الماعون
Al-Maa'un
Translation: Chewa - Khaled Ibrahim Betala · Open the surah
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يُكَذِّبُ بِٱلدِّينِ
Open ayah 107:1Kodi wamuona yemwe akutsutsa za mphoto (ndi chiwerengero cha tsiku lachimaliziro)?[1]
- Sura imeneyi ikufotokoza m’mene alili makhalidwe a anthu ambiri, ngakhale amene amadzitcha kuti ndi Asilamu. Aliyense amene ali ndi makhalidwe otere ndiye kuti sakhulupilira za tsiku la chiweruziro. Akadakhala kuti akukhulupilira za tsikuli, sibwenzi akusiya kuwachitira za chifundo osauka ndi amasiye. Sapereka chithandizo ngakhale kulimbikitsa ena ngati iye alibe.
فَذَٰلِكَ ٱلَّذِي يَدُعُّ ٱلۡيَتِيمَ
Open ayah 107:2Iye ndi yemwe akukankha wamasiye (mwankhanza).
وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ
Open ayah 107:3Ndipo salimbikitsa (ena pamodzi ndi iye mwini) kudyetsa osauka.
فَوَيۡلٞ لِّلۡمُصَلِّينَ
Open ayah 107:4Choncho kuonongeka kuli pa ena mwa opemphera swala (amene ali ndi mbiri izi);
ٱلَّذِينَ هُمۡ عَن صَلَاتِهِمۡ سَاهُونَ
Open ayah 107:5Omwe amachitira mphwayi mapemphero awo.[1]
- Kuchitira mphwayi mapemphero (Swala), kumeneku ndiko kupemphera modukizadukiza. Tsiku lina nkupempherapo, tsiku lina ayi. Kapenanso kupemphera modzionetsera kwa anthu (riyaa).
ٱلَّذِينَ هُمۡ يُرَآءُونَ
Open ayah 107:6Amenenso (akamachita mapemphero awo) amadzionetsera (kwa anthu mwachipha maso kuti apeze ulemelero ndi kutamandidwa mmitima mwa anthu).[1]
- Riyaa ndiko kuchita ntchito yabwino ndicholinga choonetsa anthu, kuti akuone kuti ndiwe wabwino, mwina kuti ukhale wokondedwa ndi anthu. Kapenanso kuti upeze za m’matumba mwawo. Amenewa ndi machitidwe a “Shiriki” (kum’phatikiza Allah ndi zolengedwa Zake pa mapemphero) ndiponso ndi njira yobera anthu.
وَيَمۡنَعُونَ ٱلۡمَاعُونَ
Open ayah 107:7Ndipo amamana ziwiya (zawo posabwereka anzawo zinthu zofunika pa moyo wa aliyense monga nkhwangwa, mpeni, mtondo ndi zina zotere).