العاديات
Al-Aadiyaat
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلۡعَٰدِيَٰتِ ضَبۡحٗا
Open ayah 100:1Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma,
فَٱلۡمُورِيَٰتِ قَدۡحٗا
Open ayah 100:2Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala),
فَٱلۡمُغِيرَٰتِ صُبۡحٗا
Open ayah 100:3Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke),
فَأَثَرۡنَ بِهِۦ نَقۡعٗا
Open ayah 100:4Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo,
فَوَسَطۡنَ بِهِۦ جَمۡعًا
Open ayah 100:5Ndikulowelera mkatikati mwa adani.
إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لِرَبِّهِۦ لَكَنُودٞ
Open ayah 100:6Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).[1]
- Tanthauzo la “kukanira Mbuye wake” ndi kuukanira mtendere Wake. Ndipo kukanira mtendere ndiko kusagwiritsira ntchito mtenderewo mnjira zabwino, monga m’mapemphero ndi zina zotero.
وَإِنَّهُۥ عَلَىٰ ذَٰلِكَ لَشَهِيدٞ
Open ayah 100:7Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake).
وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلۡخَيۡرِ لَشَدِيدٌ
Open ayah 100:8Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo).[1]
- Kapena kuti ali wofunitsitsa chuma kwambiri; kumeneko ndikumangoti mtima dyokodyoko pachuma. Ukachipeza ndikumachichitira umbombo ndipo ndikumaganiza kuti chumacho nchopambana china chilichonse.
۞أَفَلَا يَعۡلَمُ إِذَا بُعۡثِرَ مَا فِي ٱلۡقُبُورِ
Open ayah 100:9Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda,
وَحُصِّلَ مَا فِي ٱلصُّدُورِ
Open ayah 100:10Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima?
إِنَّ رَبَّهُم بِهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّخَبِيرُۢ
Open ayah 100:11Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).[1]
- “Kuwadziwa kwambiri,” kukutanthauza kuti Iye ngodziwa zazikuluzikulu ndi zazing’onozing’ono zoonekera poyera ndi zobisika. Tsiku limenelo adzawalipira chilichonse chimene adachita.