الشرح
Ash-Sharh
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
أَلَمۡ نَشۡرَحۡ لَكَ صَدۡرَكَ
Open ayah 94:1Kodi sitidachiphanule chifuwa chako (pokupatsa chiongoko ndi chikhulupiliro ndi nzeru zambiri)?
وَوَضَعۡنَا عَنكَ وِزۡرَكَ
Open ayah 94:2Ndipo takuchotsera mtolo wako (pa ntchito yolalikira pokuthandiza ndi kukufewetsera zinthu zako).
ٱلَّذِيٓ أَنقَضَ ظَهۡرَكَ
Open ayah 94:3Mtolo umene udalemetsa msana wako?
وَرَفَعۡنَا لَكَ ذِكۡرَكَ
Open ayah 94:4Ndipo takukweza kutchulidwa kwako.[1]
- Allah wakukweza kutchulidwa kwa Mtumiki Muhammad (s.a.w) pakumpatsa uneneri kumchitira zabwino kuposa aneneri ena, kuchipanga chipembedzo chake kukhala chotsiriza chosafafanizidwa ndi Mtumiki wina. Ndipo ndichopambana kuposa zipembedzo zonse zomwe zidatsogola, ndiponso ndi chomwe chingawathandize anthu onse osiyana mitundu, pa nyengo zonse ndi pamalo paliponse.
فَإِنَّ مَعَ ٱلۡعُسۡرِ يُسۡرًا
Open ayah 94:5Ndipo ndithu pali chovuta palinso zabwino (Zambiri).
إِنَّ مَعَ ٱلۡعُسۡرِ يُسۡرٗا
Open ayah 94:6Ndithu pali chovuta palinso zabwino (zambiri).
فَإِذَا فَرَغۡتَ فَٱنصَبۡ
Open ayah 94:7Basi, ukamaliza ntchito (yolalikira ndi Jihâd) limbikira kupemphera.[1]
- Tanthauzo lake nkuti: “Ukamaliza ntchito yako yolalikira kwa anthu zomwe Allah wakutuma kuti ulalikire, chita mapemphero ambiri. Umthokoze Mbuye wako pa chisomo Chake chimene wakudalitsa nacho.” Mneneri (s.a.w) adali kulimbikira kwambiri pochita mapemphero mwakuti amaima ndi kumapemphera kufikira miyendo yake kutupa. Amagwetsa mphumi pansi (sijida) mpaka kuganiziridwa kuti wafa chifukwa cha kutalika kwa nthawi yopempherayo.
وَإِلَىٰ رَبِّكَ فَٱرۡغَب
Open ayah 94:8Ndipo khala wolakalaka (zabwino zomwe zili) kwa Mbuye wako.