العلق

Al-Alaq

The Clot · Surah 96 · Ayahs: 19 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. ٱقۡرَأۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلَّذِي خَلَقَ

    Open ayah 96:1

    Werenga! (Iwe Mneneri (s.a.w), zomwe zikuvumbulutsidwa) mdzina la Mbuye wako Yemwe adalenga (zolengedwa zonse).[1]

    1. Tanena kale mndemanga 7 yamu surat - Dhuha kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) asadapatsidwe uneneri wake ndi Allah adali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi Mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira ya chiongoko. Choncho tsiku lina pamene adali ku phanga la Hiraa, pafupi ndi Makka ali mkati mopemphera, Mngelo adamuonekera mwadzidzidzi nati: “Iwe Muhammad! Ine ndine Jiburil (Gabrie!) ndipo iwe ndiwe Mtumiki wa Allah kwa zolengedwa zonse!” Pambuyo pake adamuuza kuti: “werenga!” Mneneri adayankha: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Jiburil uja adamgwira ndi kumpana mwamphamvu mpaka adavutika kwambiri. Adamsiyanso ndi kumuuza: “werenga!” Mneneri adayankha monga adamuyankhira poyamba mpaka kadakwana katatu akumuchita zokhazokhazo. Kenaka adamuwerengera ma Ayah kuchokera 1 mpaka 5. Ma Ayah amenewa ndiwo oyamba kuvumbulutsidwa m’Qur’an.
  2. خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِنۡ عَلَقٍ

    Open ayah 96:2

    Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana.[1]

    1. Madzi ambewu ya munthu, pambuyo pokhazikika mchiberekero kwa masiku makumi anayi, amatembenuka ndikukhala magazi. Ili ndilo tanthauzo la Ayah imeneyi.
  3. ٱقۡرَأۡ وَرَبُّكَ ٱلۡأَكۡرَمُ

    Open ayah 96:3

    Werenga! Ndipo Mbuye wako ndi Wopereka kwambiri.[1]

    1. Ayah 3 ndi 5 Mtumiki (s.a.w) akuyankhidwa pa kunena kwake kwa kuti: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Choncho Allah akumuuza kuti Iye ndi Mfulu weniweni, ndi Yemwe adawaphunzitsa anthu kulemba ndi cholembera ndi zonse zomwe sadali kuzidziwa. Kwa ufulu Wake wochuluka ndi mphamvu Zake pa chilichonse, sichovuta kwa Iye (Allah) kumphunzitsa Mtumiki Wake kuwerenga molakatula.
  4. ٱلَّذِي عَلَّمَ بِٱلۡقَلَمِ

    Open ayah 96:4

    Yemwe waphunzitsa (munthu kulemba) ndi cholembera.

  5. عَلَّمَ ٱلۡإِنسَٰنَ مَا لَمۡ يَعۡلَمۡ

    Open ayah 96:5

    Waphunzitsa munthu zinthu (zambiri) zomwe (iye) sadali kuzidziwa.

  6. كَلَّآ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَيَطۡغَىٰٓ

    Open ayah 96:6

    Zoona ndithu koma munthu akupyola malire (podzikweza).

  7. أَن رَّءَاهُ ٱسۡتَغۡنَىٰٓ

    Open ayah 96:7

    Chifukwa chodziona kuti walemera.

  8. إِنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ ٱلرُّجۡعَىٰٓ

    Open ayah 96:8

    Palibe chikaiko, (iwe Mneneri (s.a.w) kobwerera (onse) nkwa Mbuye wako basi; (adzawaukitsa).[1]

    1. Tanthauzo lake nkuti musanyengedwe ndi chumacho chifukwa chakuti, popanda chikaiko, mubwerera kwa Mbuye wanu ndipo chumacho sichidzakuthandizani chilichonse pa maso Pake.
  9. أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يَنۡهَىٰ

    Open ayah 96:9

    Kodi wamuona yemwe akuletsa,

  10. عَبۡدًا إِذَا صَلَّىٰٓ 

    Open ayah 96:10

    Kapolo (wa Allah) akamapemphera?

  11. أَرَءَيۡتَ إِن كَانَ عَلَى ٱلۡهُدَىٰٓ

    Open ayah 96:11

    Tandiuza ngati ali pachiongoko?

  12. أَوۡ أَمَرَ بِٱلتَّقۡوَىٰٓ

    Open ayah 96:12

    Kapena kuti akulamulira zoopa Allah?

  13. أَرَءَيۡتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰٓ

    Open ayah 96:13

    Tandiuza (za woletsayo) ngati akutsutsa (zimene wadza nazo Mneneri) ndikunyoza (chikhulupiliro ndi ntchito yabwino)?

  14. أَلَمۡ يَعۡلَم بِأَنَّ ٱللَّهَ يَرَىٰ

    Open ayah 96:14

    Kodi sakudziwa kuti Allah akuona (machitidwe ake. Ndipo adzamlipira)?

  15. كَلَّا لَئِن لَّمۡ يَنتَهِ لَنَسۡفَعَۢا بِٱلنَّاصِيَةِ

    Open ayah 96:15

    Ayi ndithu ngati sasiya timukoka tsitsi lapatsumba (tiligwira mwamphamvu tsumba lake ndikukamponya ku Moto).

  16. نَاصِيَةٖ كَٰذِبَةٍ خَاطِئَةٖ

    Open ayah 96:16

    Tsumba labodza (ndiponso) lamachimo.

  17. فَلۡيَدۡعُ نَادِيَهُۥ

    Open ayah 96:17

    Basi aliitane gulu lakelo, (la amene amakhala nawo pabwalo kuti amthandize pano pa dziko kapena tsiku lachimaliziro),

  18. سَنَدۡعُ ٱلزَّبَانِيَةَ

    Open ayah 96:18

    Nafe tiitana azabaniya (angelo a ku Moto).

  19. كَلَّا لَا تُطِعۡهُ وَٱسۡجُدۡۤ وَٱقۡتَرِب۩

    Open ayah 96:19

    Ayi ndithu usamumvere (pa zimene akukuletsazo); koma gwetsa nkhope yako pansi, ndipo dziyandikitse kwa Mbuye wako.