الفجر
Al-Fajr
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلۡفَجۡرِ
Open ayah 89:1Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa).
وَلَيَالٍ عَشۡرٖ
Open ayah 89:2Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah).[1]
- Tanthauzo la Ayah iyi ndi masiku khumi olemekezeka omwe ali mkhumi loyamba la mwezi wa Thul-Hijjah umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya Chisilamu. Amenewa ndi masiku olemekezeka kuposa masiku onse ngakhale masiku a Ramadan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi omaliza a mwezi wa Ramadan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa mapemphero m’masiku amenewa.
وَٱلشَّفۡعِ وَٱلۡوَتۡرِ
Open ayah 89:3Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika).[1]
- Shafi ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Allah pamenepa ndi kuzilumbilira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri.
وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَسۡرِ
Open ayah 89:4Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa).
هَلۡ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٞ لِّذِي حِجۡرٍ
Open ayah 89:5Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru?
أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ
Open ayah 89:6Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd).
إِرَمَ ذَاتِ ٱلۡعِمَادِ
Open ayah 89:7Aku Irama; ataliatali ngati zipilala.[1]
- (Ndime 7-9) Âdi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti: “Ndani wamphamvu kuposa ife!” Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia.
ٱلَّتِي لَمۡ يُخۡلَقۡ مِثۡلُهَا فِي ٱلۡبِلَٰدِ
Open ayah 89:8Omwe onga iwo sadalengedwe m’maiko ena?
وَثَمُودَ ٱلَّذِينَ جَابُواْ ٱلصَّخۡرَ بِٱلۡوَادِ
Open ayah 89:9Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)?
وَفِرۡعَوۡنَ ذِي ٱلۡأَوۡتَادِ
Open ayah 89:10Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)?
ٱلَّذِينَ طَغَوۡاْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ
Open ayah 89:11Amene adaipitsa m’maiko mopyola malire?
فَأَكۡثَرُواْ فِيهَا ٱلۡفَسَادَ
Open ayah 89:12Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga).[1]
- Mzinthu zoipa zimene Farawo adachita, ndi kudzitcha kuti iye ndi mulungu, kupha ana achimuna popanda chilungamo, ndi kuwazunza Aisraeli.
فَصَبَّ عَلَيۡهِمۡ رَبُّكَ سَوۡطَ عَذَابٍ
Open ayah 89:13Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa).
إِنَّ رَبَّكَ لَبِٱلۡمِرۡصَادِ
Open ayah 89:14Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire).[1]
- Apa ndikuti Allah akuwaona anthu Ake nthawi ili yonse. Palibe chimene iwo achita popanda Iye kuchiona ndi kuchilemba.
فَأَمَّا ٱلۡإِنسَٰنُ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ رَبُّهُۥ فَأَكۡرَمَهُۥ وَنَعَّمَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَكۡرَمَنِ
Open ayah 89:15Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine).
وَأَمَّآ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ فَقَدَرَ عَلَيۡهِ رِزۡقَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَهَٰنَنِ
Open ayah 89:16Koma akamuyesa mayeso ndi kumchepetsera rizq lake, (chuma) amanena (motaya rntima): Mbuye wanga wandinyoza!
كَلَّاۖ بَل لَّا تُكۡرِمُونَ ٱلۡيَتِيمَ
Open ayah 89:17Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye!
وَلَا تَحَٰٓضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ
Open ayah 89:18Ndipo simulimbikitsana za kudyetsa osauka,
وَتَأۡكُلُونَ ٱلتُّرَاثَ أَكۡلٗا لَّمّٗا
Open ayah 89:19Ndipo mukudya chuma cha masiye; kudya kosusuka.[1]
- Arabu asadalowe m’Chisilamu akazi sadali kugawiridwa chuma cha masiye kudzanso ana aang’onoang’ono a masiye sadali kuchiona chumacho.
وَتُحِبُّونَ ٱلۡمَالَ حُبّٗا جَمّٗا
Open ayah 89:20Ndiponso mukukonda chuma; kukonda kopyola muyeso.
كَلَّآۖ إِذَا دُكَّتِ ٱلۡأَرۡضُ دَكّٗا دَكّٗا
Open ayah 89:21Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza).
وَجَآءَ رَبُّكَ وَٱلۡمَلَكُ صَفّٗا صَفّٗا
Open ayah 89:22Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere.
وَجِاْيٓءَ يَوۡمَئِذِۭ بِجَهَنَّمَۚ يَوۡمَئِذٖ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ وَأَنَّىٰ لَهُ ٱلذِّكۡرَىٰ
Open ayah 89:23Ndi kubweretsedwa Jahannam pa tsikulo, basi tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzamthandiza chiyani?
يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي قَدَّمۡتُ لِحَيَاتِي
Open ayah 89:24Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno!
فَيَوۡمَئِذٖ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُۥٓ أَحَدٞ
Open ayah 89:25Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire.[1]
- (Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha Allah chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe akafiri adzanjatidwe.
وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُۥٓ أَحَدٞ
Open ayah 89:26Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah).
يَٰٓأَيَّتُهَا ٱلنَّفۡسُ ٱلۡمُطۡمَئِنَّةُ
Open ayah 89:27E iwe mzimu wokhazikika (ndi choona)![1]
- “Mzimu wokhazikika” ndi mzimu wa munthu wokhulupilira amene akuchita zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu umene udzakhale wodekha pa tsiku lachimaliziro chifukwa chakuti pa tsikulo sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula.
ٱرۡجِعِيٓ إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةٗ مَّرۡضِيَّةٗ
Open ayah 89:28Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza).[1]
- Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene udzalandira kwa Allah tsiku limenelo ndipo naye Allah adzakondwera nawo.
فَٱدۡخُلِي فِي عِبَٰدِي
Open ayah 89:29Lowa mgulu la akapolo anga abwino.
وَٱدۡخُلِي جَنَّتِي
Open ayah 89:30Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya).