الطارق
At-Taariq
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلسَّمَآءِ وَٱلطَّارِقِ
Open ayah 86:1Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku,
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلطَّارِقُ
Open ayah 86:2Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo?
ٱلنَّجۡمُ ٱلثَّاقِبُ
Open ayah 86:3Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima).
إِن كُلُّ نَفۡسٖ لَّمَّا عَلَيۡهَا حَافِظٞ
Open ayah 86:4Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake).
فَلۡيَنظُرِ ٱلۡإِنسَٰنُ مِمَّ خُلِقَ
Open ayah 86:5Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani?
خُلِقَ مِن مَّآءٖ دَافِقٖ
Open ayah 86:6Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka.
يَخۡرُجُ مِنۢ بَيۡنِ ٱلصُّلۡبِ وَٱلتَّرَآئِبِ
Open ayah 86:7Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi).
إِنَّهُۥ عَلَىٰ رَجۡعِهِۦ لَقَادِرٞ
Open ayah 86:8Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa).
يَوۡمَ تُبۡلَى ٱلسَّرَآئِرُ
Open ayah 86:9Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera.
فَمَا لَهُۥ مِن قُوَّةٖ وَلَا نَاصِرٖ
Open ayah 86:10Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi.
وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلرَّجۡعِ
Open ayah 86:11Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula.
وَٱلۡأَرۡضِ ذَاتِ ٱلصَّدۡعِ
Open ayah 86:12Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera),
إِنَّهُۥ لَقَوۡلٞ فَصۡلٞ
Open ayah 86:13Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama).
وَمَا هُوَ بِٱلۡهَزۡلِ
Open ayah 86:14Imeneyi sinkhambakamwa.
إِنَّهُمۡ يَكِيدُونَ كَيۡدٗا
Open ayah 86:15Ndithudi iwo akukonza chiwembu.[1]
- (Ndime15-16) Tanthauzo lake ndikuti akafiri (osakhulupilira) akuchita ndale kuti azimitse dangalira la Qur’an ndikuyesetsa kuti awabweze amene adakhulupilira ndiponso ndikufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Naye Allah akuwachitira ndale powaonongera ziwembu zawo zomwe amazikonza.
وَأَكِيدُ كَيۡدٗا
Open ayah 86:16Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa).
فَمَهِّلِ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَمۡهِلۡهُمۡ رُوَيۡدَۢا
Open ayah 86:17Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa).