الصف
As-Saff
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Open ayah 61:1Zonse zakumwamba ndi zapansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe osayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Yekha Ngopambana pa chilichonse; Wanzeru zakuya.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِمَ تَقُولُونَ مَا لَا تَفۡعَلُونَ
Open ayah 61:2E inu amene mwakhulupirira! Bwanji mukunena zimene simuchita?[1]
- (Ndime 2-3) Khalidwe la munthu limene limakwiyitsa Allah kwambiri ndiko kunena zokoma chikhalirecho zochita zili zoipa. Amawanyenga anthu ndi mawu otsekemera koma zochita zake ndizachinyengo zokhazokha. Munthu wa makhalidwe otere, malipiro ake ndi kulowa ku nthukutira ya Moto. Choncho zochita zanu zifanane ndi zimene mukuyankhula. Apeweni makhalidwe achiphamaso.
كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ أَن تَقُولُواْ مَا لَا تَفۡعَلُونَ
Open ayah 61:3Nzomuipira zedi Allah kunena zinthu zimene simuchita.
إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلَّذِينَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِهِۦ صَفّٗا كَأَنَّهُم بُنۡيَٰنٞ مَّرۡصُوصٞ
Open ayah 61:4Ndithu Allah amakonda amene akumenya nkhondo pa njira Yake (yofalitsa chipembedzo Chake), ali pa mzere (umodzi) uku ali monga chomanga, chomangika mwamphamvu.[1]
- Allah akufuna kuti Asilamu akhale dzanja limodzi pofalitsa Chisilamu, agwire ntchito yokomera gulu lonse mothangatana.
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ لِمَ تُؤۡذُونَنِي وَقَد تَّعۡلَمُونَ أَنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡۖ فَلَمَّا زَاغُوٓاْ أَزَاغَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمۡۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ
Open ayah 61:5Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake.
وَإِذۡ قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُم مُّصَدِّقٗا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيَّ مِنَ ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَمُبَشِّرَۢا بِرَسُولٖ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِي ٱسۡمُهُۥٓ أَحۡمَدُۖ فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٞ مُّبِينٞ
Open ayah 61:6Ndiponso (kumbuka) pamene adanena (Mtumiki) Isa (Yesu) mwana wa Mariya, kuti: “E inu ana a Israelil! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu, amene ndikuchitira umboni zimene zidadza patsogolo panga za buku la Chipangano chakale (Torah) ndipo ndikuuzani nkhani yabwino ya mthenga amene adzadze pambuyo panga, dzina lake Ahamad (Muhammad{s.a.w}).” Koma pamene adawadzera (Mtumiki wolonjedzedwayo) ndi zisonyezo zowonekera poyera (kuti iye ndi Mtumiki wa Allah). Adati: “Awa ndi matsenga owonekera.”
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُوَ يُدۡعَىٰٓ إِلَى ٱلۡإِسۡلَٰمِۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Open ayah 61:7Kodi ndani oipitsitsa kuposa yemwe wapekera Allah bodza, pomwe iye akuitanidwira ku Chisilamu (chipembedzo choona ndi chabwino)? Ndipo Allah saongola anthu achinyengo.
يُرِيدُونَ لِيُطۡفِـُٔواْ نُورَ ٱللَّهِ بِأَفۡوَٰهِهِمۡ وَٱللَّهُ مُتِمُّ نُورِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Open ayah 61:8Akufuna kuti azimitse dangalira la Allah ndi pakamwa pawo ndipo Allah Ngokwaniritsa dangalira Lake ngakhale ziwaipire osakhulupirira.[1]
- (Ndime 8-9) Allah akulonjeza kuti Chisilamu chidzapambana zipembedzo zonse ngakhale osakhulupilira akuchithira nkhondo.
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ رَسُولَهُۥ بِٱلۡهُدَىٰ وَدِينِ ٱلۡحَقِّ لِيُظۡهِرَهُۥ عَلَى ٱلدِّينِ كُلِّهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُشۡرِكُونَ
Open ayah 61:9Iye ndi amene adatuma Mtumiki Wake (Muhammad{s.a.w}) ndi chiongoko ndi chipembedzo choona, kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse, ngakhale kuti ophatikiza Allah ndi mafano zikuwaipira.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ تِجَٰرَةٖ تُنجِيكُم مِّنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ
Open ayah 61:10E inu amene mwakhulupirira! Kodi ndikudziwitseni malonda amene angakupulumutseni ku chilango chowawa?
تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِكُمۡ وَأَنفُسِكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Open ayah 61:11Muzimkhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo muzichita Jihâd pa njira ya Allah ndi chuma chanu, ndi matupi anu. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati muli odziwa.
يَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡ وَيُدۡخِلۡكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَمَسَٰكِنَ طَيِّبَةٗ فِي جَنَّٰتِ عَدۡنٖۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Open ayah 61:12Akukhululukirani machimo anu ndipo akulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, ndiponso (adzakupatsani) mokhala mwabwino ku minda yamuyaya. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
وَأُخۡرَىٰ تُحِبُّونَهَاۖ نَصۡرٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَتۡحٞ قَرِيبٞۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Open ayah 61:13Ndizina zomwe mukuzifuna. Thandizo (lonse) lichokera kwa Allah ndi kugonjetsa kumene kuli pafupi; ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُوٓاْ أَنصَارَ ٱللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ لِلۡحَوَارِيِّـۧنَ مَنۡ أَنصَارِيٓ إِلَى ٱللَّهِۖ قَالَ ٱلۡحَوَارِيُّونَ نَحۡنُ أَنصَارُ ٱللَّهِۖ فَـَٔامَنَت طَّآئِفَةٞ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَكَفَرَت طَّآئِفَةٞۖ فَأَيَّدۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ عَلَىٰ عَدُوِّهِمۡ فَأَصۡبَحُواْ ظَٰهِرِينَ
Open ayah 61:14E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana.