التين
At-Tin
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلتِّينِ وَٱلزَّيۡتُونِ
Open ayah 95:1Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri),
وَطُورِ سِينِينَ
Open ayah 95:2Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa),
وَهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ ٱلۡأَمِينِ
Open ayah 95:3Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w).
لَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ فِيٓ أَحۡسَنِ تَقۡوِيمٖ
Open ayah 95:4Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino).[1]
- M’gulu la nyama palibe yopambana kuposa munthu mkalengedwe ndi pa nzeru.
ثُمَّ رَدَدۡنَٰهُ أَسۡفَلَ سَٰفِلِينَ
Open ayah 95:5Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi.[1]
- Munthu ali ndi makhalidwe awiri: Ngati agwiritsa ntchito nzeru zake amaongoka ndipo amaiposa nyama ili yonse. Koma ngati sagwiritsa ntchito nzeru zake amasokera ndi kukhala wapansi kuposa nyama zonse.
إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونٖ
Open ayah 95:6Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha.
فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعۡدُ بِٱلدِّينِ
Open ayah 95:7Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)?[1]
- (Ndime 7-8) Allah akuuza munthu kuti: Pambuyo podziwa kuti Allah ndi Yemwe adapanga zimenezo, ndi chiyani nanga chikumukaikitsa za tsiku la chiweruziro?
أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَحۡكَمِ ٱلۡحَٰكِمِينَ
Open ayah 95:8Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse?