عبس

Abasa

He frowned · Surah 80 · Ayahs: 42 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. عَبَسَ وَتَوَلَّىٰٓ

    Open ayah 80:1

    Adachita tsinya (Mneneri) ndi kuyang’ana kumbali.[1]

    1. Tsiku lina Mneneri (s.a.w) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. Sadadziwe kuti Mneneri (s.a.w) ali wotanganidwa. Adamukuwira: “E Iwe Mneneri wa Allah! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Allah.” Ndipo ankangomubwerezera-bwerezera mawu amenewa. Mneneri (s.a.w) pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, adamchitira tsinya wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; sadamumvere. Basi pamenepa Allah akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko.
  2. أَن جَآءَهُ ٱلۡأَعۡمَىٰ

    Open ayah 80:2

    Chifukwa chakuti adamdzera wakhungu (kudzamfunsa zokhudzana ndi chipembedzo chake pamene iye adali kuyankhula ndi atsogoleri Achiquraishi).

  3. وَمَا يُدۡرِيكَ لَعَلَّهُۥ يَزَّكَّىٰٓ

    Open ayah 80:3

    Nanga chingakudziwitse nchiyani kuti mwina iye angadziyeretse (pomvera ulaliki wako watsopano)?

  4. أَوۡ يَذَّكَّرُ فَتَنفَعَهُ ٱلذِّكۡرَىٰٓ

    Open ayah 80:4

    Kapena akumbukira, ndipo kukumbukirako kumthandiza?

  5. أَمَّا مَنِ ٱسۡتَغۡنَىٰ

    Open ayah 80:5

    Koma amene wadzikwaniritsa (ndi chuma chake ndi mphamvu zake),

  6. فَأَنتَ لَهُۥ تَصَدَّىٰ

    Open ayah 80:6

    Ameneyo ndi yemwe ukumchitira chidwi.

  7. وَمَا عَلَيۡكَ أَلَّا يَزَّكَّىٰ

    Open ayah 80:7

    Palibe chilichonse pa iwe ngati sadziyeretsa.

  8. وَأَمَّا مَن جَآءَكَ يَسۡعَىٰ

    Open ayah 80:8

    Koma amene wakudzera uku akuthamanga (kufuna maphunziro ndi chiongoko),

  9. وَهُوَ يَخۡشَىٰ

    Open ayah 80:9

    Ndipo iye akuopa (Allah mu mtima mwake).

  10. فَأَنتَ عَنۡهُ تَلَهَّىٰ 

    Open ayah 80:10

    Za iye, iwe sukusamala, (ukuyikira chidwi kwa wina).

  11. كَلَّآ إِنَّهَا تَذۡكِرَةٞ

    Open ayah 80:11

    Sichoncho! Ndithudi iyi (Qur’an) ndi chikumbutso (chenjezo).[1]

    1. (Ndime 11-16) Apa Allah akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur’an ndi ulaliki chabe, amene afuna kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. Ndiponso adamufotokozera kuti Qur’an idachokera m’mabuku olemekezeka; idachokera ku “Lauhil-Mahfudh” mabuku omwe ali m’manja mwa Angelo olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi.
  12. فَمَن شَآءَ ذَكَرَهُۥ

    Open ayah 80:12

    Basi, amene wafuna alangizika (ndi Qur’an, ndipo amene sakufuna msiye).

  13. فِي صُحُفٖ مُّكَرَّمَةٖ

    Open ayah 80:13

    (Malangizowa akuchokera) mmakalata olemekezeka (kwa Allah);

  14. مَّرۡفُوعَةٖ مُّطَهَّرَةِۭ

    Open ayah 80:14

    Apamwamba ndiponso oyeretsedwa (kumbiri iliyonse yopunguka);

  15. بِأَيۡدِي سَفَرَةٖ

    Open ayah 80:15

    Omwe ali m’manja mwa Alembi (Angelo).

  16. كِرَامِۭ بَرَرَةٖ

    Open ayah 80:16

    Olemekezeka, omvera.

  17. قُتِلَ ٱلۡإِنسَٰنُ مَآ أَكۡفَرَهُۥ

    Open ayah 80:17

    Waonongeka (watembeleredwa) munthu. Nkotani kusayamika kwake kotereku.

  18. مِنۡ أَيِّ شَيۡءٍ خَلَقَهُۥ

    Open ayah 80:18

    Kuchokera mchinthu chanji chimene iye adamulenga.

  19. مِن نُّطۡفَةٍ خَلَقَهُۥ فَقَدَّرَهُۥ

    Open ayah 80:19

    Kuchokera ku dontho lamadzi (onyozeka) adamulenga, namkonzeratu mkalengedwe kosiyanasiyana.

  20. ثُمَّ ٱلسَّبِيلَ يَسَّرَهُۥ 

    Open ayah 80:20

    Kenako adamfewetsera njira (yotulukira m’mimba mwa mai ake).

  21. ثُمَّ أَمَاتَهُۥ فَأَقۡبَرَهُۥ

    Open ayah 80:21

    Ndipo amamchititsa kuti amwalire namukumbula m’manda,

  22. ثُمَّ إِذَا شَآءَ أَنشَرَهُۥ

    Open ayah 80:22

    Kenako akadzafuna adzamuukitsa (pambuyo pa imfa).

  23. كَلَّا لَمَّا يَقۡضِ مَآ أَمَرَهُۥ

    Open ayah 80:23

    Ayi ndithu (munthu) sanakwaniritsebe zimene adamulamula Mbuye wake (Allah chingakhale wakhala nthawi yaitali pa dziko lapansi).

  24. فَلۡيَنظُرِ ٱلۡإِنسَٰنُ إِلَىٰ طَعَامِهِۦٓ

    Open ayah 80:24

    Alingalire munthu (mmene chilili) chakudya chake;[1]

    1. Ngati munthu sakumbuka chilengedwe chake, ayang’ane chakudya chimene akudya momwe chimapezekera. Azindikira mphamvu za Allah.
  25. أَنَّا صَبَبۡنَا ٱلۡمَآءَ صَبّٗا

    Open ayah 80:25

    Ndithu Ife timagwetsa mvula yambiri (kuchokera ku mitambo).

  26. ثُمَّ شَقَقۡنَا ٱلۡأَرۡضَ شَقّٗا

    Open ayah 80:26

    Kenako timaing’amba nthaka kuti mmera utuluke;

  27. فَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا حَبّٗا

    Open ayah 80:27

    Ndipo timameretsa m’menemo njere (ya chakudya cha anthu ndi zina zimene amasunga mnkhokwe),

  28. وَعِنَبٗا وَقَضۡبٗا

    Open ayah 80:28

    Ndi mphesa ndi msipu.

  29. وَزَيۡتُونٗا وَنَخۡلٗا

    Open ayah 80:29

    Ndi mzitona (wabwino) ndi (zipatso za) kanjedza,

  30. وَحَدَآئِقَ غُلۡبٗا 

    Open ayah 80:30

    Ndi minda yothothana nthambi za mitengo,

  31. وَفَٰكِهَةٗ وَأَبّٗا

    Open ayah 80:31

    Ndi zipatso (zodyedwa ndi anthu) ndi msipu (wodyedwa ndi nyama);

  32. مَّتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِأَنۡعَٰمِكُمۡ

    Open ayah 80:32

    (Tazimeretsa zimenezo kuti) zikondweretse inu ndi ziweto zanu.

  33. فَإِذَا جَآءَتِ ٱلصَّآخَّةُ

    Open ayah 80:33

    Choncho likadzafika lipenga logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa makosi).

  34. يَوۡمَ يَفِرُّ ٱلۡمَرۡءُ مِنۡ أَخِيهِ

    Open ayah 80:34

    Patsikuli munthu adzathawa m’bale wake,

  35. وَأُمِّهِۦ وَأَبِيهِ

    Open ayah 80:35

    Mayi wake ndi bambo wake,

  36. وَصَٰحِبَتِهِۦ وَبَنِيهِ

    Open ayah 80:36

    Mkazi wake ndi ana ake.

  37. لِكُلِّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ يَوۡمَئِذٖ شَأۡنٞ يُغۡنِيهِ

    Open ayah 80:37

    Munthu aliyense mwa iwo, tsiku limenelo adzakhala ndi zakezake zotangwanika nazo. (Sadzalabadira za anzake).

  38. وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ مُّسۡفِرَةٞ

    Open ayah 80:38

    Tsiku limenelo nkhope zina zidzakhala zowala;[1]

    1. (Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: amene adakhulupilira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma Ayah 40 ndi 42.
  39. ضَاحِكَةٞ مُّسۡتَبۡشِرَةٞ

    Open ayah 80:39

    Zosekelera ndi zachimwemwe (chifukwa cha nkhani yabwino ya ku Munda wamtendere.)

  40. وَوُجُوهٞ يَوۡمَئِذٍ عَلَيۡهَا غَبَرَةٞ 

    Open ayah 80:40

    Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zokutidwa ndi fumbi.

  41. تَرۡهَقُهَا قَتَرَةٌ

    Open ayah 80:41

    Mdima udzazikuta.

  42. أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡكَفَرَةُ ٱلۡفَجَرَةُ

    Open ayah 80:42

    Iwo ndi anthu osakhulupirira oipa (olakwira Allah).