الإنشقاق

Al-Inshiqaaq

The Splitting Open · Surah 84 · Ayahs: 25 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنشَقَّتۡ

    Open ayah 84:1

    Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake),

  2. وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ

    Open ayah 84:2

    Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero,

  3. وَإِذَا ٱلۡأَرۡضُ مُدَّتۡ

    Open ayah 84:3

    Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake),

  4. وَأَلۡقَتۡ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتۡ

    Open ayah 84:4

    Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu,[1]

    1. Chimodzi mwa zinthu zoopsa zomwe zidzachitika tsiku lachimaliziro ndi kugwedezeka kwa nthaka mwamphamvu zedi mpaka idzalekana ndi mapiri amene ali zichiri zake zoletsa kugwedezeka kwake. Pachifukwa ichi idzatambasuka ndipo zomwe zidali mkati mwake zidzatulukira pamtunda; nthaka idzangokhala yopanda kanthu mkati mwake.
  5. وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ

    Open ayah 84:5

    Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake).[1]

    1. Allah pambuyo ponena zimenezi sadanene kuti chidzachitika chiyani. Alekera munthu mwini wake kuti aganizire chomwe chidzachitika zikadzapezeka zoopsa kuti aope kwambiri.
  6. يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدۡحٗا فَمُلَٰقِيهِ

    Open ayah 84:6

    E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako).

  7. فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ

    Open ayah 84:7

    Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja,[1]

    1. Tsiku la chiweruziro munthu adzapatsidwa kaundula wake monga momwe zanenedwa mu Ayah 10 Surah Takwir, choncho ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanja; iwo ndiwo anthu abwino. Pomwe ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanzere, chakumbali yakumsana; iwowo ndiwo anthu oipa.
  8. فَسَوۡفَ يُحَاسَبُ حِسَابٗا يَسِيرٗا

    Open ayah 84:8

    Basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka,[1]

    1. Anthu ena adzawerengedwa popanda kufunsidwa mafunso pa zimene adachita, koma adzangowauza zabwino zawo ndi zoipa zawo ndipo pambuyo pake adzawakhululukira zoipazo ndi kudzawalipira pa zabwinozo. Iwowa ndiwo anthu abwino; chimenechi ndicho chiweruzo chofewa. Ena adzaweruzidwa pofunsidwa pa chilichonse m’zimene ankachita monga kuti “Bwanji ichi udachita? Bwanji ichi sudachite”? Iwowa ndiwo anthu oipa; chiwerengero chawo chidzakhala chokhwima.
  9. وَيَنقَلِبُ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورٗا

    Open ayah 84:9

    Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa.

  10. وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ وَرَآءَ ظَهۡرِهِۦ 

    Open ayah 84:10

    Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza),

  11. فَسَوۡفَ يَدۡعُواْ ثُبُورٗا

    Open ayah 84:11

    Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira);

  12. وَيَصۡلَىٰ سَعِيرًا

    Open ayah 84:12

    Ndipo adzalowa ku Moto woyaka.

  13. إِنَّهُۥ كَانَ فِيٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا

    Open ayah 84:13

    Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake).

  14. إِنَّهُۥ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ

    Open ayah 84:14

    Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa).

  15. بَلَىٰٓۚ إِنَّ رَبَّهُۥ كَانَ بِهِۦ بَصِيرٗا

    Open ayah 84:15

    Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita).

  16. فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلشَّفَقِ

    Open ayah 84:16

    Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa).

  17. وَٱلَّيۡلِ وَمَا وَسَقَ

    Open ayah 84:17

    Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa,[1]

    1. Kubalalikana masana ndi chizolowezi cha anthu ndi nyama chifukwa chofunafuna zinthu zothandiza pa moyo wawo. Tsono usiku ukabwera amasonkhana ndi kukhala pamodzi. Ndipo ili ndilo tanthauzo la: “Usiku ndi zimene wasonkhanitsa.”
  18. وَٱلۡقَمَرِ إِذَا ٱتَّسَقَ

    Open ayah 84:18

    Ndi mwezi ukakwanira dangalira (lake),

  19. لَتَرۡكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٖ

    Open ayah 84:19

    Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza).

  20. فَمَا لَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ 

    Open ayah 84:20

    Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)?

  21. وَإِذَا قُرِئَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقُرۡءَانُ لَا يَسۡجُدُونَۤ۩

    Open ayah 84:21

    Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa).

  22. بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُكَذِّبُونَ

    Open ayah 84:22

    Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza).

  23. وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُوعُونَ

    Open ayah 84:23

    Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa.

  24. فَبَشِّرۡهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

    Open ayah 84:24

    Choncho, auze nkhani yachilango chopweteka.

  25. إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونِۭ

    Open ayah 84:25

    Kupatula awo amene akhulupirira ndikuchita ntchito zabwino, kwa iwo kuli malipiro osatha.[1]

    1. Ayah iyi ikusonyeza kuti kukhulupilira kokha sikungampulumutse munthu ku chilango cha tsiku lachimaliziro, koma nkofunikanso kuchita ntchito zabwino; m’Qur’an paliponse pamene akutchula za chikhulupiliro akutchulanso za kuchita ntchito zabwino.