkoletsedwa zedi. Maphunziro enieni amene angamzindikiritse munthu za chipembedzo, ndi omwe akupezeka m’Qur’an ndi m’mahadisi a Mtumiki (s.a.w) omwe ali owona, ndi maphunziro amene akupezeka m’mabuku ophunzitsa malamulo achipembedzo omwe ali ovomerezeka ndi atsogoleri a Chisilamu, osati buku lililonse lolembedwa ndi munthu wamba.
ثَانِيَ عِطۡفِهِۦ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۖ لَهُۥ فِي ٱلدُّنۡيَا خِزۡيٞۖ وَنُذِيقُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَذَابَ ٱلۡحَرِيقِ
Open ayah 22:9(Yemwe) akupinda khosi lake (chifukwa chodzikuza) kuti asokereze (anthu powachotsa) kunjira ya Allah; pa iye pali chilango choyalutsa pa moyo uno, ndipo patsiku la Qiyâma tikamulawitsa chilango cha Moto wotentha.
ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتۡ يَدَاكَ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَيۡسَ بِظَلَّٰمٖ لِّلۡعَبِيدِ
Open ayah 22:10(Tidzamuuza kuti): “Izi ndi zomwe manja ako adatsogoza; ndithu Allah siwachinyengo kwa akapolo (Ake).”
وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَعۡبُدُ ٱللَّهَ عَلَىٰ حَرۡفٖۖ فَإِنۡ أَصَابَهُۥ خَيۡرٌ ٱطۡمَأَنَّ بِهِۦۖ وَإِنۡ أَصَابَتۡهُ فِتۡنَةٌ ٱنقَلَبَ عَلَىٰ وَجۡهِهِۦ خَسِرَ ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةَۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡخُسۡرَانُ ٱلۡمُبِينُ
Open ayah 22:11Ndipo alipo wina mwa anthu amene akupembedza Allah cham’mphepete (mwachipembedzo). Chabwino chikampeza amatonthola nacho; koma masautso akamufika, amatembenuka ndi nkhope yake (posiya chikhulupiliro mwa Allah. Choncho) waluza moyo wa dziko lapansi ndi moyo wa tsiku la chimaliziro; kumeneko ndiko kuluza koonekera.[1]
- Allah watibweretsa pano padziko lapansi kuti tiyesedwe mayeso akulungama ndi kusalungama tsiku lachimaliziro lisanadze. Choncho tipirire ndi kugwiritsa zimene Allah ndi Mtumiki Wake atiuza. Tidziwe kuti pali mavuto pali zabwino.
يَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَضُرُّهُۥ وَمَا لَا يَنفَعُهُۥۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلضَّلَٰلُ ٱلۡبَعِيدُ
Open ayah 22:12M’malo mwa Allah, amapembedza zomwe sizingampatse masautso (ngati ataleka kuzipembedza), ndiponso zomwe sizingampatse chithandizo (akamazipembedza), ndipo kumeneko ndiko kusokera konka nako kutali.
يَدۡعُواْ لَمَن ضَرُّهُۥٓ أَقۡرَبُ مِن نَّفۡعِهِۦۚ لَبِئۡسَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَلَبِئۡسَ ٱلۡعَشِيرُ
Open ayah 22:13Akupembedza omwe masautso awo ali pafupi zedi poyerekeza ndi zabwino zawo, taonani kuipa atetezi ndiponso ndi abwenzi oipa.
إِنَّ ٱللَّهَ يُدۡخِلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡعَلُ مَا يُرِيدُ
Open ayah 22:14Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda yamtendere amene akhulupirira ndikuchita zabwino, mitsinje ikuyenda pansi (pa mindayo). Ndithu Allah amachita chimene wafuna.
مَن كَانَ يَظُنُّ أَن لَّن يَنصُرَهُ ٱللَّهُ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ بِسَبَبٍ إِلَى ٱلسَّمَآءِ ثُمَّ لۡيَقۡطَعۡ فَلۡيَنظُرۡ هَلۡ يُذۡهِبَنَّ كَيۡدُهُۥ مَا يَغِيظُ
Open ayah 22:15Amene akuganiza kuti Allah samthangata (Mtumiki Wake) pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, amange chingwe kudenga, kenako adzipachike (ngati safuna kuona Chisilamu chikufala); ndipo aone kuti kodi ndale zakezo zichotsa zimene zamkwiitsazo?
