يس
Yaseen
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
يسٓ
Open ayah 36:1Yâ-Sîn.
وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡحَكِيمِ
Open ayah 36:2Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru.
إِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 36:3Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko).
عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Open ayah 36:4(Uli) panjira yolunjika.
تَنزِيلَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ
Open ayah 36:5(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha.
لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أُنذِرَ ءَابَآؤُهُمۡ فَهُمۡ غَٰفِلُونَ
Open ayah 36:6Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena).
لَقَدۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَىٰٓ أَكۡثَرِهِمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Open ayah 36:7Ndithu mawu (onena za chilango) atsimikizika pa ambiri a iwo; poti iwo sakhulupirira.
إِنَّا جَعَلۡنَا فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ أَغۡلَٰلٗا فَهِيَ إِلَى ٱلۡأَذۡقَانِ فَهُم مُّقۡمَحُونَ
Open ayah 36:8Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana).
وَجَعَلۡنَا مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ سَدّٗا وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ سَدّٗا فَأَغۡشَيۡنَٰهُمۡ فَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ
Open ayah 36:9Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo).
وَسَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Open ayah 36:10Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, uwachenjeze ngakhale usawachenjeze sangakhulupirire.
إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلذِّكۡرَ وَخَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِۖ فَبَشِّرۡهُ بِمَغۡفِرَةٖ وَأَجۡرٖ كَرِيمٍ
Open ayah 36:11Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu.
إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَنَكۡتُبُ مَا قَدَّمُواْ وَءَاثَٰرَهُمۡۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ فِيٓ إِمَامٖ مُّبِينٖ
Open ayah 36:12Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse).
وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلًا أَصۡحَٰبَ ٱلۡقَرۡيَةِ إِذۡ جَآءَهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Open ayah 36:13Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo).
إِذۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱثۡنَيۡنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزۡنَا بِثَالِثٖ فَقَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَيۡكُم مُّرۡسَلُونَ
Open ayah 36:14Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbitsa iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife tatumidwa kwa inu.”
قَالُواْ مَآ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا وَمَآ أَنزَلَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَكۡذِبُونَ
Open ayah 36:15(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.”
قَالُواْ رَبُّنَا يَعۡلَمُ إِنَّآ إِلَيۡكُمۡ لَمُرۡسَلُونَ
Open ayah 36:16(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.”
وَمَا عَلَيۡنَآ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
Open ayah 36:17“Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).”
قَالُوٓاْ إِنَّا تَطَيَّرۡنَا بِكُمۡۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهُواْ لَنَرۡجُمَنَّكُمۡ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ
Open ayah 36:18(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.”
قَالُواْ طَٰٓئِرُكُم مَّعَكُمۡ أَئِن ذُكِّرۡتُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ مُّسۡرِفُونَ
Open ayah 36:19(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.”
وَجَآءَ مِنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ رَجُلٞ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُواْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Open ayah 36:20Kenako munthu adadza akuthamanga kuchokera ku malekezero a mzindawo (ndipo) adati: “E inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.”
ٱتَّبِعُواْ مَن لَّا يَسۡـَٔلُكُمۡ أَجۡرٗا وَهُم مُّهۡتَدُونَ
Open ayah 36:21“Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.”
وَمَا لِيَ لَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Open ayah 36:22“Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”.
ءَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةً إِن يُرِدۡنِ ٱلرَّحۡمَٰنُ بِضُرّٖ لَّا تُغۡنِ عَنِّي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا يُنقِذُونِ
Open ayah 36:23“Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.”
إِنِّيٓ إِذٗا لَّفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
Open ayah 36:24“Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”.
إِنِّيٓ ءَامَنتُ بِرَبِّكُمۡ فَٱسۡمَعُونِ
Open ayah 36:25“Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.”
قِيلَ ٱدۡخُلِ ٱلۡجَنَّةَۖ قَالَ يَٰلَيۡتَ قَوۡمِي يَعۡلَمُونَ
Open ayah 36:26Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!”
بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ
Open ayah 36:27“Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).”
۞وَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنۢ بَعۡدِهِۦ مِن جُندٖ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا كُنَّا مُنزِلِينَ
Open ayah 36:28Ndipo anthu ake sitidawatsitsire ankhondo ochokera kumwamba pambuyo pake (kuti awaononge). Ndipo pachizolowezi chathu sititsitsa (ankhondo kumwamba tikafuna kuononga, koma Mngelo mmodzi amakwanira).
إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَإِذَا هُمۡ خَٰمِدُونَ
Open ayah 36:29(Kuonongeka kwawo) kudali mkuwe umodzi, ndipo nthawi yomweyo adali akufa (izi zidachitika pamene mngelo Gabuliyele adawakuwira mkuwe wamphamvu).
يَٰحَسۡرَةً عَلَى ٱلۡعِبَادِۚ مَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Open ayah 36:30Ha! Nzodandaulitsa kwa akapolo! Palibe pamene mtumiki adawadzera popanda kumchitira chipongwe (ndi kukana kumtsata)!
أَلَمۡ يَرَوۡاْ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ أَنَّهُمۡ إِلَيۡهِمۡ لَا يَرۡجِعُونَ
Open ayah 36:31Kodi sadalingalire za mibadwo yambirimbiri imene tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo iwo sangabwelerenso kwa iwo.
وَإِن كُلّٞ لَّمَّا جَمِيعٞ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ
Open ayah 36:32Ndipo zolengedwa zonse zidzaonekera kwa Ife.
وَءَايَةٞ لَّهُمُ ٱلۡأَرۡضُ ٱلۡمَيۡتَةُ أَحۡيَيۡنَٰهَا وَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهَا حَبّٗا فَمِنۡهُ يَأۡكُلُونَ
Open ayah 36:33Ndipo chisonyezo chawo ndi nthaka yakufa; timaiukitsa (ndi madzi) ndi kutulutsa m’menemo njere, zomwe zina mwa izo amadya.
وَجَعَلۡنَا فِيهَا جَنَّٰتٖ مِّن نَّخِيلٖ وَأَعۡنَٰبٖ وَفَجَّرۡنَا فِيهَا مِنَ ٱلۡعُيُونِ
Open ayah 36:34Ndipo tapanga m’menemo minda ya kanjedza ndi mphesa; ndipo tatulutsa m’menemo akasupe.
لِيَأۡكُلُواْ مِن ثَمَرِهِۦ وَمَا عَمِلَتۡهُ أَيۡدِيهِمۡۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ
Open ayah 36:35Kuti azidya zipatso zake pomwe sizidapangidwe ndi manja awo. Kodi bwanji sathokoza (Allah)?
سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنۢبِتُ ٱلۡأَرۡضُ وَمِنۡ أَنفُسِهِمۡ وَمِمَّا لَا يَعۡلَمُونَ
Open ayah 36:36Alemekezeke (Allah), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi chachikazi, kuchokera m’zimene nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe ndi zina zimene (anthu) sakudziwa.
وَءَايَةٞ لَّهُمُ ٱلَّيۡلُ نَسۡلَخُ مِنۡهُ ٱلنَّهَارَ فَإِذَا هُم مُّظۡلِمُونَ
Open ayah 36:37Ndiponso chisonyezo chawo ndiusiku. M’menemo timachotsamo usana (womwe umabisa usiku), ndipo (anthu) amangozindikira ali mu mdima.
وَٱلشَّمۡسُ تَجۡرِي لِمُسۡتَقَرّٖ لَّهَاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
Open ayah 36:38۞ Ndipo dzuwa; limayenda m’njira ndi m’nthawi yake imene idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero chimenecho ncha (Allah) Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
وَٱلۡقَمَرَ قَدَّرۡنَٰهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَٱلۡعُرۡجُونِ ٱلۡقَدِيمِ
Open ayah 36:39Ndiponso mwezi; tidaukonzera malo oimirapo mpaka kukafika pomwe umabwerera ndi kukhala wochepa ndi wokhota monga nthambi ya mtengo wa kanjedza, youma komanso yokhota.[1]
- Ndime iyi ikufotokoza za kayendedwe ka mwezi kuti adaupangira malo 28 oimirapo. Umayamba pamalo woyamba uli wochepa ndi wokhota. Ndipo umanka nukula kuchoka pa malo ena nkufika pa malo ena mpaka kukafika pamalo pomwe umakhala wokwanira mkuwala ndi m’maonekedwe ake. Pamenepa mpamalo a 14. Tsono kuchoka apa, umayamba kuchepa pang’onopang’ono ndi kubisika mpaka utafika pa malo a 28 pomwe umabisikiratu wonse. Kayendedwe ka mwezi ndiko kamazindikiritsa anthu kutha kwa mwezi ndi chaka, pomwe kayendedwe ka dzuwa kamazindikiritsa anthu kutha kwa tsiku.
لَا ٱلشَّمۡسُ يَنۢبَغِي لَهَآ أَن تُدۡرِكَ ٱلۡقَمَرَ وَلَا ٱلَّيۡلُ سَابِقُ ٱلنَّهَارِۚ وَكُلّٞ فِي فَلَكٖ يَسۡبَحُونَ
Open ayah 36:40Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi mwezi (njira yake); nawonso usiku sungathe kupambana usana (pakudza nthawi yausana isadathe, koma zimasinthana). Ndipo chilichonse mwa izo chimasambira m’njira yake (imene Allah adachikonzera).
وَءَايَةٞ لَّهُمۡ أَنَّا حَمَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ
Open ayah 36:41Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo).
وَخَلَقۡنَا لَهُم مِّن مِّثۡلِهِۦ مَا يَرۡكَبُونَ
Open ayah 36:42Ndipo tidawapangira chonga icho chomwe akuchikwera.[1]
- Allah ndi Yemwe adapanga zombo ngakhale kuti zidapangidwa ndi manja a anthu, chifukwa Iye ndi Amene adaphunzitsa anthu kupanga zombozo.
وَإِن نَّشَأۡ نُغۡرِقۡهُمۡ فَلَا صَرِيخَ لَهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنقَذُونَ
Open ayah 36:43Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe.
إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّنَّا وَمَتَٰعًا إِلَىٰ حِينٖ
Open ayah 36:44Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera).
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّقُواْ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيكُمۡ وَمَا خَلۡفَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
Open ayah 36:45Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo).
وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٖ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ
Open ayah 36:46Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana).
وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ أَنفِقُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنُطۡعِمُ مَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ أَطۡعَمَهُۥٓ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Open ayah 36:47Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.”
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Open ayah 36:48Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”
مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ تَأۡخُذُهُمۡ وَهُمۡ يَخِصِّمُونَ
Open ayah 36:49Palibe chimene akuyembekeza, koma ndi mkuwe umodzi womwe udzawamaliza mwadzidzidzi uku iwo akukangana.
فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ تَوۡصِيَةٗ وَلَآ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ يَرۡجِعُونَ
Open ayah 36:50Ndipo sangathe kuuza wina mawu pa chinthu, ndiponso sangathe kubwerera ku maanja awo.
وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يَنسِلُونَ
Open ayah 36:51Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga.
قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا مَنۢ بَعَثَنَا مِن مَّرۡقَدِنَاۜۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَصَدَقَ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Open ayah 36:52Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.”
إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَإِذَا هُمۡ جَمِيعٞ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ
Open ayah 36:53Sipadzakhala (china) koma mkuwe umodzi basi; adzangozindikira iwo onse atabweretsedwa patsogolo Pathu.
فَٱلۡيَوۡمَ لَا تُظۡلَمُ نَفۡسٞ شَيۡـٔٗا وَلَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Open ayah 36:54“Ndipo mzimu uliwonse lero suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo munkachita.”
إِنَّ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ ٱلۡيَوۡمَ فِي شُغُلٖ فَٰكِهُونَ
Open ayah 36:55Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo.
هُمۡ وَأَزۡوَٰجُهُمۡ فِي ظِلَٰلٍ عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ مُتَّكِـُٔونَ
Open ayah 36:56Iwo ndi akazi awo ali m’mithunzi uku atatsamira mipando (ya mtengo wapamwamba).
لَهُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ
Open ayah 36:57M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna.
سَلَٰمٞ قَوۡلٗا مِّن رَّبّٖ رَّحِيمٖ
Open ayah 36:58“Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha.
وَٱمۡتَٰزُواْ ٱلۡيَوۡمَ أَيُّهَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Open ayah 36:59Ndipo dzipatuleni lero, inu oipa!
۞أَلَمۡ أَعۡهَدۡ إِلَيۡكُمۡ يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ أَن لَّا تَعۡبُدُواْ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Open ayah 36:60Kodi sindidakulangizeni, E inu ana a Adam kuti musapembedze satana? Ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa inu?
وَأَنِ ٱعۡبُدُونِيۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
Open ayah 36:61Ndikuti ndipembedzeni Ine? Imeneyi ndi njira yolunjika.
وَلَقَدۡ أَضَلَّ مِنكُمۡ جِبِلّٗا كَثِيرًاۖ أَفَلَمۡ تَكُونُواْ تَعۡقِلُونَ
Open ayah 36:62Ndithu (satana) adasokeretsa anthu ambiri mwa inu. Kodi simumaganizira mwanzeru?
