الغاشية

Al-Ghaashiya

The Overwhelming · Surah 88 · Ayahs: 26 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡغَٰشِيَةِ

    Open ayah 88:1

    Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)?

  2. وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٍ خَٰشِعَةٌ

    Open ayah 88:2

    Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,[1]

    1. Tanthauzo la nkhope apa ndi eni nkhopezo. Amene akunenedwa pamenepa ndi anthu oipa. Allah watchula nkhope chifukwa ndi chiwalo cholemekezeka pa chilengedwe cha munthu ndipo ndi pamene pali chithunzi chake.
  3. عَامِلَةٞ نَّاصِبَةٞ

    Open ayah 88:3

    Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri.

  4. تَصۡلَىٰ نَارًا حَامِيَةٗ

    Open ayah 88:4

    Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri.

  5. تُسۡقَىٰ مِنۡ عَيۡنٍ ءَانِيَةٖ

    Open ayah 88:5

    Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi.

  6. لَّيۡسَ لَهُمۡ طَعَامٌ إِلَّا مِن ضَرِيعٖ

    Open ayah 88:6

    Sadzakhala ndichakudya koma minga.

  7. لَّا يُسۡمِنُ وَلَا يُغۡنِي مِن جُوعٖ

    Open ayah 88:7

    Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala.

  8. وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ نَّاعِمَةٞ

    Open ayah 88:8

    Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala.

  9. لِّسَعۡيِهَا رَاضِيَةٞ

    Open ayah 88:9

    Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).[1]

    1. Tanthauzo la “kukondweretsedwa ndi zochita zawo’’ ndikuti anthu abwino adzakondwera ndi ntchito zawo zabwino zomwe adazichita pa dziko lapansi akadzakhala ndi malipiro abwino pa tsiku lachimaliziro.
  10. فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ 

    Open ayah 88:10

    M’minda ya pamwamba (Jannah).

  11. لَّا تَسۡمَعُ فِيهَا لَٰغِيَةٗ

    Open ayah 88:11

    Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula).

  12. فِيهَا عَيۡنٞ جَارِيَةٞ

    Open ayah 88:12

    Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).[1]

    1. (Ndime 12-16) Zosangalatsa zenizeni za tsiku lachimaliziro monga momwe adatiuzira Mneneri (s.a.w) kuti ku Jannah kuli zinthu zimene diso silidapenyepo ngakhale khutu silidamvepo ndipo sizidapitepo m’maganizo a munthu. Choncho zokondweretsa izi zimene Allah watiuza apa akungofanizira ndi zinthu zomwe tikuzidziwa.
  13. فِيهَا سُرُرٞ مَّرۡفُوعَةٞ

    Open ayah 88:13

    Mmenemo muli makama a pamwamba,

  14. وَأَكۡوَابٞ مَّوۡضُوعَةٞ

    Open ayah 88:14

    Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo),

  15. وَنَمَارِقُ مَصۡفُوفَةٞ

    Open ayah 88:15

    Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere

  16. وَزَرَابِيُّ مَبۡثُوثَةٌ

    Open ayah 88:16

    Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse.

  17. أَفَلَا يَنظُرُونَ إِلَى ٱلۡإِبِلِ كَيۡفَ خُلِقَتۡ

    Open ayah 88:17

    Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?[1]

    1. (Ndime 17-20) Allah akuwauza kuti ayang’ane chilengedwe cha ngamira, thambo, mapiri ndi nthaka. Pambuyo pake alingalire, aone kuti amene adalenga zimenezo ngotha kuchita chilichonse monga kuukitsa anthu m’manda. Cholinga cha Allah potchula zinthu zimenezi, ngakhale kuti malangizowa nga munthu aliyense, koma adali kuwauza akafiri a pa Makka amene zinthu zimenezi maso awo ankaziona nthawi ndi nthawi.
  18. وَإِلَى ٱلسَّمَآءِ كَيۡفَ رُفِعَتۡ

    Open ayah 88:18

    Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?

  19. وَإِلَى ٱلۡجِبَالِ كَيۡفَ نُصِبَتۡ

    Open ayah 88:19

    Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)?

  20. وَإِلَى ٱلۡأَرۡضِ كَيۡفَ سُطِحَتۡ 

    Open ayah 88:20

    Ndi nthaka momwe idayalidwira.

  21. فَذَكِّرۡ إِنَّمَآ أَنتَ مُذَكِّرٞ

    Open ayah 88:21

    Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi.

  22. لَّسۡتَ عَلَيۡهِم بِمُصَيۡطِرٍ

    Open ayah 88:22

    Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).[1]

    1. Ayah iyi ikukwana kuwatsutsa adani a Chisilamu amene akunena kuti, “chipembedzo cha Chisilamu chidafala ndi lupanga.” Kutanthauza kuti ankawakakamiza anthu kuti achivomere chipembedzochi. Sichodabwitsa kuona adani a Chisilamu akuchinyoza chipembedzochi, koma chodabwitsa nchakuti mawu onamawa nkumatulukanso mkamwa mwa anthu omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu. Nzoona alipo ena mwa anthu odziwa za chipembedzo (ma Ulama) amene adanena kuti chipembedzo cha Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga. Koma simonga momwe akutanthauzilira adani amene sadziwa za Chisilamu nkumangotsatira mabodza a akuluakulu awo. Cholinga cha ma Ulama ponena kuti “Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga” kumeneko ndi kudziteteza kwa adani omwe adafuna kuchithetsa, osati kuwakakamiza anthu kulowa mchipembedzo. Kukakamiza anthu kulowa mChisilamu nkosaloledwa. Amene akudziwa mbiri ya Chisilamu, akudziwa kuti Asilamu sadalamulidwe kuchita Jihâd mpaka pamene akafiri adali kuwazunza. Pali nkhani zambiri za Maswahaba (otsatira Mneneri) (s.a.w) ku Madina pamene adafuna kuwakakamiza ana awo kulowa m’Chisilamu, koma Mneneri adawakaniza kutero. Basi, munthu amene akunena zoterezo mwina akutero pa chifukwa chosadziwa za chipembedzo cha Chisilamu, mwinanso nkukhala misala basi.
  23. إِلَّا مَن تَوَلَّىٰ وَكَفَرَ

    Open ayah 88:23

    Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako),

  24. فَيُعَذِّبُهُ ٱللَّهُ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَكۡبَرَ

    Open ayah 88:24

    Allah amulanga chilango chachikulu zedi.

  25. إِنَّ إِلَيۡنَآ إِيَابَهُمۡ

    Open ayah 88:25

    Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi.

  26. ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا حِسَابَهُم

    Open ayah 88:26

    Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife.