الناس

An-Naas

Mankind · Surah 114 · Ayahs: 6 · Meccan

Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

  1. قُلۡ أَعُوذُ بِرَبِّ ٱلنَّاسِ

    Open ayah 114:1

    Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (Yemwe akulinganiza zinthu zawo).[1]

    1. Allah pokhala Mlengi wa anthu ndi amenenso amawalera kuyambira pamene ali m’mimba mpaka kumapeto a moyo wawo pano pa dziko. Kuwaleraku kuli muuzimu, mthupi, mu mpweya, ndi pa chilichonse chofunika pa moyo wawo. Kuonjezera pa zimenezi adawapatsa nzeru ndi kuwasonyeza njira zabwino za dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuzitsata njirazo. Adawasonyezanso njira zoipa za dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuti azipewe njira zoipazo.
  2. مَلِكِ ٱلنَّاسِ

    Open ayah 114:2

    Mfumu ya anthu ( Imene iri ndi mphamvu yochita chirichonse pa iwo).

  3. إِلَٰهِ ٱلنَّاسِ

    Open ayah 114:3

    Wopembedzedwa wa anthu.

  4. مِن شَرِّ ٱلۡوَسۡوَاسِ ٱلۡخَنَّاسِ

    Open ayah 114:4

    Kuzoipa za mnong’onezi (yemwe amathira unong’onezi wake m’mitimaya anthu) yemwenso amabisala (posiya unong’onezi wake ngati mwini mtimawo atankumbukira Allah).[1]

    1. Mnong’onezi wa zoipa amene amabisala ndiye Satana, yemwe ntchito yake ndi kunong’oneza zoipa m’mitima ya anthu pofuna kuwasokeretsa ndi kuwaiwalitsa Allah. Koma akakumana ndi munthu wa chikhulupiliro cha mphamvu kapena yemwe amatamanda kwambiri Mbuye wake Allah, Satanayo amalephera ndipo amathawa; kubwerera m’mbuyo.
  5. ٱلَّذِي يُوَسۡوِسُ فِي صُدُورِ ٱلنَّاسِ

    Open ayah 114:5

    Yemwe amanong’oneza mzifuwa za anthu.

  6. مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ

    Open ayah 114:6

    Wochokera m’ziwanda ndi mwa anthu.”[1]

    1. Mchiyankhulo cha Chiarabu aliyense woipitsitsa amatchedwa “shaitan” satana, munthu kapena chiwanda. Satana wa muwanthu ndiwoipitsitsa kwambiri kwa anthu kuposa wa m’ziwanda.