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖ وَأَنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يُرِيدُ
Open ayah 22:16Momwemonso taivumbulutsa (Qur’an) kuti ikhale mawu omveka; ndipo ndithu Allah amaongola amene wamfuna.
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَٱلَّذِينَ هَادُواْ وَٱلصَّٰبِـِٔينَ وَٱلنَّصَٰرَىٰ وَٱلۡمَجُوسَ وَٱلَّذِينَ أَشۡرَكُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡصِلُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٌ
Open ayah 22:17Ndithu amene akhulupirira, ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi chipembedzo cha Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi (opembedza moto), ndi ophatikiza Allah ndi mafano, ndithu Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruziro (Qiyâma). (Osokera adzaponyedwa ku Moto ndipo olungama adzawalowetsa ku Munda wamtendere). Ndithu Allah ndi Mboni pa chinthu chilichonse.
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يَسۡجُدُۤ لَهُۥۤ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ وَٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ وَٱلنُّجُومُ وَٱلۡجِبَالُ وَٱلشَّجَرُ وَٱلدَّوَآبُّ وَكَثِيرٞ مِّنَ ٱلنَّاسِۖ وَكَثِيرٌ حَقَّ عَلَيۡهِ ٱلۡعَذَابُۗ وَمَن يُهِنِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن مُّكۡرِمٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡعَلُ مَا يَشَآءُ۩
Open ayah 22:18Kodi suona kuti Allah zikumulambira zimene zili kumwamba ndi zimene zili m’nthaka, kudzanso dzuwa, mwezi, nyenyezi mapiri, mitengo, nyama ndi anthu ambiri. Koma ambirinso chilango chatsimikizika pa iwo. Ndipo amene Allah wamuyalutsa, palibe amene angampatse ulemelero; ndithu Allah amachita chimene wafuna.
۞هَٰذَانِ خَصۡمَانِ ٱخۡتَصَمُواْ فِي رَبِّهِمۡۖ فَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قُطِّعَتۡ لَهُمۡ ثِيَابٞ مِّن نَّارٖ يُصَبُّ مِن فَوۡقِ رُءُوسِهِمُ ٱلۡحَمِيمُ
Open ayah 22:19Awa ndi magulu awiri amene akangana pa za Mbuye wawo (pa zomwe zili zomuyenera, ndi zosamuyenera, ndipo ena sadakhulupirire.) Choncho amene sadakhulupirire, adzawadulira nsalu za ku Moto ndi kuwaveka; ndipo pamwamba pa mitu yawo padzathiridwa madzi otentha.
يُصۡهَرُ بِهِۦ مَا فِي بُطُونِهِمۡ وَٱلۡجُلُودُ
Open ayah 22:20Chifukwa cha madziwo zidzasungunuka zomwe zili m’mimba mwawo ndiponso makungu (awo).
وَلَهُم مَّقَٰمِعُ مِنۡ حَدِيدٖ
Open ayah 22:21Ndipo (kuonjezera pa zimenezi) adzakhala nazo nyundo zachitsulo (zowamenyera).
كُلَّمَآ أَرَادُوٓاْ أَن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَا مِنۡ غَمٍّ أُعِيدُواْ فِيهَا وَذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡحَرِيقِ
Open ayah 22:22Nthawi iliyonse akafuna kutuluka m’menemo, chifukwa chakumva kupweteka, adzabwezedwa momwemo (ndipo angelo uku akuwamenya ndi nyundo), ndi (kuwauza): “Chilaweni chilango chootcha.”
إِنَّ ٱللَّهَ يُدۡخِلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ يُحَلَّوۡنَ فِيهَا مِنۡ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٖ وَلُؤۡلُؤٗاۖ وَلِبَاسُهُمۡ فِيهَا حَرِيرٞ
Open ayah 22:23Ndithu Allah adzalowetsa amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, ku Minda ya mtendere komwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake; m’menemo akavekedwa (ndi angelo) zibangili za golide ndi ngale; ndipo zovala zawo m’menemo zidzakhala za silika.
وَهُدُوٓاْ إِلَى ٱلطَّيِّبِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ وَهُدُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡحَمِيدِ
Open ayah 22:24Ndipo adzatsogozedwa (kupita kumalo) kokamba mawu abwino okhaokha; ndiponso adzatsogozedwa ku njira ya Mwini kutamandidwa (kunjira yonkera ku Jannah).
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ ٱلَّذِي جَعَلۡنَٰهُ لِلنَّاسِ سَوَآءً ٱلۡعَٰكِفُ فِيهِ وَٱلۡبَادِۚ وَمَن يُرِدۡ فِيهِ بِإِلۡحَادِۭ بِظُلۡمٖ نُّذِقۡهُ مِنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ
Open ayah 22:25Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi.
وَإِذۡ بَوَّأۡنَا لِإِبۡرَٰهِيمَ مَكَانَ ٱلۡبَيۡتِ أَن لَّا تُشۡرِكۡ بِي شَيۡـٔٗا وَطَهِّرۡ بَيۡتِيَ لِلطَّآئِفِينَ وَٱلۡقَآئِمِينَ وَٱلرُّكَّعِ ٱلسُّجُودِ
Open ayah 22:26Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi.[1]
- Allah akuuza Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti akambire opembedza mafano zankhani ya Ibrahim yemwe iwo amati akumutsata pakupembedza kwawo mafano ndi kuichita nyumba yopatulikayo kukhala nyumba yopembedzera mafano kuti Ibrahim adamulondolera pamalo anyumbayo ndi kumlamula kuti aimange ndikuti asandiphatikize pamapemphero ndi china chilichonse, ndikuti aiyeretse nyumba ya Allah kuuve wamafano ndi uve wina uliwonse kuti pakhale pamalo pozungulira chifukwa choopa Allah. Nanga bwanji iwo apasankha kukhala popembedzera mafano.
وَأَذِّن فِي ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَجِّ يَأۡتُوكَ رِجَالٗا وَعَلَىٰ كُلِّ ضَامِرٖ يَأۡتِينَ مِن كُلِّ فَجٍّ عَمِيقٖ
Open ayah 22:27Ndipo (tidamuuza): “Lengeza kwa anthu za Hajj; akudzera (ena) oyenda ndi mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba pa chiweto choonda (chifukwa chamasautso a paulendo); adza kuchokera kunjira zamtalimtali.
لِّيَشۡهَدُواْ مَنَٰفِعَ لَهُمۡ وَيَذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ فِيٓ أَيَّامٖ مَّعۡلُومَٰتٍ عَلَىٰ مَا رَزَقَهُم مِّنۢ بَهِيمَةِ ٱلۡأَنۡعَٰمِۖ فَكُلُواْ مِنۡهَا وَأَطۡعِمُواْ ٱلۡبَآئِسَ ٱلۡفَقِيرَ
Open ayah 22:28Kuti adzaone zabwino zawo, ndikuti (achulukitse) kutchula dzina la Allah m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera m’zimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kum’dyetsa wovutika, wosauka.
ثُمَّ لۡيَقۡضُواْ تَفَثَهُمۡ وَلۡيُوفُواْ نُذُورَهُمۡ وَلۡيَطَّوَّفُواْ بِٱلۡبَيۡتِ ٱلۡعَتِيقِ
Open ayah 22:29Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse naziri (malonjezo) zawo ndikuzungulira nyumba yakale.
ذَٰلِكَۖ وَمَن يُعَظِّمۡ حُرُمَٰتِ ٱللَّهِ فَهُوَ خَيۡرٞ لَّهُۥ عِندَ رَبِّهِۦۗ وَأُحِلَّتۡ لَكُمُ ٱلۡأَنۡعَٰمُ إِلَّا مَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱجۡتَنِبُواْ ٱلرِّجۡسَ مِنَ ٱلۡأَوۡثَٰنِ وَٱجۡتَنِبُواْ قَوۡلَ ٱلزُّورِ
Open ayah 22:30Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza.
حُنَفَآءَ لِلَّهِ غَيۡرَ مُشۡرِكِينَ بِهِۦۚ وَمَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَكَأَنَّمَا خَرَّ مِنَ ٱلسَّمَآءِ فَتَخۡطَفُهُ ٱلطَّيۡرُ أَوۡ تَهۡوِي بِهِ ٱلرِّيحُ فِي مَكَانٖ سَحِيقٖ
Open ayah 22:31Uku mutapendekera kwa Allah Yekha, osati kum’phatikiza (Allah). Ndipo amene akuphatikiza Allah ndi mafano, ali ngati wogwa kuchokera kumwamba, kenako mbalame nkumuwakha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali.
ذَٰلِكَۖ وَمَن يُعَظِّمۡ شَعَٰٓئِرَ ٱللَّهِ فَإِنَّهَا مِن تَقۡوَى ٱلۡقُلُوبِ
Open ayah 22:32Zimenezo ndikuti amene alemekeze zizindikiro za chipembedzo cha Allah, kutero ndichinthu choonetsa kuopa Allah m’mitima.
لَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى ثُمَّ مَحِلُّهَآ إِلَى ٱلۡبَيۡتِ ٱلۡعَتِيقِ
Open ayah 22:33(Ziweto zimene mukutumiza ku Makka monga nsembe) muli nazo zithandizo mmenemo (monga kukwera ndi kukama mkaka) kufikira nthawi yodziwika, (yomwe ndi nthawi yozizingira); kenako malo ozizingira ndi pafupi ndi Nyumba yakalekaleyo.
وَلِكُلِّ أُمَّةٖ جَعَلۡنَا مَنسَكٗا لِّيَذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَىٰ مَا رَزَقَهُم مِّنۢ بَهِيمَةِ ٱلۡأَنۡعَٰمِۗ فَإِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ فَلَهُۥٓ أَسۡلِمُواْۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُخۡبِتِينَ
Open ayah 22:34Ndipo mpingo uliwonse tidaupangira malo ozingira nsembe zamapemphero kuti atchule dzina la Allah pa zomwe wawapatsa monga ziweto zamiyendo inayi. Choncho mulungu wanu ndi Mulungu m’modzi Yekha; gonjerani kwa Iye; ndipo odzichepetsa auze nkhani yabwino.
ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَجِلَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَٱلصَّٰبِرِينَ عَلَىٰ مَآ أَصَابَهُمۡ وَٱلۡمُقِيمِي ٱلصَّلَوٰةِ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Open ayah 22:35Omwe Allah akatchulidwa, mitima yawo imanjenjemera ndiponso amapirira pa zomwe zawapeza, ndipo amapemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka kuchokera m’zomwe tawapatsa.
وَٱلۡبُدۡنَ جَعَلۡنَٰهَا لَكُم مِّن شَعَٰٓئِرِ ٱللَّهِ لَكُمۡ فِيهَا خَيۡرٞۖ فَٱذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَا صَوَآفَّۖ فَإِذَا وَجَبَتۡ جُنُوبُهَا فَكُلُواْ مِنۡهَا وَأَطۡعِمُواْ ٱلۡقَانِعَ وَٱلۡمُعۡتَرَّۚ كَذَٰلِكَ سَخَّرۡنَٰهَا لَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Open ayah 22:36Ndipo ngamira (ng’ombe, mbuzi ndi mbelere) tadzichita kwa inu kuti zikhale mwa zizindikiro za chipembedzo cha Allah; m’zimenezo muli zabwino kwa inu; choncho litchuleni dzina la Allah pa izo pamene zikuima mondanda (uku mukuzizinga,) ndipo zikagwa cham’nthiti, idyani (nyama yake) ndikumdyetsa yemwe akungozungulirazungulira, wosapempha ndi wopempha yemwe. Momwemo tazigonjetsa kwa inu (pochita kuti zikugonjereni) kuti muthokoze.
لَن يَنَالَ ٱللَّهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَآؤُهَا وَلَٰكِن يَنَالُهُ ٱلتَّقۡوَىٰ مِنكُمۡۚ كَذَٰلِكَ سَخَّرَهَا لَكُمۡ لِتُكَبِّرُواْ ٱللَّهَ عَلَىٰ مَا هَدَىٰكُمۡۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Open ayah 22:37(Nyamazo) Allah siimfika minofu yake ngakhale magazi ake, koma kuopa kuchokera mwa inu ndiko kumene kumamfika; momwemo wazichita (nyamazo) kukhala zogonjera inu kuti mumlemekeze Allah chifukwa cha kukuongolaniku. Auze nkhani yabwino ochita zabwino.
۞إِنَّ ٱللَّهَ يُدَٰفِعُ عَنِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ خَوَّانٖ كَفُورٍ
Open ayah 22:38Ndithu Allah amawateteza amene akhulupilira, ndithu Allah sakonda aliyense wachinyengo, wosathokoza.
أُذِنَ لِلَّذِينَ يُقَٰتَلُونَ بِأَنَّهُمۡ ظُلِمُواْۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ نَصۡرِهِمۡ لَقَدِيرٌ
Open ayah 22:39Chaperekedwa chilolezo kwa (Asilamu) amene akuputidwa (ndi adani awo kuti abwezere) chifukwa chakuti iwo achitiridwa zoipa; ndipo ndithu Allah ngokhoza kuwathandiza.
ٱلَّذِينَ أُخۡرِجُواْ مِن دِيَٰرِهِم بِغَيۡرِ حَقٍّ إِلَّآ أَن يَقُولُواْ رَبُّنَا ٱللَّهُۗ وَلَوۡلَا دَفۡعُ ٱللَّهِ ٱلنَّاسَ بَعۡضَهُم بِبَعۡضٖ لَّهُدِّمَتۡ صَوَٰمِعُ وَبِيَعٞ وَصَلَوَٰتٞ وَمَسَٰجِدُ يُذۡكَرُ فِيهَا ٱسۡمُ ٱللَّهِ كَثِيرٗاۗ وَلَيَنصُرَنَّ ٱللَّهُ مَن يَنصُرُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ
Open ayah 22:40Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse.[1]
- M’ndime iyi, Allah akuti akadawalekelera anthu oipa, omwe cholinga chawo nkudzetsa chisokonezo pa dziko, popanda kusankha anthu ena kuti alimbane nawo, ndiye kuti nyumba zopempheleramo Ayuda, Akhrisitu ndi Asilamu, zikadagumulidwa. Koma Allah amasankha anthu olungama kuti alimbane ndi anthu oipawo kuti choonadi cha Allah chisazime. Ndipo amene akuteteza choonadi cha Allah, Iye walonjeza kumthangata.
ٱلَّذِينَ إِن مَّكَّنَّٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَوُاْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَمَرُواْ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَنَهَوۡاْ عَنِ ٱلۡمُنكَرِۗ وَلِلَّهِ عَٰقِبَةُ ٱلۡأُمُورِ
Open ayah 22:41Omwe akuti tikawakhazika pa dziko mwa ubwino, amachita mapemphero a Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, ndi kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa; ndipo mabwelero a zinthu nkwa Allah basi.
وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَعَادٞ وَثَمُودُ
Open ayah 22:42Ndipo ngati akukuyesa wabodza, (awa Akafiri, sizachilendo), ndithu adatsutsanso (aneneri awo) patsogolo pawo anthu a Nuh, Aadi, a Samudu.
وَقَوۡمُ إِبۡرَٰهِيمَ وَقَوۡمُ لُوطٖ
Open ayah 22:43Anthu a Ibrahim, anthu a Luti.
وَأَصۡحَٰبُ مَدۡيَنَۖ وَكُذِّبَ مُوسَىٰۖ فَأَمۡلَيۡتُ لِلۡكَٰفِرِينَ ثُمَّ أَخَذۡتُهُمۡۖ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ
Open ayah 22:44Ndi anthu a ku Madiyan; nayenso Mûsa adayesedwa wabodza (adamkana). Ndipo osakhulupirira ndidawapatsa nthawi, kenako ndidawathira m’dzanja. Nanga chidali bwanji chilango changa.
فَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَا وَهِيَ ظَالِمَةٞ فَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا وَبِئۡرٖ مُّعَطَّلَةٖ وَقَصۡرٖ مَّشِيدٍ
Open ayah 22:45Ndi midzi ingati tidaiononga yomwe inkachita zoipa? Zipupa zitagwera pa madenga ake. Ndipo ndi zitsime (zingati) zomwe zidasiidwa, ndi nyumba zikuluzikulu zomwe zidali zolimba?
أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَتَكُونَ لَهُمۡ قُلُوبٞ يَعۡقِلُونَ بِهَآ أَوۡ ءَاذَانٞ يَسۡمَعُونَ بِهَاۖ فَإِنَّهَا لَا تَعۡمَى ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَلَٰكِن تَعۡمَى ٱلۡقُلُوبُ ٱلَّتِي فِي ٱلصُّدُورِ
Open ayah 22:46Kodi sayendayenda pa dziko kuti akhale ndi mitima (yanzeru) yowazindikiritsa ndi makutu omvera? Ndithu maso sagwidwa khungu, (khungu loononga chipembedzo), koma mitima yomwe ili m’zifuwa ndi imene imagwidwa khungu (loononga chipembedzo).
وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَن يُخۡلِفَ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥۚ وَإِنَّ يَوۡمًا عِندَ رَبِّكَ كَأَلۡفِ سَنَةٖ مِّمَّا تَعُدُّونَ
Open ayah 22:47Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango. Komatu Allah sadzaswa lonjezo Lake (limene adaliika lakuti chilango chenicheni chidzakhala patsiku la chimaliziro). Ndipo ndithu tsiku limodzi kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi chimodzi mukawerengedwe kanu.
وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ أَمۡلَيۡتُ لَهَا وَهِيَ ظَالِمَةٞ ثُمَّ أَخَذۡتُهَا وَإِلَيَّ ٱلۡمَصِيرُ
Open ayah 22:48Kodi ndi (anthu a) midzi ingati amene ndidawapatsa nthawi pomwe ankachita zoipa? Kenako ndidawathira m’dzanja. Ndipo kwa Iye nkobwerera.
قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّمَآ أَنَا۠ لَكُمۡ نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Open ayah 22:49Nena: “E inu anthu! Ndithu ine kwa inu ndine Mchenjezi woonekera.”
فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَرِزۡقٞ كَرِيمٞ
Open ayah 22:50“Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chikhululuko ndi rizq laulemu zili pa iwo.”
وَٱلَّذِينَ سَعَوۡاْ فِيٓ ءَايَٰتِنَا مُعَٰجِزِينَ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ
Open ayah 22:51“Ndipo amene akulimbikira kulimbana ndi Ayah Zathu, iwowo ndi anthu a ku Moto.”
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رَّسُولٖ وَلَا نَبِيٍّ إِلَّآ إِذَا تَمَنَّىٰٓ أَلۡقَى ٱلشَّيۡطَٰنُ فِيٓ أُمۡنِيَّتِهِۦ فَيَنسَخُ ٱللَّهُ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ ثُمَّ يُحۡكِمُ ٱللَّهُ ءَايَٰتِهِۦۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ
Open ayah 22:52Ndipo palibe pamene tidatuma mtumiki ngakhale m’neneri patsogolo pako, koma akamawerenga, satana amaponya (zosokoneza) m’kuwerenga kwakeko; koma Allah amachotsa zomwe satana akuponya; kenako nkuzilongosola Ayah Zake. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Wanzeru zakuya.
لِّيَجۡعَلَ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ وَٱلۡقَاسِيَةِ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَفِي شِقَاقِۭ بَعِيدٖ
Open ayah 22:53(Izi zimachitika) kuti achichite chimene satana akuponya kukhala mayeso kwa omwe m’mitima mwawo muli matenda ndi ouma mitima yawo; ndithu osalungama ali m’kusiyana komwe kuli kutali (ndi choonadi).
وَلِيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَيُؤۡمِنُواْ بِهِۦ فَتُخۡبِتَ لَهُۥ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Open ayah 22:54Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira.
وَلَا يَزَالُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي مِرۡيَةٖ مِّنۡهُ حَتَّىٰ تَأۡتِيَهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةً أَوۡ يَأۡتِيَهُمۡ عَذَابُ يَوۡمٍ عَقِيمٍ
Open ayah 22:55Ndipo amene sadakhulupirire apitilira kukhala m’chikaiko ndi chimenecho (wadza nachocho) kufikira tsiku la chimaliziro liwadzera mowatutumutsa, kapena chiwadzera chilango pa tsiku lopanda chabwino (kwa iwo).
ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٖ لِّلَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡۚ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
Open ayah 22:56Ufumu tsiku limenelo ngwa Allah; adzaweruza (mwachilungamo) pakati pawo; choncho amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’Minda yamtendere.
وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ
Open ayah 22:57Ndipo amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndikutsutsa Ayah Zathu, iwo adzapeza chilango choyalutsa.
وَٱلَّذِينَ هَاجَرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ ثُمَّ قُتِلُوٓاْ أَوۡ مَاتُواْ لَيَرۡزُقَنَّهُمُ ٱللَّهُ رِزۡقًا حَسَنٗاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ
Open ayah 22:58Ndipo amene asamuka chifukwa cha chipembedzo cha Allah, kenako ndikuphedwa kapena kufa, ndithu Allah adzawapatsa (patsiku la chiweruziro) zopatsa zabwino. Ndithu Allah Ngwabwino popatsa kuposa opatsa.
لَيُدۡخِلَنَّهُم مُّدۡخَلٗا يَرۡضَوۡنَهُۥۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَعَلِيمٌ حَلِيمٞ
Open ayah 22:59Ndithu adzawalowetsa pamalo pomwe adzapayanja. Ndithu Allah Ngodziwa; Ngodekha.
۞ذَٰلِكَۖ وَمَنۡ عَاقَبَ بِمِثۡلِ مَا عُوقِبَ بِهِۦ ثُمَّ بُغِيَ عَلَيۡهِ لَيَنصُرَنَّهُ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَعَفُوٌّ غَفُورٞ
Open ayah 22:60Zimenezi zili chonchi, ndipo yemwe akubwezera kulanga molingana ndi momwe iye adalangidwira; kenakonso nkuchitidwa mtopola, ndithu Allah amthangata; Allah Ngofufuta uchimo; Wokhululuka kwambiri.
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَأَنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٞ
Open ayah 22:61Zimenezo nchifukwa chakuti Allah amalowetsa usiku mu usana ndikulowetsa usana mu usiku, ndi chifukwanso chakuti ndithu Allah Ngwakumva Ngopenya.
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ هُوَ ٱلۡبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ
Open ayah 22:62Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu.
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَتُصۡبِحُ ٱلۡأَرۡضُ مُخۡضَرَّةًۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٞ
Open ayah 22:63Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo nthaka imakhala yobiriwira? Ndithu Allah Ngodziwa zobisika ndiponso Ngodziwa zoonekera.
لَّهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
Open ayah 22:64Zakumwamba ndi zapansi zonse ndizake; ndithu Allah Ngwachikwanekwane; Wotamandidwa.
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَٱلۡفُلۡكَ تَجۡرِي فِي ٱلۡبَحۡرِ بِأَمۡرِهِۦ وَيُمۡسِكُ ٱلسَّمَآءَ أَن تَقَعَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِٱلنَّاسِ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٞ
Open ayah 22:65Kodi sudaone kuti Allah wakufewetserani zonse zam’nthaka ndi zombo zomwe zikuyenda panyanja mwa lamulo Lake? Ndipo wagwira thambo kuti lisagwe panthaka koma kupyolera m’chilolezo Chake; ndithu Allah Ngodekha kwa anthu Ngwachifundo.
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَحۡيَاكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يُحۡيِيكُمۡۗ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٞ
Open ayah 22:66Ndipo Iye ndi Amene adakupatsani moyo; kenako adzakupatsani imfa, ndipo kenako adzakuukitsani; ndithu munthu ngosathokoza.
لِّكُلِّ أُمَّةٖ جَعَلۡنَا مَنسَكًا هُمۡ نَاسِكُوهُۖ فَلَا يُنَٰزِعُنَّكَ فِي ٱلۡأَمۡرِۚ وَٱدۡعُ إِلَىٰ رَبِّكَۖ إِنَّكَ لَعَلَىٰ هُدٗى مُّسۡتَقِيمٖ
Open ayah 22:67Mpingo uliwonse tidauikira machitidwe amapemphero omwe akuwatsata; choncho asatsutsane nawe pachinthu ichi, ndipo itanira anthu ku chipembedzo cha Mbuye wako. Ndithu iwe uli pachiongoko changwilo.
وَإِن جَٰدَلُوكَ فَقُلِ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا تَعۡمَلُونَ
Open ayah 22:68Ndipo ngati atsutsana nawe, nena: “Allah Ngodziwa koposa zimene mukuchita.”
ٱللَّهُ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كُنتُمۡ فِيهِ تَخۡتَلِفُونَ
Open ayah 22:69“Allah adzaweruza pakati panu tsiku la Qiyâma pa zimene mudali kusiyana.”
أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّ ذَٰلِكَ فِي كِتَٰبٍۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ
Open ayah 22:70Kodi sudziwa kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu zonsezo zili m’kaundula (Wake), ndithu (kudziwika kwa) zimenezo kwa Allah nzosavuta.
وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ سُلۡطَٰنٗا وَمَا لَيۡسَ لَهُم بِهِۦ عِلۡمٞۗ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِن نَّصِيرٖ
Open ayah 22:71Ndipo akupembedza milungu yabodza, kusiya Allah, yomwe (Allah) sadaitumizire umboni wakuti (ipembedzedwe) yomwenso iwo sakuidziwa bwino. Ndipo anthu osalungama sadzakhala ndi owathandiza.
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱلۡمُنكَرَۖ يَكَادُونَ يَسۡطُونَ بِٱلَّذِينَ يَتۡلُونَ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَاۗ قُلۡ أَفَأُنَبِّئُكُم بِشَرّٖ مِّن ذَٰلِكُمُۚ ٱلنَّارُ وَعَدَهَا ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
Open ayah 22:72Koma Ayah Zathu zomveka zikawerengedwa kwa iwo, uona kunyansidwa pankhope za amene sadakhulupirire. Ndipo amakhala pafupi kuwamenya amene amawawerengera Ayah Zathu. Nena: “Kodi ndikuuzeni zoipa kwambiri kuposa izi? Ndi Moto (wa Allah) umene wawalonjeza amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) amenewo ndi mabwelero oipa zedi.”
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ضُرِبَ مَثَلٞ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَن يَخۡلُقُواْ ذُبَابٗا وَلَوِ ٱجۡتَمَعُواْ لَهُۥۖ وَإِن يَسۡلُبۡهُمُ ٱلذُّبَابُ شَيۡـٔٗا لَّا يَسۡتَنقِذُوهُ مِنۡهُۚ ضَعُفَ ٱلطَّالِبُ وَٱلۡمَطۡلُوبُ
Open ayah 22:73E inu anthu! Fanizo laperekedwa; choncho limvereni. Ndithu amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah, sangathe kulenga ntchentche ngakhale Atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchenche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. Wafooka kwenikweni wopempha ndi wopemphedwa.
مَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ
Open ayah 22:74Sadamlemekeze Allah, kulemekeza komuyenera. Ndithu Allah Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse.
ٱللَّهُ يَصۡطَفِي مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ رُسُلٗا وَمِنَ ٱلنَّاسِۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٞ
Open ayah 22:75Allah amasankha atumiki mwa angelo ndi mwa anthu. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngopenya.
يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ
Open ayah 22:76Akudziwa zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili pambuyo pawo; kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱرۡكَعُواْ وَٱسۡجُدُواْۤ وَٱعۡبُدُواْ رَبَّكُمۡ وَٱفۡعَلُواْ ٱلۡخَيۡرَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ۩
Open ayah 22:77E inu amene mwakhulupirira! Weramani ndikugwetsa nkhope zanu pansi ndipo mpembedzeni Mbuye wanu ndikuchita zabwino kuti mupambane.
وَجَٰهِدُواْ فِي ٱللَّهِ حَقَّ جِهَادِهِۦۚ هُوَ ٱجۡتَبَىٰكُمۡ وَمَا جَعَلَ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلدِّينِ مِنۡ حَرَجٖۚ مِّلَّةَ أَبِيكُمۡ إِبۡرَٰهِيمَۚ هُوَ سَمَّىٰكُمُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ مِن قَبۡلُ وَفِي هَٰذَا لِيَكُونَ ٱلرَّسُولُ شَهِيدًا عَلَيۡكُمۡ وَتَكُونُواْ شُهَدَآءَ عَلَى ٱلنَّاسِۚ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱعۡتَصِمُواْ بِٱللَّهِ هُوَ مَوۡلَىٰكُمۡۖ فَنِعۡمَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَنِعۡمَ ٱلنَّصِيرُ
Open ayah 22:78Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi.