الحاقة
Al-Haaqqa
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
ٱلۡحَآقَّةُ
Open ayah 69:1Chakudza cha choonadi (chomwe ndi Qiyâma).
مَا ٱلۡحَآقَّةُ
Open ayah 69:2Kodi chakudza cha choonadi nchiyani?
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡحَآقَّةُ
Open ayah 69:3Nanga nchiyani chikudziwitse za chakudza cha choonadicho?
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ وَعَادُۢ بِٱلۡقَارِعَةِ
Open ayah 69:4Asamudu ndi Âdi adatsutsa zakudza kwa Qiyâma (yomwe idzadzidzimutsa zolengedwa mwamphamvu ndi zoopsa zake).
فَأَمَّا ثَمُودُ فَأُهۡلِكُواْ بِٱلطَّاغِيَةِ
Open ayah 69:5Tsono Asamudu adaonongedwa ndi phokoso lopyola muyeso, (lamphamvu kwambiri).
وَأَمَّا عَادٞ فَأُهۡلِكُواْ بِرِيحٖ صَرۡصَرٍ عَاتِيَةٖ
Open ayah 69:6Ndipo Âdi adaonongedwa ndi chimphepo cha mkuntho, chozizira, champhamvu kwambiri.
سَخَّرَهَا عَلَيۡهِمۡ سَبۡعَ لَيَالٖ وَثَمَٰنِيَةَ أَيَّامٍ حُسُومٗاۖ فَتَرَى ٱلۡقَوۡمَ فِيهَا صَرۡعَىٰ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٍ خَاوِيَةٖ
Open ayah 69:7Allah adachitumiza kwa iwo pa usiku usanu ndi uwiri ndi masana asanu ndi atatu mosadukiza; kotero ukadawaona ali lambalamba mmenemo ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza yopanda kanthu m’kati mwake.
فَهَلۡ تَرَىٰ لَهُم مِّنۢ بَاقِيَةٖ
Open ayah 69:8Kodi nanga ukumuona wotsala mwa iwo?
وَجَآءَ فِرۡعَوۡنُ وَمَن قَبۡلَهُۥ وَٱلۡمُؤۡتَفِكَٰتُ بِٱلۡخَاطِئَةِ
Open ayah 69:9Ndipo Firiaun ndi amene adalipo iye asadabadwe, ndi khamu la anthu amidzi yotembenuzidwa (anthu a Luti) adadza ndi machimo (akulu).
فَعَصَوۡاْ رَسُولَ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَهُمۡ أَخۡذَةٗ رَّابِيَةً
Open ayah 69:10Ndipo (yense wa iwowa) adanyoza Mtumiki wa Mbuye wawo; choncho adawalanga chilango chopitilira muyeso.
إِنَّا لَمَّا طَغَا ٱلۡمَآءُ حَمَلۡنَٰكُمۡ فِي ٱلۡجَارِيَةِ
Open ayah 69:11Ndithu pamene madzi adasefukira mopyola muyeso (mpaka kumeza mapiri nthawi ya chigumula cha Nowa) Ife tidakukwezani mchombo choyandama ndi kuyenda.
لِنَجۡعَلَهَا لَكُمۡ تَذۡكِرَةٗ وَتَعِيَهَآ أُذُنٞ وَٰعِيَةٞ
Open ayah 69:12Kuti tichichite (chochitikacho chomwe okhulupirira adapulumuka nacho; osakhulupirira adaonongeka nacho) kukhala lingaliro ndi phunziro kwa inu, ndikuti lisunge (nkhaniyi) khutu losunga.
فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ نَفۡخَةٞ وَٰحِدَةٞ
Open ayah 69:13Choncho likadzaimbidwa lipenga, kuimba kumodzi kokha (zamoyo zonse zidzafa).
وَحُمِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ فَدُكَّتَا دَكَّةٗ وَٰحِدَةٗ
Open ayah 69:14Ndipo nthaka ndi mapiri nkuchotsedwa m’malo mwake ndi kuphwanyidwa kamodzi nkamodzi.
فَيَوۡمَئِذٖ وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ
Open ayah 69:15Chomwecho tsiku limenelo, chochitika chidzachitika (imene ili Qiyâma).
وَٱنشَقَّتِ ٱلسَّمَآءُ فَهِيَ يَوۡمَئِذٖ وَاهِيَةٞ
Open ayah 69:16Ndipo thambo lidzasweka choncho ilo tsiku limenelo lidzakhala lofooka (pamene lidali lolimba).
وَٱلۡمَلَكُ عَلَىٰٓ أَرۡجَآئِهَاۚ وَيَحۡمِلُ عَرۡشَ رَبِّكَ فَوۡقَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ ثَمَٰنِيَةٞ
Open ayah 69:17Ndipo angelo adzakhala m’mphepete mwake, ndipo pamwamba pawo tsiku limenero (angelo) asanu ndi atatu adzasenza Arsh (Mpando wachifumu) ya Mbuye wako.
يَوۡمَئِذٖ تُعۡرَضُونَ لَا تَخۡفَىٰ مِنكُمۡ خَافِيَةٞ
Open ayah 69:18Tsiku limenelo mudzabweretsedwa ku chiweruzo; sichidzabisika chilichonse chobisika mwa inu.
فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَيَقُولُ هَآؤُمُ ٱقۡرَءُواْ كِتَٰبِيَهۡ
Open ayah 69:19Tsono amene adzapatsidwa kaundula wake chakudzanja lakumanja kwake adzanena (mokondwa kwa amene ali m’phepete mwake): “Tengani! Werengani kaundula wanga!”
إِنِّي ظَنَنتُ أَنِّي مُلَٰقٍ حِسَابِيَهۡ
Open ayah 69:20“Ndithudi ine ndidatsimikiza (pa dziko lapansi) kuti ndidzakumana ndi chiwerengero changa.”
فَهُوَ فِي عِيشَةٖ رَّاضِيَةٖ
Open ayah 69:21Choncho, iye adzakhala m’moyo wosangalatsa.
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ
Open ayah 69:22M’munda wapamwamba.
قُطُوفُهَا دَانِيَةٞ
Open ayah 69:23Zipatso zake zoyandikira pansi (zosavuta kuzithyola).
كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَآ أَسۡلَفۡتُمۡ فِي ٱلۡأَيَّامِ ٱلۡخَالِيَةِ
Open ayah 69:24(Adzawauza kuti:) “Idyani, ndipo imwani mosangalala pa zimene mudatsogoza mmasiku aja adapita (a pa dziko lapansi).”
وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِشِمَالِهِۦ فَيَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي لَمۡ أُوتَ كِتَٰبِيَهۡ
Open ayah 69:25Ndipo amene adzapatsidwe kaundula wake kudzanja lake lamanzere, adzanena (modandaula): “Kalanga ine! Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa kaundula wangayu!”
وَلَمۡ أَدۡرِ مَا حِسَابِيَهۡ
Open ayah 69:26“Nkusadziwa chiwerengero changa!”
يَٰلَيۡتَهَا كَانَتِ ٱلۡقَاضِيَةَ
Open ayah 69:27“Ha! imfa ija ikadandimaliziratu (ndi kundilekanitsa ine ndi zimenezi).”
مَآ أَغۡنَىٰ عَنِّي مَالِيَهۡۜ
Open ayah 69:28“Chuma changa sichidandithandize!”
هَلَكَ عَنِّي سُلۡطَٰنِيَهۡ
Open ayah 69:29“Mphamvu zanga (ndi moyo wanga wathanzi) zandichokera!”
خُذُوهُ فَغُلُّوهُ
Open ayah 69:30(Kudzanenedwa kwa angelo oyang’anira Jahena): Mgwireni ndipo mnjateni (pomphatikiza manja ndi khosi)!
ثُمَّ ٱلۡجَحِيمَ صَلُّوهُ
Open ayah 69:31Kenako mponyeni ku Moto.
