النبإ
An-Naba
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
عَمَّ يَتَسَآءَلُونَ
Open ayah 78:1۞ Kodi akufunsana zachiyani?
عَنِ ٱلنَّبَإِ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 78:2Za nkhani yayikulu ija.
ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ مُخۡتَلِفُونَ
Open ayah 78:3Imene iwo akusiyana (maganizo).[1]
- Nkhani yaikulu imene akafiri (anthu osakhulupilira Allah) adali kufunsana wina ndi mnzake ndi nkhani yakuuka tsiku la Qiyâma ndi uneneri wa Mtumiki Muhammad. Amafunsana kuti, “Kodi nzoona tidzauka m’manda, nanga nzoona kuti Muhammad ndi Mneneri?” Adali kufunsananso kuti, “Kodi zakuti Allah ndi Mmodzi ndi zoona?”
كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ
Open ayah 78:4Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa.[1]
- Kuyankhula koti: “Kallaa” kwanenedwa kwambiri m’Qur’an. Tanthauzo lake nthawi zina ndikuletsa, nthawi zina ndikutsimikiza. Choncho mawuwa amatanthauzidwa malinga ndi momwe chiganizocho chilili.
ثُمَّ كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ
Open ayah 78:5Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira).[1]
- Allah, apa, akuwauza kuti asiye kuganizira zinthu zopanda pake. Kodi sadadziwebe mpaka pano kuti Muhammad ndi Mneneri wa Allah, ndikuti Allah ndi Mmodzi yekha? Ndikutinso kuli tsiku lachimaliziro; pamene munthu aliyense adzalipidwa pa zimene adachita? Basi tsiku lachimaliziro likadzawafikira adzadziwa kuti zimene adali kuwauza Mneneri nzoona.
أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ مِهَٰدٗا
Open ayah 78:6Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala?[1]
- Kuyambira Ayah iyi, kudzafika Ayah 16, Allah akusonyeza anthu Ake madalitso ambiri omwe wawadalitsa nawo kuti azindikire kuti Mwini kupereka madalitso amenewa m’dziko sangawasiye anthu Ake m’kusokera popanda kuwatumizira munthu wowaongolera ku njira yabwino, ndikuwadziwitsa zamtendere wapadziko ndi tsiku lachimaliziro. Ndikuti Allah amene adapanga zonsezi palibe chimene angachilephere. Ndipo tanthauzo la choyala, apa, ndi pamalo poti nkutheka munthu kuchita chimene akufuna pa moyo wake. Tanthauzo lake sikuti dothi lakhala ngati mkeka wa pabedi ayi.
وَٱلۡجِبَالَ أَوۡتَادٗا
Open ayah 78:7Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)?
وَخَلَقۡنَٰكُمۡ أَزۡوَٰجٗا
Open ayah 78:8Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi).
وَجَعَلۡنَا نَوۡمَكُمۡ سُبَاتٗا
Open ayah 78:9Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito).
وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِبَاسٗا
Open ayah 78:10Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake).
وَجَعَلۡنَا ٱلنَّهَارَ مَعَاشٗا
Open ayah 78:11Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo;
وَبَنَيۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعٗا شِدَادٗا
Open ayah 78:12Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba;
وَجَعَلۡنَا سِرَاجٗا وَهَّاجٗا
Open ayah 78:13Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa);
وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءٗ ثَجَّاجٗا
Open ayah 78:14Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula;
لِّنُخۡرِجَ بِهِۦ حَبّٗا وَنَبَاتٗا
Open ayah 78:15Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama).
وَجَنَّٰتٍ أَلۡفَافًا
Open ayah 78:16Ndi minda yothothana nthambi za mitengo.
إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ كَانَ مِيقَٰتٗا
Open ayah 78:17Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale.
يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجٗا
Open ayah 78:18Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu.
وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبٗا
Open ayah 78:19Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo.
وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا
Open ayah 78:20Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu.[1]
- Apa, ndikuti zimene munthu amaziona patsogolo pake nkumaziganizira ngati madzi pomwe sali madzi. Choncho pa tsiku limenelo mapiri adzaoneka ngati akhazikika monga m’mene adalili pomwe sichoncho, adzakhala ngati thonje louluka ndi mphepo.
إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتۡ مِرۡصَادٗا
Open ayah 78:21Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa).
لِّلطَّٰغِينَ مَـَٔابٗا
Open ayah 78:22Mbuto ya opyola malire.[1]
- Jahannam ndi dzina lamoto wodziwika wa tsiku lachimaliziro. Apa Allah akutidziwitsa kuti Jahannam ndi malo amene akudikira akafiri kuti m’menemo akalipidwe malipiro awo chifukwa chokanira aneneri pambuyo powasonyeza zizindikiro zoti iwo ndi aneneri a Allah. Ndiponso kumulakwira Allah pochita zimene adaletsa monga; kukana umodzi wa Allah, kukana utumiki wa Mahammad (s.a.w) ndi kukana uthenga wa Qur’an. Komanso kugwa mmachimo osiyanasiyana.
لَّٰبِثِينَ فِيهَآ أَحۡقَابٗا
Open ayah 78:23Adzakhala m’menemo muyaya.
لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدٗا وَلَا شَرَابًا
Open ayah 78:24Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo);
إِلَّا حَمِيمٗا وَغَسَّاقٗا
Open ayah 78:25Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto);
جَزَآءٗ وِفَاقًا
Open ayah 78:26Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo.
إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابٗا
Open ayah 78:27Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah);
وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كِذَّابٗا
Open ayah 78:28Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu.
وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ كِتَٰبٗا
Open ayah 78:29Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba.
فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا
Open ayah 78:30Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango.
إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ مَفَازًا
Open ayah 78:31Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana.
حَدَآئِقَ وَأَعۡنَٰبٗا
Open ayah 78:32Minda ndi zipatso za mphesa.
وَكَوَاعِبَ أَتۡرَابٗا
Open ayah 78:33Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu.
وَكَأۡسٗا دِهَاقٗا
Open ayah 78:34Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa.
لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوٗا وَلَا كِذَّٰبٗا
Open ayah 78:35Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza.
جَزَآءٗ مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابٗا
Open ayah 78:36Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira.[1]
- Chipembedzo cha Chisilamu chikuphunzitsa kuti pali zisangalalo ziwiri: Chisangalalo cha mzimu ndi chisangalalo cha thupi. Tsono chisangalalo cha mzimu ndiko kuyanjana kochokera kwa Allah kumene anthu Ake abwino adzakupeza. Chisangalalo cha thupi ndi monga m’mene afotokozera mu Ayah iyi ndi msura zina. Zokondweretsa monga minda, akazi okongola, mowa (osaledzeretsa) ndiponso sikudzakhala kumva chilichonse chokhumudwitsa. Taonani, zoledzeretsa ndi zoletsedwa padziko lino lapansi chifukwa cha zoipa zake. Koma mowa wa patsiku la Qiyâma udzakhala wopanda zoipa.
رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابٗا
Open ayah 78:37Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero);
يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ صَفّٗاۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابٗا
Open ayah 78:38Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola.
ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا
Open ayah 78:39Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi).
إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابٗا قَرِيبٗا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا
Open ayah 78:40Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi).