البلد

Al-Balad

The City · Surah 90 · Ayahs: 20 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. لَآ أُقۡسِمُ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ

    Open ayah 90:1

    Ndikulumbilira mzinda uwu (wa Makka).

  2. وَأَنتَ حِلُّۢ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ

    Open ayah 90:2

    Ndipo iwe udzatsikira mu mzindawu mwa ufulu (ndi kuuonjezera ulemelero).

  3. وَوَالِدٖ وَمَا وَلَدَ

    Open ayah 90:3

    Ndiponso ndikulumbilira chobereka ndi choberekedwa, (kudzera mwa iwo mtundu wa anthu udasungidwa).

  4. لَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ فِي كَبَدٍ

    Open ayah 90:4

    Ndithudi tamulenga munthu mmavuto (kuyambira chiyambi chake mpaka malekezero a moyo wake).[1]

    1. Munthu ali ndi mavuto ambiri amene nyama zina zilibe: chakudya amachipeza movutikira, ndipo kudya kwa iye nkofunikira pa moyo wake, chovala amachipeza movutikira pomwe iye ndiwoyenera kuvala. Sangathe kupilira ndi kutentha kapena kuzizira. Sangathenso kudziteteza popanda chida. Ndipo pamwamba pa izi, Allah wamukakamiza zinthu zambiri ndi kumuletsanso zinthu zambiri. Ndipo chilichonse chimene iye achita chikulembedwa. Pa tsiku lachimaliziro adzawerengedwa chilichonse chimene adachichita; chachikulu kapena chaching’ono.
  5. أَيَحۡسَبُ أَن لَّن يَقۡدِرَ عَلَيۡهِ أَحَدٞ

    Open ayah 90:5

    Kodi (munthu wolengedwa ndi mavutoyu) akuganiza kuti palibe amene angamuthe? [1]

    1. Tanthauzo lake apa nkuti munthu akuganiza kuti palibe aliyense amene angamuweruze pa zolakwa zake.
  6. يَقُولُ أَهۡلَكۡتُ مَالٗا لُّبَدًا

    Open ayah 90:6

    Akunena (monyadira kuti): “Ndaononga chuma chambiri (chifukwa choletsa Chisilamu kufala).”[1]

    1. (Ndime 6-7) Mawu awa akunenedwa kwa okanira omwe adali kupereka chuma chawo pomenyana ndi Usilamu kapena kufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Kenako adali kudzitama chifukwa chopereka chuma chambiri pa njirayo. Izi zikumukhudza aliyense amene akufuna kuti Chisilamu chionongeke. Ndipo iwo amaganiza kuti Allah sakudziwa za maganizo awo oipa.
  7. أَيَحۡسَبُ أَن لَّمۡ يَرَهُۥٓ أَحَدٌ

    Open ayah 90:7

    Kodi akuganiza kuti palibe akumuona?

  8. أَلَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ عَيۡنَيۡنِ

    Open ayah 90:8

    Kodi sitidampangire maso awiri (amene akuyang’anira)?

  9. وَلِسَانٗا وَشَفَتَيۡنِ

    Open ayah 90:9

    Ndilirime ndi milomo iwiri (zimene akulankhulira)?

  10. وَهَدَيۡنَٰهُ ٱلنَّجۡدَيۡنِ 

    Open ayah 90:10

    Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna).

  11. فَلَا ٱقۡتَحَمَ ٱلۡعَقَبَةَ

    Open ayah 90:11

    Kodi walikwera phiri lovutalo (lomwe lingakamfikitse ku Jannah)?[1]

    1. Tanthauzo lake ndikuti bwanji munthu sathokoza chifundo chimenechi (chopatsidwa maso ndi pakamwa) pogwiritsa ntchito chuma chake pa zinthu zabwino zimene Allah wazitchula m’ma Ayah akubwerawa? Ndipo tanthauzo la “kukwera phiri lovuta’’ ndiko kupereka chuma panjira ya Allah chimene chili ndinthu chovuta kwa anthu ambiri ndipo chimafanana ndikukwera phiri losongoka.
  12. وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡعَقَبَةُ

    Open ayah 90:12

    Nanga nchiyani chakudziwitsa za kukwera phiri lovutalo?

  13. فَكُّ رَقَبَةٍ

    Open ayah 90:13

    (Kutero ndiko) kupereka ufulu kwa kapolo,

  14. أَوۡ إِطۡعَٰمٞ فِي يَوۡمٖ ذِي مَسۡغَبَةٖ

    Open ayah 90:14

    Kapena kuwadyetsa (osowa) pa tsiku la njala,

  15. يَتِيمٗا ذَا مَقۡرَبَةٍ

    Open ayah 90:15

    Amasiye achibale,

  16. أَوۡ مِسۡكِينٗا ذَا مَتۡرَبَةٖ

    Open ayah 90:16

    Kapena wosauka wa fumbi lokhalokha (chifukwa cha kuvutika kwambiri),

  17. ثُمَّ كَانَ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلصَّبۡرِ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلۡمَرۡحَمَةِ

    Open ayah 90:17

    Komanso nakhala mmodzi mwa okhulupirira ndikumalangizana za kupirira, ndi kumalangizananso za chifundo.

  18. أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ

    Open ayah 90:18

    Otero ndiwo (anthu abwino) a ku dzanja lamanja.

  19. وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا هُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ

    Open ayah 90:19

    Koma amene sanakhulupirire Ayah Zathu, ndi anthu a kudzanja lamanzere (oipa).

  20. عَلَيۡهِمۡ نَارٞ مُّؤۡصَدَةُۢ 

    Open ayah 90:20

    Moto wozungulira mbali zonse udzakhala pa iwo (ndikuwatsekera makomo).