التكوير

At-Takwir

The Overthrowing · Surah 81 · Ayahs: 29 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. إِذَا ٱلشَّمۡسُ كُوِّرَتۡ

    Open ayah 81:1

    Pamene dzuwa lidzakulungidwe (ndikuchotsedwa kuwala kwake),[1]

    1. Surah zambiri zimene zidavumbulutsidwa ku Makka zimanena zododometsa za tsiku lachimaliziro.
  2. وَإِذَا ٱلنُّجُومُ ٱنكَدَرَتۡ

    Open ayah 81:2

    Ndi pamene nyenyezi zidzathothoke (ndi kuchoka dangalira lake),

  3. وَإِذَا ٱلۡجِبَالُ سُيِّرَتۡ

    Open ayah 81:3

    Ndi pamene mapiri adzayendetsedwe (kuchoka mmalo mwake),[1]

    1. Tsiku limenelo mapiri adzakhala osalimba ngati thonje limene likungouluka ndi mphepo.
  4. وَإِذَا ٱلۡعِشَارُ عُطِّلَتۡ

    Open ayah 81:4

    Ndi pamene ngamira zabere lamiyezi khumi zidzasiidwe (zopanda oziyang’anira),[1]

    1. Ngamira za bere ndi chuma cha mtengo wapatali kwa Aarabu. Akuuzidwa apa kuti tsiku limenelo adzazisiya osazilabadira konse.
  5. وَإِذَا ٱلۡوُحُوشُ حُشِرَتۡ

    Open ayah 81:5

    Ndi pamene nyama za mtchire zidzasonkhanitsidwe pamodzi (kuchokera mmalo osiyanasiyana chifukwa chakuopsa kwakukulu kwa tsikulo),[1]

    1. Mwa zina zododometsa pa tsiku limenelo ndi nyama za mtchire kusonkhanitsidwa pamodzi popanda kumenyana kapena kudyana.
  6. وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ سُجِّرَتۡ

    Open ayah 81:6

    Ndi pamene nyanja zidzayatsidwe moto,

  7. وَإِذَا ٱلنُّفُوسُ زُوِّجَتۡ

    Open ayah 81:7

    Ndi pamene mizimu idzalumikizidwe (ndi matupi ake),

  8. وَإِذَا ٱلۡمَوۡءُۥدَةُ سُئِلَتۡ

    Open ayah 81:8

    Ndi pamene mwana wamkazi yemwe adaikidwa m’manda wamoyo adzafunsidwe,[1]

    1. (Ndime 8-9) Ma Ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adalili Usilamu usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera, kumudyetsa, ndi kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. Ndipo apa Allah akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruziro, mwana uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. Iye adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda chilungamo.
  9. بِأَيِّ ذَنۢبٖ قُتِلَتۡ

    Open ayah 81:9

    Ndi tchimo lanji adaphedwera?

  10. وَإِذَا ٱلصُّحُفُ نُشِرَتۡ 

    Open ayah 81:10

    Ndi pamene makalata (momwe mudalembedwa zochita za aliyense) adzatambasulidwe ndi kugawidwa (kuti awerengedwe),[1]

    1. Awa ndi makalata achiwerengero momwe mwalembedwa zabwino za munthu ndi zoipa zake. Tsiku limenelo munthu aliyense adzapatsidwa yake kalata kuti aone iye mwini zoipa ndi zabwino zake.
  11. وَإِذَا ٱلسَّمَآءُ كُشِطَتۡ

    Open ayah 81:11

    Ndi pamene thambo lidzayalulidwe (kuchoka mmalo mwake),

  12. وَإِذَا ٱلۡجَحِيمُ سُعِّرَتۡ

    Open ayah 81:12

    Ndi pamene Jahena idzasonkhezeredwe mwamphamvu,[1]

    1. (Ndime12-13) Tsiku limenelo Jannah idzayandikitsidwa kwa ochita zabwino ndiponso Moto udzayandikitsidwa kwa ochita zoipa kuti aone kumalo kwake.
  13. وَإِذَا ٱلۡجَنَّةُ أُزۡلِفَتۡ

    Open ayah 81:13

    Ndi pamene Jannah idzayandikitsidwe,

  14. عَلِمَتۡ نَفۡسٞ مَّآ أَحۡضَرَتۡ

    Open ayah 81:14

    (Zikadzachitika zimenezi) mzimu uliwonse udzadziwa zimene wabweretsa (zabwino ndi zoipa).

  15. فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلۡخُنَّسِ

    Open ayah 81:15

    Ndikulumbilira nyenyezi zimene zimabwerera masana ndi kutulukanso usiku.

  16. ٱلۡجَوَارِ ٱلۡكُنَّسِ

    Open ayah 81:16

    Zomwe zimayenda kenako nkubisika,

  17. وَٱلَّيۡلِ إِذَا عَسۡعَسَ

    Open ayah 81:17

    Ndi usiku pamene ukulowa.

  18. وَٱلصُّبۡحِ إِذَا تَنَفَّسَ

    Open ayah 81:18

    Ndi m’mawa kukamacha;

  19. إِنَّهُۥ لَقَوۡلُ رَسُولٖ كَرِيمٖ

    Open ayah 81:19

    Ndithu iyi (Qur’an) ndi liwu la mthenga wa Allah (Jibril) wolemekezeka,[1]

    1. (Ndime 19-20) Mthenga wolemekezeka womveredwa uko kumwamba ndi Jibril (Gabriele) yemwe ndi wamkulu wa angelo onse. Iye ndiyemwe adali kubweretsa Qur’an mwa lamulo la Allah kwa Mneneri Wake Muhammad (s.a.w). Ndipo ulemelero wa Qur’an ndi ulemelero wa Mneneri (s.a.w) chifukwa choti munthu wolemekezeka amamutumizira mthenga wolemekezekanso. Ndipo uthenga wabwino umapatsidwa kwa Mneneri wabwino woposa onse.
  20. ذِي قُوَّةٍ عِندَ ذِي ٱلۡعَرۡشِ مَكِينٖ 

    Open ayah 81:20

    Mwini mphamvu ndi mwini ulemelero kwa Mwini Arsh (Mpando wa chifumu),

  21. مُّطَاعٖ ثَمَّ أَمِينٖ

    Open ayah 81:21

    Womveredwa kumeneko ndiponso wokhulupirika (pachivumbulutso).

  22. وَمَا صَاحِبُكُم بِمَجۡنُونٖ

    Open ayah 81:22

    Ndipo m’bale wanuyu siwamisala ayi.[1]

    1. (Ndime 22-25) Anthu okanira pamene adasowa chonena kwa mneneri (s.a.w) adali kunena nkhani zabodza kuti Mtumiki (s.a.w) wapenga ndikuti zomwe akuyankhula sadapatsidwe ndi Jibril.
  23. وَلَقَدۡ رَءَاهُ بِٱلۡأُفُقِ ٱلۡمُبِينِ

    Open ayah 81:23

    Ndithu ndikulumbira kuti (iye Mtumiki) (s.a.w) adamuona (Jibril) mchizimezime (chakum’mawa) chooneka bwino.

  24. وَمَا هُوَ عَلَى ٱلۡغَيۡبِ بِضَنِينٖ

    Open ayah 81:24

    Ndipo sali iye (Mtumiki) waumbombo ndi chivumbulutso (koma amafikitsa zonse ndi kuziphunzitsa kwa anthu).

  25. وَمَا هُوَ بِقَوۡلِ شَيۡطَٰنٖ رَّجِيمٖ

    Open ayah 81:25

    (Chivumbulutso chomwe chavumbulutsidwachi kwa iye) si mawu a satana wothamangitsidwa (mchifundo cha Allah);

  26. فَأَيۡنَ تَذۡهَبُونَ

    Open ayah 81:26

    Nanga mukupita kuti?

  27. إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ

    Open ayah 81:27

    (Qur’ani) iyi sichina koma ndi chikumbutso cha zolengedwa zonse.

  28. لِمَن شَآءَ مِنكُمۡ أَن يَسۡتَقِيمَ

    Open ayah 81:28

    Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda mu njira yoongoka.

  29. وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

    Open ayah 81:29

    Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.