الضحى
Ad-Dhuhaa
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلضُّحَىٰ
Open ayah 93:1Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito),
وَٱلَّيۡلِ إِذَا سَجَىٰ
Open ayah 93:2Ndi usiku pamene ukuvindikira.
مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلَىٰ
Open ayah 93:3Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude.[1]
- M’masiku oyamba pa chiyambi cha Usilamu, padapita masiku angapo Mtumiki (s.a.w) osamutsikira chivumbulutso. Iye poona izi adali kukaika ndi kudandaula kwakukulu, nao okanira a pa Makka adali kumchita chipongwe. Adali kumunena kuti: “Kodi Mbuye wako wakusiya kapena wakukwiira?’’ Basi apa Allah akumutonthoza Mneneri Wake, pamodzi ndi kuwayankha okanira aja kuti: “Sadamusiye ndipo sadakwiye naye.”
وَلَلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ لَّكَ مِنَ ٱلۡأُولَىٰ
Open ayah 93:4Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu.
وَلَسَوۡفَ يُعۡطِيكَ رَبُّكَ فَتَرۡضَىٰٓ
Open ayah 93:5Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera.[1]
- Zopatsidwa zomwe adalonjezedwa apa ndi Allah, ndi zapadziko mpaka kumwamba (Akhera). Padziko lapansi adampatsa chilichonse chimene adali kuchilakalaka monga kuwaongola anthu ake, kuchilemekeza chipembedzo chake ndi kuwagonjetsa adani ake. Zonsezi Allah adamchitira mnyengo yochepa modabwitsa.
أَلَمۡ يَجِدۡكَ يَتِيمٗا فَـَٔاوَىٰ
Open ayah 93:6Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino?
وَوَجَدَكَ ضَآلّٗا فَهَدَىٰ
Open ayah 93:7Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)?[1]
- Mneneri Muhammad (s.a.w) asanapatsidwe uneneri wake ndi Allah anali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira yachiongoko.
وَوَجَدَكَ عَآئِلٗا فَأَغۡنَىٰ
Open ayah 93:8Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa?
فَأَمَّا ٱلۡيَتِيمَ فَلَا تَقۡهَرۡ
Open ayah 93:9Basi, wamasiye usamchitire nkhanza.
وَأَمَّا ٱلسَّآئِلَ فَلَا تَنۡهَرۡ
Open ayah 93:10Ndiponso wopempha usamukalipire.
وَأَمَّا بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثۡ
Open ayah 93:11Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino).