الشمس
Ash-Shams
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلشَّمۡسِ وَضُحَىٰهَا
Open ayah 91:1Ndikulumbilira dzuwa ndi dangalira lake.
وَٱلۡقَمَرِ إِذَا تَلَىٰهَا
Open ayah 91:2Ndi mwezi pamene ukulitsatira (dzuwalo ndikulowa mmalo mwake powalitsa dziko dzuwalo litalowa).
وَٱلنَّهَارِ إِذَا جَلَّىٰهَا
Open ayah 91:3Ndi usana pamene ukulisonyeza poyera (kuti lisaphimbidwe).
وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَغۡشَىٰهَا
Open ayah 91:4Ndi usiku pamene ukuliphimba.
وَٱلسَّمَآءِ وَمَا بَنَىٰهَا
Open ayah 91:5Ndi thambo ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu) Yemwe adalimanga ndi kulitukula (mwaluso).
وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا طَحَىٰهَا
Open ayah 91:6Ndi nthaka ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu), Yemwe adaiyala (mbali zonse ndi kuichita kukhala ngati choyala).
وَنَفۡسٖ وَمَا سَوَّىٰهَا
Open ayah 91:7Ndi mzimu ndi Yemwe adawulinganiza (powupatsa mphamvu).
فَأَلۡهَمَهَا فُجُورَهَا وَتَقۡوَىٰهَا
Open ayah 91:8Ndipo adaudziwitsa zoipa zake ndi zabwino zake; (ndi kuwupatsa ufulu ndi mphamvu zochitira zimene ukufuna).
قَدۡ أَفۡلَحَ مَن زَكَّىٰهَا
Open ayah 91:9Ndithu wapambana amene wauyeretsa.[1]
- Kuyeretsa mzimu ndiko kuukongoletsa ndi maphunziro ndi ntchito zabwino. Zimenezi ndizo zimamkwanitsa munthu kuti atchulidwe munthu. Ndipo zimenezi ndizo zingapereke ulemelero kwa munthu pa dziko mpaka pa tsiku lachimaliziro.
وَقَدۡ خَابَ مَن دَسَّىٰهَا
Open ayah 91:10Ndipo ndithu wataika amene wauononga.[1]
- Kuwuononga mzimu ndiko kuuchitira mphwayi; kungoulekelera ndikumautsatira pa zimene ufuna mpaka kulowa mu uve ndi m’machimo a umbuli ndipo ndi kuonongeka pa dziko lino mpaka pa tsiku lachimaliziro.
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِطَغۡوَىٰهَآ
Open ayah 91:11Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo.[1]
- (Ndime 11-15) Asamudu atchulidwa m’surat AL-FAJR. Anthu awa adamukana Mtumiki wawo, Mtumiki Swalih (a.s); adamuuza kuti ngati afuna amukhulupirire, atulutse ngamira kuchokera mthanthwe, apo ndipo adzamukhulupilira kuti ndi Mneneri. Swalih adampempha Allah, ndipo lidasweka thanthwe lija ndikutulukamo ngamira monga momwe adafunira anthu aja. Koma sadamukhulupirirebe. Mneneri Swalih (a.s) adawauza kuti: “Chenjerani ndi ngamira ya Allah iyi, musaikhudze ndi choipa chilichonse.” Ndipo adawakakamiza kuti pa tsiku limene ngamira ija ikumwa madzi, iwo asatunge madzi. Ndiponso pa tsiku limene iwo akutunga madzi ngamira siidzamwa madzi. Koma adamkanira. Ndipo m’modzi wa iwo amene adali wamphulupulu adaipha ngamira ija. Allah nthawi yomweyo adawatsitsira chilango chifukwa cha machimo awo, chomwe chidawakwanira onse kuyambira uja wopha ngamira ndi ena onse.
إِذِ ٱنۢبَعَثَ أَشۡقَىٰهَا
Open ayah 91:12Pamene woipitsitsa wawo adadzipereka (kupha ngamira yozizwitsa).
فَقَالَ لَهُمۡ رَسُولُ ٱللَّهِ نَاقَةَ ٱللَّهِ وَسُقۡيَٰهَا
Open ayah 91:13Pamenepo Mneneri wa Allah (Swaleh) adawauza: “Isiyeni ngamira ya Allah (idye mdziko la Allah). Musailetse kumwa madzi (pa tsiku lake).”
فَكَذَّبُوهُ فَعَقَرُوهَا فَدَمۡدَمَ عَلَيۡهِمۡ رَبُّهُم بِذَنۢبِهِمۡ فَسَوَّىٰهَا
Open ayah 91:14Koma adamutsutsa ndikuipha; kwa chifukwa chimenecho Mbuye wawo (Allah) adawaononga chifukwa cha tchimo lawo; adangowafafaniza (onse mnthaka).
وَلَا يَخَافُ عُقۡبَٰهَا
Open ayah 91:15Iye saopa zotsatira za chilangochi (chifukwa amenewa ndi malipiro a chilungamo pa zomwe adachita).