التكاثر
At-Takaathur
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
أَلۡهَىٰكُمُ ٱلتَّكَاثُرُ
Open ayah 102:1Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana).[1]
- (Ndime 1-2) Ndi chizolowezi cha anthu kupikisana pa chuma ndi pa ana. Choncho, mma Ayah awa: 1-2 Allah akuwauza: Kupikisana kwawo kochuluka, kukonda za m’dziko kwambiri, kwaiwalitsa kutumikira Allah mpaka imfa kuwapeza.
حَتَّىٰ زُرۡتُمُ ٱلۡمَقَابِرَ
Open ayah 102:2Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikukalowa m’manda).
كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Open ayah 102:3Sichoncho! Mudziwa posachedwapa.[1]
- Tanthauzo lake ndilakuti, pamene idzakufikirani imfa mudzadziwa kuti mudali kutaya nthawi ndi zinthu zopanda pake.
ثُمَّ كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Open ayah 102:4Ndiponso sichoncho! Mudziwa posachedwapa.
كَلَّا لَوۡ تَعۡلَمُونَ عِلۡمَ ٱلۡيَقِينِ
Open ayah 102:5Sichoncho! mukadakhala mukudziwa, kudziwa kwachitsimikizo (sibwenzi mukutangwanika ndi za mdziko).
لَتَرَوُنَّ ٱلۡجَحِيمَ
Open ayah 102:6Ndithudi mudzauona Moto.
ثُمَّ لَتَرَوُنَّهَا عَيۡنَ ٱلۡيَقِينِ
Open ayah 102:7Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo.
ثُمَّ لَتُسۡـَٔلُنَّ يَوۡمَئِذٍ عَنِ ٱلنَّعِيمِ
Open ayah 102:8Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe munapatsidwa).[1]
- Munthu aliyense ndi chilichonse chimene ali nacho ndi mphatso yochokera kwa Allah. Choncho, pa tsiku lachimaliziro adzafunsidwa za momwe adagwiritsira ntchito mphatso zimenezi, kaya m’njira yoipa kapena yabwino.