القارعة
Al-Qaari'a
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
ٱلۡقَارِعَةُ
Open ayah 101:1Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)!
مَا ٱلۡقَارِعَةُ
Open ayah 101:2Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani?
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡقَارِعَةُ
Open ayah 101:3Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)?
يَوۡمَ يَكُونُ ٱلنَّاسُ كَٱلۡفَرَاشِ ٱلۡمَبۡثُوثِ
Open ayah 101:4Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika.[1]
- Apa, pakutanthauza kuti anthu adzakhala ali balalabalala ngati agulugufe ndipo azidzangodziponya uku ndi uku, osadziwa kopita. Imeneyo ndi nthawi yotuluka m’manda.
وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ ٱلۡمَنفُوشِ
Open ayah 101:5Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga).
فَأَمَّا مَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ
Open ayah 101:6Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa).[1]
- Tsiku limenelo ntchito zonse zabwino ndi zoipa zidzayesedwa ndi muyeso wa Allah, koma sitidadziwitsidwe kuti muyeso umenewo udzakhala wotani udzayesa zonse zazikulu ndi zazing’ono zomwe mpaka za mumtima.
فَهُوَ فِي عِيشَةٖ رَّاضِيَةٖ
Open ayah 101:7Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro).
وَأَمَّا مَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ
Open ayah 101:8Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa),
فَأُمُّهُۥ هَاوِيَةٞ
Open ayah 101:9Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya.
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا هِيَهۡ
Open ayah 101:10Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya?
نَارٌ حَامِيَةُۢ
Open ayah 101:11Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali!