الهمزة

Al-Humaza

The Traducer · Surah 104 · Ayahs: 9 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. وَيۡلٞ لِّكُلِّ هُمَزَةٖ لُّمَزَةٍ

    Open ayah 104:1

    Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime).[1]

    1. Kujeda kwa mtundu uliwonse ndi koipa. Anthu ambiri amaganiza kuti kujeda ndi chinthu chochepa, saona kuti ndi chinthu choipa, pomwe Qur’an ikuletsa kwatunthu mpaka mwakuti imamufanizira munthu wojeda ngati munthu yemwe amadya minofu ya mnzake wakufa. Mu Ayah imeneyi, Allah wanena kuti “Wayilun” lomwe tanthauzo lake ndi “Kuonongeka koopsa.” Choncho nkofunika kwa munthu aliyense kupewa khalidwe lojeda.
  2. ٱلَّذِي جَمَعَ مَالٗا وَعَدَّدَهُۥ

    Open ayah 104:2

    Yemwe wasonkhanitsa chuma ndikumachiwerengera.[1]

    1. Mmenemo ndi momwe alili munthu wa umbombo, kukoma kwa chuma kwa iye, ndikuchisonkhanitsa ndikumachiwerengera akakhala ndi danga; sikuti akufuna kudziwa kuchuluka kwake koma kungokondweretsedwa ndikuchiwerengako. Saganizira zimene zingamuthandize iye mwini kapena kuthandiza anzake. Chuma ntchito yake ndikuti chimthandize mwini chumacho pa zinthu zabwino zosiyanasiyana pamodzi ndi anzake, osati kungochikhazika ndikumangochiwerengera mokhumbiza ena.
  3. يَحۡسَبُ أَنَّ مَالَهُۥٓ أَخۡلَدَهُۥ

    Open ayah 104:3

    Akuganiza kuti chuma chakecho chimkhazika (pa dziko) nthawi yaitali (ndikumteteza ku zimene sakuzifuna).

  4. كَلَّاۖ لَيُنۢبَذَنَّ فِي ٱلۡحُطَمَةِ

    Open ayah 104:4

    Sichoncho! (Asiye maganizo amenewo) ndithudi, akaponyedwa ku Moto woononga (chifukwa cha kuipa kwa zochita zake).

  5. وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡحُطَمَةُ

    Open ayah 104:5

    Ndi chiyani chingakudziwitse za Moto woonongawu?

  6. نَارُ ٱللَّهِ ٱلۡمُوقَدَةُ

    Open ayah 104:6

    Umenewu ndi Moto wa Allah woyaka (nthawi zonse, woononga chilichonse choponyedwa mmenemo).

  7. ٱلَّتِي تَطَّلِعُ عَلَى ٱلۡأَفۡـِٔدَةِ

    Open ayah 104:7

    Umene umakwera mpaka ku mtima.[1]

    1. Moto umenewu, sukapsereza kunja kokha, ukapsereza mpaka ndi mu mtima momwe.
  8. إِنَّهَا عَلَيۡهِم مُّؤۡصَدَةٞ

    Open ayah 104:8

    Ndithu motowo ukawazinga (ndi kuwatsekera makomo).

  9. فِي عَمَدٖ مُّمَدَّدَةِۭ

    Open ayah 104:9

    Munsanamira za zitalizitali (kotero kuti sakatha kugwedezeka mmenemo kapena kupulumuka).