هَٰذِهِۦ جَهَنَّمُ ٱلَّتِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ
Open ayah 36:63Iyi ndi Jahena yomwe mumalonjezedwa.
ٱصۡلَوۡهَا ٱلۡيَوۡمَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ
Open ayah 36:64Iloweni lero, chifukwa cha kunkana kwanu (Allah).
ٱلۡيَوۡمَ نَخۡتِمُ عَلَىٰٓ أَفۡوَٰهِهِمۡ وَتُكَلِّمُنَآ أَيۡدِيهِمۡ وَتَشۡهَدُ أَرۡجُلُهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Open ayah 36:65Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula ndipo miyendo yawo ichitira umboni pa zomwe amachita.
وَلَوۡ نَشَآءُ لَطَمَسۡنَا عَلَىٰٓ أَعۡيُنِهِمۡ فَٱسۡتَبَقُواْ ٱلصِّرَٰطَ فَأَنَّىٰ يُبۡصِرُونَ
Open ayah 36:66Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma akadapenya chotani?
وَلَوۡ نَشَآءُ لَمَسَخۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمۡ فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مُضِيّٗا وَلَا يَرۡجِعُونَ
Open ayah 36:67Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo.
وَمَن نُّعَمِّرۡهُ نُنَكِّسۡهُ فِي ٱلۡخَلۡقِۚ أَفَلَا يَعۡقِلُونَ
Open ayah 36:68Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru?
وَمَا عَلَّمۡنَٰهُ ٱلشِّعۡرَ وَمَا يَنۢبَغِي لَهُۥٓۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ وَقُرۡءَانٞ مُّبِينٞ
Open ayah 36:69Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse.
لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيّٗا وَيَحِقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Open ayah 36:70Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira.
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا خَلَقۡنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتۡ أَيۡدِينَآ أَنۡعَٰمٗا فَهُمۡ لَهَا مَٰلِكُونَ
Open ayah 36:71Kodi saona kuti Ife tawalengera nyama, m’zimene manja Athu akonza, zomwe iwo akuti nzawo.
وَذَلَّلۡنَٰهَا لَهُمۡ فَمِنۡهَا رَكُوبُهُمۡ وَمِنۡهَا يَأۡكُلُونَ
Open ayah 36:72Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya.
وَلَهُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ وَمَشَارِبُۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ
Open ayah 36:73Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza?
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةٗ لَّعَلَّهُمۡ يُنصَرُونَ
Open ayah 36:74Ndipo adzipangira milungu (yabodza) kusiya Allah kuti athandizidwe nayo.
لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَهُمۡ وَهُمۡ لَهُمۡ جُندٞ مُّحۡضَرُونَ
Open ayah 36:75(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira).
فَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّا نَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَ
Open ayah 36:76Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera.
أَوَلَمۡ يَرَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن نُّطۡفَةٖ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٞ مُّبِينٞ
Open ayah 36:77Kodi munthu sazindikira kuti Ife tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala wotsutsa woonekera.
وَضَرَبَ لَنَا مَثَلٗا وَنَسِيَ خَلۡقَهُۥۖ قَالَ مَن يُحۡيِ ٱلۡعِظَٰمَ وَهِيَ رَمِيمٞ
Open ayah 36:78Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?”
قُلۡ يُحۡيِيهَا ٱلَّذِيٓ أَنشَأَهَآ أَوَّلَ مَرَّةٖۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلۡقٍ عَلِيمٌ
Open ayah 36:79Nena: “Adzawaukitsa Yemwe adawalenga panthawi yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu uliwonse.
ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلشَّجَرِ ٱلۡأَخۡضَرِ نَارٗا فَإِذَآ أَنتُم مِّنۡهُ تُوقِدُونَ
Open ayah 36:80Yemwe adakupangirani moto kuchokera mu mtengo wauwisi; kenako inu mumakoleza moto m’menemo.
أَوَلَيۡسَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۚ بَلَىٰ وَهُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ
Open ayah 36:81Kodi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza kuwalenga (iwo kachiwiri) monga momwe alili? Inde! Iye ndi Mlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri!
إِنَّمَآ أَمۡرُهُۥٓ إِذَآ أَرَادَ شَيۡـًٔا أَن يَقُولَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Open ayah 36:82Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo).
فَسُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Open ayah 36:83Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse.