المطففين
Al-Mutaffifin
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَيۡلٞ لِّلۡمُطَفِّفِينَ
Open ayah 83:1Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda.
ٱلَّذِينَ إِذَا ٱكۡتَالُواْ عَلَى ٱلنَّاسِ يَسۡتَوۡفُونَ
Open ayah 83:2Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza.
وَإِذَا كَالُوهُمۡ أَو وَّزَنُوهُمۡ يُخۡسِرُونَ
Open ayah 83:3Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo).
أَلَا يَظُنُّ أُوْلَٰٓئِكَ أَنَّهُم مَّبۡعُوثُونَ
Open ayah 83:4Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa;
لِيَوۡمٍ عَظِيمٖ
Open ayah 83:5Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)?
يَوۡمَ يَقُومُ ٱلنَّاسُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 83:6Tsiku limene adzaimilira anthu pamaso pa Mbuye wa zolengedwa.
كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡفُجَّارِ لَفِي سِجِّينٖ
Open ayah 83:7Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin.
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا سِجِّينٞ
Open ayah 83:8Nanga nchiyani chitakudziwitse za Sijjin?
كِتَٰبٞ مَّرۡقُومٞ
Open ayah 83:9Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa).
وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ
Open ayah 83:10Chilango chaukali tsiku limenelo chili pa otsutsa,[1]
- Kutsutsa kulipo kwa mitundu itatu: (a) Kutsutsa kwa mawu ndi zochita; (b) Kutsutsa kwa zochita zokha, monga ukauzidwa kuti chinthu ichi nchoipa, munthu nkudziwa kuti zoona nchoipadi koma nkudzachichita chimenecho mosalabadira; (c) Kutsutsa ndi zolankhula zokha. Kumeneko ndiko monga munthu akudziwa kuti chakutichakuti ncholetsedwa (haramu) koma m’malo mwake iye nkumati chimenecho nchovomerezeka (halali)
ٱلَّذِينَ يُكَذِّبُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ
Open ayah 83:11Amene akutsutsa za tsiku la malipiro.
وَمَا يُكَذِّبُ بِهِۦٓ إِلَّا كُلُّ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ
Open ayah 83:12Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri;
إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Open ayah 83:13Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.”
كَلَّاۖ بَلۡۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Open ayah 83:14Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola.[1]
- Munthu akachita choipa koyamba ndipo osalapa, limalowa dontho lakuda mu mtima mwake; nthawi iliyonse pamene akuonjezera machimo, dontho lija limakulirakulira mpaka kuuphimba mtima wonse. Dontho limeneli ndilo likutchedwa “Ran.” Tsono mtima ngati utaphimbidwa chotere sulabadira kuchita zoipa, ngakhale kuti auongole sungaongoke.
كَلَّآ إِنَّهُمۡ عَن رَّبِّهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّمَحۡجُوبُونَ
Open ayah 83:15Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona).
ثُمَّ إِنَّهُمۡ لَصَالُواْ ٱلۡجَحِيمِ
Open ayah 83:16Pambuyo pake adzalowa ku Moto; (oyaka)
ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
Open ayah 83:17Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).”
كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡأَبۡرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ
Open ayah 83:18Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun.
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا عِلِّيُّونَ
Open ayah 83:19Nanga nchiyani chitakudziwitse za Illiyyun?
كِتَٰبٞ مَّرۡقُومٞ
Open ayah 83:20Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino);
يَشۡهَدُهُ ٱلۡمُقَرَّبُونَ
Open ayah 83:21Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah).
إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ
Open ayah 83:22Ndithu ochita zabwino adzakhala mu mtendere,
عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ
Open ayah 83:23Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero).
تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِهِمۡ نَضۡرَةَ ٱلنَّعِيمِ
Open ayah 83:24Udzaona kuwala kwa mtendere pa nkhope zawo;
يُسۡقَوۡنَ مِن رَّحِيقٖ مَّخۡتُومٍ
Open ayah 83:25Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba;
خِتَٰمُهُۥ مِسۡكٞۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلۡيَتَنَافَسِ ٱلۡمُتَنَٰفِسُونَ
Open ayah 83:26Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana.[1]
- Apa, akutilamula kupikisana pakuchita zabwino kuti tipeze madalitso amene awakonzera anthu abwino. Kumeneko ndikuti munthu aliyense alimbikire kuchita mapemphero ndi zina zabwino.
وَمِزَاجُهُۥ مِن تَسۡنِيمٍ
Open ayah 83:27Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim.
عَيۡنٗا يَشۡرَبُ بِهَا ٱلۡمُقَرَّبُونَ
Open ayah 83:28(Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah.)
إِنَّ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ كَانُواْ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَضۡحَكُونَ
Open ayah 83:29Ndithu amene adachita machimo adali kuwaseka (mwachipongwe) okhulupirira (pa dziko lapansi);
وَإِذَا مَرُّواْ بِهِمۡ يَتَغَامَزُونَ
Open ayah 83:30(Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe);
وَإِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمُ ٱنقَلَبُواْ فَكِهِينَ
Open ayah 83:31Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira);
وَإِذَا رَأَوۡهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَضَآلُّونَ
Open ayah 83:32Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w)
وَمَآ أُرۡسِلُواْ عَلَيۡهِمۡ حَٰفِظِينَ
Open ayah 83:33Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera).
فَٱلۡيَوۡمَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنَ ٱلۡكُفَّارِ يَضۡحَكُونَ
Open ayah 83:34Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi),[1]
- (Ndime 34-36) Tanthauzo lake ndikuti okhulupilira, tsiku lachimaliziro adzakhala m’mipando ya ulemu uku akuwayang’ana ndi kuwaseka anthu osakhulupilira ali m’mavuto monga momwe iwo adali kuseka okhulupilira pa dziko lapansi.
عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ
Open ayah 83:35Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa).
هَلۡ ثُوِّبَ ٱلۡكُفَّارُ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ
Open ayah 83:36Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)?