النازعات
An-Naazi'aat
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلنَّٰزِعَٰتِ غَرۡقٗا
Open ayah 79:1Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira).[1]
- (Ndime 1-5) M’Qur’an nthawi zambiri Allah amalumbilira zolengedwa Zake; zamoyo ndi zopanda moyo, zooneka ndi zosaoneka. Cholinga ndikutilimbikitsa kuti tikhale olingalira luso Lake pa chinthu chilichonse chimene wachilumbilira kuti tizindikire ulemelero Wake ndi mphamvu Zake zoposa.
وَٱلنَّٰشِطَٰتِ نَشۡطٗا
Open ayah 79:2Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira).
وَٱلسَّٰبِحَٰتِ سَبۡحٗا
Open ayah 79:3Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera).
فَٱلسَّٰبِقَٰتِ سَبۡقٗا
Open ayah 79:4Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah.
فَٱلۡمُدَبِّرَٰتِ أَمۡرٗا
Open ayah 79:5Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa).
يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلرَّاجِفَةُ
Open ayah 79:6Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa).
تَتۡبَعُهَا ٱلرَّادِفَةُ
Open ayah 79:7Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse).
قُلُوبٞ يَوۡمَئِذٖ وَاجِفَةٌ
Open ayah 79:8Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa.
أَبۡصَٰرُهَا خَٰشِعَةٞ
Open ayah 79:9Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo);
يَقُولُونَ أَءِنَّا لَمَرۡدُودُونَ فِي ٱلۡحَافِرَةِ
Open ayah 79:10(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”
أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا نَّخِرَةٗ
Open ayah 79:11“Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”
قَالُواْ تِلۡكَ إِذٗا كَرَّةٌ خَاسِرَةٞ
Open ayah 79:12Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”
فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٞ وَٰحِدَةٞ
Open ayah 79:13(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi.
فَإِذَا هُم بِٱلسَّاهِرَةِ
Open ayah 79:14Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo).
هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ
Open ayah 79:15Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa?[1]
- Kuyambira Ayah iyi mpaka Ayah 26 Allah akumtonthoza mneneri Wake pomuuza nkhani ya Mneneri Musa momwe Farawo adamkanira, ndikuti asaganize kuti vutoli lampeza iye yekha koma kuti aneneri enanso akale lidawaonekeranso. Ndiponso m’ma Ayah amenewa muli chenjezo kwa akafiri kuti aope Allah kuti asawalange monga adamulangira Farawo ndi anthu ake amene adali kutsutsana ndi Allah.
إِذۡ نَادَىٰهُ رَبُّهُۥ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوًى
Open ayah 79:16Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa.
ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ
Open ayah 79:17(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu).
فَقُلۡ هَل لَّكَ إِلَىٰٓ أَن تَزَكَّىٰ
Open ayah 79:18Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”
وَأَهۡدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخۡشَىٰ
Open ayah 79:19“Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”
فَأَرَىٰهُ ٱلۡأٓيَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰ
Open ayah 79:20(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu.
فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ
Open ayah 79:21Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza.
ثُمَّ أَدۡبَرَ يَسۡعَىٰ
Open ayah 79:22Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah),
فَحَشَرَ فَنَادَىٰ
Open ayah 79:23Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu;
فَقَالَ أَنَا۠ رَبُّكُمُ ٱلۡأَعۡلَىٰ
Open ayah 79:24Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”
فَأَخَذَهُ ٱللَّهُ نَكَالَ ٱلۡأٓخِرَةِ وَٱلۡأُولَىٰٓ
Open ayah 79:25Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba.
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّمَن يَخۡشَىٰٓ
Open ayah 79:26Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah.
ءَأَنتُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَمِ ٱلسَّمَآءُۚ بَنَىٰهَا
Open ayah 79:27Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)?[1]
- Tanthauzo lake ndikuti: “Kodi chilengedwe chanu nchovuta kwambiri kuposa chilengedwe cha thambo pamene inu mukuganiza kuti Allah sangathe kukudzutsani pambuyo pa imfa?”
رَفَعَ سَمۡكَهَا فَسَوَّىٰهَا
Open ayah 79:28Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena).
وَأَغۡطَشَ لَيۡلَهَا وَأَخۡرَجَ ضُحَىٰهَا
Open ayah 79:29Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake.
وَٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ دَحَىٰهَآ
Open ayah 79:30Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala).
أَخۡرَجَ مِنۡهَا مَآءَهَا وَمَرۡعَىٰهَا
Open ayah 79:31Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake;
وَٱلۡجِبَالَ أَرۡسَىٰهَا
Open ayah 79:32Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika);
مَتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِأَنۡعَٰمِكُمۡ
Open ayah 79:33(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu.[1]
- Mu Ayah iyi Allah akusonyeza kuti Iye ndi Mwini mphamvu zonse zochitira chinthu chilichonse chachikulu kuposa kuwaukitsa akufa; ndiponso akukumbutsa ufulu Wake waukulu womwe adatichitira potipatsa zinthu zonsezo kuti tithandizike nazo.
فَإِذَا جَآءَتِ ٱلطَّآمَّةُ ٱلۡكُبۡرَىٰ
Open ayah 79:34Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma).
يَوۡمَ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا سَعَىٰ
Open ayah 79:35Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa).
وَبُرِّزَتِ ٱلۡجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ
Open ayah 79:36Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya.
فَأَمَّا مَن طَغَىٰ
Open ayah 79:37Tsono amene adapyola malire (pochita machimo),
وَءَاثَرَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا
Open ayah 79:38Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi,
فَإِنَّ ٱلۡجَحِيمَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ
Open ayah 79:39Ndithu Jahannam ndiwo malo ake.
وَأَمَّا مَنۡ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِۦ وَنَهَى ٱلنَّفۡسَ عَنِ ٱلۡهَوَىٰ
Open ayah 79:40Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa,
فَإِنَّ ٱلۡجَنَّةَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ
Open ayah 79:41Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake.
يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَا
Open ayah 79:42Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”
فِيمَ أَنتَ مِن ذِكۡرَىٰهَآ
Open ayah 79:43Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo).
إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَىٰهَآ
Open ayah 79:44Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake.
إِنَّمَآ أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخۡشَىٰهَا
Open ayah 79:45Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake).
كَأَنَّهُمۡ يَوۡمَ يَرَوۡنَهَا لَمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا عَشِيَّةً أَوۡ ضُحَىٰهَا
Open ayah 79:46Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa).[1]
- Apa tanthauzo lake ndikuti adzaona masiku onse amene adakhala m’dziko ngati lidali ola limodzi.