البروج

Al-Burooj

The Constellations · Surah 85 · Ayahs: 22 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡبُرُوجِ

    Open ayah 85:1

    Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu).[1]

    1. Buruj ndi nyenyezi zomwe zimakhala m’magulumagulu ndipo gulu lililonse limatchedwa Buruj. Ndipo Buruj zonse zilipo khumi ndi ziwiri (12). Zisanu ndi imodzi zili kumpoto kwa “Equator”, pomwe zisanu ndi imodzi zili kumwera kwake.
  2. وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡمَوۡعُودِ

    Open ayah 85:2

    Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa),

  3. وَشَاهِدٖ وَمَشۡهُودٖ

    Open ayah 85:3

    Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni.[1]

    1. “Woikira umboni ndi woikiridwa umboni” angathe kukhala aliyense woikira umboni ndi woikiridwa umboni pa tsiku lachimaliziro, monga aneneri adzaikira umboni anthu pa zabwino kapena zoipa; pa malo pochitira mapemphero padzamuikira umboni wazabwino yemwe adali kupempherapo. Ndipo pamalo pomwe padali kuchitikira zoipa padzawachitira umboni anthu oipa za machimo awo: ngakhale ziwalo ndi khungu nazonso pa tsiku limenelo zidzaikira umboni kwa mwini ziwalozo. Basi munthu akatsimikiza kuchita machimo akumbukire kuti ali nazo mboni zambiri zomwe zikumuona ndipo pa tsiku la chiweruziro zidzaima pa maso pa Allah kupereka umboni wokhudza munthuyo.
  4. قُتِلَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأُخۡدُودِ

    Open ayah 85:4

    Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi).[1]

    1. Pamene Ayuda a ku Najrani adalowa m’Chikhristu, (Chisilamu chisadafike ndiponso Chikhristu chisadaonongeke), idamufika nkhaniyi mfumu yawo dzina lake Dhu-Nuwas; adabwera ku Najrani ndi gulu lankhondo lalikulu; adawakakamizira anthu ku Chiyuda koma iwo adakana. Nayamba kuwapha anthu okhulupilirawo powaponya m’ngalande za moto.
  5. ٱلنَّارِ ذَاتِ ٱلۡوَقُودِ

    Open ayah 85:5

    (Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira),

  6. إِذۡ هُمۡ عَلَيۡهَا قُعُودٞ

    Open ayah 85:6

    Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo.

  7. وَهُمۡ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ شُهُودٞ

    Open ayah 85:7

    Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto).

  8. وَمَا نَقَمُواْ مِنۡهُمۡ إِلَّآ أَن يُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ

    Open ayah 85:8

    Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa,

  9. ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٌ

    Open ayah 85:9

    Yemwe ufumu wakumwamba ndi pansi ndiWake; ndipo Allah ndi mboni pachilichonse.

  10. إِنَّ ٱلَّذِينَ فَتَنُواْ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَتُوبُواْ فَلَهُمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمۡ عَذَابُ ٱلۡحَرِيقِ 

    Open ayah 85:10

    Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza,[1]

    1. Tanthauzo la “kuwazunza” apa ndiko kuwavutitsa ndi kuwathetsa mphamvu kuti asiye chikhulupiliro chawo; asakhulupirire mwa Allah. Mawuwa ngakhale akukhudzana ndi eni ngalande za moto, akukhudzanso akafiri a m’Makka omwe adali kuzunza Asilamu ndi mazunzo osiyanasiyana kuti abwelere kuchipembedzo cha mafano. Ndipo zimenezi zikhudzanso aliyense.
  11. إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّٰتٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡكَبِيرُ

    Open ayah 85:11

    Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere (momwe) mitsinje ikuyenda pansi pake; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.

  12. إِنَّ بَطۡشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ

    Open ayah 85:12

    Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri.[1]

    1. (Ndime 12-16) Allah pambuyo powatonthoza Asilamu pakuwauza zomwe zidawaonekera abale awo amene adatsogola, tsopanonso akuwatonthoza ndi ufumu Wake wolemekezeka kuti adziwe kuti awo akafiri omwe akudziona kuti ali ndi mphamvu zolangira anzawo, Iye sangamuthe. Akafuna adzawalanga ndi chilango cha dziko lapansi ndi cha tsiku lachimaliziro, kapena chimodzi mwa zilangozi; pakuti Iye Ngokhululuka kwambiri ndiponso Ngwachikondi zedi, awatembenula mitima yawo kuti achikhulupirire chimene adachikana. Chifukwa cha mphamvu Zake zoposa, Allah, adachita zonsezi ziwiri. Patapita zaka zochepa adawapatsa mphamvu omwe adali opanda mphamvu, kenaka adayamba kuwalanga osakhulupilira aja chilango cha padziko, monga Abu Jahl ndi anzake omwe adali kumutsutsa kwambiri Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi omutsatira ake. Ndipo ena adawatembenula mitima yawo nkulowa mchipembedzo cha Chisilamu; adaima ndikuchiteteza Chisilamu popereka nsembe ya mizimu yawo ndi chuma chawo.
  13. إِنَّهُۥ هُوَ يُبۡدِئُ وَيُعِيدُ

    Open ayah 85:13

    Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka);

  14. وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلۡوَدُودُ

    Open ayah 85:14

    Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera),

  15. ذُو ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡمَجِيدُ

    Open ayah 85:15

    Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake),

  16. فَعَّالٞ لِّمَا يُرِيدُ

    Open ayah 85:16

    Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika).

  17. هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡجُنُودِ

    Open ayah 85:17

    Kodi yakufika nkhani ya magulu a nkhondo,

  18. فِرۡعَوۡنَ وَثَمُودَ

    Open ayah 85:18

    Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)?

  19. بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي تَكۡذِيبٖ

    Open ayah 85:19

    Koma amene sadakhulupirire ali mkati motsutsa basi.

  20. وَٱللَّهُ مِن وَرَآئِهِم مُّحِيطُۢ 

    Open ayah 85:20

    Koma Allah awazinga mbali zonse.

  21. بَلۡ هُوَ قُرۡءَانٞ مَّجِيدٞ

    Open ayah 85:21

    Koma iyi ndi Qur’an yolemekezeka.

  22. فِي لَوۡحٖ مَّحۡفُوظِۭ

    Open ayah 85:22

    Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo).