المعارج
Al-Ma'aarij
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
سَأَلَ سَآئِلُۢ بِعَذَابٖ وَاقِعٖ
Open ayah 70:1Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa).
لِّلۡكَٰفِرِينَ لَيۡسَ لَهُۥ دَافِعٞ
Open ayah 70:2Kwa okanira palibe angachitsekereze.
مِّنَ ٱللَّهِ ذِي ٱلۡمَعَارِجِ
Open ayah 70:3Chochokera kwa Allah Mwini makwelero.
تَعۡرُجُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥ خَمۡسِينَ أَلۡفَ سَنَةٖ
Open ayah 70:4Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000).
فَٱصۡبِرۡ صَبۡرٗا جَمِيلًا
Open ayah 70:5Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino,
إِنَّهُمۡ يَرَوۡنَهُۥ بَعِيدٗا
Open ayah 70:6Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike).
وَنَرَىٰهُ قَرِيبٗا
Open ayah 70:7Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika).
يَوۡمَ تَكُونُ ٱلسَّمَآءُ كَٱلۡمُهۡلِ
Open ayah 70:8Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka.
وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ
Open ayah 70:9Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha).
وَلَا يَسۡـَٔلُ حَمِيمٌ حَمِيمٗا
Open ayah 70:10Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake.
يُبَصَّرُونَهُمۡۚ يَوَدُّ ٱلۡمُجۡرِمُ لَوۡ يَفۡتَدِي مِنۡ عَذَابِ يَوۡمِئِذِۭ بِبَنِيهِ
Open ayah 70:11Ngakhale adzawalole kuti aonane ndi kudziwana pakati pawo (sadzafunsana). Wochimwa adzalakalaka kuti akadaziwombola ku chilango cha tsiku limenelo ndi ana ake.
وَصَٰحِبَتِهِۦ وَأَخِيهِ
Open ayah 70:12Ndi mkazi wake, ndi m’bale wake.
وَفَصِيلَتِهِ ٱلَّتِي تُـٔۡوِيهِ
Open ayah 70:13Ndi akumtundu wake amene amamsunga.
وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا ثُمَّ يُنجِيهِ
Open ayah 70:14Ndi (kulipira) zonse za m’dziko, kuti zimpulumutse.
كَلَّآۖ إِنَّهَا لَظَىٰ
Open ayah 70:15Iyayi, (siya iwe wamachimo zimene ukulakalakazo)! Ndithu umenewu ndi Moto wa malawi.
نَزَّاعَةٗ لِّلشَّوَىٰ
Open ayah 70:16Wosupula mwamphamvu khungu.
تَدۡعُواْ مَنۡ أَدۡبَرَ وَتَوَلَّىٰ
Open ayah 70:17Udzaitana (potchula dzina la aliyense) amene adachitembenuzira msana choona ndi kunyoza.
وَجَمَعَ فَأَوۡعَىٰٓ
Open ayah 70:18Adasonkhanitsa (chuma) ndi kusunga (m’nkhokwe zake popanda kuperekera chopereka cha Allah).
۞إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ خُلِقَ هَلُوعًا
Open ayah 70:19Ndithu munthu walengedwa kukhala wosapirira.
إِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ جَزُوعٗا
Open ayah 70:20Mavuto akamkhudza amada nkhawa.
وَإِذَا مَسَّهُ ٱلۡخَيۡرُ مَنُوعًا
Open ayah 70:21Koma zabwino zikamkhudza amamana (ena ndi kuiwala mavuto amene adali nawo).
إِلَّا ٱلۡمُصَلِّينَ
Open ayah 70:22Kupatula opemphera Swala, (iwo alibe mbiri zoipazi).
ٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ دَآئِمُونَ
Open ayah 70:23Iwo amene sadukiza mapemphero awo a swala; (sakuwaleka ngakhale zivute chotani).
وَٱلَّذِينَ فِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقّٞ مَّعۡلُومٞ
Open ayah 70:24Ndi amene mchuma chawo muli gawo lodziwika (Zakaat),
لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ
Open ayah 70:25La wopempha ndi wosapempha.
وَٱلَّذِينَ يُصَدِّقُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ
Open ayah 70:26Ndi amene akuvomereza za tsiku la malipiro (ndi kumalikonzekera.)
وَٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ عَذَابِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ
Open ayah 70:27Ndi iwo amene akuopa chilango chochokera kwa Mbuye wawo.
إِنَّ عَذَابَ رَبِّهِمۡ غَيۡرُ مَأۡمُونٖ
Open ayah 70:28Ndithu chilango cha Mbuye wawo nchosapulumuka nacho (munthu woipa).
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ
Open ayah 70:29Ndiponso iwo amene akusunga umaliseche wawo (posachita chiwerewere),
إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ
Open ayah 70:30Kupatula kwa akazi awo ndi amene manja awo akumanja apeza; ndithu pazimenezo iwo sangadzudzulidwe.
فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ
Open ayah 70:31Koma amene angafune (zina) kusiya zimenezi iwowo ndiwo olumpha malire.
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ
Open ayah 70:32Ndi iwo amene amasunga mwaubwino zimene amasungitsidwa ndi zimene alonjeza.
وَٱلَّذِينَ هُم بِشَهَٰدَٰتِهِمۡ قَآئِمُونَ
Open ayah 70:33Ndi iwo amene amaima molungama popereka umboni wawo.
وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ
Open ayah 70:34Ndiponso iwo amene amasunga (mwaubwino) mapemphero awo a swala.
أُوْلَٰٓئِكَ فِي جَنَّٰتٖ مُّكۡرَمُونَ
Open ayah 70:35Amene ali ndi mbiri zimenezi adzakhala m’Minda (yamtendere) ali olemekezedwa.
فَمَالِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قِبَلَكَ مُهۡطِعِينَ
Open ayah 70:36Kodi kuli chiyani kwa amene akana (chikhulupiliro) akuthamangira kwa iwe (maso ali pamtunda)?
عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ عِزِينَ
Open ayah 70:37Atakuzungulira ena chakumanja ena chakumanzere.
أَيَطۡمَعُ كُلُّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ أَن يُدۡخَلَ جَنَّةَ نَعِيمٖ
Open ayah 70:38Kodi akulakalaka aliyense mwa iwo kuti akalowetsedwe ku Munda wamtendere?
كَلَّآۖ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّمَّا يَعۡلَمُونَ
Open ayah 70:39Asiye (kukhumba kwawo kokalowa ku Munda wamtendere)! Ndithu Ife tidawalenga kuchokera m’zimene akudziwa (madzi opanda pake).
فَلَآ أُقۡسِمُ بِرَبِّ ٱلۡمَشَٰرِقِ وَٱلۡمَغَٰرِبِ إِنَّا لَقَٰدِرُونَ
Open ayah 70:40Ndikulumbilira Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe konse ndithu Ndife Wokhoza.
عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ خَيۡرٗا مِّنۡهُمۡ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ
Open ayah 70:41Kuwasintha ndi kudzetsa abwino kuposa iwo; Ife palibe (chilichonse) chotipambana.
فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ
Open ayah 70:42Asiye azingolankhula zopanda pake ndi kumangosewera mpaka adzakumane ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa.
يَوۡمَ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ سِرَاعٗا كَأَنَّهُمۡ إِلَىٰ نُصُبٖ يُوفِضُونَ
Open ayah 70:43Tsiku limene adzatuluke m’manda uku akuthamanga (kudza kwa woitana) ngati kuti akuthamangira kumafano awo (amene adali kuwapembedza).
خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۚ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلَّذِي كَانُواْ يُوعَدُونَ
Open ayah 70:44Maso awo ali zyoli, (osatha kuwakweza); kuyaluka kutawaphimba! Limenelo ndilo tsiku lomwe adali kulonjezedwa (pomwe adali padziko lapansi.