السجدة
As-Sajda
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
الٓمٓ
Open ayah 32:1Alif-Lâm-Mîm.
تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ لَا رَيۡبَ فِيهِ مِن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Open ayah 32:2Chivumbulutso cha buku (la Qur’an) chilibe chikaiko mkati mwake chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۚ بَلۡ هُوَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أَتَىٰهُم مِّن نَّذِيرٖ مِّن قَبۡلِكَ لَعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ
Open ayah 32:3Kapena akunena kuti: “Walipeka yekha (bukulo)?” Iyayi, ichi nchoona chimene chachokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu ndi chimenechi, amene sadawadzere mchenjezi iwe usadadze. Kuti aongoke (ndi kutsatira njira yolungama).
ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ مَا لَكُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَلِيّٖ وَلَا شَفِيعٍۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ
Open ayah 32:4Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu); (kukhazikika kolingana ndi ulemelero Wake, kumene Iye Mwini wake akukudziwa). Inu mulibe mtetezi ngakhale muomboli kupatula Iye. Nanga kodi bwanji simulingalira?[1]
- M’ndime iyi Allah akutiuza kuti adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi. Komatu nthawi ya masiku amenewa, palibe amene akudziwa tsatanetsatane wake koma Allah Yekha. Choncho tisaganizire kuti masikuwo adali olingana ndi masiku a moyo uno wadziko lapansi.
يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يَعۡرُجُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥٓ أَلۡفَ سَنَةٖ مِّمَّا تَعُدُّونَ
Open ayah 32:5(Iye) akuyendetsa zinthu (zonse) kuchokera kumwamba kupita pansi. Kenako zidzakwera kubwerera kwa Iye, pa tsiku lolingana ndi zaka chikwi chimodzi (poyerekeza ndi zaka zadziko lapansi) mzomwe inu mumawerengera.
ذَٰلِكَ عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Open ayah 32:6Ameneyo (ndi Allah), Wodziwa zobisika ndi zoonekera; Mwini mphamvu zoposa Wachisoni chosatha.
ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقَهُۥۖ وَبَدَأَ خَلۡقَ ٱلۡإِنسَٰنِ مِن طِينٖ
Open ayah 32:7Yemwe adakonza bwino chilichonse (chomwe) adalenga. Ndipo adayambitsa chilengedwe cha munthu (Adam) kuchokera ku dongo.
ثُمَّ جَعَلَ نَسۡلَهُۥ مِن سُلَٰلَةٖ مِّن مَّآءٖ مَّهِينٖ
Open ayah 32:8Kenako adachita mbumba yake kuti ipangike kuchokera m’madzi enieni onyozeka.
ثُمَّ سَوَّىٰهُ وَنَفَخَ فِيهِ مِن رُّوحِهِۦۖ وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ
Open ayah 32:9Kenako adamkonza ndi kuuziramo mzimu Wake. Ndipo adakuikirani kumva, kupenya ndi mitima. Kuthokoza kwanu mpang’ono ndithu.
وَقَالُوٓاْ أَءِذَا ضَلَلۡنَا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَءِنَّا لَفِي خَلۡقٖ جَدِيدِۭۚ بَلۡ هُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ كَٰفِرُونَ
Open ayah 32:10Ndipo (otsutsa kuuka ku imfa) akunena: “Kodi tikadzatayika m’nthaka (ndi kusakanikirana ndi dothi), tidzakhalanso mkalengedwe katsopano?” (Iyayi), koma iwo sakhulupirira za kukumana ndi Mbuye wawo.
۞قُلۡ يَتَوَفَّىٰكُم مَّلَكُ ٱلۡمَوۡتِ ٱلَّذِي وُكِّلَ بِكُمۡ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ تُرۡجَعُونَ
Open ayah 32:11Nena: “Adzachotsa mizimu yanu Mngelo wa imfa yemwe wapatsidwa udindo umenewu pa inu. Kenako mudzabwerera kwa Mbuye wanu.”
وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلۡمُجۡرِمُونَ نَاكِسُواْ رُءُوسِهِمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ رَبَّنَآ أَبۡصَرۡنَا وَسَمِعۡنَا فَٱرۡجِعۡنَا نَعۡمَلۡ صَٰلِحًا إِنَّا مُوقِنُونَ
Open ayah 32:12Ndipo ukadawaona oipa atazolikitsa mitu yawo kwa Mbuye wawo (uku akunena): “E Mbuye wathu! Taona, ndipo tamva. Choncho tibwezeni tikachita ntchito zabwino. Ndithu tsopano tatsimikiza (kukhulupirira).”
وَلَوۡ شِئۡنَا لَأٓتَيۡنَا كُلَّ نَفۡسٍ هُدَىٰهَا وَلَٰكِنۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ مِنِّي لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِينَ
Open ayah 32:13Ndipo tikadafuna, tikadaupatsa mzimu ulionse chiongoko chake (moukakamiza monga momwe tidawachitira angelo, koma mzimu udapatsidwa mphamvu ndi ufulu wodzisankhira chimene ufuna; chabwino kapena choipa). Koma mawu atsimikizika ochokera kwa Ine: “Ndithu ndizadzazitsa Jahannam ziwanda ndi anthu; onse pamodzi (amene ali oipa).”
فَذُوقُواْ بِمَا نَسِيتُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَآ إِنَّا نَسِينَٰكُمۡۖ وَذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Open ayah 32:14“Choncho, lawani chifukwa cha kuyiwala (kusalabadila) kwanu kukumana ndi tsiku lanu ili. Ifenso tikusiyani (ku chilango monga ngati takuiwalani). Tero lawani chilango chamuyaya, chifukwa cha zomwe munkachita.”
إِنَّمَا يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِهَا خَرُّواْۤ سُجَّدٗاۤ وَسَبَّحُواْ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَهُمۡ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ۩
Open ayah 32:15Ndithu amene akukhulupirira Ayah Zathu, ndiamene akuti pamene akukumbutsidwa ndi Ayazo, amagwetsa nkhope zawo pansi (kusujudu) ndi kulemekeza Mbuye wawo pamodzi ndi kumthokoza. Ndipo iwo sadzitukumula.
تَتَجَافَىٰ جُنُوبُهُمۡ عَنِ ٱلۡمَضَاجِعِ يَدۡعُونَ رَبَّهُمۡ خَوۡفٗا وَطَمَعٗا وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Open ayah 32:16Nthiti zawo zimalekana ndi malo ogona (usiku), uku akumpempha Mbuye wawo, moopa ndi mwachiyembekezo. Ndipo amapereka (Zakaat ndi sadaka) mzimene tawapatsa.
فَلَا تَعۡلَمُ نَفۡسٞ مَّآ أُخۡفِيَ لَهُم مِّن قُرَّةِ أَعۡيُنٖ جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Open ayah 32:17Mzimu uliwonse sudziwa zimene aubisira zotonthoza diso (zosangalatsa moyo ku Munda wa mtendere) monga mphoto pa zimene unkachita.
أَفَمَن كَانَ مُؤۡمِنٗا كَمَن كَانَ فَاسِقٗاۚ لَّا يَسۡتَوُۥنَ
Open ayah 32:18Kodi yemwe ali okhulupirira angafanane ndi wotuluka m’chilamulo cha Allah? Sangafanane.
أَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلۡمَأۡوَىٰ نُزُلَۢا بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Open ayah 32:19Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzalandira Minda yokhalamo yokongola, monga phwando lawo pa zimene ankachita.
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ فَسَقُواْ فَمَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُۖ كُلَّمَآ أَرَادُوٓاْ أَن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَآ أُعِيدُواْ فِيهَا وَقِيلَ لَهُمۡ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلنَّارِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
Open ayah 32:20Koma kwa amene adachita zoipa potuluka m’chilamulo cha Allah, malo awo ndi ku Moto. Nthawi iliyonse akafuna kutulukamo, azikabwezedwamo ndipo azidzauzidwa: “Lawani chilango cha Moto, chomwe munkachitsutsa.”
وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَدۡنَىٰ دُونَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَكۡبَرِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Open ayah 32:21Ndipo ndithudi, tiwalawitsa chilango chocheperapo (pa dziko lapansi) chisanafike chilango chachikulu (cha tsiku lachimaliziro), kuti atembenuke, (alape).
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ ثُمَّ أَعۡرَضَ عَنۡهَآۚ إِنَّا مِنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ مُنتَقِمُونَ
Open ayah 32:22Kodi ndani wachinyengo kwambiri, woposa yemwe akukumbutsidwa Ayah za Mbuye wake, kenako nkuzikana? Ndithu Ife, tidzawabwezera zoipa anthu oipa.
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَلَا تَكُن فِي مِرۡيَةٖ مِّن لِّقَآئِهِۦۖ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدٗى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Open ayah 32:23Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Choncho usakhale ndi chikaiko pa zakukumana Naye (Allah). Ndipo tidalichita (bukulo) kukhala chiongoko cha ana a Israyeli.
وَجَعَلۡنَا مِنۡهُمۡ أَئِمَّةٗ يَهۡدُونَ بِأَمۡرِنَا لَمَّا صَبَرُواْۖ وَكَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يُوقِنُونَ
Open ayah 32:24Ndipo ena mwa iwo tidawachita kukhala atsogoleri oongola (anthu) mwa lamulo lathu, pamene adapirira; ndipo adali kuvomereza motsimikiza Ayah Zathu.
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَفۡصِلُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Open ayah 32:25Ndithudi Mbuye wako ndi Yemwe adzaweruze pakati pawo tsiku la Qiyâma pazimene amatsutsana.
أَوَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍۚ أَفَلَا يَسۡمَعُونَ
Open ayah 32:26Kodi sizidadziwike kwa iwo kuti ndimibadwo ingati imene tidaiononga patsogolo pawo; (chikhalirecho iwo) akudutsa mokhala mwawo? Ndithu m’zimenezo, muli zizindikiro, kodi sakumva?
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا نَسُوقُ ٱلۡمَآءَ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلۡجُرُزِ فَنُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعٗا تَأۡكُلُ مِنۡهُ أَنۡعَٰمُهُمۡ وَأَنفُسُهُمۡۚ أَفَلَا يُبۡصِرُونَ
Open ayah 32:27Kodi sakuona kuti timapereka madzi ku nthaka youma; ndipo ndi madziwo tikumeretsa mrnera umene ziweto zawo zimadya ndi iwo omwe; kodi sakupenya?
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡفَتۡحُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Open ayah 32:28Ndipo akunena: “Kulamulidwa kumeneku (kwa tsiku la chimaliziro) kudzachitika liti, ngati mukunenadi zoona?”
قُلۡ يَوۡمَ ٱلۡفَتۡحِ لَا يَنفَعُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِيمَٰنُهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ
Open ayah 32:29Nena: “Tsiku la chiweruzirolo, amene sadakhulupirire, chikhulupiriro chawo sichidzawathandiza. Ndipo sadzapatsidwa nthawi yoyembekezera (kuti mizimu yawo isachoke ayambe akhulupirira kaye, mngero wa imfa akadzawadzera).”
فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَٱنتَظِرۡ إِنَّهُم مُّنتَظِرُونَ
Open ayah 32:30Choncho apatuke; ndipo yembekezera (zimene Allah wakulonjeza). Ndithu nawonso akuyembekezera (zimene Allah wawalonjeza).