الواقعة
Al-Waaqia
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
إِذَا وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ
Open ayah 56:1Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma).
لَيۡسَ لِوَقۡعَتِهَا كَاذِبَةٌ
Open ayah 56:2Palibe wotsutsa za kuchitika kwake.
خَافِضَةٞ رَّافِعَةٌ
Open ayah 56:3Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino).
إِذَا رُجَّتِ ٱلۡأَرۡضُ رَجّٗا
Open ayah 56:4Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu.
وَبُسَّتِ ٱلۡجِبَالُ بَسّٗا
Open ayah 56:5Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa.
فَكَانَتۡ هَبَآءٗ مُّنۢبَثّٗا
Open ayah 56:6Nkukhala fumbi longouluka.
وَكُنتُمۡ أَزۡوَٰجٗا ثَلَٰثَةٗ
Open ayah 56:7Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu).
فَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ
Open ayah 56:8Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja!
وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ
Open ayah 56:9Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere!
وَٱلسَّٰبِقُونَ ٱلسَّٰبِقُونَ
Open ayah 56:10Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro).
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡمُقَرَّبُونَ
Open ayah 56:11Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah).
فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
Open ayah 56:12M’minda yamtendere.
ثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 56:13(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale.
وَقَلِيلٞ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ
Open ayah 56:14Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira.
عَلَىٰ سُرُرٖ مَّوۡضُونَةٖ
Open ayah 56:15Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide,
مُّتَّكِـِٔينَ عَلَيۡهَا مُتَقَٰبِلِينَ
Open ayah 56:16Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi).
يَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٞ مُّخَلَّدُونَ
Open ayah 56:17Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira).
بِأَكۡوَابٖ وَأَبَارِيقَ وَكَأۡسٖ مِّن مَّعِينٖ
Open ayah 56:18Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda;
لَّا يُصَدَّعُونَ عَنۡهَا وَلَا يُنزِفُونَ
Open ayah 56:19(Zakumwa zake) zosapweteketsa mutu ndiponso zosaledzeretsa;
وَفَٰكِهَةٖ مِّمَّا يَتَخَيَّرُونَ
Open ayah 56:20Ndi zipatso (zamitundumitundu) zimene azikazisankha;
وَلَحۡمِ طَيۡرٖ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ
Open ayah 56:21Ndi nyama yambalame imene mitima yawo izikafuna;
وَحُورٌ عِينٞ
Open ayah 56:22Ndi akazi ophanuka maso mokongola,
كَأَمۡثَٰلِ ٱللُّؤۡلُوِٕ ٱلۡمَكۡنُونِ
Open ayah 56:23(Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake.
جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Open ayah 56:24Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi).
لَا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوٗا وَلَا تَأۡثِيمًا
Open ayah 56:25M’menemo sakamva mawu achabe ngakhale (mawu a) machimo,
إِلَّا قِيلٗا سَلَٰمٗا سَلَٰمٗا
Open ayah 56:26Koma mawu oti: “Mtendere! Mtendere!”
وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ
Open ayah 56:27Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja!
فِي سِدۡرٖ مَّخۡضُودٖ
Open ayah 56:28(Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga.
وَطَلۡحٖ مَّنضُودٖ
Open ayah 56:29Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri.
وَظِلّٖ مَّمۡدُودٖ
Open ayah 56:30Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka,
وَمَآءٖ مَّسۡكُوبٖ
Open ayah 56:31Ndi madzi oyenda mosalekeza,
وَفَٰكِهَةٖ كَثِيرَةٖ
Open ayah 56:32Ndi zipatso zambiri,
لَّا مَقۡطُوعَةٖ وَلَا مَمۡنُوعَةٖ
Open ayah 56:33Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna).
وَفُرُشٖ مَّرۡفُوعَةٍ
Open ayah 56:34Ndi zoyala zapamwamba (zawofuwofu).
إِنَّآ أَنشَأۡنَٰهُنَّ إِنشَآءٗ
Open ayah 56:35Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba.
فَجَعَلۡنَٰهُنَّ أَبۡكَارًا
Open ayah 56:36Tidzawapanga kukhala anamwali.
عُرُبًا أَتۡرَابٗا
Open ayah 56:37Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu,
لِّأَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
Open ayah 56:38A anthu akudzanja la manja.
ثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 56:39Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba.
وَثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ
Open ayah 56:40Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza.
وَأَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ
Open ayah 56:41Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere!
فِي سَمُومٖ وَحَمِيمٖ
Open ayah 56:42Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira.
وَظِلّٖ مِّن يَحۡمُومٖ
Open ayah 56:43Ndi mumthunzi wa utsi wakuda.
لَّا بَارِدٖ وَلَا كَرِيمٍ
Open ayah 56:44Siwoziziritsa ndiponso siwosangalatsa.
إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُتۡرَفِينَ
Open ayah 56:45Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah),
وَكَانُواْ يُصِرُّونَ عَلَى ٱلۡحِنثِ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 56:46Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa).
وَكَانُواْ يَقُولُونَ أَئِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ
Open ayah 56:47Ndipo amanena (motsutsa); “Kodi tikadzafa nkusanduka fumbi ndi mafupa ofumbwa, tidzaukitsidwanso?”
أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ
Open ayah 56:48“Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)”
قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَوَّلِينَ وَٱلۡأٓخِرِينَ
Open ayah 56:49Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo),
لَمَجۡمُوعُونَ إِلَىٰ مِيقَٰتِ يَوۡمٖ مَّعۡلُومٖ
Open ayah 56:50Adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa.
ثُمَّ إِنَّكُمۡ أَيُّهَا ٱلضَّآلُّونَ ٱلۡمُكَذِّبُونَ
Open ayah 56:51Kenako inu osokera (njira yachilungamo), otsutsa (za kuuka,)
لَأٓكِلُونَ مِن شَجَرٖ مِّن زَقُّومٖ
Open ayah 56:52Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam).
فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ
Open ayah 56:53Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni).
فَشَٰرِبُونَ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡحَمِيمِ
Open ayah 56:54(Mkhuto wa mtengowo) adzamwera madzi owira;
فَشَٰرِبُونَ شُرۡبَ ٱلۡهِيمِ
Open ayah 56:55Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu!
هَٰذَا نُزُلُهُمۡ يَوۡمَ ٱلدِّينِ
Open ayah 56:56Ili ndi phwando lawo tsiku lamalipiro.
نَحۡنُ خَلَقۡنَٰكُمۡ فَلَوۡلَا تُصَدِّقُونَ
Open ayah 56:57Ife tidakulengani kodi nchifukwa ninji simukukhulupirira?
أَفَرَءَيۡتُم مَّا تُمۡنُونَ
Open ayah 56:58Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero,
ءَأَنتُمۡ تَخۡلُقُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡخَٰلِقُونَ
Open ayah 56:59Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga?
نَحۡنُ قَدَّرۡنَا بَيۡنَكُمُ ٱلۡمَوۡتَ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ
Open ayah 56:60Ife tidalamula imfa pakati panu ndipo Ife sitili wolephera,
عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ أَمۡثَٰلَكُمۡ وَنُنشِئَكُمۡ فِي مَا لَا تَعۡلَمُونَ
Open ayah 56:61Kubweretsa ena m’malo mwanu ndi kukulengani mwamaonekedwe ena omwe simumawadziwa.
وَلَقَدۡ عَلِمۡتُمُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُولَىٰ فَلَوۡلَا تَذَكَّرُونَ
Open ayah 56:62Ndipo ndithu mukdziwa kalengedwe koyamba; nanga bwanji simukukumbukira.
أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَحۡرُثُونَ
Open ayah 56:63Tandiuzani za zimene mukubzala?
ءَأَنتُمۡ تَزۡرَعُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلزَّٰرِعُونَ
Open ayah 56:64Kodi ndinu amene mukuzimeretsa kapena ndife Amene tikuzimeretsa?
لَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَٰهُ حُطَٰمٗا فَظَلۡتُمۡ تَفَكَّهُونَ
Open ayah 56:65Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula.