ثُمَّ فِي سِلۡسِلَةٖ ذَرۡعُهَا سَبۡعُونَ ذِرَاعٗا فَٱسۡلُكُوهُ
Open ayah 69:32Kenakonso mulowetseni mtcheni lotalika mikwamba makumi asanu ndi awiri!
إِنَّهُۥ كَانَ لَا يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 69:33Ndithudi, iye sadali kukhulupirira mwa Allah wamkulu.
وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ
Open ayah 69:34Sadalinso kulimbikitsa zodyetsa osauka.
فَلَيۡسَ لَهُ ٱلۡيَوۡمَ هَٰهُنَا حَمِيمٞ
Open ayah 69:35Basi, lero kuno alibe bwenzi (lomthandiza).
وَلَا طَعَامٌ إِلَّا مِنۡ غِسۡلِينٖ
Open ayah 69:36Ngakhale chakudya kupatula mafinya (a anthu a ku Moto).
لَّا يَأۡكُلُهُۥٓ إِلَّا ٱلۡخَٰطِـُٔونَ
Open ayah 69:37Zomwe palibe angazidye kupatula ochimwa (mwadala).
فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَا تُبۡصِرُونَ
Open ayah 69:38Choncho ndikulumbilira zimene mukuziona.
وَمَا لَا تُبۡصِرُونَ
Open ayah 69:39Ndi zimene simukuziona.
إِنَّهُۥ لَقَوۡلُ رَسُولٖ كَرِيمٖ
Open ayah 69:40Ndithudi iyi (Qur’an) ndiliwu la mthenga wolemekezeka (Jibril).
وَمَا هُوَ بِقَوۡلِ شَاعِرٖۚ قَلِيلٗا مَّا تُؤۡمِنُونَ
Open ayah 69:41Ndipo simawu a mlakatuli, ndi zochepa zimene mukuzikhulupirira.
وَلَا بِقَوۡلِ كَاهِنٖۚ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ
Open ayah 69:42Ndiponso simawu a mlosi, ndizochepa zimene mmakumbukira!
تَنزِيلٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 69:43(Ichi ndi) chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
وَلَوۡ تَقَوَّلَ عَلَيۡنَا بَعۡضَ ٱلۡأَقَاوِيلِ
Open ayah 69:44Ndipo (Mneneri) akadatipekera bodza linalake.
لَأَخَذۡنَا مِنۡهُ بِٱلۡيَمِينِ
Open ayah 69:45Tikadamgwira (mwamphamvu) ndimkono wamanja.
ثُمَّ لَقَطَعۡنَا مِنۡهُ ٱلۡوَتِينَ
Open ayah 69:46Ndipo tikadadula mwa iye mtsempha wa moyo (kotero kuti ndikuferatu nthawi yomweyo).
فَمَا مِنكُم مِّنۡ أَحَدٍ عَنۡهُ حَٰجِزِينَ
Open ayah 69:47Sipakadapezeka aliyense mwa inu womteteza (kuchilango Chathu).
وَإِنَّهُۥ لَتَذۡكِرَةٞ لِّلۡمُتَّقِينَ
Open ayah 69:48Ndithu iyi (Qur’an) ndi phunziro labwino kwa owopa (Allah.)
وَإِنَّا لَنَعۡلَمُ أَنَّ مِنكُم مُّكَذِّبِينَ
Open ayah 69:49Ndithu Ife, tikudziwa kuti ena mwa inu ndiotsutsa (Qur’an).
وَإِنَّهُۥ لَحَسۡرَةٌ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Open ayah 69:50Ndipo ndithu iyi (Qur’an) idzakhala chowadandaulitsa (chachikulu) osakhulupirira (pamene adzaona chilango chawo ndi mtendere wa okhulupirira).
وَإِنَّهُۥ لَحَقُّ ٱلۡيَقِينِ
Open ayah 69:51Ndithu iyoyi ndichoonadi Chotsimikizika; (mulibe chikaiko),
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Open ayah 69:52Basi, lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu (pitiriza kutamanda dzina Lake).