الليل
Al-Lail
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَغۡشَىٰ
Open ayah 92:1Ndikulumbilira usiku pamene ukuphimba (chilichonse).
وَٱلنَّهَارِ إِذَا تَجَلَّىٰ
Open ayah 92:2Ndi usana pamene kukuyera.
وَمَا خَلَقَ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ
Open ayah 92:3Ndiponso Yemwe adalenga chachimuna ndi chachikazi.
إِنَّ سَعۡيَكُمۡ لَشَتَّىٰ
Open ayah 92:4Ndithu zochita zanu nzosiyanasiyana.[1]
- Tanthauzo lake ndikuti mwa anthu alipo ena amene amachita zabwino ndipo ena amachita zoipa. Ena amagwira ntchito zothandiza pambuyo pa imfa pamodzi ndi kutumikira Allah. Ndipo pali ena omwe amangokhala otanganidwa ndi zadziko lapansi. Ena amachita zinthu zopindula pomwe ena satero.
فَأَمَّا مَنۡ أَعۡطَىٰ وَٱتَّقَىٰ
Open ayah 92:5Tsono yemwe akupereka (pa njira ya Allah) ndikumamuopa (Mbuye wake ndikupewa zoletsedwa),[1]
- Tanthauzo lake apa ndikupereka chuma ndi kudzipereka pa zauzimu. Ndiye kuti munthu agwiritsire ntchito chuma chake m’njira ya Allah ndiponso kwa anthu anzake. Ayeneranso kudzipereka iye mwini pa moyo wauzimu.
وَصَدَّقَ بِٱلۡحُسۡنَىٰ
Open ayah 92:6Ndikumavomereza zinthu zabwino; (komwe kuli kukhulupirira Allah mwanzeru),[1]
- Tanthauzo la “Kuvomereza zinthu zabwino” ndiko kugwirizana nazo zimene Allah walamula, chifukwa chakuti Iye amalamula zinthu zabwino zokhazokha ndikuletsa zoipa.
فَسَنُيَسِّرُهُۥ لِلۡيُسۡرَىٰ
Open ayah 92:7Choncho timufewetsera njira yompititsa ku zabwino.[1]
- Tanthauzo la Ayah imeneyi ndikuti: Timufewetsera njira yochitira zinthu zabwino mpaka kufikira kuti akapanda kuchita chinthu chabwino sapeza mtendere mu mtima mwake.
وَأَمَّا مَنۢ بَخِلَ وَٱسۡتَغۡنَىٰ
Open ayah 92:8Koma uyo achite umbombo ndikuganiza za kuti iye payekha ngokwana;
وَكَذَّبَ بِٱلۡحُسۡنَىٰ
Open ayah 92:9Ndi kumatsutsa zinthu zabwino,
فَسَنُيَسِّرُهُۥ لِلۡعُسۡرَىٰ
Open ayah 92:10Choncho timufewetsera njira yompititsa ku mavuto (a muyaya).
وَمَا يُغۡنِي عَنۡهُ مَالُهُۥٓ إِذَا تَرَدَّىٰٓ
Open ayah 92:11Ndipo chuma chake sichidzamthandiza (chilichonse) akadzagwera ku Moto.
إِنَّ عَلَيۡنَا لَلۡهُدَىٰ
Open ayah 92:12Ndithu Ife ndi amene timawalongosolera anthu njira yabwino ndi njira yoipa.
وَإِنَّ لَنَا لَلۡأٓخِرَةَ وَٱلۡأُولَىٰ
Open ayah 92:13Ndipo ndithu moyo womaliza ndi moyo woyamba uli m’manja mwathu.
فَأَنذَرۡتُكُمۡ نَارٗا تَلَظَّىٰ
Open ayah 92:14Basi, ndikukuchenjezani za Moto woyaka mwa mphamvu.
لَا يَصۡلَىٰهَآ إِلَّا ٱلۡأَشۡقَى
Open ayah 92:15Sakaulowa koma (kafiri) woipitsitsa kwambiri.
ٱلَّذِي كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ
Open ayah 92:16Yemwe amatsutsa (choona) ndi kunyoza (zisonyezo za Allah).
وَسَيُجَنَّبُهَا ٱلۡأَتۡقَى
Open ayah 92:17Koma yemwe akuopa Allah kwambiri akatalikitsidwa ndi Moto.
ٱلَّذِي يُؤۡتِي مَالَهُۥ يَتَزَكَّىٰ
Open ayah 92:18Amene akupereka chuma chake ndi cholinga chodziyeretsa.
وَمَا لِأَحَدٍ عِندَهُۥ مِن نِّعۡمَةٖ تُجۡزَىٰٓ
Open ayah 92:19Ndipo palibe aliyense kwa iye, amene adamchitira za chifundo zomwe zikulipidwa.[1]
- (Ndime 19-20)Tanthauzo la ma Ayah awiriwa nkuti munthu uyu sakupereka chuma chake chifukwa chobwezera chifundo cha anthu, kapena kuti adzamubwezerenso iye chifundo, koma akupereka chifukwa chofuna chikondi cha Mbuye wake basi.
إِلَّا ٱبۡتِغَآءَ وَجۡهِ رَبِّهِ ٱلۡأَعۡلَىٰ
Open ayah 92:20Koma (akuchita zimenezi) kufuna chikondi cha Mbuye wake Wapamwambamwamba.
وَلَسَوۡفَ يَرۡضَىٰ
Open ayah 92:21Ndipo posachedwa adzasangalala.[1]
- Tanthauzo lake apa ndikuti Allah adzamukondweretsa ndi malipiro Ake abwino kufikira munthuyo adzakondwera. Ma Ayah, kuyambira 17 mpaka 21, adatsika chifukwa cha Sayyidina Abu Bakr (r.a) yemwe adali kupereka chuma chake powagula akapolo omwe adali kuzunzidwa ndi mabwana awo chifukwa cholowa Chisilamu, pambuyo pake amawapatsa ufulu. Ndipo m’modzi wa iwowa ndi Sayyidina Bilal (r.a) amene adali Muazzini wa Mneneri Muhammad (s.a.w). Chomwechonso Ayah zimenezi zikumkhudza aliyense amene akugwiritsa ntchito chuma chake mnjira yopulumutsira chipembedzo.