إِنَّا لَمُغۡرَمُونَ
Open ayah 56:66(Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”
بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ
Open ayah 56:67“Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”
أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلۡمَآءَ ٱلَّذِي تَشۡرَبُونَ
Open ayah 56:68Kodi mukuwaona madzi amene mukumwa!
ءَأَنتُمۡ أَنزَلۡتُمُوهُ مِنَ ٱلۡمُزۡنِ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنزِلُونَ
Open ayah 56:69Kodi ndinu amene mudawatsitsa ku mitambo kapena ndife Amene timawatsitsa?
لَوۡ نَشَآءُ جَعَلۡنَٰهُ أُجَاجٗا فَلَوۡلَا تَشۡكُرُونَ
Open ayah 56:70Tikadafuna tikadawapanga kukhala amchere; nanga nchifukwa ninji simuthokoza?
أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلنَّارَ ٱلَّتِي تُورُونَ
Open ayah 56:71Kodi mukuwuona moto umene mumaukoleza?
ءَأَنتُمۡ أَنشَأۡتُمۡ شَجَرَتَهَآ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنشِـُٔونَ
Open ayah 56:72Kodi ndinu amene mudameretsa mitengo yake kapena Ndife tidaipanga?
نَحۡنُ جَعَلۡنَٰهَا تَذۡكِرَةٗ وَمَتَٰعٗا لِّلۡمُقۡوِينَ
Open ayah 56:73Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu).
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 56:74Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.
۞فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَوَٰقِعِ ٱلنُّجُومِ
Open ayah 56:75Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa).
وَإِنَّهُۥ لَقَسَمٞ لَّوۡ تَعۡلَمُونَ عَظِيمٌ
Open ayah 56:76Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya).
إِنَّهُۥ لَقُرۡءَانٞ كَرِيمٞ
Open ayah 56:77Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri).
فِي كِتَٰبٖ مَّكۡنُونٖ
Open ayah 56:78Idachokera mu buku lotetezedwa.
لَّا يَمَسُّهُۥٓ إِلَّا ٱلۡمُطَهَّرُونَ
Open ayah 56:79Salikhudza kupatula okhawo oyeretsedwa (angelo).
تَنزِيلٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 56:80Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.
أَفَبِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ أَنتُم مُّدۡهِنُونَ
Open ayah 56:81Kodi nkhani iyi (ya Qur’an) ndiyomwe inu mukuinyozera?
وَتَجۡعَلُونَ رِزۡقَكُمۡ أَنَّكُمۡ تُكَذِّبُونَ
Open ayah 56:82Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani?
فَلَوۡلَآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلۡحُلۡقُومَ
Open ayah 56:83Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa).
وَأَنتُمۡ حِينَئِذٖ تَنظُرُونَ
Open ayah 56:84Uku inu panthawi imeneyo mukuona zimenezo.
وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنكُمۡ وَلَٰكِن لَّا تُبۡصِرُونَ
Open ayah 56:85Pomwe Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu, koma inu simuona,
فَلَوۡلَآ إِن كُنتُمۡ غَيۡرَ مَدِينِينَ
Open ayah 56:86Mukadakhala kuti simuzalipidwa (pa zomwe mukuchita),
تَرۡجِعُونَهَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Open ayah 56:87Bwenzi mukuubweza (mzimuwo) ngati mukunena zoona.
فَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ
Open ayah 56:88Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah;)
فَرَوۡحٞ وَرَيۡحَانٞ وَجَنَّتُ نَعِيمٖ
Open ayah 56:89Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere.
وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
Open ayah 56:90Ndipo ngati adali mmodzi wa anthu akudzanja lamanja,
فَسَلَٰمٞ لَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
Open ayah 56:91(Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”
وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ٱلضَّآلِّينَ
Open ayah 56:92Koma ngati adali mmodzi wa anthu otsutsa, osokera,
فَنُزُلٞ مِّنۡ حَمِيمٖ
Open ayah 56:93Phwando lamadzi owira (ndilake).
وَتَصۡلِيَةُ جَحِيمٍ
Open ayah 56:94Ndi kupsa m’moto wa Jahena.
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ حَقُّ ٱلۡيَقِينِ
Open ayah 56:95Ndithu izi ndizoona, zotsimikizika.
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 56:96Choncho lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.